Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi ‘Mukutsalima Pachothwikira’?
    Nsanja ya Olonda—2003 | October 1
    • Kodi ‘Mukutsalima Pachothwikira’?

      M’NTHAŴI za m’Baibulo, kachikwapu​—kamtengo kakatali kamene nthaŵi zambiri ankaika msomali kumapeto kwake​—anali kukagwiritsa ntchito poyendetsa ndi kulondolera nyama zimene zinali kukoka katundu wolemera. Kodi n’chiyani chinkachitika ngati nyama inasonyeza kukula mtima, osasamala kubaya kwa kachikwapuko, n’kumakhala ngati ikubwerera m’mbuyo? M’malo moti ipeze mpumulo, inali kungodzipweteka yokha.

      Yesu Kristu ataukitsidwa analankhula za chothwikira kapena kuti kachikwapu pamene anaonekera kwa mwamuna wotchedwa Saulo, amene anali kupita kukagwira ena mwa ophunzira a Yesu. Ataona kuwala kothobwa m’maso, Saulo anamva Yesu akunena kuti: “Saulo, Saulo, undilondalonderanji ine? nkukuvuta kutsalima pachothwikira.” Mwa kuzunza Akristu, Saulo anali kulimbana ndi Mulungu, anali kuchita zinthu zimene zikanamupweteka yekha.​—Machitidwe 26:14.

      Kodi zingachitikenso kuti ife mosadziŵa ‘tikutsalima pachothwikira’? Baibulo limati “mawu a anzeru” ali ngati zisonga, kapena kuti kachikwapu kamene kamatitsogolera kuti tiyende m’njira yoyenera. (Mlaliki 12:11) Malangizo ouziridwa a m’Mawu a Mulungu angatilimbikitse ndi kutitsogolera moyenera, ngati tiwalola kuti atero. (2 Timoteo 3:16) Kutsutsana ndi malangizo ameneŵa kudzangotipweteka.

      Saulo anamvera mawu a Yesu, anasintha khalidwe lake, ndipo anadzakhala Mkristu wokondedwa, mtumwi Paulo. N’chimodzimodzinso ndi ife. Kumvera malangizo a Mulungu kudzatibweretsera madalitso osatha.​—Miyambo 3:1-6.

  • Kodi Mungafune Kukuchezerani?
    Nsanja ya Olonda—2003 | October 1
    • Kodi Mungafune Kukuchezerani?

      Ngakhale m’dziko lino lodzala ndi mavuto, mungapeze chimwemwe mwa kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi chifuniro chake chabwino kwambiri kwa anthu. Ngati mukufuna kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani Mboni za Yehova, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 2.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena