Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 139-tsamba 143
  • Gulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gulu
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Otetezereka m’Gulu Lolinganizidwa la Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Gulu Lowoneka la Mulungu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Yehova Ndi Mulungu Wadongosolo
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 139-tsamba 143

Gulu

Tanthauzo: Mgwirizano kapena chiungwe cha anthu amene zoyesayesa zawo zimagwirizanitsidwa kaamba ka ntchito yapadera kapena chifuno. Ziŵalo za gulu zimagwirizanitsidwa ndi makonzedwe oyendetsa zinthu ndi mwa miyezo kapena zofunika. Anthu amene ali mboni zodzipatulira ndi zobatizidwa za Yehova amaloŵa m’gulu la Yehova modzisankhira iwo eni, osati mwa kubadwiramo kapena mwa kukakamizidwa kulikonse. Iwo akokedwera kugulu lake lapadziko lapansi chifukwa cha ziphunzitso zake ndi ntchito ndipo chifukwa chakuti akufuna kugwira nawo ntchito imene likuchita.

Kodi Yehova alidi ndi gulu pano padziko lapansi?

Kuti tiyankhe funsolo, talingalirani zotsatirazi:

Kodi zolengedwa zakumwamba za Mulungu, angelo, nzolinganizidwa?

Dan. 7:9, 10: “Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu nikhalapo Nkhalamba yakale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofeŵa, ndi tsitsi lapamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malaŵi amoto, ndi njinga zake moto woyaka. Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosaŵerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabukhu anatsegulidwa.”

Sal. 103:20, 21: “Lemekezani Yehova, inu angelo ake; amphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa iye.” (“Khamu” ndiro kagulu kolinganizidwa.)

Kodi ndimotani mmene Mulungu anaperekera malangizo kwa atumiki ake padziko lapansi m’nthaŵi zakale?

Pamene olambira Yehova anali ochepa m’chiŵerengero, iye anapereka malangizo kumitu ya mabanja monga ngati Nowa ndi Abrahamu, ndiyeno iwo anachita monga olankhulira Yehova kumabanja awo. (Gen. 7:1, 7; 12:1-5) Pamene Yehova analanditsa Aisrayeli ku Igupto, anawapatsa malangizo kupyolera mwa Mose. (Eks. 3:10) Pa Phiri la Sinai, Mulungu analinganiza anthu kukhala mtundu, akumapatsa malamulo ndi malangizo oyendetsera kulambira kwawo ndi maunansi awo kwa wina mnzake. (Eks. 24:12) Iye anakhazikitsa unsembe kuti utsogolere m’nkhani za kulambira ndi kulangiza anthu m’zofunika za Yehova, panthaŵi zina iye anadzutsanso aneneri kupereka chilimbikitso ndi chenjezo zofunikazo kwa anthu. (Deut. 33:8, 10; Yer. 7:24, 25) Motero ngakhale kuli kwakuti Yehova anamvetsera mapemphero a olambirawo aliyense payekha, iye anapereka malangizo kwa iwo kupyolera mwa kakonzedwe ka gulu.

Pamene nthaŵi inayandikira yakuti Yehova ayambe kugwirizanitsa olambira owona ndi iyemwini kupyolera mwa Yesu Kristu, Mulungu anamtumiza kudziko lapansi kukachita monga wolankhulira Wake. (Aheb. 1:1, 2) Ndiyeno ndi kutsanuliridwa kwa mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E., mpingo Wachikristu unayambitsidwa. Yesu atabwerera kumwamba, mpingo uwu unafikira kukhala kakonzedwe ka Yehova ka kulangizira ndi kugwirizanitsira zoyesayesa za Akristu alionse paokha. Panali oyang’anira otsogolera m’mipingo yamomwemo, ndipo bungwe lolamulira la pamalikulu linapanga zosankha zofunika ndipo linathandizira kugwirizanitsa ntchito. Mwachiwonekere, Yehova anachititsa gululo kukhalako padziko lapansi lopangidwa ndi Akristu owona.—Mac. 14:23; 16:4, 5; Agal. 2:7-10.

Kodi ntchito ya Yehova ya chilengedwe chowoneka imasonyeza kuti iye ali Mulungu wagulu?

Yes. 40:26, NW: “Kwezani maso anu kumwamba muwone. Kodi ndani amene walenga zinthu zonsezi? Ndiye Amene ali kumatulutsa khamu lawo ngakhale mwa chiŵerengero, zonsezo iye amaziitana ngakhale ndi dzina. Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu yaikulu, iyenso pomakhala wolimba mu mphamvu, palibe chimodzi cha izo chikusoŵeka.” (Nyenyezi ziri mmagulu a milalang’amba ndipo zimayenda mogwirizana ina ndi inzake, ngakhale kuli kwakuti machitidwe a nyenyezi iriyonse ali osiyana. Maplaneti amayenda mwa nthaŵi yeniyeni, m’njira zozungulira zogaŵiridwa. Maelekitroni opezedwa m’maatomu alionse a chinthu chirichonse ali ndi njira zozungulira. Ndipo mpangidwe wa chinthu chirichonse umachita mogwirizana ndi zitsanzo za masamu zimene ziri zolondola kwambiri kotero kuti kunali kotheka kwa asayansi kuneneratu kukhalako kwa zinthu zina asanafikiredi pa kuzitulukira. Zonsezi zikupereka umboni wa kulinganizika kwapadera.)

Kodi Baibulo limasonyeza kuti Akristu owona ayenera kukhala anthu olinganizika?

