Nyimbo 42
“Muthandize Ofookawo”
Losindikizidwa
1. Tonse tili n’zofo’ka
Pamoyo wathu.
Komabetu Yehova
Amatikonda.
Iye n’ngwachifundo,
Atisamalira.
Tisonyeze chikondi
Kwa ovutika.
2. Kodi ndani safo’ka
Panthawi zina?
Khristu anatigula,
Tipeze moyo.
Ofo’ka n’nga M’lungu,
Awalimbikitsa.
Timve zovuta zawo
Tiwatonthoze.
3. Tisanyoze ofo’ka,
Tiwakumbuke
Inde, tiwasonyeze
Kukoma mtima.
Tichitedi khama,
Powalimbikitsa.
Tikawathandizadi
Atonthozedwa.
(Onaninso 2 Akor. 11:29; Yes. 35:3, 4; Agal. 6:2.)