Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • N’chifukwa Chiyani Tifunika Kubatizidwa?
    Nsanja ya Olonda—2002 | April 1
    • kwathu sitinadzipatulire pa ntchito kapena kwa munthu koma kwa Mulungu.

      15. N’chifukwa chiyani anthu ofuna kubatizidwa amawamiza m’madzi?

      15 Tikadzipatulira kwa Mulungu kudzera mwa Kristu, timasonyeza kutsimikiza mtima kwathu kugwiritsa ntchito moyo wathu pochita zimene Mulungu amafuna zomwe zili m’Malemba. Ofuna kubatizidwa amawamiza m’madzi monga chizindikiro cha kudzipatulira koteroko monganso mmene Yesu anabatizidwira mu mtsinje wa Yordano monga chizindikiro cha kudzipereka kwake kwa Mulungu. (Mateyu 3:13) N’zochititsa chidwi kuti Yesu anali kupemphera pa nthaŵi yofunika kwambiri imeneyo.​—Luka 3:21, 22.

      16. Kodi tingasangalale bwanji moyenera tikamaona anthu akubatizidwa?

      16 Ubatizo wa Yesu sunali chinthu chamaseŵera komabe unali wosangalatsa. N’chimodzimodzinso ndi ubatizo wachikristu lerolino. Tikamaona anthu akusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu, tingasangalale mwa kuwomba m’manja mwaulemu ndi kuwayamikira mwachikondi. Koma timapewa kukuwa, kuimba malikhweru, ndi kuchita zina zofanana ndi zimenezi poganizira kuti kusonyeza chikhulupiro kumeneku n’kopatulika. Timasangalala mwaulemu.

      17, 18. Kodi n’chiyani chimathandiza kuona ngati munthu akuyenerera ubatizo?

      17 Mosiyana ndi amene amawaza madzi makanda kapena kuumiriza anthu amene sanaphunzire Malemba kuti abatizidwe, Mboni za Yehova siziumiriza munthu kuti abatizidwe. Ndipotu, izo sizibatiza munthu amene alibe ziyeneretso za Malemba. Munthu asanakhale wofalitsa uthenga wabwino wosabatizidwa, akulu achikristu amaonetsetsa kuti munthuyo akudziŵa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo, akutsatira ziphunzitsozo, ndipo amayankha kuti inde funso lakuti, “Kodi mukufunadi kukhala Mboni ya Yehova?”

      18 Nthaŵi zambiri, munthu akamagwira nawo ntchito yolalikira Ufumu ndi kufuna kubatizidwa, akulu achikristu amakambirana naye munthuyo kuti atsimikize kuti ndi wokhulupiriradi amene wadzipatulira kwa Yehova ndipo akukwanitsa ziyeneretso za Mulungu za ubatizo. (Machitidwe 4:4; 18:8) Akulu amaona ngati munthuyo akukwaniritsa ziyeneretso za m’Malemba kuti abatizidwe pamene ayankha yekha mafunso oposa 100 okhudza ziphunzitso za m’Baibulo. Ena sakwaniritsa ziyeneretsozo motero sawalola kubatizidwa.

      Kodi Pali Chinachake Chimene Chikukulepheretsani?

      19. Malinga ndi Yohane 6:44, kodi ndani amene adzalamulira limodzi ndi Yesu?

      19 Anthu ambiri amene anawaumiriza kubatizidwa ayenera kuti anawauza kuti adzapita kumwamba akamwalira. Koma Yesu ponena za otsatira mapazi ake, anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.” (Yohane 6:44) Yehova wakokera kwa Kristu anthu 144, 000 amene adzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wa kumwamba. Kubatiza moumiriza sikunayeneretse wina aliyense kuti akakhale malo aulemerero amenewo m’makonzedwe a Mulungu.​—Aroma 8:14-17; 2 Atesalonika 2:13; Chivumbulutso 14:1.

