Kodi Mwapemphapo Wina Aliyense Kuti Muziphunzira Naye Baibulo?
1 Buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, patsamba 98 ndi 99, limatithandiza kuzindikira mwayi umene tili nawo wothandiza ena mwauzimu pochititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Tsamba 99 lili ndi malangizo akuti: “Ngati n’kotheka, khalani ndi cholinga choti muzichititsa phunziro la Baibulo la panyumba nthawi zonse, ngakhale limodzi.” Tonsefe tingayesetse kukwanitsa cholinga chabwino chimenechi mwa kupempha anthu, tikapeza mpata uliwonse, kuti tiziphunzira nawo Baibulo. Anthu ambiri amadziwa choonadi chifukwa chophunzira Baibulo. (1 Tim. 2:3, 4) Kodi phunziro la Baibulo lapanyumba tingaliyambe bwanji? Ndi anthu ochepa kwambiri amene amatipempha kuti tiphunzire nawo Baibulo. Nthawi zambiri inuyo ndiye amene muyenera kuyamba kuwapempha kuti muziphunzira nawo.
2 N’chiyani Chomwe Tingachite? Choyamba, munthu aliyense amene tam’gawira mabuku athu tizimuona kuti akufunika ulendo wobwereza. Choncho, m’pofunika kusunga bwino zimene timalemba tikakhala mu ulaliki wa nyumba ndi nyumba. Pamene tikupanga maulendo obwereza, cholinga chathu chizikhala kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Ngakhale pamene tili mu ulaliki wa khomo ndi khomo, bwanji osawapempha eninyumbawo kuti muwaonetse mmene timachitira phunziro la Baibulo lapanyumba? Ambiri amene tsopano ali abale ndi alongo, anayamba kuphunzira Baibulo mwa njira imeneyi.
3 Bwanji nanga za anzanu ndi achibale anu? Kodi n’kutheka kuti ena mwa iwo angakonde kuphunzira ndi inuyo koposa kuphunzira ndi munthu wachilendo? Kodi munawapemphapo za zimenezi? Ndiponso, m’mipingo yambiri chiwerengero cha anthu ofika pa misonkhano chikuwonjezereka mowirikiza. Kodi anthu enawa ndiwo ati? Kodi onsewa akuchita phunziro la Baibulo lapanyumba? Ngati mukuganiza kuti ena sakutero, bwanji osawapempha? Maphunziro ambiri amene akuchita bwino anayambira pa misonkhano ya mpingo. Mwina mu mpingo wanu muli amene ali ndi maphunziro a Baibulo ambiri ndiponso ali ndi ena amene akuyembekeza kuti ayambe kuphunzira nawo koma sangawakwanitse onsewa. Ofalitsa ngati amenewa angakonde kukuthandizani kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba. Bwanji osawapempha? Mungapemphe aliyense mu mpingo amene akuoneka kuti akuchita bwino pa ntchito imeneyi.
4 Njira inanso yofunika yoyambitsira maphunziro a Baibulo ndiyo kugwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana paulendo woyamba womwewo. Patsamba 13, pamutu wakuti “Phunziro la Baibulo Lapanyumba,” buku la Kukambitsirana lili ndi ndime ziwiri za mawu olunjika opemphera mwininyumba kuti muyambe naye phunziro. Mawu amenewo amadziwitsa eninyumba kuti cholinga chathu powafikira ndicho kuwapempha kuti tiyambe nawo phunziro la Baibulo lapanyumba. Kaya tigwiritse ntchito ulaliki wotani, tiyenera kuwapempha kuti tiwasonyeze mmene timaphunzirira. Eninyumba ambiri ali nawo kale ena mwa mabuku athu. Tingagwiritse ntchito omwewo. Ngati munthu wakana buku, tingagwiritse ntchito thirakiti kuyambitsira phunziro. Izi zingachitike ngati kungakhale bwino kutero ndipo mwininyumbayo walola.
5 Mungauzenso woyang’anira phunziro la buku kuti akhale akudziwa kuti mukufuna kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Angakuthandizeni bwino chifukwa nthawi zina ofalitsa ndiponso woyang’anira dera amapereka anthu ofuna kuphunzira kwa iye. Bwanji osafunsa? Komano, ngati mwapatsidwa dzina la munthu wachidwi, mufunikira kukumbukira kuti umenewo ndi udindo waukulu zedi. Mokulira, mwayi wakuti munthuyo adzakhale ndi moyo wosatha waikidwa m’manja mwanu. Limbikirani kukulitsa chidwi chomwe angakhale nacho.
6 Ngati pakali pano simukuchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba, koma mukufunitsitsa kutero, pali njira zinanso zoti mutsatire. Bwanji osauza Yehova nkhawa zanu m’pemphero? Ndiponso, pemphani nzeru kwa woyang’anira utumiki. Woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo, kapena wofalitsa wina aliyense waluso angakuthandizeni. Ofalitsa ena akhoza kuyambitsa maphunziro mwa kungopempha anthu achidwi kuti awerengere nawo limodzi bulosha la Mulungu Amafunanji.
7 Palibe munthu amene amabadwa ali wophunzira kale, tonse timachita kuphunzitsidwa. Choncho, munthu sangapitedi patsogolo mwauzimu ngati wina sakuchita naye phunziro la Baibulo lapanyumba. Popeza timayamikira phindu lauzimu limene mabuku athu ali nalo, tifunika kufalitsa kwambiri bulosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso. Pamene tikutero, tizikumbukira mawu olimbikitsa a mwamuna wina wanzeru akuti: “Mamawa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.”—Mla. 11:6.