-
Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 7Utumiki wa Ufumu—2005 | April
-
-
Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 7
Kupereka Pemphero pa Phunziro
1. (a) N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuyamba ndi kumaliza phunziro la Baibulo ndi pemphero? (b) Kodi tingatani kuti tiyambe kumapemphera pa phunziro la Baibulo?
1 Kuti ophunzira Baibulo apite patsogolo mwauzimu, m’pofunika dalitso la Yehova. (1 Akor. 3:6) Choncho, ndi bwino kuyamba ndi kumaliza phunziro ndi pemphero. Tikhoza kumachita zimenezi pa phunziro loyambirira lenileni ngati tikuyamba kuphunzira ndi anthu amene ndi okonda zopembedza. Koma kwa ena, tingafunike kuona nthawi yabwino imene tingayenere kuyamba kumapemphera pa phunziro. Mungathe kugwiritsa ntchito Salmo 25:4, 5 ndi 1 Yohane 5:14 kuti muthandize wophunzira kuona chifukwa chake payenera kuperekedwa pemphero ndiponso mungagwiritse ntchito Yohane 15:16 kufotokoza kufunika kopemphera kwa Yehova kudzera mwa Yesu Kristu.
2. Ngati mlongo apita ndi mbale wobatizidwa kapena mwamuna wofalitsa wosabatizidwa ku phunziro la Baibulo, kodi ndani amene adzapereka pemphero?
2 Kodi ndani amene ayenera kupereka pemphero pa phunziro la Baibulo? Ngati mbale wobatizidwa apita ndi mlongo kuphunziro, mbaleyo ayenera kupereka pemphero, ngakhale kuti mlongoyo angachititse phunzirolo atavala chophimba kumutu. (1 Akor. 11:5, 10) Koma ngati mwamuna wofalitsa Ufumu wosabatizidwa apita ndi mlongo ku phunziro, mlongoyo ayenera kupereka pemphero. Ngati zili choncho, mlongoyo ayenera kuvala chophimba kumutu popemphera ndiponso pochititsa phunzirolo.
3. Kodi ndi zinthu zofunika ziti zimene tingaziphatikize m’mapemphero operekedwa pa phunziro la Baibulo?
3 Zimene Mungaziphatikize M’pemphero: Mapemphero a pa phunziro la Baibulo sayenera kukhala aatali, koma ayenera kukhala olunjika. Kuwonjezera pa kupempha dalitso la Mulungu pa phunzirolo ndiponso kuthokoza chifukwa cha choonadi chimene mukuphunzira, n’koyenera kupereka ulemerero kwa Yehova monga Gwero la malangizo. (Yes. 54:13) Tingaphatikizemonso mawu osonyeza kuti tikukondwera naye wophunzirayo ndiponso kuyamikira gulu limene Yehova akugwiritsa ntchito. (1 Ates. 1:2, 3; 2:7, 8) Kupempha Yehova kuti adalitse khama la wophunzirayo pamene akuyesetsa kugwiritsa ntchito zimene akuphunzira, kungamuthandize kuona kufunika kokhala ‘wakuchita mawu.’—Yak. 1:22.
4. Kodi kuyamba ndi kumaliza phunziro la Baibulo ndi pemphero, kumabweretsa phindu liti?
4 Pemphero lili ndi phindu lalikulu. Limabweretsa dalitso la Mulungu. (Luka 11:13) Limasonyeza kuti kuphunzira Mawu a Mulungu ndi nkhani yaikulu. Pamene wophunzira akumvetsera mapemphero athu, amaphunzira mmene angapempherere. (Luka 6:40) Ndiponso, mapemphero ochokera mu mtima wokonda Mulungu ndiponso osonyeza kuti timayamikira makhalidwe ake osayerekezeka akhoza kuthandiza wophunzira kukhala paubwenzi ndi Yehova.
-
-
Zomwe Munganene Pogawira MagaziniUtumiki wa Ufumu—2005 | April
-
-
Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Apr. 15
“Kodi si zoona kuti masiku ano pali nkhani zambirimbiri zofunika kuzidziwa? [Yembekezani ayankhe.] Komabe, pankhani zonsezo palibe yofunika kwambiri kuposa imene ikufotokozedwa mu lemba ili. [Werengani Yohane 17:3.] Magazini iyi ikufotokoza tanthauzo la mawu akuti ‘moyo wosatha’ ndiponso mmene tingadziwire zimene zingatitsogolere ku moyo umenewo.”
Galamukani! May 8
“Ngakhale kuti Yesu Kristu amadziwika kwambiri mwina kuposa munthu aliyense amene wakhalapo, anthu ambiri amadabwa kuti kodi iyeyu kwenikweni ndi ndani. Kodi mukudziwa kuti ngakhalenso atumwi ake a Yesu anaganizapo zimenezi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Marko 4:41.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pankhani yoti kodi Yesuyo ndi ndani kwenikweni.”
Nsanja ya Olonda May 1
“Munthu amene timamukonda akamwalira, mwachibadwa timafuna kudzamuonanso. Kodi inu simukuvomereza zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Lonjezo la m’Baibulo lakuti akufa adzauka limatonthoza mtima anthu ambiri. [Werengani Yohane 5:28, 29.] Magazini iyi ikufotokoza za nthawi imene akufa adzauka ndiponso amene kwenikweni adzapindule ndi zimenezo.”
Galamukani! May 8
“Makolo ambiri amasankha zimene ana awo ayenera kuonera. Kodi zakhala zikukuvutani kupeza mafilimu abwino oyenera banja lanu? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Aefeso 4:17.] Magazini iyi ikufotokoza mmene makolo angathandizire ana awo kusankha zosangalatsa zabwino.”
-