Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kutengedwa m’Thupi
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Mungayanke kuti: ‘Ndimawona kuti anthu sali ofanana palingaliro la zimene kutengedwa m’thupi kumathanthauza. Ndingafunse amene ali malingaliro anu pa mfundoyi? . . . Pankhani iriyonse, kuli kopindulitsa kuyerekezera malingaliro athu ndi zimene Baibulo lenilenilo limanena. (Gwiritsirani ntchito zigawo za nkhani yapamwambapayi zimene zimagwira ntchito.)’

      Kapena mungananene kuti: ‘Kutengedwa m’thupi kwalongosoledwa kwa ine kukhala makonzedwe a Akristu akuzemba. Ambiri amalingalira kuti imeneyi ndiyo njira imene adzazemba nayo chisautso chachikulu chirinkudza. Kodi inu mumalingalira motero?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani: (1) ‘Ndithudi ife tifuna chitetezo cha Mulungu panthaŵiyo, ndipo ndimawawona kukhala olimbikitsa kwambiri malemba ena amene amasonyeza mmene tingapindulire nacho. (Zef. 2:3)’ (2) ‘Mokondweretsa, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzatetezera okhulupirika pompano padziko lapansi. (Miy. 2:21, 22) Zimenezo ziri zogwirizana ndi chifuno cha Mulungu pamene iye choyamba analenga Adamu ndi kumuika m’Paradaiso poyambapo, Kodi sichoncho?’

      Kuthekera kwina: ‘Mwa kunena kuti kutengedwa m’thupi inu mukutanthauza kuti Akristu okhala ndi moyo pamapeto a dongosolo la zinthu adzatengedwa kumka nawo kumwamba, kodi sichoncho? . . . Kodi mudayamba mwadabwa zimene iwo adzachita pamene afika kumwambako? . . . Tawonani zimene Chivumbulutso 20:6 (ndi 5:9, 10) chimanena. . . . Koma kodi iwo adzalamulira yani? (Sal. 37:10, 11, 29)’

  • Kuulula
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kuulula

      Tanthauzo: Chilengezo kapena kuvomereza, poyera kapena mtseri, (1) cha zimene munthuyo amakhulupirira kapena (2) cha machimo ake.

      Kodi dzoma la kuyanjana, kuphatikizapo kuulula konong’ona (kuulula kwamunthu kochitidwira m’khutu la wansembe), monga momwe kukuphunzitsidwira ndi Tchalitchi cha Katolika Nzamalemba?

      Dongosolo mu limene wansembe amatchulidwira

      Dongosolo lozoloŵereka, logwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri, nlakuti: “Ndidalitseni, Abambo, pakuti ndachimwa. Papita [nthaŵi yaitali] kuyambira pa Kuulula kwanga kotsirizira.”—Magazine a U.S. Catholic, October 1982, p. 6.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena