Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 388-tsamba 391
  • Ulosi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulosi
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ngati Wina Anena Kuti—
  • Ufumu
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Dzikoli Lidzatha Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Mavuto Onsewa Atha Posachedwapa
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Mutu wa Njoka Udzaphwanyidwa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 388-tsamba 391

Ulosi

Tanthauzo: Uthenga wouziridwa; vumbulutso la chifuniro ndi chifuno cha Mulungu. Ulosi ungakhale kunenedweratu kwa kanthu kena kalinkudza, chiphunzitso chabwino chouziridwa, kapena mawu amalangizo ochokera kwa Mulungu.

Kodi ndizonenedweratu ziti zolembedwa m’Baibulo zimene zakwaniritsidwa kale?

Kaamba ka zitsanzo zina, wonani mitu yaikulu yakuti “Baibulo,” “Masiku Otsiriza,” ndi “Madeti,” ndiponso bukhu la “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” tsamba 343-346.

Kodi ndiati amene ali ena a maulosi apadera a Baibulo amene sanakwaniritsidwebe?

1 Ates. 5:3, NW: “Pamene kuli kwakuti iwo akunena: ‘Mtendere ndi chisungiko!’ pamenepo chiwonongeko chamwadzidzidzi chidzawafikira modzidzimutsa mofanana ndi zoŵaŵa za nsautso pamkazi wapakati; ndipo iwo m’njira iriyonse sadzapulumuka.”

Chiv. 17:16: “Nyanga khumi udaziwona, ndi chirombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo [Babulo Wamkulu], nizidzamkhalitsa wabwinja wausiŵa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto.”

Ezek. 38:14-19: “Uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israyeli [wauzimu] sudzachidziŵa kodi? Ndipo udzatuluka m’malo mwako m’malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu . . . ” “Ndipo kudzachitika tsiku ilo, tsiku loti Gogi adzadza kulimbana ndi dziko la Israyeli, ati Ambuye Yehova, ukali wanga udzakwera m’mphuno mwanga. Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m’moto wa kuzaza kwanga.”

Dan. 2:44: “Ufumu [wokhazikitsidwa ndi Mulungu] . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [aumunthu], nudzakhala chikhalire.”

Ezek. 38:23: “Ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”

Chiv. 20:1-3: “Ndinawona mngelo anatsika kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthaŵi.”

Yoh. 5:28, 29: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene anachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”

Chiv. 21:3, 4: “Ndinamva mawu aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena, ‘Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misodzi yonse kuyichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa, zoyambazo zapita.’”

1 Akor. 15:24-28: “Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu ndiye Atate, . . . Ndipo pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.”

Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukhala okondweretsedwa kwambiri m’maulosi a Baibulo?

Mat. 24:42: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake la kufika kwa Ambuye wanu.”

2 Pet. 1:19-21: “Tiri nawo mawu a chinenero okhazikika koposa [chifukwa cha zimene zinawoneka pakusandulika kwa Yesu]; amene muchita bwino powasamalira . . . Pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.”

Miy. 4:18: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.”

Mat. 4:4, NW: “Munthu ayenera kukhala ndi moyo, osati ndi mkate wokha, koma ndi mawu alionse akutuluka m’kamwa mwa Yehova.” (Zimenezo zimaloŵetsamo malonjezo ake aakulu olosera.)

2 Tim. 3:16: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” (Motero Mawu onse olembedwa a Mulungu ngoyenera kuti tiwapunzire mwaphamphu.)

Ngati Wina Anena Kuti—

‘Mumaika chigogomezero chonkitsa paulosi. Chofunika chokha ndicho kuvomereza Kristu kukhala Mpulumutsi wanu ndi kukhala ndi moyo wabwino Wachikristu’

Mungayankhe kuti: ‘Kuzindikira malo antchito a Yesu Kristu kulidi kofunika. Koma kodi munadziŵa kuti chifukwa chimodzi chimene Ayuda m’zaka za zana loyamba analepherera kumvomereza chinali chakuti sanalabadire ulosi mokwanira?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Maulosi m’Malemba Achihebri anali ataneneratu pamene Mesiya (Kristu) akawonekera ndi zimene akachita. Koma Ayuda ambiri sanalabadire zimene maulosi amenewo ananena. Iwo anali ndi malingaliro awoawo ponena za zimene Mesiya anayenera kuchita, ndipo chifukwa cha zimenezo iwo anakana Mwana wa Mulungu. (Wonani tsamba 425, pamutu wakuti “Yesu Kristu.”)’ (2) ‘Ife lerolino tikukhala ndi moyo m’nthaŵi imene Kristu wayamba kulamulira monga Mfumu yakumwamba ndipo akulekanitsa anthu a mitundu yonse, ncholinga cha kumoyo kapena chiwonongeko. (Mat. 25:31-33, 46) Koma anthu ambiri akufunafuna kanthu kosiyana.’

Kapena munganene kuti: ‘Ndikuvomereza kuti kukhala Mkristu wabwino nkofunika. Koma kodi ndikakhala Mkristu wabwino ngati ndinachita zina za zinthu zimene anaphunzitsa koma kunyalanyaza zimene ananena kuti tiyenera kuziika poyamba m’moyo? . . . Tawonani zimene iye ananena monga momwe zalembedwera pano pa Mateyu 6:33.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Kodi sizowona kuti Yesu anatiphunzitsa kupempherera Ufumu umenewo, ngakhaledi kuwuika patsogolo pa kupempa kwathu chikhululukiro chifukwa cha chikhulupiriro chathu mwa iye monga Mpulumutsi? (Mat. 6:9-12)’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena