Nyimbo 42
“Njira Ndiiyi”
1. M’lungu aitana; Yendani m’njira,
Njira yomwe M’lungu watisonyeza.
Ali ndi ngalande yapaderadi,
Nasankha kutichenjezera nayo.
Nayi njira yendanimo.
Musaime! Kukayika!
Timamva momvekera chiitanocho.
Tilankhule za ichotu.
Mzimu wa M’lungu udzatiyendetsa.
Tiyendetu m’mabande owongoka.
2. Mawu okoma tiwamva kumbuyo,
Mlangizi Wamkulu asonya njira.
Timamva mwaluntha ndi kumvetsera.
Tisamale kuti tisasokere.
Yendanitu ndi Mulungu,
Njirayo njachiyerotu.
Tikhulupilira mtendere udzadza,
Kristu akulamulira.
Sitidzapambuka m’njirayo konse,
Koma tidzayenda m’njira ya M’lungu.
3. Njira ya Yehova tiuze ena
Omwe adzamvetsera m’dziko lonse.
Monga nkhunda zidza kuzisa zawo
Nizidza kwa M’lungu,
Ngaka, ndi Thanthwe.
Njira ya M’lungu njabata.
Talanditsidwa kudziko.
Akutitsogoza m’njira zolungama
za ku moyo wamuyaya.
Titukula mitu tifulumire,
Maso alunjika ku Ufumuwo.