-
Phunziro Kuchokera kwa Woyendetsa ChomboNsanja ya Olonda—2000 | August 15
-
-
Phunziro Kuchokera kwa Woyendetsa Chombo
KUYENDETSA chombo uli wekhawekha m’nyanja yaikulu kungakhale kotopetsa kwabasi. Zotsatira zosayembekezeka za kutopako zingasonkhezere mosavuta woyendetsa chombo ameneyu kuchita zinthu mosalabadira, kotero kuti angalakwitse zinthu ndi kusankha zochita mosayenera. Pa chifukwa chimenecho, amazindikira kufunika kwa nangula. Nangula amapereka mpata wopuma kwa woyendetsa chombo wotopayo ndi kuti apezenso nyonga popanda chombocho kutengedwa ndi mphepo mochititsa mantha. Panthaŵi imodzimodziyo, nangula amakakamiza kutsogolo kwa chombocho kuloza komwe mphepo ndi mafunde zikuchokera ndi kuchititsa chombocho kuti chikhale malo amodzi osasunthasuntha.
Monga momwe oyendetsa chombo amakumanira ndi ngozi zosiyanasiyana panyanja, Akristu nawonso amakumana ndi mavuto osatha m’dzikoli ndipo amaona kuti n’koyenera kuti apume. Ndithudi, Yesu nthaŵi inayake anauza ophunzira ake kuti: “Idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi.” (Marko 6:31) Lerolino, ena angapite koyenda kwa milungu ingapo kapena kuchoka kumapeto kwa mlungu n’kupita kukacheza ndi mabanja awo. Nthaŵi zoterezi zingakhale zotsitsimula ndi zopezetsa mpumulo. Komabe, kodi tingatsimikizire motani kuti tili otetezeka mwauzimu panthaŵi ngati zimenezo? N’chiyani chomwe chingakhale ngati nangula wathu wauzimu wotithandiza kuti tisasunthesunthe ndi kuti tikhale malo amodzimodzi?
Mowoloŵa manja, Yehova watipatsa chithandizo. Ndipotu si chinanso ayi, koma Mawu ake Opatulika, Baibulo. Mwa kuliŵerenga tsiku ndi tsiku, tingayandikire kwa Yehova ndi kumamatirabe kwa iye osasunthika. Malangizo ake angatithandize kukhala osagwedera ndi kutikhozetsa kupirira mayesero a Satana ndi dziko lakeli. Kupitirizabe kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse, ngakhale ngati sitikutsatira ndandanda yathu yanthaŵi zonse, kungatichirikize mwauzimu monga nangula.—Yoswa 1:7, 8; Akolose 2:7.
Wamasalmo akutikumbutsa kuti “wodala munthuyo” amene “m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” (Salmo 1:1, 2) Kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku kudzatipatsa zotsatira zosangalatsa za kukhaladi otsitsimulidwa ndi kupeza mpumulo, kukonzekeretsedwa kupitirizabe njira yathu yachikristu.
-
-
Kodi Mungafune Kukuchezerani?Nsanja ya Olonda—2000 | August 15
-
-
Kodi Mungafune Kukuchezerani?
Ngakhale m’dziko lino lodzala ndi mavuto, mungapeze chimwemwe mwa kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi chifuniro chake chabwino kwambiri kwa anthu. Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 2.
-