Sungani
Kodi Ndimaiona Bwanji Nkhani Yokhudza Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zachipatala Zogwiritsa Ntchito Magazi Anga Omwe?
Baibulo limalamula Akristu kuti “apewe . . . magazi.” (Mac. 15:20) Choncho Mboni za Yehova sizivomera kuikidwa magazi athunthu kapena zigawo zikuluzikulu zinayi za magazi, zomwe ndi maselo ofiira a m’magazi, maselo oyera a m’magazi, maselo othandiza magazi kuundana, ndi madzi a m’magazi. Ndiponso, sizipereka magazi kapena kusunga magazi awo kuti adzawathire m’tsogolo.—Lev. 17:13, 14; Mac. 15:28, 29.
Kodi tizigawo ta magazi n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani nkhani yogwiritsa ntchito timeneti ili yofunika kuti Mkristu aliyense adzisankhire yekha chochita?
Tizigawo ta magazi ndi tinthu ting’onoting’ono topezeka m’magazi timene amatha kutichotsa m’magazi. Mwachitsanzo, madzi a m’magazi, omwe ndi chigawo chimodzi mwa zigawo zinayi zikuluzikulu za magazi, akhoza kuwagawa kuti akhale m’zigawo zotsatirazi: madzi, omwe amapanga pafupifupi 91 peresenti ya magazi; mapuloteni, monga maalubumini, magulobulini, ndi fibulinojeni, zomwe zimapanga pafupifupi 7 peresenti ya magazi; ndi zinthu zina, monga zakudya, mahomoni, mpweya, mavitamini, zoipa za m’thupi, ndi michere ya m’thupi, zomwe zimapanga pafupifupi 1.5 peresenti ya magazi.
Kodi lamulo loti tipewe magazi limakhudzanso tizigawo ta magazi? Sitingapereke yankho lachindunji. Baibulo silipereka malangizo achindunji okhudza tizigawo ta magazi.a N’zoona kuti tizigawo tambiri ta magazi timatengedwa ku magazi amene aperekedwa ku chipatala. Mkristu aliyense ayenera kugwiritsa ntchito chikumbumtima chake kusankha kuvomera kapena kukana kugwiritsira ntchito zinthu zimenezi monga mankhwala.
Posankha zimenezi, ganizirani mafunso otsatirawa: Kodi ndikudziwa kuti kukana tizigawo tonse ta magazi kukutanthauza kuti sindingalandire mankhwala ena, monga mankhwala ena amene amalimbana ndi mavairasi ndi matenda, kapena amene amathandiza magazi kuundana n’kusiya kutuluka? Kodi ndingathe kufotokozera dokotala chifukwa chimene ndikukanira kapena kuvomerera tizigawo tina ta magazi?
Kodi n’chifukwa chiyani njira zachipatala zogwiritsira ntchito magazi anga omwe zili zofunika kuti ndisankhe ndekha chochita?
Ngakhale kuti Akristu sapereka magazi kapena kusunga magazi awo kuti adzawathire m’tsogolo, njira zina zochiritsira kapena kuyezera matenda zogwiritsa ntchito magazi a munthu sizichita kusemphaniranatu ndi mfundo za m’Baibulo. Choncho aliyense ayenera kugwiritsa ntchito chikumbumtima chake kusankha kuvomera kapena kukana njira zina zachipatala zogwiritsa ntchito magazi ake omwe.
Posankha zimenezi, dzifunseni mafunso otsatirawa: Ngati ena mwa magazi anga adzatulutsidwa kunja kwa thupi langa ndipo mwina akhoza kusiya kuyenda kwakanthawi, kodi chikumbumtima changa chidzandilola kuona kuti magazi amenewa akadali mbali ya thupi langa, choncho si ofunika kuti ‘athiridwe pansi’? (Deut. 12:23, 24) Kodi chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo chingandivutitse ngati pondiyeza kapena pondipatsa chithandizo chinachake m’chipatala anditenga magazi, n’kuwapanga zina ndi zina, kenako n’kuwabwezeranso m’thupi mwanga? Kodi ndikudziwa kuti kukana njira zonse zachipatala zogwiritsa ntchito magazi anga omwe kukutanthauza kuti ndikukana njira zoperekera chithandizo monga kugwiritsa ntchito makina osefa magazi kapena makina ogwira ntchito ya mtima ndi mapapo? Kodi ndapemphera kwa Mulungu poganizira za nkhani imeneyi ndisanasankhe zochita?b
Kodi ndasankha chiyani?
