Aliyense Angapatse Yehova Chinachake
1 Kodi mukudziwa kuti anthu ali ndi zinthu zimene angapereke kwa Mulungu? Abele anapereka nsembe ziweto zake zabwino kwambiri kwa Yehova, Nowa ndi Yobu nawonso anachita chimodzimodzi. (Gen. 4:4; 8:20; Yobu 1:5) N’zoona kuti nsembe zimenezi sizinamulemeretse Mlengi mwa njira iliyonse, chifukwa zinthu zonse ndi zake kale. Koma nsembe zimenezo zinasonyeza kuti amuna okhulupirika amenewo anali kukonda kwambiri Mulungu. Masiku ano tingagwiritse ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu ndi chuma chathu, popereka kwa Yehova “nsembe yachitamando.”—Aheb. 13:15.
2 Nthawi: N’kofunika kwambiri ‘kuwombola’ nthawi ku zinthu zosafunika kwenikweni kuti tikhale ndi nthawi yokwanira yochita utumiki. (Aef. 5:15, 16) Mwina tingasinthe zochita zathu kuti tichite upainiya wothandiza mwezi umodzi kapena ingapo pachaka. Kapena tingawonjezere nthawi imene timakhala mu utumiki. Ngati titawonjezera mphindi 30 mlungu uliwonse, pamwezi tingapeze maola ena awiri.
3 Mphamvu: Kuti tikhale ndi mphamvu zochitira utumiki, timafunika kupewa zosangalatsa zotopetsa ndiponso kupewa kulowa ntchito imene ingamatitopetse kwambiri. Zinthu zimenezi zingatilepheretse kutumikira Yehova ndi mphamvu zathu zonse. Sitifunikiranso kudera nkhawa zinthu zambirimbiri, chifukwa nkhawazo ‘zingaweramitse’ mtima wathu ndi kutilanda mphamvu zimene tingagwiritse ntchito potumikira Mulungu. (Miy. 12:25) Ngakhale titakhala ndi chifukwa chomveka chodandaulira, zimakhala bwino kwambiri ‘kusenzetsa Yehova nkhawa zathu.’—Sal. 55:22; Afil. 4:6, 7.
4 Chuma: Tingathenso kupereka chuma chathu kuti chithandize pa ntchito yolalikira. Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘aziika kenakake pambali’ kuti nthawi zonse akhale ndi chopatsa osowa. (1 Akor. 16:1, 2) Ifenso masiku ano, tingaike pambali ndalama zoti tizipereka pothandiza zosowa za mpingo wathu ndiponso ntchito ya padziko lonse. Yehova amayamikira zimene timapereka ndi mtima wonse, ngakhale zitakhala zochepa.—Luka 21:1-4.
5 Yehova watipatsa zinthu zambiri. (Yak. 1:17) Timasonyeza kuyamikira zimene watipatsazi posaumira nthawi yathu, mphamvu zathu ndi chuma chathu pom’tumikira. Tikamatero timasangalatsa Yehova, “pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.”—2 Akor. 9:7.