Pemphero
Tanthauzo: Kulankhula kopembedza, kaya mofuula kapena mwakachetechete mmalingaliro a munthu, kwa Mulungu wowona kapena kwa milungu yonyenga.
Kodi mumalingalira, monga momwe amachitira ambiriwo, kuti simumapeza yankho kumapemphero anu?
Kodi ndimapemphero ayani amene Mulungu ali wofunitsitsa kumva?
Sal. 65:2; Mac. 10:34, 35: “Wakumva pemphero inu, zamoyo zonse zizadza kwa inu.” “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Mtundu wa munthu, mawonekedwe a khungu la munthu, kapena mikhalidwe yazachuma ya munthu sindizo kanthu. Koma zisonkhezero za mtima wa munthu ndi njira ya moyo ya munthuyo zimatero.)
Luka 11:2: “Pamene mupemphera nenani, Atate, dzina lanu liyeretsedwe.” (Kodi mapemphero anu amalunjikitsidwa kwa Atate, uyo amene dzina lake Baibulo limamutcha Yehova? Kapena, mmalo mwake, mumapereka mapemphero anu kwa “oyera mtima”?)
Yoh. 14:6, 14: “Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine ngati mudzapempha kanthu mu dzina langa, ndidzachita.” (Kodi mumapemphera m’dzina la Yesu Kristu, mukumavomereza kuti monga munthu wochimwa mufunikira kuti akutetezereni?)
1 Yoh. 5:14: “Uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera. (Komabe, kuti mukhale ndi chidaliro chotero, muyenera choyamba kudziŵa chifuniro cha Mulungu. Ndiyeno tsimikizirani kuti mapemphero anu ngogwirizana nacho.)
1 Pet. 3:12: “Maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Ambuye iri pa wochita zoipa.” (Kodi inu mwapeza nthaŵi ya kuphunzira zimene Yehova amanena kupyolera mwa Mawu ake ponena za cholungama ndi choipa?)
1 Yoh. 3:22, NW: “Chirichonse tipempha, tilandira kwa iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zokodweretsa pamaso pake.” (Kodi chiridi chikhumbo chanu kukondweretsa Mulungu, ndi kuyesayesa mwamphamvu kumvera malamulo ake amene mumadziŵa kale?)
Yes. 55:6, 7: “Funani Yehova popezeka iye, itanani Iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi Mulungu wathu, pakuti adzakhululukira koposa.” (Mwachifundo, Yehova amaitana ngakhale anthu amene anachita zoipa kumfikira m’pemphero. Koma, kuti apeze chiyanjo cha Mulungu, iwo ayenera kulapa mowona mtima njira zawo zochimwa ndi malingaliro ndi kusintha njira yawo.)
Kodi nchiyani chimene chingapangitse mapemphero a munthu kukhala osavomerezeka pamaso pa Mulungu?
Mat. 6:5: “Pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masinagoge, ndi pamphambano zamakwalala, kuti awonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, iwo alandiriratu mphoto zawo.” (Ndiponso Luka 18:9-14)
Mat. 6:7: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga momwe amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo.”
Miy. 28:9: “Wopeŵetsa khutu lake kuti asamve chilamulo [cha Mulungu], ngakhale pemphero lake linyasa.”
Mika 3:4: “Pamenepo adzapfuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthaŵi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe awo.”
Yak. 4:3: “Mupempha, ndipo simulandila, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.”
Yes. 42:8, Dy; Mat. 4:10, JB: “Ine, Ambuye [“Yahweh,” JB; “Yehova,” NW]: ndilo dzina langa. Sindidzapatsa munthu aliyense ulemerero wanga kapena chitamando changa kumafano osemedwa.” “Uyenera kulambira Ambuye Mulungu wako [“Yehova Mulungu wako,” NW], ndi kumtumikira iye yekha.” (Ndiponso Salmo 115:4-8, kapena 113:4-8 mpambo wachiŵiri wa chiŵerengero mu Dy) (Pemphero ndilo mpangidwe wa kulambira. Ngati mupemphera pamaso pa zinthu zosemedwa kapena mafano, kodi zimenezo zidzakondweretsa Mulungu?)
Yes. 8:19: “Pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa alauli, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang’ung’udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wawo? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?”
Yak. 1:6, 7: “Apemphe ndi chikhulupiriro, osakaika konse; pakuti wokaikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuŵinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye.”
Kodi ndiponena za nkhani zoyenerera zotani zimene tingapempherere?
Mat. 6:9-13: “Pempherani inu chomwechi: ‘[1] Atate wathu Wakumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. [2] Ufumu wanu udze. [3] Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. [4] Mutipatse ife lero chakudya chathu cha lero. [5] Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu. [6] Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.’” (Tawonani kuti dzina la Mulungu ndi chifuno ziyenera kukhala zoyambirira.)
Sal. 25:4, 5: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’chowonadi chanu, ndipo mundiphunzitse pakuti inu ndinu Mulungu wachipulumutso changa.”
Luka 11:13: “Ngati inu okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akupempha iye.”
1 Ates. 5:17, 18: “Pempherani kosaleka; m’zonse yamikani.”
Mat. 14:19, 20: “[Yesu] anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziŵirizo, ndipo pamene anayang’ana kumwamba anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo. Ndipo anadya onse, nakhuta.”
Yak. 5:16, NW: “Pemphereranani.”
Mat. 26:41: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa.”
Afil. 4:6: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.”
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Yambani mwapemphera nane, ndiyeno ndilalikireni uthenga wanu’
Mungayankhe kuti: ‘Ndiri wokondwera kudziŵa kuti ndinu munthu woyamikira kufunika kwa pemphero. Mboni za Yehova nazonso zimapemphera nthaŵi zonse. Koma pali kanthu kena kamene Yesu ananena ponena za nthaŵi ndi mmene tingapempherere kamene kangakhale katsopano kwa inu. Kodi munali kudziŵa kuti anauza ophunzira ake kusapereka mapemphero apoyera ndi cholinga chakuti ena awone kuti iwo anali opembedza, anthu opemphera? . . . (Mat. 6:5)’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Tamverani zimene iye anapitirizabe kunena kuti ziyenera kukhala nkhaŵa yathu yaikulu ndi zimene tiyenera kuika poyamba m’mapemphero athu. Ndizo zimene ndadzagaŵana nanu. (Mat. 6:9, 10)’
Kapena munganene kuti: ‘Ndidziŵa kuti oimira magulu ena a zipembedzo amachita zimenezo. Koma Mboni za Yehova sizimatero chifukwa chakuti Yesu adalangiza ophunzira ake kuchita ntchito yawo yolalikira mu mpangidwe wina. Mmalo mwakunena kuti, “poloŵa m’nyumba, yambani mwapemphera,” tamverani zimene ananena monga momwe zikupezekera pa Mateyu 10:12, 13. . . . Ndipo tawonani pano muvesi 7 zimene anayenera kukambitsirana. . . . Kodi ndimotani mmene Ufumuwo ungathandizire anthu onga inu ndi ine? (Chiv. 21:4)’