Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kulitsani Chidwi cha Amene Mumakawapatsira Magazini
    Utumiki wa Ufumu—2005 | May
    • Kulitsani Chidwi cha Amene Mumakawapatsira Magazini

      1. Kodi tingakulitse bwanji chidwi cha amene timakawapatsira magazini?

      1 Anthu ambiri amene timakumana nawo mu utumiki amatilandira bwino ndipo amalandira mabuku athu mosangalala koma amazengereza kuti tizichita nawo phunziro lokhazikika la Baibulo. Njira imodzi imene tingakulitsire chidwi chawo ndiyo kukhala ndi chizolowezi chomakawapatsira magazini. Mukagawira magazini, muzilemba dzina la munthuyo ndi adiresi yake, deti limene mwamugawira, magazini imene walandira, ndi lemba limene mwakambirana, pamodzi ndi chilichonse chimene chakusonyezani kuti munthuyo ali ndi chidwi. Magazini iliyonse yatsopano ikafika, muziyang’ana mfundo zimene zikhoza kukhala zosangalatsa kwa anthu amene mumakawapatsira magaziniwo, ndi kukakambirana zimenezo pamene mwapitakonso ulendo wotsatira. (1 Akor. 9:19-23) M’kupita kwa nthawi, akhoza kuwerenga zinthu zina m’magaziniwa zimene zikhoza kudzutsa chidwi chawo n’kuwapangitsa kufuna kuphunzira zambiri.

      2. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ayenera kufunafuna Yehova panopa mofulumira, ndipo n’chiyaninso china chomwe tingachite kuti tiwathandize?

      2 Tikudziwa kuti anthu ambiri sangakhale atumiki a Yehova pongowerenga okha magazini. Popeza kuti anthu ayenera kufunafuna Yehova panopa mofulumira, kodi n’chiyaninso china chomwe tingachite kuti tiwathandize? (Zef. 2:2, 3; Chiv. 14:6, 7) Tikhoza kukulitsa chidwi chawo mwa kukambirana nawo lemba limodzi limene talisankha mosamala bwino. Tingakambirane lembalo panthawi iliyonse imene tapita kukawapatsira magazini.

      3. (a) Kodi tingachite chiyani kuti tikonze makambirano angapo a lemba limodzi? (b) Kodi ndi nkhani ziti zimene anthu a m’gawo lanu amafuna kumva?

      3 Kukambirana Lemba Limodzi: Choyamba ganizirani kaye za anthu amene mumakawapatsira magazini, ndiyeno apezereni malemba aliyense lakelake mogwirizana ndi zimene aliyense akufunikira. (Afil. 2:4) Mwachitsanzo, ngati wina wokondedwa wake wamwalira posachedwapa, mungapiteko maulendo angapo kukakambirana naye zimene Baibulo limanena zokhudza akufa ndi chiyembekezo choti akufa adzauka. Nkhani za m’buku la Kukambitsirana pansi pa mutu wakuti “Imfa” ndi “Chiukiriro” mungazigwiritse ntchito pokonza zokakambirana naye lemba limodzi ulendo uliwonse. Mapeto ake, mungadzakambiranenso nkhani zina zokhudzana ndi zimenezi, monga mmene matenda, ukalamba, ndi imfa zidzathere. Chofunika kwambiri ndicho kupeza nkhani imene ingamusangalatse munthuyo ndiyeno n’kumamusonyeza pang’onopang’ono zimene Baibulo limanena pa nkhaniyo.

      4. N’chifukwa chiyani m’pofunika kuthandiza anthu kumvetsetsa mfundo zofunika pamene tikuwerenga Malemba, ndipo zimenezi tingazichite bwanji?

      4 Athandizeni Kumvetsetsa: Ngakhale kuti ndi bwino ngati kukambirana kumeneku kungamakhale kosavuta ndi kwachidule, m’pofunikabe zambiri m’malo mongowerenga lemba limene tasankhalo. Satana wachititsa khungu mitima ya anthu kuti asazindikire uthenga wabwino. (2 Akor. 4:3, 4) Ngakhalenso anthu amene amalidziwa Baibulo, amafunika thandizo kuti athe kulimvetsetsa. (Mac. 8:30, 31) Motero, khalani ndi nthawi yokwanira bwino yoti muthe kufotokoza bwino ndi kupereka fanizo pa lembalo, monga mmene mumachitira mukakhala kuti mukukamba nkhani ya mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. (Mac. 17:3) Onetsetsani kuti munthuyo akutha kuona kufunika kwa Mawu a Mulungu pa moyo wake.

      5. Kodi zingatheke bwanji kuti amene timakawapatsira magazini akhale phunziro la Baibulo?

      5 Ngati munthuyo wayamba kusangalala ndi zimene akuphunzira, pang’onopang’ono muzitalikitsa makambiranowo mwa kuwonjezera malemba awiri kapena atatu a m’Baibulo ulendo uliwonse. Yesani kupeza mpata womusonyezera bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso. Mwanjira imeneyi, amene mumakawapatsira magazini akhoza kukhala phunziro la Baibulo m’kupita kwa nthawi.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki wa Ufumu—2005 | May
    • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

      Nsanja ya Olonda May 15

      “Kodi mukuganiza kuti tidzalionadi dziko lopanda umphawi? [Yembekezani ayankhe.] Tamvani zimene Mulungu akulonjeza. [Werengani Yesaya 65:21.] Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikufotokoza momwe lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwire.” Konzani zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lakuti: Kodi lonjezo la kusintha kumeneku lidzakwaniritsidwa liti?

      Galamukani! June 8

      “Anthu ambiri amvapo kuti masewera olimbitsa thupi ndi ofunika kuti munthu akhale ndi thanzi labwino, koma ambiri amati sachita masewerawa mokwanira. Kodi si zoona kuti anthu ambiri sachita masewera olimbitsa thupi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza phindu lochita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse ndiponso njira zina zotithandiza mmene tingachitire zimenezi ngakhale kuti ndife otanganidwa.”

      Nsanja ya Olonda June 1

      “Ngakhale kuti pafupifupi aliyense amakamba za mtendere, anthu alephera kugwirizana padziko lonse. Kodi mukuganiza kuti zoti anthu padziko lonse angagwirizane ndi nkhambakamwa chabe? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikukamba za boma limene lidzagwirizanitsa anthu padziko lonse.” Werengani Salmo 72:7, 8, ndi kukonza zodzabweranso kuti mudzafotokoze kuti zimenezi zidzachitika bwanji.

      Galamukani! June 8

      “Kodi mwaona kuti anthu ambiri akuda nkhawa ndi mmene khansa yapakhungu ikuchulukira? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ya Galamukani! ikufotokoza chifukwa chake ifeyo masiku ano tili pangozi yaikulu yodwala matenda amenewa komanso zimene tingachite kuti tidziteteze.” Pomaliza werengani lonjezo lotonthoza mtima lomwe lili pa Yobu 33:25.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena