Ukwati
Tanthauzo: Kugwirizanitsidwa kwa mwamuna ndi mkazi kukhalira limodzi monga mwamuna ndi mkazi okwatirana mogwirizana ndi miyezo yolembedwa m’Malemba Opatulika. Ukwati uli kakonzedwe ka Mulungu. Umapereka unansi wapafupi pakati pa mwamuna ndi mkazi okwatirana limodzi ndi lingaliro lachisungiko chifukwa chakuti pali mkhalidwe wachikondi ndi chifukwa cha pangano limene linapangidwa ndi aliyense wa a muukwatiwo. Poyambitsa ukwati, Yehova sanatero kokha kuti agaŵire tsamwali wapafupi amene akakwaniritsa mwamuna chabe komanso kuti apange makonzedwe obalira anthu owonjezereka ndipo kutero mkati mwa kakonzedwe ka banja. Kulembetsa unansi waukwati m’kaundula kumene kuli kovomerezedwa mumpingo Wachikristu nkofunika paliponse ngati kuli kotheka.
Kodi kulidi kofunika kukwatira mogwirizana ndi zofunika zalamulo?
Tito 3:1: “Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera.” (Pamene anthu alabadira malangizo amenewa, dzina la aliyense wa a mumgwirizanowo limakhala lopanda mtonzo ndipo ana alionse amatetezeredwa kuchitonzo chimene chimakhala pa ana amene ali ndi makolo osakwatirana mwalamulo. Ndiponso, kulembetsa ukwati m’kaundula kumatetezera kuyenera kwa pa katundu kwa ziŵalo za banja ngati imfa ingagwere mmodzi wa okwatiranawo.)
Aheb. 13:4: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (Kulembetsa ukwati kumakhala ndi mbali yaikulu m’kuchititsa ukwati kukhala wovomerezedwa monga “wolemekezeka.” Polongosola tanthauzo la “dama” ndi “chigololo,” tiyenera kukumbukira zimene zafotokozedwa pa Tito 3:1, wogwidwa mawu pamwambapa.
1 Pet. 2:12-15: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuwona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira. Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino. Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa.”
Kodi panali “madzoma a lamulo” alionse pamene Adamu ndi Hava anayamba kukhalira pamodzi?
Gen. 2:22-24: “Ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu. Ndipo Adamu anati Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo azatchedwa mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna. Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Tawonani kuti anali Yehova Mulungu mwini, Mfumu yachilengedwe chonse, amene anabweretsa Adamu ndi Hava pamodzi. Imeneyi siinali nkhani yakuti mwamuna ndi mkazi asankhe kukhalira limodzi popanda kudera nkhaŵa ndi ulamuliro wa boma. Ndiponso wonani, chigogomezero chimene Mulungu anaika pa kukhalitsa kwa mgwirizanowo.)
Gen. 1:28: “Mulungu ndipo anadalitsa iwo [Adamu ndi Hava], ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m’nyanja, ndi pambalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.” (Panopa kugwirizanitsidwa kwawo kunali ndi dalitso la Waukumu walamulo wapamwamba koposa onse, iwo analolezedwa mwalamulo kupatsana mangaŵa awo aukwati ndipo anapatsidwa gawo limene likadzaza miyoyo yawo ndi tanthauzo.)
Kodi munthu angakwatire mitala ngati lamulo la m’dziko lake liiloleza?
1 Tim. 3:2, 12: “Woyang’anira akhale wopanda chirema, mwamuna wa mkazi mmodzi . . . Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi.” (Sikokha kuti amuna amenewa anaikiziridwa thayo komanso iwo anali zitsanzo zotsanziridwa ndi ena m’mpingo Wachikristu.)
1 Akor. 7:2: “Chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.” (Panopa palibe chilolezo cha kukhala ndi okwatirana ochuluka ku mbali iriyonse.)
Kodi nchifukwa ninji Mulungu analoleza Abrahamu, Yakobo, ndi Solomo aliyense wa iwo kukhala ndi mkazi woposa mmodzi?
Yehova sindiye woyambitsa mitala. Anapatsa Adamu mkazi mmodzi yekha. Pambuyo pake, Lameki, mbadwa ya Kaini, anadzitengera akazi aŵiri. (Gen. 4:19) M’kupita kwa nthaŵi ena anatsatira chitsanzo chake, ndipo ena anatenga akapolo achikazi kukhala adzakazi. Mulungu analekelera chizoloŵezicho, ndipo m’Chilamulo cha Mose anatchulamo mawu otsimikizira kuchitiridwa moyenerera kwa akazi amene anali ndi unansi wotere. Iye anachita zimenezi kufikira kukhazikitsidwa kwa mpingo Wachikritsu, ndiyeno pambuyo pake anafuna kuti atumiki ake abwerere kumuyezo umene iyemwini anayambitsa m’Edene.
Ponena za Abrahamu, iye anatenga Sarai (Sara) kukhala mkazi wake. Pamene iye anali pafupifupi zaka 75 zakubadwa nalingalira kuti sakabala mwana konse, iye anapempha mwamuna wake kugona ndi mdzakazi wake kotero kuti Sarai akakhale ndi mwana wapalamulo mwa iye. Abrahamu anatero, koma zimenezi zinatsogolera ku mkangano waukulu m’banja lake. (Gen. 16:1-4) Yehova anakwaniritsa lonjezo lake kwa Abrahamu lonena za “mbewu” mwa kuchititsa Sara iye mwiniyo kukhala ndi pakati mozizwitsa. (Gen. 18:9-14) Panali pambuyo pa imfa ya Sara kuti Abrahamu anakwatira mkazi wina.—Gen. 23:2; 25:1.
Yakobo anakhala wamitala chifukwa cha chinyengo chochitidwa ndi apongozi ake. Sindizo zimene Yakobo anali kuzilingalira pamene iye anapita kukafunafuna mkazi ku Padanaramu. Cholembedwa cha Baibulo chimasimba mwatsatanetsatane kwambiri ponena za mkangano womvetsa chisoni pakati pa akazi ake.—Gen. 29:18–30:24.
Kuli kodziŵika bwino lomwe kuti Solomo anali ndi akazi ambiri kuphatikizapo adzakazi. Koma sionse amene amazindikira kuti, mwakutero, iye anali kuswa lamulo la Yehova lofotokozedwa momvekera bwino lakuti mfumu ‘siyenera kudzichulukitsira akazi, kuti ungapatuke mtima wake.’ (Deut. 17:17) Kuyenera kudziŵikanso kuti, chifukwa cha chisonkhezero cha akazi ake achilendo, Solomo anatembenukira kukulambira milungu yonyenga ndipo ‘anayamba kuchita zoipa mmaso mwa Yehova . . . ndipo Yehova anakwiyira Solomo.’—1 Maf. 11:1-9.
Ngati okwatirana sangakhale konse pamodzi mu mtendere, kodi kulekana nkololeka?
1 Akor. 7:10-16: “Okwatitsidwawo ndiwalamulira, siine ayi, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna, komanso ngati amsiya akhale wosakwatiwa kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi. Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, [koma, monga vesi 40 likusonyezera, Paulo anatsogozedwa ndi mzimu woyera]: Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye. Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo. Pakuti mwamuna wosakhulupirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera. Koma ngati wosakhulupirayo achoka, achoke. M’milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere. Pakuti udziŵa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziŵa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?” (Kodi nchifukwa ninji wokhulupirira akafunikira kupirira mazunzo ndi kuyesayesa mwamphamvu kusunga ukwati kuti usathe? Chifukwa cha kuchitira ulemu Mulungu amene ali magwero aukwati ndi chiyembekezo chakuti m’kupita kwa nthaŵi wosakhulupirirayo angathandizidwe kukhala mtumiki wa Mulungu wowona.)
Kodi nchiyani chimene chiri lingaliro la Baibulo ponena za chisudzulo ncholinga cha kukwatiranso?
Mal. 2:15, 16: ‘Sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi waubwana wake ndi mmodzi yense. Pakuti ndidana nacho [chisudzulo], ati Yehova Mulungu wa Israyeli.’
Mat. 19:8, 9: “[Yesu] ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho. Ndipo ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo [kugonana kunja kwa ukwati], nadzakwatira wina, achita chigololo.” (Chotero wa muukwati wosalakwa amaloledwa, osati kukakamizidwa, kusudzula mnzake amene wachita “chigololo.”)
Aroma 7:2, 3: “Mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa kulamulo la mwamunayo. Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.”
1 Akor. 6:9-11: “Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna . . . sadzaloŵa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.” (Zimenezi zikugogomezera kuopsa kwa nkhaniyo. Achigololo osalapa sadzakhala ndi mbali mu Ufumu wa Mulungu. Chikhalirechobe, anthu amene kalero anali kuchita chigololo, mwinamwake kukwatiranso mosayenerera, angapeze chikhululukiro cha Mulungu ndi mkhalidwe woyera pamaso pake ngati iwo alapa mowona mtima nasonyeza chikhulupiriro mumtengo wa nsembe yotetezera machimo ya Yesu.)
Kodi nchifukwa ninji kalero Mulungu anali kuloleza ukwati pakati pa mbale ndi mlongo wake?
Cholembedwa cha Baibulo chimasonyeza kuti Kaini anakwatira mmodzi wa alongo ake (Gen. 4:17; 5:4) ndi kuti Abramu anakwatira mlongo wake mwa amayi wina. (Gen. 20:12) Koma pambuyo pake, m’Chilamulo choperekedwa kupyolera mwa Mose, maukwati otere analetsedwa mwachindunji. (Lev. 18:9, 11) Samaloledwa pakati pa Akristu lerolino. Kukwatirana ndi wachibale wapafupi kumachititsa kuthekera kwakukulukulu kwambiri kwakuti ziyambukiro zovulaza zachibadwa zidzapitirizidwira kwa ana awo.
Kodi nchifukwa ninji ukwati wa mbale ndi mlongo sunali wosayenera pachiyambi m’mbiri ya anthu? Mulungu analenga Adamu ndi Hava ali angwiro ndipo analinganiza kuti anthu onse achokere mwa iwo. (Gen. 1:28; 3:20) Mwachiwonekere kukwatirana kwa ena ndi achibale apafupi, makamaka m’kati mwa mibadwo yochepa yoyambirira, kukachitika. Ngakhale pambuyo pachiyambi cha uchimo, panali upandu wochepa wa kupunduka kodziŵika mwa ana mkati mwa mibadwo yoyambirira, chifukwa chakuti fuko laumunthu linali pafupi kwambiri ndi ungwiro umene Adamu ndi Hava anali nawo panthaŵiyo. Zimenezi zatsimikiziridwa ndi kutalika kwa nthaŵi ya moyo wa anthu. (Wonani Genesis 5:3-8; 25:7.) Koma pafupifupi zaka 2 500 Adamu atachimwa, Mulungu analetsa ukwati wa pachibale. Zimenezi zinatumikira kutetezera ana ndipo zinapititsa patsogolo miyezo ya makhalidwe abwino akugonana ya atumiki a Yehova kuposa ya anthu oŵazungulira amene panthaŵiyo anali kumachita machitachitama oluluzika amitundu yonse.—Wonani Levitiko 18:2-18.
Kodi nchiyani chimene chingathandize kuwongolera ukwati?
(1) Kuphunzirira Mawu a Mulungu pamodzi mokhazikika ndi kupemphera kwa Mulungu kaamba ka chithandizo m’kuthetsa mavuto.—2 Tim. 3:16, 17; Miy. 3:5, 6; Afil. 4:6, 7.
(2) Kuzindikira lamulo lamakhalidwe abwino la umutu. Limeneli limaika thayo lalikulu pamwamuna. (1 Akor. 11:3; Aef. 5:25-33; Akol. 3:19) Limafunikiritsa kuyesayesa kwamphamvu kumbali ya mkazi.—Aef. 5:22-24, 33; Akol. 3:18; 1 Pet. 3:1-6.
(3) Kulekezera mangaŵa a ukwati pa mnzanu wa muukwati. (Miy. 5:15-21; Aheb. 13:4) Kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka zosoŵa za mnzanu wa muukwati kungathandizire kumtetezera ku chiyeso cha kuchita cholakwa.—1 Akor. 7:2-5.
(4) Kulankhula m’mkhalidwe wachifundo, wodera nkhaŵa kwa wina ndi mnzake; kupeŵa mkwiyo, kulongolola, ndi mawu aukali osuliza.—Aef. 4:31, 32; Miy. 15:1; 20:3; 21:9; 31:26, 28.
(5) Kukhala wachangu ndi wodalirika m’kusamalira malo okhala banja ndi zovala, ndiponso m’kukonza chakudya chabwino.—Tito. 2:4, 5; Miy. 31:10-31.
(6) Kugwiritsira ntchito modzichepetsa uphungu wa Baibulo kaya mukulingalira kuti munthu winayo akuchita zothekera kapena sakutero.—Aroma 14:12; 1 Pet. 3:1, 2.
(7) Kupereka chisamaliro ku kakulidwe ka munthuwe kamkhalidwe wauzimu.—1 Pet. 3:3-6; Akol. 3:12-14; Agal. 5:22, 23.
(8) Kupereka chikondi chofunika, kuphunzitsa, ndi kulanga ana, ngati pali alionse.—Tito 2:4; Aef. 6:4; Miy. 13:24; 29:15.