Musasiye Chikondi Chimene Munali Nacho Poyamba
1 Yesu waulemerero anadzudzula mpingo wa ku Efeso kuti: “Ndakupeza ndi mlandu uwu, unasiya chikondi chimene unali nacho poyamba.” (Chiv. 2:4) Zikuoneka kuti ambiri anali atasiya kukonda Yehova ngati mmene ankamukondera poyamba. Pamene tinali kuphunzira choonadi, tinayamba kukonda kwambiri Mulungu ndi anzathu, ndipo zimenezi zinatichititsa kuuza ena mwachangu za chiyembekezo chathu, chomwe tinali titangochipeza kumene. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisasiye chikondi chimene tinali nacho poyamba ndi kuti tisazilale mu utumiki?
2 Kuchita Phunziro Laumwini ndi Kupezeka pa Misonkhano: Kodi n’chifukwa chiyani tinayamba kukonda Mulungu ndi anzathu titangophunzira kumene choonadi? Kodi si chifukwa cha zinthu zonse zimene tinaphunzira m’Malemba zokhudza Yehova? (1 Yoh. 4:16, 19) Choncho, kuti chikondi chathu “chipitirize kukula,” tiyenera kupitiriza kuphunzira zinthu zolondola, inde, kufufuza “zinthu zozama za Mulungu.”—Afil. 1:9-11; 1 Akor. 2:10.
3 Kutsatira ndandanda yabwino ya phunziro laumwini kukhoza kukhala kovuta masiku otsiriza ano, amene ali odzadza ndi nkhawa ndi zododometsa zambiri. (2 Tim. 3:1) Tiyenera kukhala ndi nthawi yodyera chakudya chauzimu. Kupezeka pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse n’kofunikanso kwambiri, makamaka ‘pamene tikuona kuti tsikulo likuyandikira.’—Aheb. 10:24, 25.
4 Kulalikira: Kulalikira mwachangu kumatithandiza kukondabe Mulungu ngati mmene tinkamukondera poyamba. Tikamalalikira uthenga wabwino, timadzikumbutsa za malonjezo achikondi a Yehova, ndipo zimenezi zimatithandiza kukhala ndi chiyembekezo cholimba ndi chikondi champhamvu. Kuti tiphunzitse ena mfundo za choonadi za m’Baibulo, timafunika kuchita kafukufuku kuti ifeyo patokha tizimvetse bwino mfundozo, ndipo kuchita zimenezi kumalimbitsa chikhulupiriro chathu.—1 Tim. 4:15, 16.
5 Yehova ndi woyenerera zinthu zonse, kuphatikizapo chikondi chathu. (Chiv. 4:11) Musalole kuti chikondi chanu chizilale. Khalanibe ndi chikondi cholimba chomwe munali nacho poyamba mwa kuchita phunziro la Baibulo laumwini, kupezeka pa misonkhano nthawi zonse, ndi kulalikira mwachangu zinthu zimene mumazikonda kwambiri.—Aroma 10:10.