Takulandirani ku Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
KUZUNGULIRA dziko lonse lapansi, m’mayiko pafupifupi 200, ophunzira ofika m’mamiliyoni akupindula mlungu ndi mlungu ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Ena ndi atsopano. Ena akhala m’sukuluyi zaka zambiri. Sukulu imeneyi imachitika m’malo osiyanasiyana zikwizikwi. Kulikonse kumene mukukhala padziko lapansi, pulogalamu ya maphunziro yofananayo iliko imene mukhoza kupindula nayo. Anthu a misinkhu yosiyanasiyana, mitundu, ndi maphunziro osiyanasiyana akulandira malangizo aumulungu amenewo popanda malipiro.
Pamene sukuluyi inakhazikitsidwa m’mipingo ya Mboni za Yehova mu 1943, cholinga chake chinafotokozedwa motere: “Ndicho kukonzekeretsa ‘anthu okhulupirika onse,’ awo amene amva Mawu a Mulungu ndi kuwakhulupirira, kuti ‘akathe kuphunzitsa ena’ . . . ndi cholinga chokonzekeretsa mmodzi ndi mmodzi . . . kulengeza poyera chiyembekezo chimene ali nacho.” (Course in Theocratic Ministry, tsa. 4) Cholinga cha sukuluyi chikali chomwecho mpaka lero.
Kunena zoona, kodi chinthu chabwino koposa chimene munthu angachite ndi mphatso ya kulankhula imene Mulungu anatipatsa n’chiyani? Baibulo limayankha kuti: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova.” (Sal. 150:6) Tikatero, timasangalatsa mtima wa Atate wathu wakumwamba. Umakhala umboni kwa iye wakuti mitima yathu ikulabadira moyamikira ubwino wake ndi chikondi chake. Ndiye chifukwa chake Akristu nthaŵi zonse amalimbikitsidwa kuti ‘apereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake’! (Aheb. 13:15) Pofuna kukuthandizani kukulitsa luso lanu lopatsidwa ndi Mulungu logwiritsa ntchito mphatso zanu zotamandira Yehova, tikukulandirani monga wophunzira m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Ngakhale kuti sukuluyi imaphunzitsa kwambiri za kuŵerenga pamaso pa anthu ndi luso la kulankhula ndi kuphunzitsa, mapindu a maphunziro ake sali ku mbali yokhayo. Pamene mutengamo mbali, mudzathandizidwa kukulitsa maluso ofunika monga kuŵerenga panokha, kumvetsera ndi kukumbukira, kuphunzira panokha, kufufuza nkhani, kupenda mfundo ndi kuzisanja, kukambirana, kuyankha mafunso, ndi kulemba malingaliro anu. Baibulo lenilenilo komanso mabuku ena ozikidwa pa Baibulo ndiwo magwero a nkhani zoŵerenga ndi mayankho owapereka komanso nkhani zokambidwa m’sukulu imeneyi. Pamene mudzaza maganizo anu ndi mfundo zamtengo wapatali za choonadi cha m’Mawu a Mulungu, mudzaphunzira kukhala ndi malingaliro a Mulungu. Ha, kupindulitsa kwake nanga kwa zimenezo pamoyo wa tsiku ndi tsiku! Ponena za phindu la Mawu a Mulungu, katswiri wina wa zamaphunziro pa yunivesite ina wa m’zaka za m’ma 1900, William Lyon Phelps, analemba kuti: “Aliyense amene amalidziŵa bwino Baibulo anganenedwe kuti ndi munthu wophunziradi. . . . Ineyo ndimakhulupirira kuti kulidziŵa Baibulo popanda maphunziro a kukoleji n’kwaphindu kusiyana ndi maphunziro a kukoleji koma osalidziŵa Baibulo.”
Mmene Mungapindulire Mokwanira
Inde, kuti mupindule mokwanira ndi maphunziro operekedwa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, inuyo monga wophunzira, muyenera kuchita khama. Mtumwi Paulo analimbikitsa Mkristu mnzake Timoteo kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako [“kupita kwako patsogolo,” NW] kuonekere kwa onse.” (1 Tim. 4:15) Kodi ndi m’njira zotani zimene inuyo mungasonyeze khama limenelo?
Ngati n’kotheka, fikani pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu sabata iliyonse. Gwiritsani ntchito mwanzeru buku lophunzirira limeneli lakuti, Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Lembani dzina lanu pamalo operekedwawo patsamba lolembedwa mutu wa buku. Nthaŵi zonse tengani bukuli pobwera ku sukulu. Buku lophunzirira limeneli lilinso buku lolembamo. Pamene muŵerenga mfundo zofunika zimene muona kuti zikuthandizani, lembani mzera kunsi kwake. Gwiritsani ntchito malo a m’mphepete aakuluwo polembamo mfundo zothandiza zimene mwaphunzira pamakambirano a m’sukulu.
Pulogalamu yosindikizidwa yoitsatira mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu idzatumizidwa payokha. Ndandandayo idzakhalanso ndi malangizo a mmene sukuluyo izichitikira. Kungakhale kothandiza kusungira ndandandayo m’buku lino, kuti izikhala pafupi.
Pokonzekera makalasi a mlungu ndi mlungu a sukuluyi, kumbukirani kuti Baibulo ndilo buku lophunzirira lalikulu. Choyambirira, ŵerengani mbali iliyonse ya Baibulo imene yandandalikidwa mlunguwo. Ngati mungakhoze kuŵerengeratu nkhani zosiyanasiyana, mudzapindulanso kwambiri.
M’kati mwa sukuluyo, pangakhale mipata yakuti omvera atengepo mbali. Gwiritsani ntchito mwayi umenewo mokwanira. Kutenga mbali m’makambirano oterowo kungathandize kwambiri kukumbukira zimene mumamva ndi kutha kuzigwiritsa ntchito pamoyo wanu.
Inde, ophunzira onse adzakhala ndi mwayi wokamba nkhani kapena kupereka zitsanzo pamaso pa mpingo. Gwiritsani ntchito bwino mipata imeneyo. Limbikirani ndithu kuti muwongolere luso lililonse la kulankhula limene mwalangizidwa kukonzekera. Azikupatsani malangizo ndi cholinga chakuti muzipitabe patsogolo osalekeza. Landirani thandizo limenelo ndi mtima wonse. M’buku mwanumo, lembani maganizo ofunika amene mwapatsidwa pa zimene muyenera kuchita kuti muwongolere. Popeza n’kovuta kuti munthu adzione mmene ena amamuonera, maganizo achikondi ndi malangizo ozikidwa m’Baibulo operekedwa angakuthandizeni kwambiri kupita patsogolo. Zimenezo n’zoona ngakhale kuti mwakhala m’sukuluyo zaka zambiri.—Miy. 1:5.
Kodi mungakonde kupita patsogolo mofulumirirapo? Ngati muli ndi khama lochita zinthu panokha, mukhoza kutero. Ŵerengani pasadakhale mbali zimene zidzakambidwe m’nkhani ya wophunzira iliyonse. Ngati padzafunika wokamba nkhani wogwirizira, inuyo mukhoza kudzipereka, ndipo mwa kutero mudzakhala mukuzoloŵera. Ndipo pamene ena akamba nkhani zawo, tcherani khutu ndi kuona mmene akufotokozera mfundo zawo. Timaphunzira kwa wina ndi mnzake.
Kuwonjezera pa zimenezo, ngati mikhalidwe ilola, mutha kupita patsogolo mofulumira mwa kuŵerengeratu zinthu m’bukuli. Mutaphunzira bwino lomwe zomwe zili m’maphunziro 15 otsatiraŵa, pitirizani ndi khama lanu m’gawo lakuti “Pulogalamu Yophunzitsa Luso la Kulankhula ndi Kuphunzitsa.” Mbali imeneyi ikuyambira patsamba 78. Choyamba, ŵerengani phunziro lililonse, ndipo chitani mbali ya zochita ya phunzirolo. Gwiritsani ntchito mu ulaliki zimene mumaphunzira. Zimenezo zingakuthandizeni kwambiri kupita patsogolo monga wolankhula ndi wophunzitsa Mawu a Mulungu.
Kuphunzira kwanu pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kudzakuthandizani kukonzekera zinthu zofunika koposa pamoyo. Popeza kuti tili ndi moyo mwa chifuniro cha Mulungu, ngati tim’tamanda timaonetsa kuti timazindikira cholinga chenicheni chimene tikukhalira ndi moyo. Chitamando cha mtundu wopambana koposa n’chimene chiyenera kupita kwa Yehova Mulungu. (Chiv. 4:11) Maphunziro amene timalandira m’sukulu imeneyi ndiwo njira yochitira zimenezo, kotero kuti tithe kulingalira bwino, kuchita zinthu mwanzeru, ndi kuphunzitsa mogwira mtima choonadi chopambana cha m’Mawu a Mulungu ouziridwa.