Mat. 24:14; 28:19, 20, NW: “Mbiri yabwino imeneyi yaufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” “Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, mukumawabatiza . . . mukumawaphunzitsa.” (Kodi izi zingakwaniritsidwe motani popanda gulu? Pamene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake oyambirira kaamba ka ntchitoyi, Iye sanangouza aliyense payekha kumka kumene anakhumba ndi kukagaŵira chikhulupiriro chake mwanjira iriyonse imene anasankha. Iye anawaphunzitsa, nawapatsa malangizo ndipo anawatumiza mu mpangidwe wolinganizidwa. Wonani Luka 8:1; 9:1-6; 10:1-16.)

Aheb. 10:24, 25, NW: “Tiyeni tilingalirane kufulumizana ku chikondi ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga momwe ena aliri ndi chizoloŵezi, ndipo makamaka pamene mukuwona tsikulo likuyandikira.” (Koma kodi nkuti kumene munthu angatsogozeko anthu okondwerera kotero kuti amvere lamulo iri ngati panalibe gulu la misonkhano yanthaŵi zonse kumene akanasonkhanako?)

1 Akor. 14:33, 40, NW: “Mulungu saali Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere. . . . zinthu zonse zichitiketu molongosoka ndi molinganizidwa.” (Panopa mtumwi Paulo akulankhula za mchitidwe wolinganizika pamisonkhano yampingo. Kugwiritsira ntchito uphungu wouziridwa uwu kumafunikiritsa kuchitira ulemu gulu.)

1 Pet. 2:9, 17, NW: “Koma inu ndinu ‘fuko losankhika, unsembe wachifumu, mtundu wopatulika, anthu a chuma chapadera, kuti mulengeze kutali zabwino za iye amene anakuitanani kutuluka mu mdima kuloŵa m’kuunika kwake kodabwitsa. . . . Kondani mgwirizano wonse wa abale.” (Mgwirizano wa anthu umene zoyesayesa zake zalunjikitsidwa pa kukwaniritsa ntchito yapadera ndiro gulu.)

Kodi awo amene ali atumiki okhulupirika a Mulungu ali kokha anthu alionse paokha amene amwazikira m’matchalitchi osiyanasiyana a Dziko Lachikristu?

2 Akor. 6:15-18: “Wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira? . . . Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo ndipo patukani, ati ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo ine ndidzalandira inu. Ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.” (Kodi munthu alidi mtumiki wokhulupirika wa Mulungu ngati apitirizabe kukhala ndi phande m’kulambira limodzi ndi awo amene amasonyeza njira yawo ya moyo kuti alidi osakhulupirira? Wonani mutu waukulu wakuti “Babulo Wamkulu.”)

1 Akor. 1:10, NW: “Tsopano ndikupemphani, abale, kupyolera m’dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu kuti muyenera nonse kulankhula mogwirizana, ndi kuti pasakhale magaŵano pakati panu, koma kuti mukakhale ogwirizana bwino lomwe m’maganizo amodzimodzi ndi m’mzera umodzimodzi wa ganizo.” (Umodzi wotero sukupezeka pakati pa matchalitchi osiyanasiyana a Dziko Lachikristu.)

Yoh. 10:16: “Nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola iri; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Popeza kuti Yesu akachititsa anthu oterowo kukhala “gulu limodzi,” kodi sikuli kwachiwonekere kuti iwo sakakhala omwazikira m’zipembedzo za Dziko Lachikristu?)

Kodi gulu lowoneka la Yehova m’tsiku lathu lingadziŵidwe motani?

(1) Limalemekezadi Yehova monga Mulungu wowona yekha, kukuza dzina lake.—Mat. 4:10; Yoh. 17:3.

(2) Limazindikira mokwanira mbali ya Yesu Kristu m’chifuno cha Yehova—monga wochirikiza wa ufumu wa Yehova, Woimira Wamkulu wamoyo, mutu wampingo Wachikristu, Mfumu Yaumesiya yolamulirayo.—Chiv. 19:11-13; 12:10; Mac. 5:31; Aef. 1:22, 23.

(3) Limamamatira kwambiri ku Mawu ouziridwa a Mulungu, kuzika ziphunzitso zake zonse ndi miyezo ya khalidwe pa Baibulo.—2 Tim. 3:16, 17.

(4) Limalekana ndi dziko.—Yak. 1:27; 4:4.

(5) Limasunga muyezo wapamwamba wa chiyero cha makhalidwe pakati pa ziŵalo zake, chifukwa chakuti Yehova iyemwiniyo ngwoyera.—1 Pet. 1:15, 16; 1 Akor. 5:9-13.

(6) Limapereka zoyesayesa zake zazikulu kukuchitidwa kwa ntchito imene Baibulo lidaneneratu kaamba ka tsiku lathu, ndiko kuti, kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu m’dziko lonse kaamba ka umboni.—Mat. 24:14.

(7) Mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwaumunthu, ziŵalo zake zimakulitsa ndi kutulutsa zipatso za mzimu wa Mulungu—chikondi, chisangalalo, mtendere, kuleza mtima, chifundo, ubwino, chikhulupiriro, chifatso, kudziletsa—likumatero kumlingo wakuti zikuwapanga kukhala olekana ndi dziko lonse.—Agal. 5:22, 23; Yoh. 13:35.

Kodi tingasonyeze motani ulemu kaamba ka gulu la Yehova?

1 Akor. 10:31: “Chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”

Aheb. 13:17, NW: “Khalani omvera awo amene akutsogoza pakati panu ndi kukhala ogonjera, pakuti iwo akupitirizabe kuyang’anira miyoyo yanu monga awo amene adzafotokoza.”

Yak. 1:22: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha.”

Tito 2:11, 12: “Chawonekera chisomo cha Mulungu cha kupulumutsa anthu onse, ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.”

1 Pet. 2:17, NW: “Kondani mgwirizano wonse wa abale.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena