Anachita Chifuniro cha Yehova
Zopereka Zaufulu Zopititsa Patsogolo Kulambira Koyera
AISRAYELI anali mboni zoona ndi maso mphamvu zopulumutsa za Yehova. Anaona madzi a Nyanja Yofiira akugaŵanika mozizwitsa, kuwalola kuti adutse panthaka youma ndi kuthaŵa gulu lankhondo la Igupto. Kutsidya linalo, ali pamalo abwino anaonerera pamene madzi omwewo anabwerera ndikuwomba gulu lowalondolalo mwamphamvu. Yehova anapulumutsa miyoyo yawo!—Eksodo 14:21-31.
Komabe momvetsa chisoni, Aisrayeli ena anapeputsa zimene Mulungu wawo anachita. Mose ali paphiri la Sinai, iwo anapatsa Aroni miyala yokongola yagolidi ndi kumuumiriza kuwapangira fano kuti alilambire. Pobwerera, Mose anapeza khamu la opanduka limeneli likudya, kumwa, kuvina, ndi kugwadira mwana wa ng’ombe wagolidi! Atalamulidwa ndi Yehova, anthu ngati 3,000, makamaka oyambitsa enieni a chipandukocho anaphedwa. Tsiku limenelo, anthu a Mulungu anatenga phunziro lofunika kwambiri lokhudza kufunika kwa kudzipereka kotheratu kwa Yehova.—Eksodo 32:1-6, 19-29.
Pambuyo pa chochitika chimenechi, Mose anakonzekera kuchita zimene Mulungu anam’lamula za kumanga chihema cholambiriramo chonyamulika. Ntchito yomanga imeneyi inafunikira zipangizo za mtengo wapatali ndi ogwira ntchito aluso. Kodi zimenezi zikanachokera kuti? Nanga tingaphunzirepo chiyani pa nkhani ya m’Baibulo imeneyi?
Kupereka Zipangizo ndi Maluso
Kudzera mwa Mose, Yehova analamula Aisrayeli kuti: “Mum’tengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima wom’funitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova.” Chopereka cha mtundu wanji? Mwa zinthu zimene Mose anatchula panali golidi, siliva, mkuwa, ulusi wolukira nsalu, nsalu, zikopa, mitengo, ndi miyala yamtengo wapatali.—Eksodo 35:5-9.
Aisrayeli anali ndi njira zambiri zopezera chopereka chaufulu chimenechi. Kumbukirani, pamene ankatuluka mu Igupto, anatuluka ndi zinthu za golidi ndiponso za siliva, pamodzi ndi nsalu zambiri. Ndithudi, ‘anawafunkha Aigupto.’a (Eksodo 12:35, 36) M’mbuyomo, Aisrayeliwo anali atapereka mooloŵa manja miyala yawo yokongola kuti apange fano la kulambira konyenga. Kodi tsopano iwo adzisonyeza kukhala ofunitsitsa kupereka kuti apititse patsogolo kulambira koona?
Musaiŵale kuti Mose sanaike mlingo wa kuchuluka kwa zinthu zimene aliyense anayenera kupereka, komanso sanawakakamize kupereka mwa kuwapangitsa kumva ngati a mlandu kapena kuwachititsa manyazi n’cholinga chowasonkhezera kuti apereke. M’malo mwake, iye anangopempha “aliyense wa mtima wom’funitsa mwini.” Mwachionekere Mose sanaone chifukwa choumirizira anthu a Mulungu. Anali ndi chikhulupiriro kuti aliyense angapereke zonse zomwe angathe.—Yerekezani ndi 2 Akorinto 8:10-12.
Komabe, ntchito yomanga inafunikira zambiri kuwonjezera pa zopereka za zipangizo. Yehova anauzanso Aisrayeli kuti: ‘Abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova wanena.’ Inde, ntchito yomanga imeneyi inafuna ogwira ntchito aluso. Ndithudi, “ntchito zilizonse,” kuphatikizapo kupala matabwa, kusula zitsulo, ndiponso kukongoletsa ndi miyala ya mtengo wapatali zinali zofunika kuti ntchito yomanga imeneyi imalizidwe. Ndithudi, Yehova ndiye anali kudzatsogolera maluso a ogwira ntchitowo, ndipo chiyamikiro chonse kaamba ka chipambano cha ntchitoyo chinayeneradi kupita kwa iye.—Eksodo 35:10, 30-35; 36:1, 2.
Aisrayeli anavomera ndi mtima wonse pempho limeneli la kupereka chuma chawo ndi maluso awo. Nkhani ya m’Baibuloyo imati: “Anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wam’funitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi kuutumiki wake wonse, ndi kuzovala zopatulika. Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eniake.”—Eksodo 35:21, 22.
Phunziro kwa Ife
Lerolino ntchito yaikulu ya kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ikuchitidwa ndi zopereka zaufulu. Nthaŵi zambiri, zopereka zaufulu zimenezi zimakhala ndalama. Nthaŵi zina, abale ndi alongo achikristu amagwiritsa ntchito maluso awo ochulukawo kuthandiza kumanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano ndi ofesi za nthambi. Ndiyeno pali ntchito imene ikuchitika panyumba za Beteli zoposa zana limodzi padziko lonse, ntchito imene imafuna maluso osiyanasiyana. Onse a mitima yofunitsitsa amene apanga zopereka zimenezi n’ngotsimikiza kuti Yehova sadzaiŵala ntchito yawo yaikulu!—Ahebri 6:10.
Zilinso chimodzimodzi ndi gawo limene aliyense wa ife ali nalo muutumiki wachikristu. Onse akulimbikitsidwa kuchita changu kuti akhale a khama pa kulalikira. (Mateyu 24:14; Aefeso 5:15-17) Ena amachita zimenezi monga alaliki a nthaŵi zonse, kapena apainiya. Chifukwa cha mikhalidwe, ena satha kuthera nthaŵi yochuluka mu utumiki monga momwe mpainiya amachitira. Komabe, nawonso akum’kondweretsa Yehova. Monga momwe zinalili ndi zopereka za chihema, Yehova saika mlingo wa kuchuluka kwa zimene aliyense ayenera kupereka. Komabe, zimene iye amafuna, ndi kuti aliyense wa ife am’tumikire ndi mtima wake wonse, moyo wake wonse, nzeru zake zonse, ndi mphamvu zake zonse. (Marko 12:30) Ngati tikuchita zimenezo, tingatsimikize kuti iye adzatipatsa mphotho chifukwa cha zopereka zaufulu zomwe timachita kuti tipititse patsogolo kulambira koona.—Ahebri 11:6.
[Mawu a M’munsi]
a Kumeneku sikuti kunali kuba. Aisrayeli anapempha zopereka kuchokera kwa Aigupto, ndipo zimenezi zinaperekedwa mwaufulu. Kuwonjezera pamenepo, chifukwa chakuti Aigupto poyambirira analibe ufulu wosandutsa Israyeli kukhala kapolo, iwo anali ndi mangaŵa kwa anthu a Mulungu ameneŵa chifukwa cha zaka zawo za muukapolo.