Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 2/11 tsamba 22-23
  • Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimagwirizana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimagwirizana?
  • Galamukani!—2011
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sayansi Ili ndi Malire
  • Baibulo Linanena Zinthu Zimene Asayansi Anali Asanazidziwe
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaona Bwanji Sayansi?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Kodi Sayansi Imatithandiza Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Chilengedwe Chonsechi Ndiponso Zamoyozi Zinakhalako Bwanji?
    Galamukani!—2002
  • Kulenga
    Galamukani!—2014
Onani Zambiri
Galamukani!—2011
g 2/11 tsamba 22-23

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Sayansi ndi Baibulo Zimagwirizana?

“Ndikatulukira zinthu zatsopano, ndimaona kuti sayansi ndi yaphindu komanso yosangalatsa. Kenako mumtima ndimati, ‘Kani ndi mmene Mulungu anazipangira?’”—HENRY SCHAEFER, PULOFESA WA SAYANSI YA MMENE ZINTHU ZOSIYANASIYANA ZIMAPANGIDWIRA.

SAYANSI imatithandiza kwambiri kuti tizimvetsa zinthu zam’chilengedwe. Imasonyeza kuti zinthu zam’chilengedwe zimachitika mwadongosolo komanso mogometsa kwambiri, moti anthu ambiri amaona kuti zinthu zimenezi zinalengedwa ndi Mulungu, yemwe ali ndi nzeru komanso mphamvu zosayerekezereka. Iwo amaona kuti sayansi imafotokoza mmene zinthu zosiyanasiyana zam’chilengedwe zimachitikira komanso mmene Mulungu amaganizira.

Mfundo imeneyi ikugwirizananso ndi zimene Baibulo limanena m’mavesi ambiri. Mwachitsanzo, lemba la Aroma 1:20 limati: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Komanso lemba la Salimo 19:1, 2 limati: “Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu. Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake. Tsiku lililonse limanena mawu, ndipo usiku uliwonse umasonyeza nzeru.” Ngakhale kuti chilengedwe n’chogometsa, sitingaphunzire zinthu zonse zokhudza Mlengi pongoona chilengedwecho.

Sayansi Ili ndi Malire

Pali mfundo zambiri zokhudza Mulungu zimene sayansi singathe kufotokoza. Mwachitsanzo, wasayansi ataunika bwinobwino keke akhoza kukufotokozerani mmene kekeyo inapangidwira, koma kodi iye angathe kukufotokozerani kuti kekeyo anaphikira ndani kapenanso kuti anaiphika chifukwa chiyani? Kuti munthu adziwe yankho la mafunso amenewa, omwe anthu ambiri angaone kuti ndi ofunika kwambiri, afunika kufunsa munthu amene anaphika kekeyo.

Mofanana ndi chitsanzo chimenechi, wasayansi wina wa ku Austria amene analandirapo mphoto ya Nobel, dzina lake Erwin Schrödinger, anati: “[Sayansi] imayankha mafunso ambiri okhudza mmene zinthu zinapangidwira, koma sinena chilichonse pa zinthu zofunika kwambiri zimene anthufe timafuna titazidziwa bwino.” Wasayansiyu ananenanso kuti sayansi sinena chilichonse chokhudza “Mulungu komanso moyo wamuyaya.” Mwachitsanzo, ndi Mulungu yekha amene angathe kuyankha mafunso monga akuti, ‘N’chifukwa chiyani zinthu zomwe timaonazi zilipo? N’chifukwa chiyani dziko lapansi lili ndi zamoyo zambirimbiri, kuphatikizapo anthu? Ngati Mulungu ali Wamphamvuyonse, n’chifukwa chiyani amalola kuti padziko lapansi pazichitika zinthu zoipa komanso kuti anthu azivutika?’ Ndiponso lakuti, ‘Kodi anthu amene anafa, ali ndi chiyembekezo chilichonse?’

Mulungu amayankha mafunso amenewa ndipo mayankho ake amapezeka m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi ndingatsimikizire bwanji kuti Baibulo ndi lochokeradi kwa Mulungu?’ Ngati Baibulo lili lolondola, zimene limanena zokhudza dziko lathuli ziyenera kugwirizana ndi mfundo zotsimikizirika za sayansi zokhudza chilengedwe, chifukwa Mulungu sangadzitsutse yekha. Ndiye kodi zimene zili m’Baibulo zimagwirizana ndi sayansi? Taganizirani zitsanzo izi.

Baibulo Linanena Zinthu Zimene Asayansi Anali Asanazidziwe

Pa nthawi imene Baibulo linkalembedwa, anthu ambiri ankakhulupirira kuti kuli milungu yosiyanasiyana imene imalamulira kuyenda kwa dzuwa, mwezi, kusintha kwa nyengo, kubereka, ndi zinthu zina zotero. Iwo sankadziwa kuti zinthu zimenezi zimayenda motsatira malamulo a m’chilengedwe. Koma aneneri a Mulungu achiheberi ankadziwa zolondola. Iwo ankadziwanso kuti Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zolamulira kuyenda kwa zinthu zam’chilengedwe ndiponso kuti iye anachitadi zimenezi nthawi zingapo. (Yoswa 10:12-14; 2 Mafumu 20:9-11) Pulofesa wina wamasamu payunivesite ya Oxford, ku England, dzina lake John Lennox, ananena kuti aneneri amenewo “sanalembe zoti milungu ndi imene imalamulira kuyenda kwa zinthu zam’chilengedwe . . . chifukwatu iwo sankakhulupirira n’komwe milungu imeneyo. Chimene chinawathandiza kuti azidziwa zolondola pa nkhani imeneyi n’chakuti ankakhulupirira Mulungu mmodzi yekha woona, yemwe analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”

Kodi chikhulupiriro chimenechi chinawathandiza bwanji kupewa zinthu zabodza? Mwa zina, Mulungu woonayo anawavumbulira kuti iye amalamulira zinthu zonse pogwiritsa ntchito malamulo amene iye anakhazikitsa. Mwachitsanzo, zaka zoposa 3,500 zapitazo, Yehova Mulungu anafunsa mtumiki wake Yobu kuti: “Kodi malamulo akuthambo ukuwadziwa?” (Yobu 38:33) Komanso m’zaka za m’ma 600 B.C.E., mneneri Yeremiya analemba za “malamulo . . . akumwamba ndi dziko lapansi.”—Yeremiya 33:25.

Choncho anthu onse amene anakhalapo nthawi imeneyo, omwe ankakhulupirira zimene aneneriwa analemba m’Baibulo, ankadziwa kuti zinthu zam’chilengedwe siziyenda molamulidwa ndi milungu yosadziwika bwino komanso yankhanza, koma zimayenda motsatira malamulo a Mulungu wanzeru. N’chifukwa chake anthu okonda Mulungu amenewa sankalambira zinthu zimene Mulunguyo analenga, monga dzuwa, mwezi kapena nyenyezi, ndipo sankachita nazo mantha. (Deuteronomo 4:15-19) M’malomwake, iwo ankaona kuti kuphunzira za zinthu zimenezi kungawathandize kudziwa makhalidwe a Mulungu monga nzeru zake, mphamvu zake, ndi zina zotero.—Salimo 8:3-9; Miyambo 3:19, 20.

Mogwirizana ndi zimene asayansi ambiri amanena masiku ano, Aheberi ankakhulupiriranso kuti zinthu zam’chilengedwe zinali ndi chiyambi. Lemba la Genesis 1:1 limati: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Komanso zaka 3,500 zapitazo, Mulungu anaululira mtumiki wake Yobu kuti “anakoloweka dziko lapansi m’malere.” (Yobu 26:7) Ndiponso zaka zoposa 2,500 zapitazo, mneneri Yesaya analemba kuti dziko lapansi ndi lozungulira.—Yesaya 40:22.a

M’nkhaniyi taona kuti Baibulo limagwirizana ndi sayansi pofotokoza za zinthu za m’chilengedwe. Ndipotu kuwonjezera pa kugwirizana, sayansi ndi Baibulo zimathandiza kuti munthu afike pomudziwa bwino kwambiri Mulungu. Kunyalanyaza chimodzi kuli ngati kukana kutsegula khomo limene lingakuthandizeni kuti mudziwe zambiri zokhudza Mulungu.—Salimo 119:105; Yesaya 40:26.

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza mfundo yakuti Mulungu alipo komanso yakuti Baibulo ndi lolondola, werengani Galamukani! ya September 2006 ya mutu wakuti “Kodi Mlengi Alipo?” ndi ya November 2007 ya mutu wakuti “Kodi Tiyenera Kukhulupirira Baibulo?”

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● Kodi tingaphunzire zotani zokhudza Mulungu kuchokera m’zinthu zam’chilengedwe?—Aroma 1:20.

● Kodi n’zinthu zotani zokhudza Mulungu zimene sayansi singathe kufotokoza?—2 Timoteyo 3:16.

● Kodi n’chiyani chinathandiza aneneri a Mulungu akale kuti asamakhulupirire zinthu zolakwika zokhudza chilengedwe?—Yeremiya 33:25.

[Mawu Otsindika patsamba 23]

Zinthu zam’chilengedwe zimayendera malamulo olondola kwambiri, amene amatchedwa ‘malamulo akumwamba ndi dziko lapansi.’—YEREMIYA 33:25

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena