Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kugwira Ntchito “M’munda” Nyengo Yotuta Isanafike
    Nsanja ya Olonda—2000 | October 15
    • pang’ono kumwalira. Pamene George Storrs anayembekeza kubweranso kwa Kristu kuti kudzakhala kosaoneka, anaganiza kuti m’kupita kwa nthaŵi adzaoneka. Komabe, zikuoneka kuti amuna onse aŵiriŵa anali oona mtima, ndipo choonadi sanali nacho patali poyerekeza ndi ena ambiri.

      “Munda” umene Yesu ananena m’fanizo la tirigu ndi namsongole mbewu zake zinali zisanache kuti nyengo yotuta iyambe. (Mateyu 13:38) Grew, Storrs, ndi ena anali kugwira ntchito “m’munda” pokonzekera kututa.

      Charles Taze Russell, amene anayamba kusindikiza magazini ano mu 1879, analemba za zaka zake zoyambirira kuti: “Ambuye anatithandiza ndi anthu ambiri pophunzira Mawu Ake, amene mwa iwo panali wodziŵika bwino kwambiri, mbale wathu wokondedwa komanso wokalamba, George Storrs, amene anatithandiza kwambiri ponse paŵiri mwa kulankhula, komanso mwa kulemba. Koma sitinafune n’komwe kukhala otsatira anthu, kaya akhale abwino kapena anzeru motani, koma ‘Otsatira Mulungu monga ana okondedwa.’” Inde, ophunzira Baibulo oona mtima akanapindula ndi kuyesetsa kwa amuna ngati Grew ndi Storrs, koma kunali kofunikabe kuti apende Mawu a Mulungu, Baibulo, monga gwero lenileni la choonadi.​—Yohane 17:17.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2000 | October 15
    • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

      Potsatira malamulo a m’Baibulo onena za ntchito yoyenera ya magazi, kodi Mboni za Yehova zimaziona motani njira zakuchipatala zogwiritsa ntchito magazi ako omwe pokupatsa chithandizo?

      M’malo mongosankha malinga ndi zimene akulingalira kapena zimene wauzidwa ndi achipatala, Mkristu aliyense ayenera kulingalira mozama zimene Baibulo limanena. Ndi nkhani yokhudza iyeyo ndi Yehova.

      Yehova, amene ndiye mwini miyoyo yathu, analamula kuti magazi sayenera kudyedwa. (Genesis 9:3, 4) M’Chilamulo chimene anapatsa Aisrayeli akale, Mulungu anawaletsa kugwiritsa ntchito magazi chifukwa chakuti amaimira moyo. Analamula kuti: “Moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu.” Bwanji munthu atapha nyama kuti akadye? Mulungu anati: “Azikhetsa [“azitaya,” NW] mwazi wake, naufotsere ndi dothi.”a (Levitiko 17:11, 13) Yehova ananena lamulo limeneli mobwerezabwereza. (Deuteronomo 12:16, 24; 15:23) Buku lachiyuda lotchedwa Soncino Chumash limati: “Magaziwo sayenera kusungidwa koma ayenera kutayidwa pansi chifukwa ndi osayenera kudya.” Palibe Mwisrayeli aliyense amene anayenera kutenga, kusunga, ndi kugwiritsa ntchito magazi a cholengedwa china, chomwe moyo wake mwiniwake ndi Mulungu.

      Kuyambira pamene Mesiya anafa, anthu salinso okakamizika kutsatira Chilamulo cha Mose. Komano, Mulungu amaonabe magazi kukhala opatulika. Posonkhezeredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, atumwi analangiza Akristu ‘kusala mwazi.’ Limenelo linali lamulo lalikulu. Pankhani ya khalidwe, lamulolo linali lofunika mofanana ndi malamulo akuti apeŵe dama kapena kupembedza mafano. (Machitidwe 15:28, 29; 21:25) Pamene kupereka magazi ndi kuika anthu magazi kunafala m’zaka za m’ma 1900, Mboni za Yehova zinadziŵa kuti kuchita zimenezo n’kosemphana ndi Mawu a Mulungu.b

      Nthaŵi zina, dokotala amatha kuuza wodwala kuti apereke magazi ake kutatsala milungu ingapo kuti am’pange opaleshoni (m’Chingelezi njirayi imatchedwa preoperative autologous blood donation, kapena kuti PAD mwachidule) kuti ngati wodwalayo angadzafune magazi, adzamuike magazi ake omwe osungidwawo. Koma kutenga magazi kumeneku, kuwasunga, ndi kumuikanso wodwalayo kukuwombana mwachindunji ndi zimene zikunenedwa m’Levitiko ndi m’Deuteronomo. Magazi sayenera kusungidwa; ayenera kutayidwa​—kuwabwezera kwa Mulungu, tingatero kunena kwake. N’zoona kuti masiku ano sitikulamulidwa ndi Chilamulo cha Mose. Koma ngakhale zili tero, Mboni za Yehova zimamvera mfundo zachikhalidwe zimene Mulungu

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena