Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2004 | July 15
    • Nsembe ya dipo ya Yesu Kristu ndiyo chinthu chimene Mulungu anakonza pofuna kumasula anthu ku ukapolo wa uchimo.a (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; 1 Yohane 2:1, 2) Kodi ndi liti pamene Akristu amamasulidwa ku lamulo la uchimo? Polankhula ndi Akristu odzozedwa, mtumwi Paulo anati: “Chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.” (Aroma 8:2) Anthu oyembekezera kukakhala ndi moyo kumwamba amalandira ufulu umenewu akadzozedwa ndi mzimu woyera. Ngakhale kuti matupi awo ndi anyama ndi mwazi ndiponso ndi opanda ungwiro, Mulungu amawaona kuti ndi olungama ndipo amawatenga kukhala ana ake auzimu. (Aroma 3:24; 8:16, 17) Kwa odzozedwa onse monga gulu limodzi, Chaka Choliza Lipenga chachikristu chinayamba pa Pentekoste m’chaka cha 33 Kristu Atabwera.

      Nanga bwanji za “nkhosa zina,” zimene zikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi? (Yohane 10:16) Kwa ankhosa zina, Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu udzakhala nthaŵi yobwezeretsa zinthu mwakale ndiponso yobweretsa ufulu. M’Chaka Choliza Lipenga cha Zaka 1,000 chimenechi, Yesu adzagwiritsira ntchito phindu la nsembe yake ya dipo kwa anthu okhulupirira ndipo adzathetsa zoipa zonse zobwera chifukwa cha uchimo. (Chivumbulutso 21:3, 4) Podzafika kumapeto kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu, anthu adzafika pokhala angwiro ndipo adzamasukiratu ku uchimo ndi imfa zomwe amabadwa nazo. (Aroma 8:21) Zimenezi zikadzachitika, Chaka Choliza Lipenga chachikristu chidzathera pomwepo.

  • “Yense Wochenjera Amachita Mwanzeru”
    Nsanja ya Olonda—2004 | July 15
    • “Yense Wochenjera Amachita Mwanzeru”

      ZIMENE limatilangiza Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, ‘n’zofunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa.’ (Salmo 19:7-10) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “malamulo a wanzeru [Yehova] ndiwo kasupe wa moyo, apatutsa ku misampha ya imfa.” (Miyambo 13:14) Tikawagwiritsira ntchito, malangizo a m’Malemba sikuti amangotithandiza kukhala moyo wabwino koma amatithandizanso kupeŵa misampha imene ingawononge moyo wathuwo. Motero, m’pofunika kwambiri kufunafuna nzeru za m’Malemba n’kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene taphunzira.

      Malingana ndi zimene lemba la Miyambo 13:15-25 limanena, Mfumu Solomo ya dziko lakale la Israyeli inapereka malangizo amene amatithandiza kuchita zinthu mwanzeru kuti tikhale ndi moyo wabwino komanso wautali.a Mfumuyi inagwiritsira ntchito miyambi yosapita m’mbali posonyeza kuti Mawu a Mulungu angatithandize kuti tiziyanjana ndi ena, tizikhala okhulupirika mu utumiki wathu, tizimvera malangizo, ndiponso tizisankha anzathu mwanzeru. Inatchulaponso kuti n’kwanzeru kusiyira ana athu choloŵa komanso kuwalanga mwachikondi.

      Nzeru Yabwino Imapatsa Chisomo

      Solomo anati: “Nzeru yabwino ipatsa chisomo; koma njira ya achiwembu ili makolokoto.” (Miyambo 13:15) Buku lina linati mawu amene anawamasulira kuti “nzeru yabwino,” kapena kuti kumvetsetsa bwino, “amanena za kutha kuganiza m’njira zosiyanasiyana zosonyeza nzeru zozama.” Munthu amene ali ndi nzeru zoterezi savutika kupeza chisomo kapena kuti kuyanjidwa ndi anthu ena.

      Taganizirani nzeru zimene Paulo anasonyeza pa zimene anachita ndi Mkristu mnzake Filemoni pomwe ankabweza kapolo wa Filemoniyo wotchedwa Onesimo, yemwe anathaŵa koma pambuyo pake n’kudzakhala Mkristu. Paulo analimbikitsa Filemoni kuti amulandirenso bwino Onesimo, monga mmene angalandirire Pauloyo. Ndipotu, Paulo ananena kuti ngati Onesimo ali ndi ngongole iliyonse ndi Filemoni, Pauloyo anadzipereka kubweza ngongoleyo m’malo mwake. Komatu Paulo akanatha kugwiritsira ntchito mphamvu zake n’kulamula Filemoni kuti am’landire bwino Onesimo. M’malomwake mtumwiyu anaganiza zoyendetsa nkhaniyi mosamala ndiponso mwachikondi. Potero, Paulo sanakayikire kuti Filemoni amvera mochita kufuna yekha, n’kuchita zina kuwonjezera pa zinthu zimene Pauloyu anam’pempha. Kodi nafenso sitiyenera kuchita chimodzimodzi ndi okhulupirira anzathu?​—Filemoni 8-21.

      Komano njira ya achiwembu, ili makolokoto kapena kuti “n’njolimba.” Kodi n’njolimba motani? Malingana n’kunena kwa katswiri wina wa maphunziro, mawu amene anatchula pamenepa amatanthauza “chinthu cholimba, ndipo amanena za kukakala mtima kwa anthu oipa. . . . Munthu amene watsimikiza kuchita zinthu zoipa, osamvera ngakhale pang’ono malangizo anzeru a anzake, ndiye kuti akupita kuchiwonongeko.”

      Solomo anapitiriza kunena kuti: “Yense wochenjera amachita mwanzeru; koma wopusa aonetsa utsiru.” (Miyambo 13:16) Munthu wochenjerayu si kamberembere ayi. Kuchenjera kumeneku n’koyenderana ndi kudziŵa bwino zinthu ndipo n’kuchenjera kwa munthu wanzeru, amene amayamba waganiza kaye mosamala asanachite chinthu. Munthu wochenjera chonchi amadziletsa akamanenedwa kapena kunyozedwa ali wosalakwa. Mwapemphero, amayesetsa kuonetsa chipatso cha mzimu woyera n’cholinga choti zimenezi zisam’pweteke mtima kwambiri. (Agalatiya 5:22, 23) Munthu wochenjera m’njira imeneyi salola kuti anthu ena amulakwitse. M’malomwake amaugwira mtima, moti amapeŵa mapokoso amene anthu amtima wapachala amachita kaŵirikaŵiri ena akawalakwira.

      Munthu wochenjera amaganiza kaye mofatsa asanachite zinthu. Iye amadziŵa kuti zinthu zanzeru kaŵirikaŵiri sizichitika mongolota, mongotengeka maganizo, kapena mongotsatira zimene anthu ambiri akuchita. Motero, amayamba waiganizira kaye bwinobwino nkhaniyo. Amaona kaye chilichonse chofunikira kudziŵa n’kuganizira njira zina zimene angayendetsere nkhaniyo. Kenaka amafufuza m’Malemba n’kuona malamulo kapena mfundo za m’Baibulo zimene zikugwirizana ndi nkhaniyo. Njira ya munthu wotere imakhala yowongoka nthaŵi zonse.​—Miyambo 3:5, 6.

      “Mtumiki Wokhulupirika Alamitsa”

      Poti ndife Mboni za Yehova, tinapatsidwa ntchito yolengeza uthenga

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena