Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/06 tsamba 4-5
  • Kugulitsa Malonda pa Misonkhano Yathu Yachigawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugulitsa Malonda pa Misonkhano Yathu Yachigawo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 7/06 tsamba 4-5

Kugulitsa Malonda pa Misonkhano Yathu Yachigawo

1 Pamene misonkhano yathu yachigawo yakuti ‘Chipulumutso Chayandikira’ ikuyandikira, taona kuti n’koyenera kukukumbutsani zina ndi zina zokhudza khalidwe lathu pamisonkhano imeneyi. Malipoti a misonkhano yachigawo yapitayo akusonyeza kuti abale ena amachoka pa malo a msonkhano kukagula chakudya kwa anthu oyala malonda m’misewu ndi kumalesitilanti akufupi ndi malo amsonkhanowo, mwinanso amatero msonkhano uli m’kati. Ena mwa anthu omvera msonkhano apezekapo akudya msonkhanowo uli m’kati. Kumeneku n’kupanda ulemu.

2 Kumalo ena, anthu ogulitsa zakudya afika mpaka poumirira kuti apatsidwe malo ogulitsirapo malonda awo chapafupi ndi malo a msonkhanowo. Kulola zimenezi kungapangitse kuti pamisonkhano pazikhala anthu ambiri akunja amene angasokoneze bata lathu pamisonkhanoyi.

3 Pamisonkhano ina yachigawo, abale ena amakambirana nkhani zosiyanasiyana zamalonda. Ena amabweretsa malonda awo monga nzimbe, mbatata, chinangwa, mpunga, mandasi, zitumbuwa, nthochi, ndiwo zamasamba ndi zina zambiri, n’cholinga choti agulitse kwa Akristu anzawo. Khalidwe limeneli si labwino konse. Tiyenera kupeweratu chilichonse chokhudza kapena cholimbikitsa malonda pamalo a misonkhano yachigawo. Zinthu zimenezi n’zosagwirizana n’komwe ndi cholinga chathu cha m’Malemba chosonkhanira pamodzi.—Aheb. 10:24, 25.

4 M’pofunika Kusamala: Aliyense amene apite ku msonkhano wachigawo wa chaka chino wakuti ‘Chipulumutso Chayandikira’ akufunika kukumbukira zotsatirazi:

◼ Abale asadzabweretse zinthu zogulitsa pamalo a msonkhano wachigawo.

◼ Abale ndi alongo komanso anthu achidwi asadzagule kanthu kalikonse kwa aliyense wogulitsa chakudya amene angadzayale malonda ake pamalo a msonkhano, chifukwa n’zosakayikitsa kuti ogulitsa malonda adzapezekapo. Kuti tipitirize kukhala audongo ndi adongosolo, m’pofunika kuti ogulitsa malonda asadzapezekepo n’komwe pamalo a msonkhano. Ngati abale akufuna kugula zinthu, agule zinthuzo kumsika kapena kusitolo, ndipo achite zimenezo msonkhano usanayambe kapena utatha.

◼ Msonkhano usanayambe, akalinde ayenera kuuza ogulitsa malonda onse mwaulemu kuti achoke pamalo athu olambirira. Ngati akufuna angakayale malonda awowo kutali ndi malo athu a msonkhano.

5 Ndife osangalala kwambiri kuti misonkhano yathu yachigawo yakuti ‘Chipulumutso Chayandikira’ ikuyamba posachedwapa! Tiyeni tonse tionetsetse kuti takonzekera kukakhala nawo pamsonkhano wonse, kuti tidzapindule kwambiri ndi phwando labwino lauzimu limene Yehova watikonzera kudzera m’gulu lake. Potero tidzakhala ‘okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino’ m’masiku otsatira.—2 Tim. 3:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena