PHUNZIRO 20
Kutchula Malemba Moyenerera
MALEMBA ndiwo maziko a zimene zimaphunzitsidwa pamisonkhano yampingo. Malemba a m’Baibulo alinso gwero la zimene timanena mu utumiki wa kumunda. Komabe, kuti malemba athandize kwenikweni pankhani yomwe tikukambirana, zimadaliranso mawu omwe timanena otsogolera ku malembawo.
Pali zina zofunikira kuposa kungotchula lemba ndi kupempha wina kuti aŵerengere limodzi nanu. Potchula mawu oŵerengera lemba, khalani ndi zolinga ziŵiri izi: (1) Kukopa chidwi, ndipo (2) kumveketsa chifukwa choŵerengera lembalo. Zolingazi tingazikwaniritse m’njira zosiyanasiyana.
Perekani Funso. Njira imeneyi imakhala yothandiza kwambiri ngati omverawo sakudziŵa yankho lake. Perekani funsolo m’njira yochititsa anthu kuganiza. N’zimene Yesu anachita. Afarisi atafika kwa iye m’kachisi ndi kumuyesa pamaso pa anthu pofuna kuona ngati amadziŵa Malemba, Yesu anawafunsa kuti: “Muganiza bwanji za Kristu? ali mwana wa yani?” Iwo poyankha anati: “Wa Davide.” Ndiyeno Yesu anafunsa kuti: “Ndipo Davide mu Mzimu am’tchula bwanji iye Ambuye”? Atanena izi anagwira mawu Salmo 110:1. Zitatero Afarisi aja anangochita kakasi kusoŵa chonena. Koma khamu lonse lomwe linali pamenepo linamvetsera kwa Yesu mwachidwi.—Mat. 22:41-46.
Mu utumiki wa kumunda, mungapereke mafunso otchulira lemba ngati aŵa: “Inu ndi ine tili ndi mayina athuathu. Kodi Mulungunso ali ndi dzina lakelake? Timapeza yankho pa Salmo 83:18.” “Kodi m’tsogolomu pangadzakhale boma limodzi la anthu onse? Taonani mmene limayankhira lemba la Danieli 2:44.” “Kodi Baibulo limanenadi za makhalidwe a masiku ano? Yerekezani zimene zatchulidwa pa 2 Timoteo 3:1-5 ndi makhalidwe amene mumawadziŵa bwino.” “Kodi kuvutika ndi imfa zidzatha konse? Baibulo limayankha pa Chivumbulutso 21:4, 5.”
Pokamba nkhani, kugwiritsa ntchito bwino mafunso otchulira malemba kungachititse omvera anu kukhala ndi chidwi pa malembawo, ngakhale kuti ndi omwe amawadziŵa kale. Koma kodi chidwicho adzakhaladi nacho? Zimenezo zimadalira inuyo kupereka mafunso amene angawakhudzedi. Ngakhale pamene nkhaniyo ili yowakhudza omverawo, maganizo awo angayambe kuyendayenda pamene muŵerenga malemba amene awamvapo nthaŵi zambiri. Kuti muletse zimenezo, iganizireni mofatsa mfundoyi kuti mukakambe nkhani yosangalatsa.
Tchulani Vuto. Mungatchule vuto kenako n’kusonyeza lemba limene lingathandize pavutolo. Musapangitse omverawo kuyembekezera zambiri kuposa zimene muwafotokozere. Kaŵirikaŵiri, lemba limayankha mbali imodzi ya vuto. Koma pamene mukuŵerenga lembalo, mungapemphe omverawo kulingalira mmene lingawathandizire kupeza njira yothanira ndi vutolo.
Mofananamo, mungatchule mfundo ya khalidwe laumulungu kenako gwiritsani ntchito chochitika cha m’Baibulo chosonyeza nzeru yotsatira njirayo. Okamba nkhani ena amauza omvera awo kuti lembalo lili ndi mfundo ziŵiri (kapena zoposerapo) zokhudzana ndi nkhaniyo, kenako amapempha omverawo kupeza mfundo zimenezo. Ngati vutolo n’losati omverawo n’kulimvetsa, mungawathandize kulingalira mwa kuwatchulira njira zosiyanasiyana kenako n’kulola lembalo ndi tanthauzo lake kuti zipereke yankho.
Sonyezani Baibulo Kukhala Maziko a Zimene Mukunena. Ngati mwakopa kale chidwi pankhani yanu ndipo mwatchula mfundo imodzi kapena zingapo pambali ina, munganene mawu otchulira lemba akuti: “Taonani zimene Mawu a Mulungu amanena pamfundoyi.” Zimenezi zimasonyeza kuti mawu amene muŵerenge ndi odalirika.
Yehova anagwiritsa ntchito amuna ngati Yohane, Luka, Paulo, ndi Petro polemba mabuku a m’Baibulo. Koma iwo anali ngati masekeletale; Mwiniwake ndi Yehova. Makamaka polankhula ndi anthu osaphunzira Malemba Oyera, mawu otchulira lemba akuti “Petro analemba kuti” kapena “Paulo anati” sangakhale ndi mphamvu kwenikweni yoonetsa kuti mukufuna kuŵerenga mawu a Mulungu. N’chifukwa chake nthaŵi zina, Yehova pouza Yeremiya kupereka zilengezo zake anamuuza kuyamba ndi mawu akuti: “Tamvani mawu a Yehova.” (Yer. 7:2; 17:20; 19:3; 22:2) Kaya titchule kapena tisatchule dzina la Yehova m’mawu otsogolera ku lemba, tisanamalize nkhani yathu timveketse mfundo yakuti mawu a m’Baibulo alidi mawu a Mulungu.
Dziŵani Zochitika Zotchulidwa pa Lembalo. Muyenera kudziŵa zochitika za palemba posankha mawu otchulira lemba. Nthaŵi zina mungatchule zochitikazo; komabe, zochitikazo zingakhudze mmene munganenere mawu anu. Mwachitsanzo, kodi mungatchule mawu a Yobu woopa Mulunguyo monga mmene munganenere mawu a mmodzi wa om’tonthoza mtima onyenga aja? Buku la Machitidwe analemba ndi Luka, koma anagwira mawu a Yakobo, Petro, Paulo, Filipo, Stefano, angelo ndi enanso, kuphatikizapo Gamaliyeli ndi Ayuda ena omwe sanali Akristu. Kodi mungati mukuŵerenga mawu ayani palemba limene mwasankha? Kumbukiraninso kuti si Davide analemba Masalmo onse ndipo si Solomo analemba Miyambo yonse. N’kopindulitsanso kudziŵa kuti wolemba Baibuloyo anali kulankhula kwa ndani ndipo anali kukambirana naye nkhani yanji.
Gwiritsani Ntchito Mfundo Zina Zokhudza Lembalo. Zimenezi zimakhala zothandiza makamaka pofuna kusonyeza kuti mikhalidwe ya panthaŵi ya chochitika cha m’Baibulo inali yofanana ndi imene mukufotokoza. Nthaŵi zina, mfundo zina zokhudza nkhaniyo zimakhala zofunikira pofuna kumveketsa lembalo. Mwachitsanzo, ngati mungagwiritse ntchito Ahebri 9:12, 24 m’nkhani yonena za dipo, musanaŵerenge lemba mungafotokoze mwachidule za chipinda chopatulikitsa cha chihema, chimene malinga n’kunena kwa malemba, chinaphiphiritsa malo amene Yesu anakaloŵako pamene anakwera kumwamba. Koma musaphatikizepo mfundo zina zambirimbiri chifukwa zingasokoneze lemba limene mukufuna kuŵerenga.
Kuti mupeze luso lonenera mawu otchulira lemba, onetsetsani mmene amachitira okamba nkhani ozoloŵera. Onani njira zosiyanasiyana zimene amagwiritsa ntchito. Yerekezani njirazo kuti muone njira yogwira mtima kwambiri. Pokonzekera nkhani zanu, pezani malemba ofunika kwambiri, ndipo lingalirani mofatsa cholinga chimene mukufuna kuŵerengera lemba lililonse. Konzani mosamala mawu otchulira lemba lililonse kotero kuti akhale ogwira mtima koposa. M’kupita kwa nthaŵi, chitani chimodzimodzi ndi malemba onse amene mukugwiritsa ntchito. Pamene luso limeneli likupita m’tsogolo, mudzathandiza ambiri kuŵerenga Mawu a Mulungu.