Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 1
  • Chikondi N’chofunika Kuti Utumiki Ukhale Wopindulitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi N’chofunika Kuti Utumiki Ukhale Wopindulitsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Phunzitsani Mwachikondi Ngati Yesu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kondani Mulungu Amene Amakukondani
    Nsanja ya Olonda—2006
  • “Tizisonyezana Chikondi Chenicheni M’zochita Zathu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 1

Chikondi N’chofunika Kuti Utumiki Ukhale Wopindulitsa

1 “Bwerani kwa ine, . . . ndipo ndidzakutsitsimutsani.” (Mat 11:28) Yesu anali kukondadi anthu, choncho analankhula mawu ochokera pansi pa mtima amenewa. Monga atumiki achikhristu, timafuna kutsanzira Yesu posonyeza kuti timakonda anthu omwe alemetsedwa ndi dziko lopanda chikondili. Kodi tingachite bwanji zimenezi tikamalalikira uthenga wabwino?

2 M’mawu: Yesu anagwiritsira ntchito mpata uliwonse kulalikira uthenga wabwino chifukwa chakuti ankakonda anthu. (Yoh. 4:7-14) Chikondi chimatithandiza kuti tisazengereze kuchitira umboni mwamwayi. Mtsikana wina wa zaka 6, anachitira umboni wabwino kwa mzimayi wina amene anayandikana naye podikirira kuti aonane ndi dokotala kuchipatala. Kodi n’chiyani chimene chinam’chititsa zimenezo? Iye anafotokoza kuti, “Mzimayiyo ankaoneka kuti akufuna kudziwa za Yehova.”

3 Tingasonyeze kuti timaganizira anthu mwa kuwamwetulira mochokera pansi pa mtima ndi kulankhula nawo mwaubwenzi. Tingasonyezenso chikondi pomvetsera mosamala zimene ena akunena, kuzindikira nkhawa zawo, ndi kuwasonyeza chidwi chenicheni. (Miy. 15:23) Potsanzira Yesu, tiyenera kunena motsindika za uthenga wa Ufumu ndiponso za chikondi ndi chifundo chimene Yehova ali nacho pa anthu.—Mat. 24:14; Luka 4:18.

4 M’zochita: Yesu ankaganizira ena powapatsa thandizo lofunikira mwachangu. (Mat. 15:32) Ife tingapezenso mwayi wochita ntchito zosonyeza kukoma mtima kwachikondi tikamachita utumiki. Mlongo wina anaona kuti mzimayi wina akulephera kumvana bwino ndi munthu wina patelefoni. Mlongo wathuyo anadzipereka kumasulira uthenga wa patelofoniwo. Ntchito yosonyeza chikondi imeneyi inachititsa kuti ayambe kukambirana za m’Malemba zomwe zinathandiza kuti mzimayiyo avomereze phunziro la Baibulo. Nthawi ina mbale wina yemwe anali paulendo wobwereza, anapeza mwininyumba wina atathedwa nzeru, chifukwa choti mpando wa sofa wolemera unaphata pa khomo la nyumba yake. Atathandiza mwininyumbayo kuchotsa sofayo pakhomopo, mbaleyo posapita nthawi anakhala pa sofa yomweyo n’kuyamba phunziro la Baibulo ndi mwininyumba woyamikira ameneyu.

5 Tikamachita nawo utumiki, timasonyeza chikondi kwa Mulungu ndi kwa anansi athu. (Mat. 22:36-40) Kusonyeza chikondi m’mawu ndiponso m’zochita kumathandiza anthu oona mtima kuzindikira kuti tili ndi choonadi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena