Mmene Mungayankhire Oyembekezera Kuimitsa Kukambitsirana
Ndemanga: Ziyembekezo za moyo wa anthu zimadalira pamkhalidwe wawo kulinga kwa Yehova Mulungu ndi Ufumu wake mwa Kristu Yesu. Uthenga wa Ufumu wa Mulungu ngwochititsa chidwi, ndipo umasonya ku chiyembekezo chokha chodalirika cha anthu. Ndiwo uthenga umene umasanduliza miyoyo. Timafuna kuti aliyense aumve. Timazindikira kuti ochepekera okha adzaulandira molabadira, koma tidziŵa kuti anthu ngofunikiradi kuumva ngati iwo ati apange chosankha chotsimikizirika. Komabe siyense amene ali wofunitsitsa kumvetsera, ndipo ife sitimayesayesa kuwakakamiza. Koma kaŵirikaŵiri mwaluso kuli kotheka kusanduliza oyembekezera kuimitsa kukambitsirana kukhala mwaŵi wa kukambitsirana kowonjezereka. Pano pali zitsanzo za zimene Mboni zachidziŵitso zagwiritsira ntchito m’zoyesayesa zawo za kufunafuna anthu oyenerera. (Mat. 10:11) Ife sitikuvomereza kuti muloŵeze pamtima alionse amayankho ameneŵa koma kuti muloŵetse lingalirolo m’maganizo, liikeni m’mawu a inu mwini ndi kulinena mwanjira imene imasonyeza chikondwerero chanu chowona mtima mwa munthu amene mukulankhula naye. Pamene mukutero, mungathe kukhala ndi chidaliro chakuti awo amene ali ndi mitima yolungama adzamvetsera ndi kuyankha molabadira ku zimene Yehova akuchita kuwakokera ku makonzedwe ake achikondi a moyo.—Yoh. 6:44; Mac. 16:14.
‘SINDIRI WOKONDWERERA’
● ‘Ndikufunseni, Kodi mukutanthauza kuti simuli wokondwerera Baibulo kapena ndicho chipembedzo chonse chimene simuli wokondwera nacho? Ndikufunsa motero chifukwa chakuti takumana ndi ambiri amene panthaŵi zina anali achipembedzo koma amene saali kupitanso kutchalitchi chifukwa chakuti amawona chinyengo m’matchalitchi (kapena, iwo akulingalira kuti chipembedzo ndicho bizinesi lina lopangira ndalama; kapena, iwo samavomereza kuloŵerera kwa chipembedzo m’ndale zadziko; ndi zina zotero). Baibulo nalonso silimavomereza zizoloŵezi zotero ndipo limatipatsa maziko okha oyang’anira mtsogolo ndi chidaliro.’
● ‘Ngati mutanthauza kuti simuli wokondwera ndi chipembedzo china, ndingathe kumvetsetsa zimenezo. Koma mwachiwonekere kwambiri muli wokondwera ndi mtundu wamtsogolo mmene tingathe kuyembekezera chifukwa cha chiwopsezo cha nkhondo yanyukliya (kapena, mmene tingatetezerere ana athu ku kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka; kapena, zimene zingachitidwe ponena za upandu kotero kuti sitidzafunikira kuchita mantha kuyenda m’makwalala; ndi zina zotero). Kodi mungathe kuwona chiyembekezo chirichonse cha njira yeniyeni yothetsera?’
● ‘Kodi chiri chifukwa chakuti muli kale ndi chipembedzo? . . . Tandiuzani, Kodi muganiza kuti tidzawona nthaŵi pamene munthu aliyense adzakhala wa chipembedzo chimodzimodzi? . . . Kodi nchiyani chimene chikuwonekera kukhala chopinga? . . . Kuti icho chikhale chopereka tanthauzo, kodi ndimaziko amtundu wotani amene akafunika?’
● ‘Ndingathe kuzindikira zimenezo. Zaka zoŵerengeka zapitazo ndinalingalira mwanjira yofananayo. Koma ndinaŵerenga kanthu kena m’Baibulo kamene kanandithandiza kuwona zinthu mosiyana. (Sonyezani munthuyo zimene kanthuko kanali.)’
● ‘Kodi mungakondwere ngati nditakusonyezani kuchokera m’Baibulo mmene mukanawonera akufa anu okondedwa kachiŵirinso (kapena, chimene kwenikweni chiri chifuno cha moyo; kapena, mmene lingatithandizire kusunga mabanja athu ali ogwirizana; ndi zina zotero)?’
● ‘Ngati mutanthauza kuti simuli wokondwera kugula kanthu kena, tandilolani kumasula maganizo anu. Ine sindikuchita ntchito yotsatsa malonda. Koma kodi mukakondwerera mwaŵi wakukhala ndi moyo padziko lapansi la paradaiso, lopanda matenda ndi upandu, limodzi ndi anansi amene kwenikweni amakukondani?’
● ‘Kodi limenelo ndilo yankho lanu lanthaŵi zonse pamene Mboni za Yehova zikufikirani? . . . Kodi kwenikweni munayamba mwadabwa chifukwa chake timapitirizabe kufika kapena zimene timanena? . . . Mwachidule, chifukwa chimene ndadzakuwonerani chiri chakuti ndimadziŵa kanthu kena kamene inunso muyenera kudziŵa. Bwanji osamvetsera kamodzi kokha kano?’
‘SINDIRI WOKONDWERA NDI CHIPEMBEDZO’
● ‘Ndingathe kumvetsetsa mmene mukulingalirira. Mosabisa mawu, matchalitchi sakupanga dziko lino kukhala malo otetezereka kwambiri a kukhalamo, kodi iwo akutero? . . . Ndiloleni ndikufunseni, Kodi inu nthaŵi zonse munali kulingalira mwanjira imene mukuchitira tsopano? . . . Koma kodi mumakhulupirira Mulungu?’
● ‘Pali anthu ambiri amene ali ndi lingaliro lanu. Kwenikweni chipembedzo sichinawathandize. Ndicho chifukwa china chimene tafikira—chifukwa chakuti matchalitchi sanauze anthu chowonadi chonena za Mulungu ndi chifuno chake chodabwitsa kaamba ka anthu.’
● ‘Koma ndiri wotsimikizira kuti muli wokondwera ndi mtsogolo mwa inu mwini. Kodi munadziŵa kuti Baibulo lidaneneratu mikhalidwe yeniyeni imene iri m’dziko lerolino? . . . Ndipo limasonyeza chimene chidzakhala chotulukapo chake.’
● ‘Kodi inu nthaŵi zonse mwalingalira mwanjirayo? . . . Kodi mumalingalira motani ponena za mtsogolo?’
‘SINDIRI WOKONDWERA NDI MBONI ZA YEHOVA’
● ‘Anthu ambiri amatiuza zimenezo. Kodi munayamba mwadabwa chifukwa chake anthu onga ine amadzipereka kucheza ndi anthu ngakhale kuli kwakuti timadziŵa kuti eninyumba ambiri sangatilandire? (Perekani mfundo yaikulu ya Mateyu 25:31-33, mukumalongosola kuti kulekanitsidwa kwa anthu amitundu yonse kukuchitika ndi kuti kulabadira kwawo ku uthenga wa Ufumu ndiko mbali yofunika m’zimenezi. Kapena longosolani mfundo yaikulu ya Ezekieli 9:1-11, mukumalongosola kuti, pamaziko a kulabadira kwa anthu ku uthenga wa Ufumu, aliyense ‘akuikidwa chizindikiro’ kaya cha kusungika kupulumuka chisautso chachikulu kapena cha kuwonongedwa ndi Mulungu.)’
● ‘Ndingathe kuzindikira zimenezo, chifukwa chakuti ndinali kulingalira mwanjira imodzimodziyo. Koma, kuti ndichite bwino, ndinasankha kumvetsera kwa mmodzi wa iwo. Ndipo ndinapeza kuti sindidauzidwa chowonadi ponena za iwo. (Tchulani chinenezo chimodzi chonama chodziŵika ndiyeno longosolani zimene timakhulupirira.)’
● ‘Sikale kwambiri pamene ndinanena chinthu chofananacho kwa Mboni ina imene inafika pakhomo panga. Koma iyo isanachoke ndinadzutsa funso limene ndinali wotsimikizira kuti sikakhoza kuyankha. Kodi mungakonde kumva chimene funsolo linali? . . . (Mwachitsanzo: Kodi nkuti kumene Kaini anapeza mkazi wake?)’ (Choti chigwiritsiridwe ntchito ndi awo amene analidi ndi chokumana nacho chimenechi.)
● ‘Ngati muli munthu wachipembedzo, ndingathe kuzindikira zimenezo. Mosakaikira chipembedzo chanu chimatanthauza zambiri kwa inu. Koma ndiganiza kuti mudzavomereza kuti aŵiri tonsefe tiri okondwerera mu (tchulani mutu wankhani wokambitsirana).’
● ‘Pamenepa mosakaikira inu muli ndi chipembedzo chanu. Kodi ndingafunse chimene chiri chipembedzocho? . . . Timasangalala kulankhula ndi anthu a chipembedzo chanu. Kodi mumalingalira motani za (tchulani mutu wanu wankhani wokambitsirana)?’
● ‘Inde, ndamva. Koma chifukwa chimene tafikira chiri chakuti ndife banja limene likakonda kuwona anthu akukhalira pamodzi m’mtendere. Tanyansidwa ndi kutopa nazo nkhani zamadzulo alionse zosimba zochitika zankhondo ndi kuvutika. Ndikhulupirira kuti ziri choncho kwa inu. . . . Koma kodi nchiyani chimene chingadzetse masinthidwe ofunikawo? . . . Tapeza chilimbikitso mu malonjezo Abaibulo.’
● ‘Ndikuyamikira kundiuza kwanu mmene mukulingalirira. Kodi mungakonde kundiuza chimene simumakonda pa ife? Kodi ziri zimene timakusonyezani kuchokera m’Baibulo, kapena kodi kuli kufika kwathu kudzacheza nanu?’
‘NDIRI NDI CHIPEMBEDZO CHANGA’
● ‘Kodi mungandiuze kuti, Chipembedzo chanu chimaphunzitsa kuti nthaŵi idzafika pamene anthu amene amakonda chilungamo adzakhala padziko lapansi kosatha? . . . Limenelo liri lingaliro losangalatsa, kodi sichoncho? . . . Liri muno m’Baibulo. (Sal. 37:29; Mat. 5:5; Chiv. 21:4)’
● ‘Ndikuvomereza kuti m’nkhaniyi munthu aliyense ayenera kupanga chosankha cha iye mwini. Koma kodi munadziŵa kuti Mulungu mwiniyo akufunafuna mtundu wina wa anthu kukhala olambira ake owona? Tawonani pano pa Yohane 4:23, 24. Kodi kukatanthauzanji kulambira Mulungu “m’chowonadi”? . . . Kodi Mulungu watipatsanji kutithandiza kudziŵa chimene chiri chowona ndi chimene sichiri? . . . (Yoh. 17:17) Ndipo tawonani mmene kuliri kofunika kwa ife mwachindunji. (Yoh. 17:3)’
● ‘Kodi mwakhala muli munthu wopembedza kwa moyo wanu wonse? . . . Kodi muganiza kuti anthu adzagwirizana m’chipembedzo chimodzi? . . . Ndalingalira kwambiri ponena za zimenezo chifukwa cha zimene zalembedwa pano pa Chivumbulutso 5:13. . . . Kodi nchiyani chimene chiri chofunika kwa ife kuti tiyenerere chithunzithunzi chimenechi?’
● ‘Ndinali kuyembekezera kupeza munthu wofanana ndi inu amene ali ndi chikondwerero m’zinthu zauzimu. Anthu ochuluka kwambiri lerolino saali. Kodi ndingafunse mmene mumalingalirira lonjezo la Baibulo lakuti Mulungu adzachotsa kuipa konse ndi kupanga dziko lino lapansi kukhala malo amene anthu okonda chilungamo okha adzakhalamo? Kodi zimenezo zimakukondweretsani?’
● ‘Kodi ndinu wokangalika kwambiri m’nkhani zatchalitchi? . . . Kodi kaŵirikaŵiri tchalitchicho chimadzala thothotho kaamba ka maulaliki masiku ŵano? . . . Kodi mumapeza kuti mamembala ambiri akusonyezadi chikhumbo chowona mtima cha kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu m’moyo wawo watsiku ndi tsiku? (Kapena, Kodi mumapeza kuti pali chigwirizano cha kuganiza pakati pa mamembala ponena za njira yothetsera mavuto amene akuyang’anizana ndi dziko?) Timapeza phunziro laumwini Labaibulo kukhala lothandiza.’
● ‘Mwachiwonekere muli wokhutira ndi chipembedzo chanu. Koma anthu ambiri saali okhutira ndi mikhalidwe ya dziko. Mwinamwake zimenezo ziri choncho ndi inunso; kodi sichoncho? . . . Kodi zonsezi zikutsogolera ku chiyani?’
● ‘Kodi ndinu munthu amene mumasangalala kuŵerenga Baibulo? . . . Kodi mumapeza nthaŵi ya kuliŵerenga pamlingo wokhazikika?’
● ‘Ndikuyamikira kuti mwandiuza zimenezo. Ndiri wotsimikizira kuti mudzavomereza kuti, mosasamala kanthu za chiyambi chathu cha chipembedzo, tonsefe tiri okondwera kwambiri ndi mtendere wadziko (kapena, njira zotetezerera ana athu ku ziyambukiro zoipa; kapena, ku kukhala ndi chitaganya m’chimene anthu amakondanadi wina ndi m’zake; kapena, kukhala ndi maunansi abwino ndi anthu ena, ndipo chimenecho chingathe kudzetsa chitokoso pamene munthu aliyense ali wotsenderezeka).’
● ‘Ndiri wokondwera kudziŵa kuti ndinu munthu wokonda chipembedzo. Anthu ambiri lerolino samalingalira chipembedzo mwamphamvu. Ena amatoganiza kuti kulibe Mulungu. Koma, mogwirizana ndi zimene mwaphunzitsidwa, kodi muganiza kuti Mulungu ndimunthu wamtundu wanji? . . . Tawonani kuti Baibulo limatipatsa dzina lake laumwini. (Eks. 6:3; Sal. 83:18)’
● ‘Pamene Yesu anatuma ophunzira ake kukalalikira, iye anawauza kupita kumbali iriyonse yadziko lapansi, motero iwo akakomana ndi anthu ambiri amene chipembedzo chawo chinali chosiyana ndi chawo. (Mac. 1:8) Koma iye anadziŵa kuti awo akumva njala ndi ludzu la chilungamo akamvetsera. Kodi ndiuthenga weniweni wotani umene adanena kuti ukaperekedwa m’tsiku lathu? (Mat. 24:14) Kodi Ufumu umenewo umatanthauzanji kwa ife?’
‘NDIFE AKRISTU KALE PANO’
● ‘Ndiri wokondwera kudziŵa zimenezo. Pamenepo inu mosakaikira mumadziŵa kuti Yesu anachita ntchito yonga iyi, kufikira anthu m’nyumba zawo, ndipo iye anatumanso ophunzira ake kuichita. Kodi inu muli wozoloŵerana ndi mutu wankhani wa kulalikira kumene adachita? . . . Ndizo zimene tadzera kudzalankhula lerolino. (Luka 8:1; Dan. 2:44)’
● ‘Pamenepo ndiri wotsimikizira kuti mudzadziŵa kufunika kwa zimene Yesu adanena pano mu Ulaliki wa pa Phiri. Iye anali wolunjika kwambiri komanso wosonyeza chikondi pamene adati . . . (Mat. 7:21-23) Pamenepa, funso limene tifunikira kudzifunsa, ndi iri, Kodi ndimadziŵa chifuniro cha Atate wakumwamba bwino motani? (Yoh. 17:3)’
‘NDIRI WOTANGANITSIDWA’
● ‘Pamenepo ndidzanena mwachidule kwambiri. Ndadzera kudzagaŵana nanu mfundo imodzi yokha yofunika. (Longosolani mfundo yaikulu ya mutu wankhani yanu wokambitsirana pafupifupi m’mawu aŵiri.)’
● ‘Chabwino. Ndidzakondwera kudzafika panthaŵi ina, pamene kudzakhala koyenerera kwambiri. Koma ndisanachoke, ndikakonda kuŵerenga lemba limodzi lokha limene limatipatsadi kanthu kena kofunika kakukalingalira.’
● ‘Ndamva. Monga mayi (kapena, mwamuna wogwira ntchito; kapena, wophunzira) ndirinso ndi programu yotanganitsidwa. Chotero ndidzachita mwachidule. Tonsefe timayang’anizana ndi mkhalidwe wowopsa. Baibulo limasonyeza kuti tiri pafupi kwambiri ndi nthaŵi pamene Mulungu adzawononga dongosolo loipa liripoli la zinthu. Koma padzakhala opulumuka. Funsolo nlakuti, Kodi inu ndi ine tiyenera kuchitanji kuti tikhale pakati pawo? Baibulo limayankha funso limenelo. (Zef. 2:2, 3)’
● ‘Mudziŵa, ndicho chifukwa chenichenicho chimene ndafikira. Tonsefe tiri otanganitsidwa—otanganitsidwa kwambiri kotero kuti nthaŵi zina zinthu zofunika kwambiri m’moyo zimanyalanyazidwa, kodi sichoncho? . . . Ndidzanena mwachidule kwambiri, koma ndiri wotsimikiza kuti mudzakondwera ndi lemba limodzi lokha iri. (Luka 17:26, 27) Palibe aliyense wa ife amene amafuna kudzipeza mu mkhalidwe umenewu, chotero timafuna kuti tipeze nthaŵi ya kuchita zimene Baibulo limanena m’miyoyo yathu yotanganitsidwa. (Perekani chogaŵira chabukhu.)’
● ‘Kodi kukakhala koyenerera koposerapo ngati tingadzafikenso pambuyo pa pafupifupi theka la ora, titatha kucheza ndi ena a anansi anu?’
● ‘Pamenepo sindidzakuchedwetsani. Mwinamwake ndingathe kudzafika tsiku lina. Koma ndisanachoke, ndingakonde kukupatsani mwaŵi wa kupeza chogaŵira chapadera ichi. (Sonyezani chogaŵira cha mweziwo.) Bukhu limeneli liri ndi kosi ya phunziro limene lidzakuzoloŵezetsani ndi mayankho Abaibulo lenilenilo pa mafunso onga akuti (tchulani limodzi lokha kapena aŵiri).’
● ‘Pepani kuti ndakufikirani panthaŵi yosayenerera. Monga mudziŵa, ndine mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndinafuna kugaŵana nanu mfundo yofunika kwambiri yochokera m’Baibulo. Koma popeza kuti pakali pano mulibe nthaŵi ya kumvetsera, ndikupatsani thirakiti iyi yofotokoza za (tchulani nkhani yake). Siikutengerani nthaŵi yaitali kuŵerenga, ndipo mudzasangalala nayo kwambiri.’
● ‘Zimenezo siziri zovuta kwa ine kuzimvetsetsa. Sikukuwonekeradi kukhala nthaŵi yokwanira ya kuchita kanthu kalikonse. Koma kodi munayamba mwalingalira mmene moyo ungakhalire wosiyana ngati mukanakhala ndi moyo kosatha? Ndidziŵa kuti zimenezo zingamvekere kukhala zachilendo. Koma taimani ndikusonyezeni lemba la Baibulo limodzi lokha limene limafotokoza mmene chinthu chotero chiriri chotheka. (Yoh. 17:3) Chotero, zimene tifunikira kuchita tsopano ndizo kuloŵetsa chidziŵitso chimenechi cha Mulungu ndi Mwana wake. Ndicho chifukwa chake tikusiya bukhu iri.’
‘KODI NCHIFUKWA NINJI ANTHU INU MUMAFIKA MWAKAŴIRIKAŴIRI?’
● ‘Chifukwa chakuti timakhulupirira kuti tikukhala ndi moyo m’masiku otsiriza onenedwa m’Baibulo. Timalingalira kuti kuli kofunika kwa ife tonse kulingalira za chimene chidzakhala chotulukapo cha mikhalidwe yamakonoyi. (Tchulani chochitika chimodzi kapena ziŵiri zaposachedwapa kapena mikhalidwe yatsopano.) Funsolo ndiiri, Kodi ife timafunikira kuchitanji ngati titi tipulumuke mapeto a dongosolo iri la zinthu?’
● ‘Chifukwa chakuti timakonda Mulungu ndi anansi athu. Ndizo zimene tonsefe tiyenera kuchita, kodi sichoncho?’
‘NDIRI WOZOLOŴERANA KALE NDI NTCHITO YANU’
● ‘Ndakondwera kwambiri kumva zimenezo. Kodi muli ndi wachibale wapafupi kapena bwenzi la amene ali Mboni? . . . Ntakufunsani: Kodi mumakhulupirira zimene timaphunzitsa kuchokera m’Baibulo, ndiko kuti, kuti tikukhala ndi moyo ‘m’masiku otsiriza,’ kuti mwamsanga Mulungu adzawononga oipa, ndi kuti dziko lapansi iri lidzakhala paradaiso mmene anthu angakhalemo ndi moyo kosatha m’thanzi langwiro pakati pa anansi amene amakondanadi wina ndi mnzake?’
‘TIRIBE NDALAMA’
● ‘Ife sitikupempha ndalama. Koma tikugaŵira kosi yaulere ya phunziro la Baibulo lapanyumba. Imodzi ya nkhani zimene imafola njakuti (gwiritsirani ntchito mutu wankhani wa chaputala china m’bukhu latsopano). Kodi ndingatenge mphindi zoŵerengeka kukusonyezani mmene limagwirira ntchito? Simudzafunikira kulipira khobidi lirilonse.’
● ‘Tikufuna anthu, osati ndalama zawo ayi. (Pitirizani makambiranowo. Asonyezeni buku ndi kuwafotokozera mmene lingawathandizire. Ngati aonetsa chidwi chenicheni ndipo alonjeza kuti akaŵerenga, asiyireni. Ngati kuli koyenera, fotokozani kumene ndalama zimachokera zothandiza pantchito yathu yolalikira padziko lonse.)’
PAMENE MUNTHU ANENA KUTI, ‘NDINE MBUDDHA’
● Musangonena kuti zikhulupiriro za munthuyo ziri zofanana ndi za Abuddha ena onse. Ziphunzitso Zachibuddha ziri zocholoŵana ndipo matanthauziridwe amasiyana pa anthu osiyanasiyana. Chibuddha cha ku Japani chiri chosiyana ndi Chibuddha cha ku Southeast Asia. Nawonso, anthu alionse paokha amasiyana m’lingaliro lawo. Komabe, kaŵirikaŵiri, mfundo zotsatirazi zingakhale zothandiza: (1) Chibuddha sichimakhulupirira kuti kuli Mulungu wakunja, Mlengi amene ali munthu. Koma Abuddha ambiri amalambira mafano ndi zinthu zopatulika za Buddha. (2) Siddhartha Gautama, amene anapatsidwa dzina laulemu lakuti Buddha, anafikira pa kuwonedwa kukhala chitsanzo chachipembedzo cha otsatira ake, woyenera kutsanziridwa ndi iwo. Iye analimbikitsa kupeza kuunikiridwa mwa kuphunzira anthu mwa lingaliro la anthu, ndiponso kuchotsa magwero a kuvutika mwa kulamulira maganizo kuti achotse zikhumbo zonse za dziko lapansi. Anaphunzitsa kuti mwanjira imeneyi munthu angafikire Nirvana, womasuka ku kubadwanso m’cholengedwa china. (3) Abuddha amalambira makolo awo akale, chifukwa chakuti amawona amenewa monga magwero a moyo wawo.
Malingaliro a kukambitsirana: (1) Polankhula ndi Abuddha, auzeni kuti simuli mbali ya Dziko Lachikristu. (2) Abuddha amachitira ulemu “mabukhu opatulika,” ndipo kaamba ka chifukwa chimenecho kaŵirikaŵiri amalemekeza Baibulo. Mmalo mwa kutaya nthaŵi yaitali pa nthanthi ndi nzeru Zachibuddha, perekani uthenga wotsimikizirika wa Baibulo. Adziŵitseni kuti Baibulo siliri chabe nzeru ya anthu koma Mawu okhala ndi ukumu a Mlengi wa anthu, Yehova Mulungu. Funsani mwachifatse ngati mungawasonyeze mfundo ina yokondweretsa m’bukhu lopatulika limeneli, Baibulo. (3) Abuddha ambiri amakondwerera kwambiri mtendere ndi moyo wabanja ndipo amafuna kukhala ndi miyoyo ya makhalidwe abwino. Kaŵirikaŵiri makambitsirano okhudza mfundo zimenezi amalandiridwa. (4) Sonyezani kuti Baibulo limasonya kuboma lakumwamba lachilungamo lodzalamulira padziko lapansi kukhala njira yeniyeni yothetsera mavuto oyang’anizana ndi anthu. Limalongosola mtsogolo mwa dziko lapansi ndi chiyembekezo chodabwitsa cha kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso. (5) Mungasonyeze kuti Baibulo limalongosola magwero a moyo, tanthauzo la moyo, mkhalidwe wa akufa ndi chiyembekezo cha chiukiriro, chifukwa chimene kuipa kwakhalirapo. Ulaliki woperekedwa mokoma mtima wa chowonadi chenicheni cha Mawu a Mulungu udzapeza kulabadira kwabwino m’mitima ya onga nkhosa.
Kabukhu kakuti In Search of a Father kanalinganizidwira makamaka kuthandiza Abuddha owona mtima.
PAMENE MUNTHU ANENA KUTI, ‘NDINE MHINDU’
● Mufunikira kudziŵa kuti nthanthi Yachihindu njocholoŵana kwambiri ndipo njosakhoza kulongosoleka. Mungakupeze kukhala kothandiza kuzindikira mfundo zotsatirazi: (1) Chihindu chimaphunzitsa kuti mulungu Waubrahma amaphatikizapo mipangidwe itatu—Brahma Mlengi, Vishnu Wotetezera, ndi Siva Wowononga. Koma Ahindu samaganiza za mulungu weniweni amene amakhala ndi moyo payekha. (2) Ahindu amakhulupirira kuti zinthu zonse za chilengedwe ziri ndi moyo umene sumafa konse, kuti kwenikweni moyo uli ndi zungulirezungulire wosatha wa kubadwanso, kuti mipangidwe imene umabadwiranso imatsimikiziridwa ndi ntchito (Karma), kuti kumasuka kuchokera ku “gudumu losatha” limeneli kuli kotheka kokha mwa kuchotsa zikhumbo zonse zakuthupi, ndi kuti zimenezi zitatulukiridwa, moyowo ukatsagana ndi mzimu wa chilengedwe chonse. (3) Kaŵirikaŵiri, Ahindu amalemekeza zipembedzo zina. Ahindu amakhulupirira kuti, mosasamala kanthu za chenicheni chakuti zimaphunzitsa ziphunzitso zotsutsana, zipembedzo zonse zimatsogolera ku chowonadi chimodzimodzi.
Mmalo mwa kuyesayesa kuyang’anizana ndi zocholoŵana za nthanthi Yachihindu, perekani chowonadi chokhutiritsa maganizo chopezedwa m’Baibulo Lopatulika. Makonzedwe achikondi a Yehova kaamba ka moyo ngotsegukira anthu amitundu yonse, ndipo chowonadi chomvekera bwino m’Mawu ake chidzafikira mitima ya akumva njala ndi ludzu la chilungamo. Baibulo lokha limapereka chiyembekezo chamtsogolo chokhaladi ndi maziko abwino; Baibulo lokha limapereka mayankho okhutiritsadi a mafunso ofunika amene amayang’anizana ndi anthu onse. Apatseni mwaŵi wa kumva mayankho amenewo. Kuli kokondweretsa kuti nyimbo Yachihindu Rig-Veda, 10. 121, iri ndi mutu wakuti “Kwa Mulungu Wosadziŵika.” M’zochitika zina mungakupeze kukhala koyenerera kusonya kumfundoyi mwanjira yofanana ndi mmene mtumwi Paulo anasonyera guwa lansembe lotchedwa “Kwa Mulungu Wosadziŵika” mu Atene. (Mac. 17:22, 23) Mokondweretsa, dzina la Mulungu wa Ahindu Vishnu, popanda lemba loyambirira, ndiye Ish-nuh, limene m’Chikaldayo limatanthauza “mwamunayo Nowa.” Sonyezani zimene Baibulo limanena ponena za tanthauzo la Chigumula chadziko lonse m’masiku a Nowa. Awo amene ali onyansidwa ndi chiyembekezo cha kubadwanso kosatha angathandizidwe ndi mawu a patsamba 177-179, pamutu wakuti “Kudziveka Thupi Lanyama.”
Timabukhu ta The Path of Divine Truth Leading to Liberation ndi From Kurukshetra to Armageddon—And Your Survival tiri ndi mawu amene adzakhala othandiza kwambiri kwa Ahindu owona mtima.
PAMENE WINA ANENA KUTI, ‘NDINE MYUDA’
● Choyamba, pendani mmene munthuyo amadziwonera monga Myuda. Ochepa ngachipembedzo. Kwa ambiri, kukhala Myuda kuli chabe mtundu wawo.
Nazi mfundo zoŵerengeka zimene ziri zothandiza kuzilingalira: (1) Ayuda opembedza amawona kutchulidwa kwa dzina la Mulungu kukhala koletsedwa. (2) Ayuda ambiri amalingalira “Baibulo” kukhala bukhu Lachikristu, koma ngati mutchula kuti “Malemba Achihebri,” “Malemba Opatulika,” kapena “Tora,” vuto limeneli silimabuka. (3) Mwambo ndiwo mbali yaikulu ya chikhulupiriro chawo ndipo umawonedwa ndi Ayuda ambiri opembedza kukhala ndi ulamuliro wofanana ndi Malemba. (4) Angagwirizanitse Yesu Kristu ndi chizunzo chankhanza chimene Ayuda anakumana nacho padzanja la Dziko Lachikristu m’dzina la Yesu. (5) Kaŵirikaŵiri iwo amakhulupirira kuti Mulungu amafuna kuti Ayuda asunge Sabata, chikhulupiriro chimene chimaphatikizapo kusagwira ndalama patsiku limenelo.
Kuti mupeze mfundo zimene mungamvanepo, munganene kuti: (1) ‘Inu mosakaikira mukavomereza kuti, mosasamala kanthu ndi chiyambi chathu, tonsefe timayang’anizana ndi mavuto amodzimodzi m’dziko lamakono. Kodi mumakhulupirira kuti padzakhaladi njira yokhalitsa yothetsera mavuto aakulu amene ayang’anizana ndi mbadwo uno? (Sal. 37:10, 11, 29; Sal. 146:3-5; Dan. 2:44)’ (2) ‘Sitiri mbali ya Dziko Lachikristu ndipo sitimakhulupirira Utatu koma timalambira Mulungu wa Abrahamu. Tiridi okondwera ndi nkhani ya chowonadi cha chipembedzo. Kodi ndingafunse mmene mumadziŵira chimene chiri chowona, makamaka chifukwa cha chenicheni chakuti pali kusiyana kwakukulu kwa zikhulupiriro pakati pa anthu Achiyuda? . . . (Deut. 4:2; Yes. 29:13, 14; Sal. 119:160)’ (3) ‘Tiri okondwerera kwambiri lonjezo la Mulungu kwa Abrahamu lakuti kupyolera mwa mbewu yake anthu amitundu yonse adzadalitsidwa. (Gen. 22:18)’
Ngati munthuyo asonyeza kupanda chikulupiriro mwa Mulungu, funsani ngati iye walingalira mwanjirayo nthaŵi zonse. Pamenepo mwinamwake kambitsiranani chifukwa chake Mulungu walola kuipa ndi kuvutika. Zikumbukiriro za chipiyoyo cha Nazi zachititsa Ayuda ambiri kudera nkhaŵa nchimenechi.
Ngati mukambitsirana za kufunika kwa kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu, choyamba pezani mmene munthu winayo amalilingalirira. Sonyezani kuti Eksodo 20:7 amaletsa kutchula dzina la Mulungu pachabe, koma samaletsa kuligwiritsira ntchito mwaulemu. Ndiyeno lingalirani pamalemba monga Eksodo 3:15 (kapena Salmo 135:13); 1 Mafumu 8:41-43; Yesaya 12:4; Yeremiya 10:25; Malaki 3:16.
Pamene mukambitsirana za Mesiya: (1) Choyamba lankhulani za madalitso amtsogolo muulamuliro wake, mmalo mwakuti iye ndani. (2) Ndiyeno lingalirani malemba amene amasonya kwa Mesiya weniweni. (Gen. 22:17, 18; Zek. 9:9, 10; Dan. 7:13, 14) (3) Mungafunikire kukambitsirana kudza kuŵiri kwa Mesiya. (Siyanitsani Danieli 7:13, 14 ndi Danieli 9:24-26.) (4) Polankhula za Yesu, teroni ndi lingaliro limene limagogomezera mpangidwe wopita patsogolo wa chifuno cha Mulungu. Tchulani kuti pamene Yesu anaphunzitsa, nthaŵi inali pafupi pamene Mulungu analola kachisi wachiŵiri kuwonongedwa, wosadzamangidwanso. Koma Yesu anagogomezera kukwaniritsidwa kwa Chilamulo ndi Aneneri ndi mtsogolo mwaulemerero ku zimene zinthuzi zikatsogolera anthu okhulupirira.