Anthu ena amene ankadziona kuti ndi Akhristu anapitirizabe kulimbikitsa mdulidwe ngakhale kuti bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi linali litathetsa nkhaniyo. Mtumwi Paulo ananena kuti iwo anali “abale achinyengo” amene ankafuna “kupotoza uthenga wabwino wonena za Khristu.”—Agal. 1:7; 2:4; Tito 1:10.
Zikuoneka kuti cholinga cha gulu la Ayuda amenewa, omwe ankalimbikitsa kwambiri miyambo yawo, chinali chakuti asangalatse Ayuda ena kuti asamatsutse Akhristu ndiponso asamawazunze. (Agal. 6:12, 13) Gulu la Ayuda limeneli linkanena kuti munthu sangakhale wolungama ngati sakutsatira Chilamulo cha Mose pa nkhani ya chakudya, mdulidwe komanso zikondwerero za Ayuda.—Akol. 2:16.
M’pake kuti Akhristu a Chiyuda amene ankakhulupirira mfundo zimenezi sankamasuka kukhala ndi Akhristu anzawo amene sanali Ayuda. Ndipo n’zomvetsa chisoni kuti ngakhale Akhristu ena a Chiyuda odziwika bwino ankasonyezanso khalidwe limeneli. Mwachitsanzo, Akhristu amene anatumizidwa ku Antiokeya kuchokera ku Yerusalemu, anadzipatula ndipo sankachita zinthu limodzi ndi abale awo a mitundu ina. Ngakhale Petulo, amene poyamba ankacheza momasuka ndi anthu a mitundu ina, anadzipatula ndipo anasiya kudya nawo. Apatu Petulo anachita zinthu zosemphana ndi mfundo zimene iye poyamba ankalimbikitsa. Chifukwa cha zimenezi, Paulo anam’patsa uphungu wamphamvu kwambiri.—Agal. 2:11-14.