Kugulitsa Malonda pa misonkhano Yathu Yachigawo
1 Popeza kuti misonkhano yachigawo ya chaka chino yakuti “Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova” yayandikira, tikufuna kukukumbutsani zinthu zina zokhudza khalidwe lathu pa misonkhano imeneyi. Malinga ndi zimene zinachitika pa misonkhano ya m’mbuyomu, zikuoneka kuti abale ena amachokabe pamalo a msonkhano kuti akagule chakudya kwa ogulitsa malonda m’mphepete mwa msewu kapena kumalesitilanti omwe ali pafupi panthawi yopuma. Ena amachita zimenezi msonkhano uli mkati. Kuwonjezera apo, enanso amadya kumene, nkhani za msonkhano zikukambidwa. Kuchita zimenezi ndi kupanda ulemu.
2 Kumalo ena, anthu ogulitsa zakudya afika mpaka poumirira kuti apatsidwe malo ogulitsirapo malonda awo chapafupi ndi malo a msonkhanowo. Kulola zimenezi kungapangitse kuti pa misonkhano pazikhala anthu ambiri amene si Mboni amene angasokoneze bata lathu pa misonkhanoyi.
3 Pa misonkhano ina yachigawo, abale ena amakambirana nkhani zosiyanasiyana zamalonda. Ena amabweretsa malonda awo monga nzimbe, mbatata, chinangwa, mpunga, mandasi, zitumbuwa, nthochi, ndiwo zamasamba ndi zinthu zina, n’cholinga choti agulitse kwa Akhristu anzawo. Si bwino kuchita zimenezi. Tiyenera kupeweratu kukambirana zamalonda kapena kugulitsa zinthu pamalo a misonkhano yachigawo. Kuchita zimenezi n’kosagwirizana ngakhale pang’ono ndi zifukwa zathu zosonkhanira pamodzi zimene Malemba amafotokoza.—Aheb. 10:24, 25.
4 M’pofunika Kusamala: Aliyense amene apite ku msonkhano wachigawo wa chaka chino wakuti “Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova” afunika kukumbukira zotsatirazi: Aliyense sakuloledwa kubweretsa zinthu zogulitsa pamalo a msonkhano wachigawo. N’kutheka kuti anthu ena angadzayale malonda awo pamalo a msonkhano, choncho abale ndi alongo komanso anthu ena amene asonkhana nafe asadzagule kanthu kalikonse kwa anthu amenewa. Kuti tipitirize kukhala aukhondo ndi adongosolo, m’pofunika kuti ogulitsa malonda asadzapezekepo n’komwe pamalo a msonkhano. Ngati abale akufuna kugula zinthu, akagule zinthuzo kumsika kapena kusitolo, ndipo achite zimenezo asanabwere ku msonkhano kapena akaweruka. Msonkhano usanayambe, akalinde ayenera kuuza ogulitsa malonda onse mwaulemu kuti asayale malonda awo pamalo athu olambirira. Ngati akufuna angakayale malonda awowo kutali ndi malo athu a msonkhano.
5 Ndife osangalala kwambiri kuti misonkhano yathu yachigawo yakuti “Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova” iyamba posachedwapa. Tiyeni tonse tionetsetse kuti takonzekera kukakhala nawo pa msonkhano wonse, kuti tidzapindule kwambiri ndi phwando labwino lauzimu limene Yehova watikonzera kudzera m’gulu lake. Tikachita zimenezi, tidzakhala ‘okonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino’ m’tsogolo muno.—2 Tim. 3:17.