Taonani zikalata ziwiri zomwe zili pa masamba otsatirawa. Chikalata Choyamba chili ndi tizigawo tina timene timatengedwa m’magazi ndi mmene timagwiritsidwira ntchito nthawi zambiri kuchipatala. Lembani zomwe mwasankha, kuti kaya mukuvomera kapena kukana kugwiritsira ntchito kalikonse ka tizigawo timeneti. Chikalata Chachiwiri chili ndi njira zina zachipatala zofala zogwiritsa ntchito magazi anu omwe. Lembani zomwe mwasankha, kuti kaya mukuvomera kapena kukana kugwiritsira ntchito njira zimenezi. Zikalata zimenezi zilibe mphamvu ya lamulo, koma mukhoza kugwiritsa ntchito mayankho amene mwalemba pa zikalata zimenezi kuti akuthandizeni polemba khadi lanu la Chikalata Chosasinthika Chopatsa Munthu Mphamvu Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA).
Muyenera kusankha nokha zochita, osati kutengera zimene munthu wina wasankha chifukwa cha chikumbumtima chake. Mofanana ndi zimenezi, aliyense asadzudzule Mkristu wina chifukwa cha zosankha zake. Pa nkhani zimenezi, “aliyense ayenera kunyamula katundu wakewake.”—Agal. 6:4, 5.
[Mawu a M’munsi]
a Mfundo zothandiza pa nkhani imeneyi zikupezeka mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, tsamba 29 mpaka 31.
b Mfundo zothandiza pa nkhani imeneyi mukhoza kuzipeza mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2000, tsamba 30 mpaka 31, ndi m’mavidiyo kapena DVD ya Transfusion Alternative Strategies—Documentary Series.
[Tchati patsamba 5]
Chikalata Choyamba
ZOSAVOMEREZEKA ZOTI MUSANKHE NOKHA
KWA AKRISTU
MAGAZI Zimene Muyenera
ATHUNTHU TIZIGAWO TA MAGAZI Kusankha
MADZI A M’MAGAZI ALUBUMINI—AMATHA KUKWANA 4% YA MADZI A M’MAGAZI
Amenewa ndi mapulotini amene
amatengedwa m’madzi a m’magazi.
Mitundu ina ya alubumini imapezekanso
m’zomera, m’zakudya monga
mkaka ndi mazira, ndi mu mkaka wa mayi
woyamwitsa. Alubumini wa
m’magazi nthawi zina amaikidwa ․․ Ndikuvomera
m’madzi ochulukitsa magazi alubumini kapena
pothandiza munthu amene wavulala ․․ Ndikukana alubumini
kapena kupsa kwambiri.Madzi ochulukitsira
magazi amenewa akhoza kukhala ndi alubumini
wokwana mpaka 25% ya madzi onsewo. Alubumini
wochepa kwambiri amagwiritsidwa ntchito popanga
mankhwala ambiri, kuphatikizapo mitund ina ya
mankhwala omwe amachititsa kuti maselo ofiira
ambiri azipangidwa mkati mwa mafupa,
otchedwa erythropoietin (EPO).
MAGULOBULINI OTETEZA THUPI KU MATENDA
AMATHA KUKWANA 3% YA MADZI a M’MAGAZI
Awa ndi mapulotini omwe angagwiritsidwe
ntchito m’mankhwala amene amalimbana
ndi mavairasi ndiponso matenda, monga
chifuwa chokoka mtima, kafumbata, ․․Ndikuvomera
matenda a chiwindi oyambitsidwa magulobulini oteteza
ndi mavairasi, ndi chiwewe. thupi ku matenda kapena
Akhozanso kugwiritsidwa ․․Ndikukana magulobulini
ntchito kuteteza ku matenda oteteza thupi ku matenda
ena amene amaopseza moyo
wa khanda lomwe
silinabadwe ndi kuthetsa
mphamvu ya ululu wa
njoka kangaude.
MAPULOTINI OTHANDIZA MAGAZI KUUNDANA
—SAKWANA 1% YA MADZI A M’MAGAZI
Pali mapulotini osiyanasiyana
amene amathandiza magazi kuundana
n’kuwasiyitsa kutuluka. Ena amaperekedwa ․․Ndikuvomera mapulotini
kwa odwala amene sachedwa kutuluka othandiza magazi kuundana
Magazi.Amagwiritsidwanso ntchito mu opangidwa kuchokera ku magazi
gluu wa kuchipatala kuti atseke mabala kapena Ndikukana
ndi kusiyitsa magazi kutuluka munthu ․․ mapulotini othandiza
akachitidwa opaleshoni. Mtundu umodzi magazi kuundana
wa mapulotini othandiza opangidwa kuchokera kumagazi
magazi kuundana umatchedwa
cryoprecipitate. Dziwani izi:
Mapulotini ena
othandiza magazi kuundana
tsopano amapangidwa
kuchokera ku zinthu
zina, osati magazi.
MASELO OFIIRA HIMOGULOBINI—AMAKWANA 33% YA
A M’MAGAZI MASELO OFIIRA a M’MAGAZI
Amenewa ndi mapulotini amene
amanyamula mpweya wabwino kuupititsa
m’thupi monse ndi kuchotsa mpweya ․․ Ndikuvomera himogulobini
woipa m’mapapo. Mankhwala amene hemoglobin
akupangidwa kuchokera ku himogulobini kapena
wa m’magazi a anthu kapena a zinyama, ․․ Ndikukana
akhoza kugwiritsidwa ntchito himogulobini
kuchiza odwala amene
atha magazi kwambiri.
HEMINI—SAKWANA 2% YA
MASERO OFIIRA A M’MAGAZI
Awa ndi mapulotini ochokera
ku himogulobini amene amagwiritsidwa
ntchito kuchiza matenda omwe ․․ Ndikuvomera
si ofala kwambiri a m’magazi otengera hemini kapena
ku makolo, amene amagwira ziwalo ․․ Ndikukana hemini
zokhudzana ndi kugaya chakudya,
kutumiza mauthenga ku ubongo,
ndi kuyenda kwa magazi.
MASELO OYERA A M’MAGAZI MAINTAFIRONI—KACHIGAWO KAKANG’ONO
KWAMBIRI KA MASELO OYERA A M’MAGAZI
Awa ndi mapulotini amene amalimbana
ndi matenda ena oyambitsidwa ndi ․․ Ndikuvomera maintafironi
mavairasi ndi mitundu ina ochokera ku magazi
ya khansa. Maintafironi ambiri
sachokera ku magazi. Ena kapena
amapangidwa kuchokera ku tizigawo ․․ Ndikukana
ta maselo oyera a maintafironi
m’magazi a anthu. ochokera ku magazi
MASELO OTHANDIZA MAGAZI KUUNDANA Panopa, palibe tizigawo ta
maselo othandiza magazi
kuundana timene tikugwiritsidwa
ntchito mwachindunji ngati mankhwala.
[Tchati patsamba 6]
CHIKALATA CHACHIWIRI
ZOTI MUSANKHE NOKHA
NJIRA ZACHIPATALA ZOGWIRITSIRA NTCHITO MAGAZI ANU OMWE
*Dziwani izi: Kagwiritsidwe ntchito ka iliyonse ya njira zoperekera chithandizo zimenezi kamasiyanasiyana malinga ndi dokotala wake. Muziuza dokotala wanu kuti akufotokozereni bwinobwino za njira iliyonse imene akufuna kugwiritsa ntchito, kuti muonetsetse kuti ndi yogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo komanso ndi chikumbumtima chanu.
DZINA LA CHOLINGA Zimene Muyenera
CHITHANDIZO CHAKE Kusankha
(Mwina mungachite bwino
kulankhula ndi
dokotala wanu
musanavomere kapena
kukana iliyonse
ya njira zimenezi.)
KUPULUMUTSA MAGAZI Kumachepetsa magazi otayika.
Magazi amatengedwa
pabala kapena m’thupi ․․ Ndikuvomera
pochita opaleshoni. ․․ Ndikhoza kuvomera*
Amatsukidwa kapena ․․ Ndikukana
kusefedwa, kenaka amabwezeredwa
kwa wodwalayo,
mwina popanda kuwaimitsa.
KUSUNGUNULA MAGAZI Kumachepetsa magazi otayika.
Pochita opaleshoni, magazi
amapatutsidwira ku matumba
n’kulowedwa m’malo ndi madzi
owonjezera magazi m’thupi. Choncho ․․ Ndikuvomera
magazi otsala m’thupi la wodwalayo ․․ Ndikhoza kuvomera*
pochita opaleshoni amakhala osungunuka, ․․ Ndikukana
okhala ndi maselo ofiira ochepa.
M’kati mwa opaleshoniyo kapena
pamapeto pake, magazi
opatutsidwa aja
amabwezeredwa kwa
wodwalayo.
MAKINA OGWIRA NTCHITO Amathandiza magazi kupitirizabe kuyenda.
YA MTIMA NDI MAPAPO Magazi amapatutsidwira
ku makina ogwira ntchito ya mtima ․․ Ndikuvomera
ndi mapapo kumene amasakanizidwa ․․ Ndikhoza kuvomera*
ndi mpweya wa okosijeni ․․ Ndikukana
n’kubwezeretsedwa kwa wodwalayo.
MAKINA OSEFA MAGAZI Amagwira ntchito ngati chiwalo cha m’thupi.
Magazi amazungulira
m’makina mmene ․․ Ndikuvomera
amasefedwa ․․ Ndikhoza kuvomera*
n’kuyeretsedwa ․․ Ndikukana
asanawabwezere kwa wodwala.
KUMATA PABALA Kumasiyitsa kuchucha kwa madzi a mu msana.
NDI MAGAZI Magazi ochepa a wodwalayo
amaikidwa mu jakisoni
yemwe amabayidwa ․․ Ndikuvomera
mu mnofu wozungulira ․․ Ndikhoza kuvomera*
fupa la mu msana. ․․ Ndikukana
Amagwiritsidwa ntchito
kumatapabala pomwe
pakuchucha madzi a mumsana.
KUSEFA MADZI A M’MAGAZI Kumachiza matenda.
Magazi amachotsedwa m’thupi
n’kusefedwa kuti achotsemo Madzi.
Kenaka amathiramo zinthu
zina kuti zilowe m’malo mwa
madziwo, ndipo magaziwo ․․Ndikuvomera
amabwezeredwa kwa wodwalayo. ․․ Ndikhoza kuvomera*
Madokotala ena angafune ․․ Ndikukana
kugwiritsira ntchito madzi a m’magazi
a munthu wina kuti alowe m’malo mwa madzi
a m’magazi a wodwalayo. Ngati
angatero, zimenezi zikhoza
kukhala zosavomerezeka kwa Mkristu.
KUIKA MAGAZI Kumathandiza kutulukira kapena kuchiza matenda.
CHIZINDIKIRO Amatengako magazi pang’ono,
kuwasakaniza ndi mankhwala, ․․Ndikuvomera
kenaka n’kuwabwezera kwa ․․ Ndikhoza kuvomera*
wodwala. Nthawi imene magazi ․․ Ndikukana
a munthu ali kunja kwa thupi lake
ikhoza kukhala yosiyanasiyana.
GLUU WOPANGIDWA NDI Amamata zilonda, amachepetsa
MASELO OTHANDIZA MAGAZI magazi otaika.
KUUNDANA (WOPANGIDWA Magazi ena amawatulutsa
NDI MAGAZI m’thupi n’kuwasakaniza
ANU OMWE) ndi madzi okhala ndi
mapulotini ambiri oundanitsa ․․ Ndikuvomera
magazi komanso maselo oyera ․․ Ndikhoza kuvomera*
a m’magazi. Msakanizo umenewu ․․ Ndikukana
amaupaka pa mabala a opaleshoni
kapena pa zilonda zina. Dziwani izi:
Nthawi zina, amagwiritsa ntchito
zinthu zothandiza magazi
kuundana zochokera ku magazi a ng’ombe.