Uthenga Umene Tiyenera Kulengeza
Yehova watipatsa udindo ndi mwayi waukulu kwambiri, potiuza kuti: “Inu ndinu mboni zanga, . . . ndipo Ine ndine Mulungu.” (Yes. 43:12) Sitili okhulupirira chabe ayi. Timachitira umboni kwa anthu za mfundo zofunika za choonadi cha Mawu amene Mulungu anawauzira. Kodi ndi uthenga wanji umene Yehova watituma kuti tiulengeze m’masiku athu ano? Ndi uthenga wonena za Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi Ufumu wa Mesiya.
‘OPANI MULUNGU WOONA, SUNGANI MALAMULO AKE’
KALE kwambiri Chikristu chisanakhale, Yehova anauza Abrahamu wokhulupirikayo za makonzedwe akuti “mitundu yonse ya dziko lapansi” ikadalitsidwa. (Gen. 22:18) Anauziranso Solomo kuti alembe za chinthu chofunika kwambiri kwa anthu onse kuti: ‘Opani Mulungu [woona, NW], sungani malamulo ake. Pakuti ndicho choyenera anthu onse.’ (Mlal. 12:13) Koma kodi anthu a mitundu yonse yosiyanasiyana akanadziŵa bwanji zinthu zimenezi?
Ngakhale kuti anthu ena okhulupirira mawu a Mulungu akhalapo nthaŵi zonse, Baibulo limasonyeza kuti ntchito yaikulu koposa yochitira umboni padziko lonse ndiponso yolalikira uthenga wabwino ku mitindu yonse idzachitika mu “tsiku la Ambuye.” Tsiku limeneli linayamba mu 1914. (Chiv. 1:10) Kunena za nthaŵiyo, Chivumbulutso 14:6, 7 chinaneneratu kuti kulengeza kofunika kotsogoleredwa ndi angelo kukachitika ku “mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” Anthuwo akauzidwa kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo m’lambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.” Ndi chifuniro cha Mulungu kuti uthenga umenewu uperekedwe. N’chifukwa chake uli mwayi waukulu kwa ife kutenga mbali m’ntchito imeneyi.
“Mulungu Woona.” Pamene Yehova analengeza kuti, “Inu ndinu mboni zanga,” panali mkangano wakuti Mulungu woona ndani. (Yes. 43:10) Uthenga wofunika kuulengeza si wakungoti anthu akhale ndi chipembedzo kapena kuti akhale ndi mulungu basi amene angam’khulupirire, ayi. M’malo mwake, tiyenera kuwapatsa mwayi wakuti aphunzire kuti Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi ndiye Mulungu yekha woona. (Yes. 45:5, 18, 21, 22; Yoh. 17:3) Mulungu woona yekhayo ndiye angathe kulosera molondola za m’tsogolo. Ifeyo tili ndi mwayi wowafotokozera anthu kuti mawu a Yehova amene anakwaniritsidwa m’mbuyomu amapereka umboni wodalirika kwa okhulupirira kuti zonse zimene walonjeza m’tsogolonso zidzachitikadi.—Yos. 23:14; Yes. 55:10, 11.
Anthu ambiri amene timawalalikira amalambira milungu yawo ndipo ena amati salambira mulungu aliyense. Kuti amvetsere zimene tikunena, tiyenera kuyamba ndi zinthu zimene iwonso angazione kukhala zofunika. Chitsanzo chopezeka pa Machitidwe 17:22-31 chingatithandize. Ngakhale kuti mtumwi Paulo anali kulankhula mosamala, tikuona kuti ananena mwachimvekere kuti anthu onse ali ndi udindo kwa Mulungu amene ali Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi.
Kudziŵitsa Dzina la Mulungu. Musalephere kutchula dzina la Mulungu woona. Yehova amakonda dzina lake. (Eks. 3:15; Yes. 42:8) Amafunanso kuti anthu alidziŵe dzinalo. N’chifukwa chake anachititsa kuti dzina lake lolemekezekalo lilembedwe m’Baibulo nthaŵi zopitirira 7,000. Choncho ndi udindo wathu kuwadziŵitsa anthu za dzinalo.—Deut. 4:35.
Madalitso a moyo wa m’tsogolo kwa anthu onse amadalira kum’dziŵa Yehova ndi kuitanira pa dzina lake m’chikhulupiriro. (Yow. 2:32; Mal. 3:16; 2 Ates. 1:8) Komabe, anthu ochuluka samudziŵa Yehova. Kuphatikizapo ngakhale anthu ambiri amene amati amalambira Mulungu wa m’Baibulo. Ngakhale kuti Baibulo ali nalo ndipo amaliŵerenga, m’povuta kuti alidziŵe dzina lakelake la Mulungu chifukwa linachotsedwa m’mabaibulo ambiri amakono. Chokha chimene ena akudziŵa pa dzina lakuti Yehova n’chakuti atsogoleri awo achipembedzo amawaletsa kulitchula.
Kodi anthu tingawadziŵitse motani dzina la Mulungu? Njira yothandiza kwambiri ndiyo kuwasonyeza m’Baibulo lawo ngati n’kotheka. M’mabaibulo ena dzinalo limapezeka kambirimbiri. M’mabaibulo ena lingapezeke kokha pa Salmo 83:18 kapena pa Eksodo 6:3-6, kapenanso m’mawu a m’munsi pa Eksodo 3:14, 15 kapena 6:3. M’mabaibulo angapo, m’malo amene zinenero zoyambirira zinali ndi dzina lakelake la Mulungu, amalembamo “Ambuye” kapena “Mulungu.” Ngati omasulira Baibulo amakono anachotseratu dzina la Mulungu m’Baibulo latsopano, mungagwiritse ntchito Baibulo lakale pofuna kusonyeza anthu zimene anthu achita. M’mayiko ena, munganene za dzina la Mulungu lotchulidwa m’nyimbo zina zachipembedzo kapena lolembedwa pakhoma la nyumba inayake.
Ngakhale kwa aja olambira milungu ina, mungagwiritse ntchito Yeremiya 10:10-13 m’Baibulo la New World Translation. Silimangotchula dzina la Mulungu komanso limam’fotokoza bwino kwambiri.
Musabise dzina la Yehova ndi mayina akuti “Mulungu” ndi “Ambuye,” mmene Matchalitchi Achikristu achitira. Pamenepa sitikutanthauza kuti pokambirana nkhani iliyonse tiziyamba tatchula dzinalo ayi. Ngati tichita zimenezo, anthu ena angadule makambiranowo chifukwa chokhala kale ndi maganizo oipidwa. Koma mutakhazikitsa mfundo zokambirana, musachite manyazi kutchula dzina la Mulungu.
N’zosangalatsa kudziŵa kuti Baibulo limatchula dzina lakelake la Mulungu nthaŵi zambiri kuposa ngakhale kuphatikiza pamodzi nthaŵi zimene limatchula mayina akuti “Ambuye” ndi “Mulungu.” Ngakhale ndi choncho, olemba Baibulo sanalembe dzina la Mulungu m’sentensi iliyonse. Iwo analitchula mwachibadwa, momasuka, komanso mwaulemu. Ndi mmene ifenso tiyenera kuchitira.
Kum’dziŵa Mulungu wa Dzinalo. Ngakhale kuti mfundo yakuti Mulungu ali ndi dzina lakelake ndi yofunika kwambiri, yangokhala chiyambi chabe.
Kuti anthu am’konde Yehova ndi kuitanira pa dzina lake m’chikhulupiriro, ayenera kudziŵa kuti iye ndi Mulungu wotani. Pamene Yehova anadziŵitsa dzina lake kwa Mose pa Phiri la Sinai, sanangotchula dzina lakuti “Yehova.” Anafotokoza ena mwa makhalidwe Ake apadera. (Eks. 34:6, 7) Tiyenera kutengera chitsanzo chimenecho.
Kaya ndi polalikira kwa okondwerera atsopano kapena pokamba nkhani pampingo, pamene mulankhula za madalitso a Ufumu, fotokozani zimene amasonyeza ponena za makhalidwe a Mulungu wopereka malonjezowo. Ponena za malamulo ake, tsindikani nzeru ndi chikondi chake chimene malamulowo amasonyeza. Mveketsani kuti zimene Mulungu amafuna sizikhala mtolo kwa ife, m’malo mwake, zimatipindulitsa. (Yes. 48:17, 18; Mika 6:8) Sonyezani mmene mphamvu ya Yehova yooneka m’zinthu zosiyanasiyana imasonyezera kuti iye ndi Mulungu wotani, miyezo yake, ndi cholinga chake. Sonyezani mmene Yehova amasonyezera makhalidwe ake pamlingo woyenera. Kalankhulidwe kanu kasonyeze kwa ena mmene mukumvera ponena za Yehova. Chikondi chanu pa Yehova chingachititse ena kum’kondanso kwambiri.
Uthenga wofunika mwamsanga masiku ano ndi wakuti anthu aope Mulungu. Mwa zimene timanena, tiyenera kuthandiza ena kukhala ndi mantha amenewo. Mantha abwino. Mantha a kulemekeza Yehova. (Sal. 89:7) Manthawo amaphatikizapo kuzindikira kuti Yehova ndiye Woweruza wamkulu ndi kuti madalitso a moyo wathu wam’tsogolo amadalira kumvera iye. (Luka 12:5; Aroma 14:12) Choncho, kuopa Mulungu kumeneko kumayendera pamodzi ndi kumukonda, komanso kukhala wofunitsitsa kum’kondweretsa. (Deut. 10:12, 13) Kuopa Mulungu kumatithandizanso kudana ndi choipa, kumvera malamulo a Mulungu, ndi kum’lambira ndi mtima wonse. (Deut. 5:29; 1 Mbiri 28:9; Miy. 8:13) Kumatithandiza kusakonda zinthu za dziko pamene tikutumikira Mulungu.—1 Yoh. 2:15-17.
Dzina la Mulungu Ndilo “Linga Lolimba.” Anthu amene amam’kondadi Yehova amakhala otetezeka kwambiri. Zili choncho si chifukwa chongoti amatha kutchula dzina lake kapena kufotokoza ena mwa makhalidwe ake ayi. Koma chifukwa chakuti amakhulupirira Yehova weniweniyo. Ponena za amenewo, Miyambo 18:10 imati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.”
Gwiritsani ntchito mipata yolimbikitsira ena kuwathandiza kudalira Yehova. (Sal. 37:3; Miy. 3:5, 6) Chidaliro choterocho chimasonyeza chikhulupiriro mwa Yehova ndi malonjezo ake. (Aheb. 11:6) Pamene anthu ‘aitanira pa dzina la Yehova’ podziŵa kuti ndiye Mfumu ya Chilengedwe Chonse, pokonda njira zake, ndi pokhulupirira ndi mtima wonse kuti chipulumutso chenicheni chimachokera kwa iye yekha, pamenepo Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti iwo adzapulumuka. (Aroma 10:13, 14) Pamene mukuphunzitsa ena, athandizeni kukhala ndi chikhulupiriro chotero pambali iliyonse ya moyo wawo.
Anthu ambiri amakumana ndi mavuto aakulu pamoyo wawo. Angakhale asakuona njira yotulukira m’mavutowo. Alimbikitseni kuphunzira njira za Yehova, kum’dalira iye, ndi kugwiritsa ntchito zimene amaphunzira. (Sal. 25:5) Alimbikitseni kuti azipemphera ndi mtima wonse kuti Mulungu awathandize ndi kuti azimuyamikira kaamba ka madalitso ake. (Afil. 4:6, 7) Pamene afika pom’dziŵa Yehova mwa kuŵerenga mawu ake m’Baibulo ndi kuona kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake pamiyoyo yawo, adzayamba kuona kuti ndi otetezeka chifukwa cha kumvetsa tanthauzo la dzina la Yehova.—Sal. 34:8; Yer. 17:7, 8.
Tengerani mwayi uliwonse kuti muthandize anthu kuona kuti n’kwanzeru kuopa Yehova, Mulungu woona, ndi kusunga malamulo ake.
‘KUCHITIRA UMBONI ZA YESU’
YESU KRISTU ataukitsidwa koma asanabwerere kumwamba, anapereka malangizo kwa ophunzira ake akuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.” (Mac. 1:8) Atumiki a Mulungu okhulupirika m’masiku athu ano akuchita ‘ntchito yochitira umboni za Yesu.’ (Chiv. 12:17, NW) Kodi mumachita khama pa ntchito yochitira umboni imeneyo?
Anthu ambiri amene amanena moona mtima kuti amakhulupirira Yesu sadziŵa kuti iye anayamba wakhalako kumwamba asanadzakhale munthu. Sadziŵa kuti pamene iye anali padziko lapansi analidi munthu weniweni. Samvetsa kuti kukhala kwake Mwana wa Mulungu kumatanthauzanji. Sadziŵa kwenikweni mbali imene Yesu ali nayo pothandiza kuti chifuniro cha Mulungu chikwaniritsidwe. Iwo sadziŵa kuti iye akuchita chiyani tsopano, ndipo sakuzindikira kuti zimene Yesu adzachita m’tsogolo zidzakhudza motani miyoyo yawo. Angaganizenso molakwa kuti Mboni za Yehova sizikhulupirira Yesu. Ndiye chifukwa chake uli mwayi wathu kuti tiwathandize anthu kudziŵa zoona zake pankhani zimenezi.
Palinso anthu ena amene sakhulupirira kuti Yesu wofotokozedwa m’Baibulo anakhalakodi. Ena amaganiza kuti Yesu anali chabe mmodzi wa anthu otchuka kwambiri. Ambiri amakana zakuti anali Mwana wa Mulungu. Kuti ‘tichitire umboni za Yesu’ kwa anthu otero tiyenera kuyesetsa mwakhama, kuleza mtima, ndi kuchita mwaluso.
Kaya omvera anu ali ndi maganizo otani, kuti akalandire moyo wosatha kwa Mulungu, afunikira kudziŵa za Yesu Kristu. (Yoh. 17:3) Chifuniro cha Mulungu chounikidwa bwino lomwe n’chakuti amoyo onse “avomereze kuti Yesu ali Ambuye” ndipo amugonjere. (Afil. 2:9-11) Choncho, tisangoipeŵa nkhaniyo pamene tikumana ndi anthu okhala ndi maganizo amphamvu koma olakwika. Ngakhale kuti nthaŵi zina tingalankhule momasuka za Yesu Kristu—ngakhale paulendo woyamba—nthaŵi zina tiyenera kusamala kalankhulidwe kathu pofuna kuthandiza omvera athu kuyamba kulingalira zoyenera ponena za Yesu. Tingaganizirenso njira zodzayambira kukambirana mfundo zina zokhudza nkhaniyo pamaulendo ena obwereza. Komabe, mwina sizingatheke kukambirana zonse zokhudza nkhaniyo tisanakhazikitse phunziro la Baibulo kwa munthuyo.—1 Tim. 2:3-7.
Mbali ya Yesu Yofunika Kwambiri pa Chifuniro cha Mulungu. Tiyenera kuthandiza anthu kuzindikira kuti Yesu pokhala “njira” ndipo ‘palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa iye,’ n’zosatheka kuti munthu akhale paubwenzi ndi Mulungu popanda kukhulupirira Yesu Kristu. (Yoh. 14:6) Munthu akapanda kuzindikira mbali yofunika kwambiri imene Yehova wagaŵira Mwana wake woyambayo, n’zosatheka kulimvetsa Baibulo. Chifukwa chiyani? Chifukwa Yehova anaika Mwana wake ameneyu kukhala munthu wofunika kwambiri pokwaniritsa zolinga Zake. (Akol. 1:17-20) Maulosi a m’Baibulo agona pa mfundo imeneyi. (Chiv. 19:10) Yesu Kristu ndiye njira yothetsera mavuto onse oyambitsidwa ndi kupanduka kwa Satana ndi uchimo wa Adamu.—Aheb. 2:5-9, 14, 15.
Kuti munthu amvetse mbali ya Kristu, ayenera kuzindikira kuti anthu ali mumkhalidwe womvetsa chisoni umene sangadziwonjolemo okha. Tonse tinabadwa mu uchimo. Zotsatira zake zimatikhudza mosiyanasiyana pamiyoyo yathu. Chifukwa cha zimenezo, imfa imatha kutipeza nthaŵi iliyonse. (Aroma 3:23; 5:12) Kambiranani mfundo imeneyo ndi amene mukuwalalikira. Ndiyeno tchulani kuti mwa nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, Yehova mwa chikondi chake, wakonza zowonjola anthu okhulupirira makonzedwe amenewo ku uchimo ndi imfa. (Marko 10:45; Aheb. 2:9) Zimenezi zimawatsegulira njira yokalandira moyo wosatha wangwiro. (Yoh. 3:16, 36) Palibenso njira ina yopezera madalitso amenewo. (Mac. 4:12) Monga mphunzitsi, kaya ndi kumbali kapena mumpingo, thandizani omvera anu kudziŵa zochulukirapo. Osangotchula mfundo n’kusiyira pomwepo. Mwachifundo komanso moleza mtima, thandizani omvera anu kukhala ndi mtima woyamikira mbali ya Kristu ngati Momboli. Kuyamikira makonzedwe ameneŵa kungathandize munthu kusintha maganizo ake, khalidwe lake, ndi zolinga zake m’moyo.—2 Akor. 5:14, 15.
Zoona, Yesu anapereka nsembe moyo wake kamodzi kokha. (Aheb. 9:28) Komabe, iye tsopano akutumikira ngati Mkulu wa Ansembe. Athandizeni ena kumvetsa tanthauzo la zimenezi. Kodi anthuwo akuvutika maganizo? Kodi ndi okhumudwa? Kodi ali pavuto linalake? Kapena kodi akukumana ndi mavuto chifukwa cha nkhanza za anthu owazungulira? Pamene Yesu anali munthu padziko, anakumana ndi zonsezi. Akudziŵa mmene timamvera. Pokhala anthu opanda ungwiro, kodi tikuona kuti m’pofunika kuti Mulungu atimvere chifundo? Ngati timapempha kuti Mulungu atikhululukire mwa nsembe ya Yesu, Yesuyo amachitapo kanthu monga ‘Nkhoswe kwa Atate.’ Yesuyo pakumva chifundo, ‘amatipempherera.’ (1 Yoh. 2:1, 2; Aroma 8:34) Pamaziko a nsembe ya Yesu komanso mwa utumiki wake ngati Mkulu wa Ansembe, timatha kufika ku “mpando wachifumu wachisomo” wa Yehova kuti tilandireko thandizo panthaŵi yake. (Aheb. 4:15, 16) Ngakhale kuti tili opanda ungwiro, thandizo limene Yesu amapereka monga Mkulu wa Ansembe limatithandiza kutumikira Mulungu ndi chikumbumtima choyera.—Aheb. 9:13, 14.
Kuwonjezera pamenepo, Yesu ali ndi ulamuliro waukulu monga woikidwa ndi Mulungu kukhala Mutu wa mpingo wachikristu. (Mat. 28:18; Aef. 1:22, 23) Motero, amachita utsogoleri wake mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Pamene mukuphunzitsa ena, athandizeni kuzindikira kuti Mutu wa mpingo ndi Yesu Kristu basi, ndipo palibenso munthu wina. (Mat. 23:10) Pamene mwangoyamba kucheza ndi anthu oonetsa chidwi, aitanireni kumisonkhano ya mpingo wanu, kumene timaphunzira Baibulo mothandizidwa ndi mabuku ofalitsidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Afotokozereni kuti “kapolo” ameneyo ndani, komanso Mbuyeyo, kuti adziŵe udindo wa Yesu ngati mutu. (Mat. 24:45-47) Asonyezeni kwa akulu, ndipo fotokozani ziyeneretso za m’Malemba zimene akulu amayembekezeka kukwaniritsa. (1 Tim. 3:1-7; Tito 1:5-9) Auzeni kuti mpingo si wa akulu ayi, koma kuti iwo amatithandiza kuyenda m’mapazi a Yesu Kristu. (Mac. 20:28; Aef. 4:16; 1 Pet. 5:2, 3) Thandizani okondwererawo kuona kuti pali gulu la padziko lonse limene likuyendetsedwa pansi pa udindo wa Kristu monga mutu.
Kuchokera m’Mauthenga Abwino Anayi, timaphunzira kuti pamene Yesu analoŵa m’Yerusalemu imfa yake itayandikira, ophunzira ake anam’tamanda kuti “Mfumuyo ikudza m’dzina la Ambuye.” (Luka 19:38) Mmene anthu akuphunzira Baibulo mozamirapo, amayamba kudziŵa kuti Yehova tsopano wapereka ulamuliro kwa Yesu umene umakhudza mitundu yonse ya anthu. (Dan. 7:13, 14) Pokamba nkhani mumpingo kapena pochititsa maphunziro, thandizani anthu kumvetsa mmene ulamuliro wa Yesu umatikhudzira tonsefe.
Tsindikani kuti mmene tikukhalira ndi moyo timasonyeza ngati timakhulupiriradi kuti Yesu Kristu ndi Mfumu ndipo timafunadi kugonjera ulamuliro wake. Unikani ntchito imene Yesu anagaŵira otsatira ake kuti aichite pamene anaikidwa kukhala Mfumu. (Mat. 24:14; 28:18-20) Fotokozani zimene Yesu, monga Wauphungu Wodabwitsa, ananena kukhala zinthu zofunika kopambana pamoyo wa munthu. (Yes. 9:6, 7; Mat. 6:19-34) Longosolani za mzimu umene Kalonga Wamtendere anati otsatira ake akausonyeza. (Mat. 20:25-27; Yoh. 13:35) Koma samalani kuti musakhale woweruza poganiza kuti ena sakuchita zokwanira. M’malo mwake alimbikitseni kuti aganizire ngati zochita zawo zikusonyeza kuti akugonjera ulamuliro wa Kristu. Mmene mukutero, zindikirani kuti inunso muyenera kuchita zofananazo.
Kumanga Pamaziko a Kristu. Baibulo limayerekeza ntchito yopanga wophunzira wachikristu ngati kumanga nyumba pa maziko a Yesu Kristu. (1 Akor. 3:10-15) Kuti zimenezi zichitike, thandizani anthuwo kumudziŵa Yesu mmene Baibulo limamufotokozera. Koma samalani, asaganize kuti akukhala otsatira a inu. (1 Akor. 3:4-7) Lozerani mitima yawo kwa Yesu Kristu.
Ngati mazikowo ayalidwa bwino, ophunzira amazindikira kuti Kristu ‘anatisiyira chitsanzo kuti tilondole mapazi ake.’ (1 Pet. 2:21) Kuti mumange pamaziko amenewo, limbikitsani ophunzirawo kuŵerenga Mauthenga Abwino Anayiwo. Asawaŵerenge ngati mbiri chabe yakale yoona ayi, koma ngati njira yoti aziitsatira. Athandizeni kuti azikumbukira ndi kulabadira maganizo ndi makhalidwe amene Yesu anasonyeza. Alimbikitseni kuona mmene Yesu anaonera Atate wake, mmene anachitira ndi ziyeso ndi mayesero, mmene anagonjera kwa Mulungu, ndi mmene anachitira ndi anthu m’zochitika zosiyanasiyana. Unikani ntchito zimene Yesu anataganidwa nazo m’moyo wake. Mukatero, wophunzirayo akadzakumana ndi nkhani yofuna kupanga chosankha kapena mayesero m’moyo wake, adzatha kudzifunsa kuti: ‘Kodi Yesu akanachita motani pankhani imeneyi? Kodi zimene ndichite zidzaonetsa kuti ndikuyamikira zimene iye anandichitira?’
Pokamba nkhani mu mpingo, musaganize kuti chifukwa abale anu ali kale ndi chikhulupiriro mwa Yesu, m’posafunikira kuwafotokozera mfundo zofunika zokhudza iye. Zimene munganene zingawathandize kwambiri ngati zikhala zolimbikitsa chikhulupiriro chawo. Polankhula za misonkhano, muloŵetsenipo Yesu ndi mfundo yakuti ndiye Mutu wa mpingo. Pofotokoza za utumiki wa kumunda, unikani mtima umene Yesu anasonyeza pochita ntchito yolalikira. Ndipo unikani kugwirizana kwa utumikiwo ndi zimene Kristu monga Mfumu akuchita pofuna kusonkhanitsa anthu kuti adzapulumuke ndi kuloŵa m’dziko latsopano.
N’zachionekere kuti anthu ayenera kudziŵa zambiri m’malo mongophunzira mfundo zoyambirira zokha zokhudza Yesu. Kuti anthu akhale Akristu enieni, ayenera kusonyeza chikhulupiriro chawo mwa iye ndi kum’kondadi. Chikondi choterocho chimalimbikitsa kumvera mokhulupirika. (Yoh. 14:15, 21) Chimathandiza anthu kuchirimika m’chikhulupiriro pokumana ndi mavuto. Chimawathandizanso kuyendabe m’mapazi a Kristu masiku onse a moyo wawo. Amakhalanso Akristu okhwima mwauzimu ndi ‘ozika mizu’ ndi okhazikika pamazikowo. (Aef. 3:17) Kachitidwe koteroko kamapereka ulemu kwa Yehova amene ndi Mulungu komanso Atate wa Yesu Kristu.
“UTHENGA UWU WABWINO WA UFUMU”
YESU pofotokoza mbali zosiyanasiyana za chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mapeto a dziko lakaleli ananeneratu kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mat. 24:14.
Kodi uthengawo makamaka ndi wotani umene uyenera kufalitsidwa chotero? Ndi uthenga wonena za Ufumu umene Yesu anatiphunzitsa kuupempherera kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze.” (Mat. 6:10) Pa Chivumbulutso 11:15 amaufotokoza kuti ndi ‘ufumu wa Ambuye wathu [Yehova], ndi wa Kristu wake,’ chifukwa mphamvu yolamulira imachokera kwa Yehova, koma waipereka m’manja mwa Kristu monga Mfumu. Komabe, onani kuti uthenga umene Yesu anati ukalengezedwa uli ndi zambiri kuposa umene otsatira ake analalikira m’zaka 100 zoyambirira. Iwo anauza anthu kuti: “Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.” (Luka 10:9) Yesuyo, amene anadzozedwa kukhala Mfumu, anali pakati pawo panthaŵiyo. Koma monga timaŵerengera pa Mateyu 24:14, Yesu ananeneratu za kulengeza padziko lonse za chochitika chofunika kwambiri pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu.
Mneneri Danieli anapatsidwa masomphenya a chochitika chimenecho. Iye anaona “wina ngati mwana wa munthu,” Yesu Kristu, akulandira kwa “Nkhalamba ya kale lomwe,” Yehova Mulungu, “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire.” (Dan. 7:13, 14) Chochitika chimenecho chokhudza chilengedwe chonse chinachitikira kumwamba m’chaka cha 1914. Pambuyo pake, Mdyerekezi ndi ziŵanda zake anaponyedwa ku dziko lapansi. (Chiv. 12:7-10) Panthaŵiyo, dziko lakaleli linaloŵa m’masiku ake otsirizira. Koma asanalichotseretu, chilengezo cha padziko lonse chikuyamba chaperekedwa chakuti Mfumu Mesiya ya Yehova tsopano ikulamulira kuchokera pampando wake wachifumu wakumwamba. Chenjezo likuperekedwa kwa anthu ponseponse. Mmene amalabadirira amasonyeza maganizo awo kulinga kwa Wam’mwambamwamba amene ndi Wolamulira mu “ufumu wa anthu.”—Dan. 4:32.
Kunena zoona, pakali zambiri zoti zichitike, ndipo n’zambiridi! Timapempherabe kuti, “Ufumu wanu udze,” koma sitikutanthauza kuti kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu kukali m’tsogolo ayi. Koma tanthauzo lake n’lakuti Ufumu wakumwamba uchitepo kanthu komalizira pokwaniritsa maulosi ngati Danieli 2:44 ndi Chivumbulutso 21:2-4. Ufumuwo udzasinthiratu dziko lapansili kukhala paradaiso wodzaza anthu okonda Mulungu ndi anthu anzawo. Pamene tikulalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu,” timafotokoza madalitso a m’tsogolo amenewo. Koma timanenanso ndi chidaliro kuti Yehova wapereka kale mphamvu zokwanira kwa Mwana wake. Kodi inu mumatsindika uthenga wabwino umenewu mukamalalikira za Ufumuwo?
Ulongosoleni Ufumuwo. Kodi ntchito yathu yolengeza Ufumu wa Mulungu tiyenera kuichita motani? Tingakope chidwi cha anthu mwa kuyamba kukambirana nawo nkhani zosiyanasiyana, koma posapita nthaŵi ayenera kuona kuti uthenga wathu ukunena za Ufumu wa Mulungu.
Mbali yofunika kwambiri pantchito imeneyi ndiyo kuŵerenga kapena kugwira mawu malemba amene amanena za Ufumuwo. Pamene mulankhula za Ufumu, onetsetsani kuti omvera anu akumvetsa kuti Ufumuwo ndi chiyani. Ndi bwino kufotokoza bwinobwino, kusiyana n’kungonena kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma. Ena zingawavute kuganizira boma limene sakuliona. Mungakambirane nawo m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mphamvu yogwetsa zinthu pansi siioneka, koma imakhudza kwambiri miyoyo yathu. Sitingathe kumuona amene anapanga mphamvu yogwetsa zinthu pansi, koma n’zoonekeratu kuti iye ali ndi mphamvu zodabwitsa. Baibulo limamutcha “Mfumu yosatha.” (1 Tim. 1:17) Kapenanso munganene kuti m’mayiko ena aakulu, anthu ambiri sanapitepo ku likulu kapena sanaonepo wolamulira wawo pamasom’pamaso. Amangoonera m’nkhani za panyuzi. Mofananamo, Baibulo, limene lafalitsidwa m’zinenero zopitirira 2,200, limatiuza za Ufumu wa Mulungu; limatiuzanso amene wapatsidwa ulamuliro ndi zimene Ufumuwo ukuchita. Cholinga cha Nsanja ya Olonda, imene imafalitsidwa m’zinenero zambiri koposa magazini ina iliyonse, ndicho ‘Kulengeza Ufumu wa Yehova,’ monga imanenera patsamba lake lakuchikuto.
Kuti muthandize anthu kumvetsa kuti Ufumuwo n’chiyani, mungatchule zinthu zina zimene iwo amafuna kuti maboma awachitire: chitetezo pankhani ya zachuma, mtendere, kuthetsa upandu ndi kusankhana mitundu, kupereka maphunziro kwa onse, ndi moyo wathanzi. Sonyezani kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzapereka zimenezi ndi zina zonse zabwino zimene anthu amazikhumba.—Sal. 145:16.
Thandizani anthuwo kukhala ndi chidwi chokhala nzika za Ufumuwo, umene Yesu Kristu ndiye Mfumu yolamulira. Sonyezani kuti zozizwitsa zimene anachita zinali chithunzi chabe cha zimene adzachite ngati Mfumu yakumwamba. Lankhulani mobwerezabwereza za makhalidwe abwino amene iye anasonyeza. (Mat. 8:2, 3; 11:28-30) Fotokozani kuti anapereka moyo wake m’malo mwa ife ndi kuti pachifukwa chimenecho, Mulungu anamuukitsira ku moyo wosakhoza kufa kumwamba. Akulamulira ngati Mfumu ali kumwamba kumeneko.—Mac. 2:29-35.
Tsindikani kuti Ufumu wa Mulungu tsopano ukulamulira kuchokera kumwamba. Komabe, kumbukirani kuti anthu ambiri sakuona zochitika zimene zingakhale umboni wa ulamuliro umenewo. Vomerezani mfundo imeneyo, koma funsani ngati iwo akudziŵa umboni umene Yesu Kristu ananena. Fotokozani mbali zina za umboni wopezeka pa Mateyu chaputala 24, Marko chaputala 13, kapena Luka chaputala 21. Ndiyeno funsani chifukwa chake zinthu zimenezo zinayamba kuchitika Kristu atakhazikitsidwa pampando wachifumu kumwamba. Kambiranani Chivumbulutso 12:7-10, 12.
Pofuna kusonyeza umboni weniweni wa zimene Ufumu wa Mulungu ukuchita, ŵerengani Mateyu 24:14, ndipo fotokozani ntchito ya padziko lonse yophunzitsa Baibulo imene ikuchitika tsopano. (Yes. 54:13) Auzeni anthu za masukulu osiyanasiyana amene Mboni za Yehova zimapindula nawo—onse ophunzitsa za m’Baibulo, ndipo ndi aulere. Fotokozani kuti kuwonjezera pa ulaliki wathu wa nyumba ndi nyumba, timaphunzira Baibulo ndi anthu ndi mabanja awo ulere panyumba pawo m’mayiko opitirira 230. Ndi boma liti la anthu limene lingathe kupereka maphunziro otero kwa nzika zawo komanso kwa anthu onse padziko lapansi? Itanirani anthu ku Nyumba ya Ufumu, ndi ku misonkhano ikuluikulu ya Mboni za Yehova. Akafike kumeneko kuti akadzionere okha mmene maphunzirowo amasinthira miyoyo ya anthu.—Yes. 2:2-4; 32:1, 17; Yoh. 13:35.
Koma kodi mwininyumbayo angadziŵe mmene zimenezi zikukhudzira moyo wake? Mosamala, munganene kuti cholinga cha kucheza kwanu n’chakuti mukambirane za mwayi umene ulipo wakuti anthu asankhe kukakhala ndi moyo ngati nzika za Ufumu wa Mulungu. Motani? Mwa kuphunzira zimene Mulungu amafuna ndi kuzigwiritsa ntchito pamoyo tsopano.—Deut. 30:19, 20; Chiv. 22:17.
Kuthandiza Ena Kuika Ufumu Patsogolo. Ngakhale munthu atalandira uthenga wa Ufumu, pamakhala nkhani zikuluzikulu zofuna kusankha chochita mosamala. Kodi Ufumu wa Mulungu adzauika pamalo otani m’moyo wake? Yesu analangiza ophunzira ake kuti ‘athange afuna Ufumu.’ (Mat. 6:33) Kodi tingawathandize motani Akristu anzathu kuchita zimenezo? Mwa kupereka chitsanzo chabwino ifeyo, ndi kukambirana mipata imene imakhalapo yochitira zimenezo. Nthaŵi zina, mwa kufunsa ngati munthuyo anaganizirapo kutenga mwayi wa kuchitako zakutizakuti komanso kukambirana naye mmene ena achitira. Mwa kukambirana nkhani za m’Baibulo mwa njira yolimbikitsa chikondi chake kwa Yehova. Mwa kugogomeza kuti Ufumuwo ndi weniweni. Mwa kutsindika kufunika kwa ntchito yolengeza Ufumu. Tingathandize kwambiri anthu mwa kuwalimbikitsa kukhala ndi chidwi chochita zofunikira, osati kungowauza zoyenera kuchita.
Mosakayika, uthenga wofunika kwambiri umene tonsefe tiyenera kulengeza umanena makamaka za Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi Ufumuwo. Tiyenera kutsindika mfundo za choonadi zokhudza zimenezo polalikira kwa anthu, m’mipingo yathu, ndi m’miyoyo yathu. Tikamachita zimenezo, tidzasonyeza kuti tikupinduladi ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.