PHUNZIRO 8
Mphamvu ya Mawu Yoyenerera
NGATI wokamba nkhani pamaso pa anthu alankhula ndi mawu opola, omvera ena angayambe kuodzera kapena kuti kusinza. Ngati wofalitsa alankhula mopola mu utumiki wa kumunda, sangakope chidwi cha mwininyumba. Ndipo opereka ndemanga pamisonkhano ngati alankhula ndi mawu apansi, enawo salandira chilimbikitso chofunikiracho. (Aheb. 10:24, 25) Komanso, ngati wokamba nkhani akweza mawu ake panthaŵi yolakwika, omvera angaipidwenso—ngakhale kukwiya kumene.—Miy. 27:14.
Lingalirani Omvera Anu. Kodi mukulankhula kwa ndani? kwa munthu mmodzi? ku banja? ku gulu lokumana pokonzekera utumiki wa kumunda? ku mpingo wonse? kapena pa msonkhano wadera kapena wachigawo? N’kwachidziŵikire kuti mphamvu ya mawu yoyenerera pachochitika china, ingakhale yosayenera pachochitika china.
Pazochitika zosiyanasiyana, atumiki a Mulungu alankhula ku makamu aakulu. Potsegulira kachisi ku Yerusalemu m’masiku a Solomo, kunalibe zipangizo zokwezera mawu. Choncho, Solomo anaimirira pamalo okwera ndipo anadalitsa anthu “ndi mawu okweza.” (1 Maf. 8:55; 2 Mbiri 6:13) Patapita zaka mazana angapo, mzimu woyera utatsanulidwa pa Pentekoste wa mu 33 C.E., khamu la anthu—ena oyamikira, ena otonza—anazinga kagulu ka Akristu mu Yerusalemu. Posonyeza nzeru yothandiza, Petro “anaimirira . . . nakweza mawu ake.” (Mac. 2:14) Ulaliki wamphamvu unaperekedwa pamenepo.
Nanga mungadziŵe bwanji ngati mphamvu ya mawu imene mukulankhula nayo ndi yoyenerera pachochitikacho? Choyesera chabwino ndicho kuona mmene omvera akulabadirira. Ngati muona kuti ena akuchita kupendamitsa mutu poyesetsa kutchera khutu, wonjezerani mphamvu ya mawu.
Kaya tikulankhula kwa munthu mmodzi kapena gulu la anthu, ndi chanzeru kuona amene ali m’gulumo. Ngati pali amene amamva movutikira, mungafunikire kukweza mawu anu. Koma kukuwa kudzangopangitsa anthu kunyansidwa nanu. Dziŵani kuti ena amalabadira mochedwerapo, osati chifukwa chosatchera khutu ayi, koma ukalamba. Ndipo ena kukuwako angakuone ngati mwano. Kumadera ena, kukweza mawu kwambiri kumatanthauza kuti munthuyo wakwiya kapena ndi waphuma.
Ganizirani za Phokoso Losokoneza. Pamene muli mu utumiki wa kumunda, mphamvu ya mawu yoyenerera polalikira imadalira mikhalidwe imene mungakumane nayo. Mungafunikire kupikisana mawu ndi phokoso la magalimoto, kusokosera kwa ana, kuuwa kwa agalu, nyimbo zapawailesi zokwera kwambiri, kapena phokoso la wailesi yakanema. Komanso, m’madera amene nyumba n’zoyandikana kwambiri, munganyazitse mwininyumba ngati mulankhula mokweza kwambiri mpaka kusokosera anansi ake.
Abale amene amakamba nkhani mumpingo kapena pamisonkhano yaikulu ayeneranso kulimbana ndi mikhalidwe ina yosiyanasiyana. Kulankhula pamaso pa anthu pabwalo n’kosiyana kwambiri ndi kukamba nkhani m’holo mmene mawu amamveka mosavuta. Ku Latin America, amishonale aŵiri anagaŵana kukamba nkhani ya onse pakhonde la nyumba ya munthu wokondwerera. Nkhaniyo ili m’kati, mafayawekisi anali kuphulitsidwa m’misewu yapafupi komanso tambala anali kulira mosalekeza chapafupipo!
M’kati mwa nkhani, chinthu china chingachitike chimene chingafune kuti muyembekeze mpaka phokosolo litatha kapena kuti mukweze mawu anu. Mwachitsanzo, ngati msonkhano ukuchitikira m’nyumba ya malata (achitsulo), mvula ikayamba kugwa kungakhale kovuta kuti anthu amve zimene wokamba nkhani akunena. Ndiponso mwana wolira kapena anthu ofika mochedwa amadodometsa omvera. Phunzirani kuthana ndi zosokoneza zoterozo kuti omvera anu apindule kwathunthu ndi nkhani yanu.
Zipangizo zokwezera mawu ndi zothandiza zikakhalapo, koma sikuti wokamba nkhani sayenera kukweza mawu ake kukakhala kofunikira. Kumadera amene magetsi amathimathima, okamba nkhani amakakamizika kupitiriza nkhani zawo mosagwiritsa ntchito cholankhulira.
Ganizirani Uthenga wa Nkhani Yanu. Mphamvu ya mawu anu iyenera kudaliranso uthenga wa nkhaniyo. Ngati uthengawo ukufuna kuti mulankhule mwamphamvu, musaufooketse mwa kulankhula mofeŵa kwambiri. Mwachitsanzo, pamene mukuŵerenga chidzudzulo m’Malemba, mawu anu ayenera kukhala amphamvu kusiyana ndi poŵerenga uphungu wa kusonyeza chikondi. Gwirizanitsani mphamvu ya mawu ndi uthengawo, koma samalani kuti musachite zimenezo m’njira yochititsa omvera kumangoganiza za inuyo.
Ganizirani Cholinga Chanu. Ngati cholinga chanu ndi kulimbikitsa omvera kuti akhale okangalika pantchito, lankhulani ndi mawu amphamvu yokulirapo. Ngati mukufuna kusintha malingaliro awo, musawanyanyule mtima mwa kukweza mawu mopambanitsa. Ngati mukufuna kuwakhazika mtima pansi, kaŵirikaŵiri mawu ofeŵa ndiwo amachita bwino kwambiri.
Kugwiritsa Ntchito Mphamvu ya Mawu Mwaluso. Pamene mukuyesa kukopa chidwi cha munthu wotanganidwa, kaŵirikaŵiri mawu okwererapo amathandiza. Makolo amadziŵa zimenezi, ndiye chifukwa chake amakweza mawu poitana ana awo ikatha nthaŵi yoseŵera. Kukweza mawu kungakhalenso kofunikira pamene tcheyamani apempha anthu kukhala bata poyambitsa msonkhano wa mpingo kapena msonkhano waukulu. Pamene ofalitsa ali mu utumiki wa kumunda, angakweze mawu popereka moni kwa anthu ogwira ntchito panja.
Ngakhale mutakopa chidwi cha munthu, m’pofunikira kulankhulabe ndi mawu amphamvu oyenerera. Kulankhula ndi mawu otsinira kungamveke ngati wolankhulayo sanakonzekere bwino kapena ali wosatsimikiza kwenikweni zimene akunena.
Limodzi ndi kupereka chenjezo, kukweza mawu kungalimbikitse anthu kuchitapo kanthu. (Mac. 14:9, 10) Mofananamo, kuchenjeza mokweza mawu kungapeŵetse ngozi. Ku Filipi, wosunga ndende wina anatsala pang’ono kudzipha poganiza kuti akaidi omwe ankawayang’anira athaŵa. “Paulo anafuula ndi mawu akulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno.” Mwa njira imeneyi, munthu uja anapulumuka imfa yodzinyonga. Atatero, Paulo ndi Sila anakachitira umboni kwa wosunga ndendeyo limodzi ndi banja lake, moti onse analandira choonadi.—Mac. 16:27-33.
Mmene Mungakulitsire Luso Lolankhula ndi Mphamvu Yoyenerera. Anthu ena amafunikira kuyesetsa kwambiri kuti adziŵe kulankhula ndi mphamvu ya mawu yoyenerera. Munthu angamalankhule ndi mawu ochepa mphamvu chifukwa chokhala ndi mawu aang’ono. Komabe, mwakulimbikira akhoza kuchita bwino, ngakhale kuti angamalankhulebe mopolerapo. Samalani kapumidwe ndi kaimidwe kanu. Yesezani kukhala tsonga ndi kuimirira mowongoka. Kankhirani mapewa anu kumbuyo ndi kukoka mpweya wambiri. Onetsetsani kuti mukudzaza mpweya m’gawo la m’munsi la mapapu anu. Mpweya umenewu, mwa kupuma bwino, ndi umene umakuthandizani kusintha bwino mphamvu ya mawu polankhula.
Kwa ena, vuto limakhala kulankhula mokweza kwambiri. Mwina anakhala ndi chizoloŵezi chimenecho chifukwa chogwira ntchito panja kapena m’malo aphokoso kwambiri. Mwinanso anakulira pakati pa anthu okonda kulankhula mofuula ndi kudulana mawu. Pachifukwa chimenecho, iwo angaone kuti njira yokha yakuti amveke ndiyo kulankhula mokweza kuposa anzawo. Pamene akupitiriza kulabadira uphungu wa m’Baibulo wa kuvala “mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima,” angawongolere mphamvu ya mawu awo polankhula ndi ena.—Akol. 3:12.
Kukonzekera bwino, kuzoloŵera kutenga mbali mu utumiki wa kumunda nthaŵi zonse, ndi mapemphero kwa Yehova zidzakuthandizani kulankhula ndi mphamvu ya mawu yoyenerera. Kaya mukulankhulira papulatifomu kapena mu utumiki wa kumunda kwa munthu mmodzi, onetsetsani mmene munthuyo angathandizikire ngati amvera zimene mukunena.—Miy. 18:21.