      20. Kodi n’chiyani chingathandize anthu amene sanabatizidwe mpaka pano?

      20 Khamu la anthu amene akuyembekeza kudzapulumuka “chisautso chachikulu” ndi kudzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi aloŵa nawo m’gulu la “nkhosa zina” za Yesu makamaka kuyambira pakati pa m’ma 1930. (Chivumbulutso 7:9, 14; Yohane 10:16) Amayenerera ubatizo chifukwa chakuti amatsatira Mawu a Mulungu pa zochita zawo ndipo amamukonda ndi ‘mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi mphamvu zawo zonse, ndi nzeru zawo zonse.’ (Luka 10:25-28) Ngakhale kuti anthu ena amadziŵa kuti Mboni za Yehova ‘zimalambira Mulungu mumzimu ndi m’choonadi,’ sanatsatirebe chitsanzo cha Yesu ndi kusonyeza poyera umboni wa chikondi chenicheni ndi kulambira Yehova yekha mwa kubatizidwa. (Yohane 4:23, 24; Deuteronomo 4:24; Marko 1:9-11) Mapemphero ochokera pansi pa mtima ndiponso osapita m’mbali angawalimbikitse ndi kuwapatsa nyonga kuti atsatire Mawu a Mulungu, kudzipatulira kotheratu kwa Yehova Mulungu, ndi kubatizidwa.

      21, 22. Kodi n’zifukwa ziti zimene zimalepheretsa ena kudzipatulira ndi kubatizidwa?

      21 Ena sadzipatulira ndi kubatizidwa chifukwa chakuti atanganidwa kwambiri ndi zinthu za m’dzikoli kapena kufunafuna chuma kotero kuti alibe nthaŵi yokwanira yochita zinthu zauzimu. (Mateyu 13:22; 1 Yohane 2:15-17) Koma ngati akanasintha maganizo awo ndi zolinga zawo akanasangalalatu kwambiri. Kuyandikira kwa Mulungu kukanawalemeretsa mwauzimu, kukanawathandiza kuchepetsa nkhaŵa, ndiponso kukanawapatsa mtendere ndi chikhutiro zimene zimabwera ngati munthu achita chifuniro cha Mulungu.​—Salmo 16:11; 40:8; Miyambo 10:22; Afilipi 4:6, 7.

      22 Ena amanena kuti amakonda Yehova koma sadzipatulira ndi kubatizidwa chifukwa amaganiza kuti kusadzipatulira kuwathandiza kupeŵa kukhala ndi udindo kwa Mulungu. Komatu tonsefe, aliyense payekha ayenera kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu. Tinalandira udindo titamva mawu a Yehova. (Ezekieli 33:7-9; Aroma 14:12) Aisrayeli akale monga ‘anthu osankhidwa,’ anabadwira mu mtundu wodzipatulira kwa Yehova ndipo motero anali ndi udindo womutumikira mokhulupirika mogwirizana ndi malamulo ake. (Deuteronomo 7:6, 11) Lerolino, palibe amene amabadwira mumtundu wodzipatulira kwa Yehova, koma ngati talandira malangizo olondola a m’Malemba, tifunika kuchitapo kanthu mwachikhulupiriro.

      23, 24. Kodi ndi zinthu ziti zimene siziyenera kulepheretsa munthu kubatizidwa?

      23 Ena angalephere kubatizidwa chifukwa chodzikayikira kuti sakudziŵa zambiri. Komatu, pali zambiri zoti tonsefe tiziphunzire chifukwa “palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.” (Mlaliki 3:11) Taganizani za mdindo wa ku Etiopia. Iye monga wotembenukira ku Chiyuda, ankadziŵa Malemba koma sakanatha kuyankha mafunso onse okhudza zolinga za Mulungu. Komabe, ataphunzira za makonzedwe a Yehova a chipulumutso kudzera mu nsembe ya dipo ya Yesu, anabatizidwa m’madzi nthaŵi yomweyo.​—Machitidwe 8:26-38.

      24 Ena amazengereza kudzipatulira kwa Mulungu chifukwa amaopa kuti sadzakwaniritsa kudzipatulira kwawo. Mtsikana wina wa zaka 17 dzina lake Monique anati: “Ndakhala ndikukayika zoti ndibatizidwe chifukwa choopa kuti sindidzatha kupitiriza kukwaniritsa kudzipatulira kwanga.” Komabe, ngati tikhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse, ‘adzawongola mayendedwe athu.’ Adzatithandiza ‘kuyendabe m’choonadi’ monga atumiki ake odzipatulira okhulupirika.​—Miyambo 3:5, 6; 3 Yohane 4.

      25. Kodi ndi funso liti limene lifunika kukambirana?

      25 Kukhulupirira Yehova kotheratu ndi kumukonda ndi mtima wonse kumachititsa anthu ambirimbiri kudzipatulira ndi kubatizidwa chaka chilichonse. Ndipo n’zosachita kufunsa kuti atumiki odzipatulira a Mulungu onse amafuna kukhulupirika kwa iye. Komabe, tikukhala m’nthaŵi zowawitsa ndipo timakumana ndi mayeso a chikhulupiriro osiyanasiyana. (2 Timoteo 3:1-5) Kodi tingatani kuti tikwaniritse kudzipatulira kwathu kwa Yehova? Tikambirana funso limeneli m’nkhani yotsatirayi.

  • Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wokhazikika
    Nsanja ya Olonda—2002 | April 1
    • Pitirizani Kutumikira Yehova ndi Mtima Wokhazikika

      “Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima.”​—SALMO 57:7.

      1. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza mtima monga anachitira Davide?

      YEHOVA angatithandize kukhala okhazikika m’chikhulupiriro chachikristu kuti timamatire ku chikristu choona monga atumiki ake odzipatulira. (Aroma 14:4) Motero, tingakhale otsimikiza mtima monga wamasalmo Davide amene anaimba kuti: “Wakhazikika mtima wanga, Mulungu.” (Salmo 108:1) Mtima wathu ukakhala wokhazikika, udzatilimbikitsa kukwaniritsa kudzipatulira kwathu kwa Mulungu. Ndipo ngati tipempha iye kuti atitsogolere ndi kutipatsa mphamvu, tingakhale olimba pa kutsimikiza mtima kwathu ndi chikhulupiriro chathu monga anthu okhulupirika, “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse.”​—1 Akorinto 15:58.

      2, 3. Kodi malangizo a Paulo amene ali pa 1 Akorinto 16:13 akutanthauza chiyani?

      2 Mtumwi Paulo polangiza otsatira a Yesu mu mpingo wakale wa Korinto, malangizo omwe akugwiranso ntchito kwa Akristu lerolino, anati: “Dikirani, chirimikani m’chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.” (1 Akorinto 16:13) M’Chigiriki, mawu onseŵa akusonyeza kuti zimenezi ziyenera kuchitika mopitiriza. Kodi malangizo ameneŵa akutanthauza chiyani?

      3 ‘Tingadikire’ mwauzimu mwa kutsutsa Mdyerekezi ndi kuyandikira kwa Mulungu. (Yakobo 4:7, 8) Kudalira Yehova kumatithandiza kukhalabe ogwirizana ndi ‘kuchirimika m’chikhulupiriro chachikristu.’ Ife​—kuphatikizapo akazi ambiri amene tili nawo limodzi​—‘timadzikhalitsa amuna’ mwa kutumikira Mulungu molimba mtima monga olengeza Ufumu. (Salmo 68:11) ‘Timalimbika’ mwa kupitiriza kupempha Atate wathu wakumwamba kuti atipatse mphamvu kuti tichite zimene iye amafuna.​—Afilipi 4:13.

      4. Kodi tinachita chiyani kuti tibatizidwe monga Akristu?

      4 Tinasonyeza kuti talandira choonadi pamene tinadzipatulira kotheratu kwa Yehova ndi

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena