-
Satana MdyerekeziKukambitsirana za m’Malemba
-
-
‘mphamvu, mpando wachifumu ndi ulamuliro waukulu’ ku dongosolo la ulamuliro wa ndale zadziko padziko lonse. Danieli 10:13, 20 amavumbula kuti Satana wakhala ali ndi akalonga auchiŵanda olamulira pamaufumu aakulu a dziko lapansi. Aefeso 6:12 amasonya kwa ameneŵa kukhala ‘maboma, maulamuliro, olamulira a dziko amdima uno, makamu a mizimu yoipa mmalo akumwamba.’
Mposadabwitsa kuti 1 Yohane 5:19 amati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Koma mphamvu yake iri kokha ya nyengo yochepa ya nthaŵi ndipo iri kokha mwa chilolezo cha Yehova, amene ali Mulungu Wamphamvuyonse.
Kodi Satana adzaloledwa kusocheza anthu kwautali wotani?
Kaamba ka umboni wakuti ife tsopano tiri m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu loipa la Satana, wonani tsamba 231-234, pamutu wakuti “Madeti,” ndi mutu waukulu wakuti “Masiku Otsiriza.”
Makonzedwe a mpumulo ku chisonkhezero choipa cha Satana afotokozedwa mophiphiritsira motere: “Ndinawona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthaŵi.” (Chiv. 20:1-3) Ndiyeno chiyani? “Mdyerekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure.” (Chiv. 20:10) Kodi uku kutanthauzanji? Chivumbulutso 21:8 chikuyankha: “Ndiyo imfa yachiŵiri.” Adzawonongedwa kosatha!
Kodi ‘kuponyedwa kuphompho’ kwa Satana kumatanthauza kuti adzabindikiritsidwa kudziko lapansi lapululu lopanda munthu aliyense wooti iye anyenge kwa zaka 1 000?
Anthu ena matchula Chivumbulutso 20:3 (chogwidwa mawu pamwambapa) kuchirikiza lingaliro limeneli. Iwo amanena kuti “phompho,” kapena “dzenje lopanda mapeto” (KJ), limaimira dziko lapansi mu mkhalidwe wapululu. Kodi limatero? Chivumbulutso 12:7-9, 12 (KJ) chimasonyeza kuti panthaŵi ina kuikidwa kwake kuphompho kusanachitike Satana “akuponyedwa” kuchokera kumwamba kudza kudziko lapansi, kumene akudzetsa masoka owonjezereka pa anthu. Chotero, pamene Chivumbulutso 20:3 (KJ) chimanena kuti Satana ‘akuponyedwa . . . m’dzenje lopanda mapeto,’ iye ndithudi sakungosiyidwa pamene iye ali kale—wosawoneka koma wobindikiritsidwira kumalo a dziko lapansi. Iye ali kutali ndi kumeneko, “kuti asanyengenso amitundu, kufikira zikatha zaka chikwi.” Tawonani kuti Chivumbulutso 20:3 chimanena kuti, pamapeto a zaka chikwi, ndiye Satana, osati amitundu, amene amasulidwa kuphompho. Pamene Satana amasulidwa, anthu amene kalelo anapanga mitundu imeneyo adzakhala aliko kale.
Yesaya 24:1-6 ndi Yeremiya 4:23-29 (KJ) nthaŵi zina amatchulidwa kuchirikiza chiphunzitso chimenechi. Ameneŵa amati: “Tawonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula . . . dziko lidzapululuka konse, ndi kupasulidwa ndithu; pakuti Yehova ananena mawu ameneŵa.” “Ndinawona dziko lapansi, ndipo tawona linali lopasuka lopanda kanthu . . . ndinawona, ndipo tawona panalibe munthu . . . pakuti Yehova atero dziko lonse lidzakhala bwinja . . . midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu mmenemo.” Kodi nchiyani chimene maulosi ameneŵa amatanthauza? Anali ndi kukwaniritsidwa kwawo koyamba pa Yerusalemu ndi padziko la Yuda. M’kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu, Yehova analola Ababulo kugonjetsa dzikolo. Potsirizira pake linasiyidwa lonse labwinja ndi lapululu. (Wonani Yeremiya 36:29.) Koma Mulungu sanakhalitse labwinja dziko lonse panthaŵiyo, ndiponso iye sadzatero tsopano. (Wonani tsamba 131-133, pamutu wakuti “Dziko Lapansi,” ndiponso mutu waukulu wakuti “Kumwamba.”) Komabe, iye adzapululutsa kotheratu ponse paŵiri mnzake wamakono wa Yerusalemu wosakhulupirika, Dziko Lachikristu, limene limatonza dzina la Mulungu mwa makhalidwe ake oipa, ndi mbali yonse yotsala ya gulu lowoneka la Satana.
Mmalo mwa kukhala lapululu ndi labwinja, mkati mwa Zaka Chikwi za Kulamulira kwa Kristu, ndipo pamene Satana ali chiponyedwere m’mphompho, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. (Wonani “Paradaiso.”)
-
-
TchimoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Tchimo
Tanthauzo: Kwenikweni, kuphonyedwa kwa chizindikiro, mogwirizana ndi kunena kwa malemba apamanja a Baibulo Achihebri ndi Achigiriki. Mulungu mwini amakhazikitsa “chizindikiro” chimene zolengedwa zake zaluntha ziyenera kufikira. Kuphonya chizindikiro chimenecho ndiko tchimo, limenenso liri chisalungamo, kapena kusayeruzika. (Aroma 3:23; 1 Yoh. 5:17; 3:4) Tchimo ndiro
-