PHUNZIRO 48
Njira Yokambirana
TILI oyamikira kwambiri chifukwa cha mmene Mawu a Mulungu asinthira miyoyo yathu, ndipo tikufuna kuti enanso apeze mapindu amene tili nawo. Ndiponso timadziŵa kuti, kuti anthu akapeze madalitso m’tsogolo, zimadalira kulabadira kwawo choonadi. (Mat. 7:13, 14; Yoh. 12:48) Timafunitsitsa kuti iwo alandire choonadi. Komabe, kufunitsitsa kwathuko limodzi ndi changu chathu ziyenera kutsagana ndi kuzindikira kumeneko kuti tipindule anthu ambiri.
Mfundo ya choonadi yachindunji yoonetsa kuti chikhulupiriro chimene munthu amachikonda n’chabodza, ngakhale mutapereka Malemba ambiri oikira umboni, kaŵirikaŵiri imakanidwa. Mwachitsanzo, ngati tingotsutsa zikondwerero zofala ndi kunena kuti n’zachikunja, anthuwo sangasinthe maganizo awo pa zikondwerero zimenezo. Koma kukambirana nawo n’kumene kungawathandize. Kodi kukambiranako kuyenera kuchitika motani?
Malemba amatiuza kuti “nzeru yochokera kumwamba . . . ndi yamtendere, yololera.” (Yak. 3:17, NW) Liwu lachigiriki lomasuliridwa kuti ‘kulolera’ limatanthauza “kugonjera.” Mabaibulo ena amati “kuganizirana,” “kufeŵa,” kapena “kuleza mtima.” Onani kuti kulolera akugwirizanitsa ndi kukhala wamtendere. Pa Tito 3:2, NW, “kulolera” akutchula limodzi ndi kufatsa ndipo akusiyanitsa ndi kukhala wandewu. Afilipi 4:5, NW, amatilimbikitsa kuti tidziŵike kukhala anthu “ololera.” Munthu wololera amaganizira moyo wa munthu amene akulankhula naye, komanso maganizo ake. Amakhala wokonzeka kugonjera pamene kukhala kofunikira. Kuchita ndi ena mwa njira imeneyo kumatsegula maganizo ndi mitima yawo moti amalabadira pamene tikambirana nawo za m’Malemba.
Poyambira Pake. Wolemba zochitika za m’mbiri, Luka, akusimba kuti pamene mtumwi Paulo anali ku Atesalonika, anagwiritsa ntchito Malemba, “natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa.” (Mac. 17:2, 3) Dziŵani kuti Paulo anachita zimenezi mu sunagoge wa Ayuda. Amene anali kulankhula nawo anali kukhulupirira Malemba Achihebri. Choncho, kunali koyenera kuyambira pa zinthu zimene anali kuvomereza kale.
Pamene Paulo anali kulankhula kwa Agiriki ku Areopagi ku Atene, sanayambe mwa kutchula Malemba. M’malo mwake, anayamba ndi zinthu zimene anthuwo anazidziŵa ndi kuzikhulupirira, ndipo iye anagwiritsa ntchito zomwezo powatengera ku mfundo zokhudza Mlengi ndi zolinga Zake.—Mac. 17:22-31.
Masiku ano, pali anthu ambirimbiri amene Baibulo saliona kukhala lofunika pa moyo wawo. Koma mavuto a padzikoli amakhudza munthu aliyense. Anthu amalakalaka moyo wabwino. Ngati choyamba musonyeza nkhaŵa pa zimene zimawavutitsa, kenako n’kusonyeza mmene Baibulo limafotokozera zinthuzo, njira yokambirana imeneyo ingawalimbikitse kuti amve zimene Baibulo limanena za chifuniro cha Mulungu pa anthu.
N’kutheka kuti munthu amene mumaphunzira naye Baibulo makolo ake anam’patsa choloŵa cha kum’phunzitsa chipembedzo ndi miyambo ina. Tsopano munthuyo akuphunzira kuti chipembedzocho ndi miyamboyo n’zosam’kondweretsa Mulungu, ndipo akuzikana ndi kukhulupirira zimene akuphunzira m’Baibulo. Kodi angawafotokozere bwanji makolo ake kuti iye akusiya zimenezo? Makolowo angaone kuti mwana wawoyo pokana choloŵa cha chipembedzo chimene anam’phunzitsa, akukana iwo. Wophunzira Baibuloyo angaone kuti ndi bwino kuyamba watsimikizira makolo akewo kuti amawakonda ndi kuwalemekeza asanafotokoze zifukwa za m’Baibulo zimene wasankhira kuchita zimenezo.
Pamene Muyenera Kulolera. Ngakhale kuti Yehova ali ndi mphamvu yolamula chilichonse, iye amaganizira ena. Populumutsa Loti ndi banja lake mu Sodomu, angelo a Yehova anawafulumiza kuti: “Thaŵira kuphiri, kuti unganyeke.” Komabe, Loti anadandaula nati: “Iyayitu mfumu.” Anachonderera kuti am’lole kuthaŵira ku Zoari. Yehova anam’ganizira Loti mwa kum’lola kuthaŵira kumeneko; choncho pamene mizinda ina inawonongedwa, mzinda wa Zoari unatsala. Komabe, pambuyo pake Loti anadzatsatira zimene Yehova anam’langiza poyamba, ndipo anasamukira kudera la kumapiri. (Gen. 19:17-30) Yehova anadziŵa kuti njira yake inali yoyenera, koma analolera moleza mtima kufikira Loti atazindikira zimenezo.
Kuti tithandize anthu ena, ifenso tiyenera kukhala ololera. Tingakhale otsimikiza kuti zimene munthu winayo akunena si zoona, ndipo tingakhale ndi mfundo zamphamvu zotsimikizira zimenezo. Koma nthaŵi zina ndi bwino kusam’gometsa munthuyo. Tikati kulolera sitikutanthauza kukhotetsa miyezo ya Yehova. Mungachite bwino kungomuyamikira munthuyo polankhula zimene amakhulupirira kapena kusanenapo kanthu pa zolakwa zimene wanena, kotero kuti kukambirana kwanu kukhale pa mfundo yothandiza. Ngakhale atatsutsa zimene mumakhulupirira, musanyanyuke mtima. Mungam’funse chifukwa chake akuganiza zimenezo. Mvetserani mosamala pamene akuyankha. Zimenezo zingakuthandizeni kuzindikira kalingaliridwe kake. Komanso mungatsegule mpata wodzakambirananso m’tsogolo.—Miy. 16:23; 19:11.
Yehova anapatsa anthu ufulu wosankha zinthu. Amawalola kugwiritsa ntchito ufulu umenewo, ngakhale kuti nthaŵi zina saugwiritsa ntchito bwino. Yoswa, monga wolankhulira Yehova, anafotokoza zochitika za pakati pa Mulungu ndi Israyeli. Ndiyeno anati: “Ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzam’tumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m’dziko lawo; koma ine, ndi a m’nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.” (Yos. 24:15) Ntchito yathu lero ndi kuchitira ‘umboni,’ ndipo timalankhula motsimikiza mtima, koma sitiyesa kuumiriza anthu ena kuti akhulupirire. (Mat. 24:14) Iwo ayenera kusankha okha, ndipo sitiwaletsa ufulu wawowo.
Perekani Mafunso. Yesu anapereka chitsanzo chokambirana bwino ndi anthu. Iye anaganizira makhalidwe awo ndipo anagwiritsa ntchito mafanizo amene anthu anawakhulupirira mosavuta. Anaperekanso mafunso ogwira mtima. Mwakutero, anapatsa ena mwayi wolankhula momasuka ndi kunena zakukhosi kwawo. Zinathandizanso anthuwo kulingalirapo pa nkhani imene anali kukambirana.
Munthu wodziŵa Chilamulo anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, ndidzaloŵa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?” Yesu akanafuna, akanangoyankha. Koma anafunsa munthuyo kuti alankhule zimene iye anali kuganiza. Iye anati: “M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uŵerenga bwanji?” Mwamunayo anayankha molondola. Kodi atayankha molondola moteromo, kukambirana kwawo kunathera pomwepo? Ayi. Yesu analola mwamunayo kupitiriza, ndipo funso limene mwamunayo anafunsa linavumbula kuti anali kuyesa kudzionetsa wolungama. Iye anati: “Mnansi wanga ndani?” Yesu akanamasulira tanthauzo la “mnansi,” mwina munthuyo akanatsutsa chifukwa cha mmene Ayuda ambiri anaonera Akunja ndi Asamariya. Choncho, Yesu ananena fanizo kuti akambirane naye. Linali la Msamariya wachifundo amene anathandiza wapaulendo wina amene achifwamba anam’bera ndi kum’menya kwambiri, koma wansembe ndi Mlevi anangom’lambalala. Mwa funso losavuta limene Yesu anapereka, mwamunayo anamvetsa mfundo ya fanizolo. Njira yokambirana ya Yesu inachititsa munthuyo kuzindikira tanthauzo lina la mawu akuti “mnansi” limene sanaganizirepo ndi kale lonse. (Luka 10:25-37) Chitsanzo chabwino kwambiri chimenechi! M’malo mongolankhula ife tokha, kuchita ngati kuti mwininyumbayo sakuganiza payekha, dziŵani kupereka mafunso ndi mafanizo mwaluso kuti mulimbikitse womverayo kulingalira.
Perekani Zifukwa. Pamene mtumwi Paulo analankhula m’sunagoge ku Tesalonika, sanangoŵerenga chabe mawu amene omvera ake anali kuwakhulupirira. Luka akunena kuti Paulo anafotokoza, anapereka umboni, ndipo anasonyeza phindu la zimene anaŵerenga. Chifukwa cha zimenezo, “ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila.”—Mac. 17:1-4.
Kalankhulidwe koteroko kamapindulitsa aliyense amene angakhale pakati pa omvera anu. Kamathandizanso kwambri polalikira achibale, polankhula kwa anzanu a kuntchito kapena anzanu a kusukulu; polankhula ndi anthu mu ulaliki, pochititsa phunziro la Baibulo, kapena pokamba nkhani mu mpingo. Pamene muŵerenga lemba, tanthauzo lake lingakhale lodziŵika bwino kwa inu, koma osati kwa munthu winayo. Kulongosola kapena kutanthauzira kwanu kungangomveka ngati kulimbikitsa zimene mumakhulupirira basi. Kodi kusankhapo mawu ena ofunika kwambiri m’lembalo ndi kuwafotokoza kungathandize? Kodi mungapereke umboni wake, mwina wochokera pamavesi ozungulira lembalo kapena pa lemba lina lokhudza nkhani imeneyo? Kodi fanizo lingathandize kumveketsa zimene mwafotokoza? Kodi mafunso angathandize omvera anu kuona mfundo ya nkhaniyo? Kukambirana koteroko kumapereka chithunzi chabwino ndipo kumalimbikitsa ena kuganizapo kwambiri.