Kugonana
Tanthauzo: Mikhalidwe ya zolengedwa za padziko lapansi imene imatumikira monga njira yobalira mwa makolo aŵiri ochita mogwirizana. Kusiyana pakati pa mpheto za amuna ndi akazi kuli ndi ziyambukiro zofika patali m’moyo wa anthu. Popeza Mulungu mwiniyo ndiye Magwero a moyo ndipo popeza anthu anafunikira kusonyeza mikhalidwe yake, mphamvu ya kupitirizira moyo mwa maunansi a kugonana iyenera kuchitiridwa ulemu waukulu.
Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti maunansi a kugonana ali uchimo?
Gen. 1:28: “Mulungu ndipo anadalitsa iwo [Adamu ndi Hava], ndipo Mulungu adati kwa iwo, mubalane, muchuluke, mudzadze dziko lapansi.” (Kuti akwaniritse lamulo la Mulungu iri kukafunikira kuti akhale ndi maunansi a kugonana, kodi sichoncho? Kutero sikukakhala kuchimwa koma kukakhala kogwirizana ndi chifuno cha Mulungu kaamba ka kudzadza dziko lapansi ndi anthu. Anthu ena alingalira kuti ‘chipatso choletsedwa’ mu Edene mwinamwake chinali dzina lophiphiritsira lamulo la Mulungu kapena kuletsedwa kwa maunansi a kugonana pakati pa Adamu ndi Hava. Koma zimenezo zikutsutsana ndi lamulo la Mulungu logwidwa mawu pamwambapa. Zimatsutsananso ndi chenicheni chakuti, ngakhale kuli kwakuti Adamu ndi Hava anadya chipatso choletsedwa m’Edene, kutchulidwa koyamba kwa kukhala kwawo ndi unansi wa kugonana kunali pambuyo pa kuchotsedwa kwawo mmenemo.—Gen. 2:17; 3:17, 23; 4:1.)
Gen. 9:1: “Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane muchuluke, mudzadze dziko lapansi.” (Dalitso lowonjezereka iri, limodzi ndi kutchulanso lamulo la Mulungu la kubala ana, linaperekedwa pambuyo pa Chigumula cha dziko lonse m’tsiku la Nowa. Lingaliro la Mulungu kulinga ku kuloledwa kwa maunansi a kugonana silidasinthe.)
1 Akor. 7:2-5: “Chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha. Mwamunayo apereke kwa mkazi mangaŵa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna. . . . Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwanthaŵi, . . . kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.” (Motero chimene chiri cholakwa chasonyezedwa kukhala dama lachigololo, osati mangaŵa aukwati oyenerera pakati pa mwamuna ndi mkazi wake.)
Kodi maunansi a kugonana ukwati usanachitike ngolakwa?
1 Ates. 4:3-8: “Ichi ndichifuniro cha Mulungu . . . kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziŵe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeretso ndi ulemu, kosati m’chiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziŵa Mulungu; asapitirireko munthu, nanyenga mbale wake mmenemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni. Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso. Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wa kupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.” (Liwu Lachigiriki por·neiʹa, lotembenuzidwa kukhala “dama lachigololo,” limanena za unansi wa kugonana pakati pa anthu osakwatirana, ndiponso maunansi a kugonana kunja kwa ukwati kochitidwa ndi anthu okwatirana.)
Aef. 5:5: “Wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe choloŵa mu ufumu wa Kristu ndi Mulungu.” (Ichi sichitanthauza kuti aliyense amene kalero anali wachigololo sangakhale ndi madalitso a Ufumu wa Mulungu, koma ayenera kuleka njira imeneyo ya moyo kuti akhale ndi chivomerezo cha Mulungu. Wonani 1 Akorinto 6:9-11.)
Kodi Baibulo limavomereza kukhalira pamodzi monga mwamuna ndi mkazi popanda ukwati walamulo?
Wonani tsamba 383, 384, pamutu wakuti “Ukwati.”
Kodi Baibulo limanenanji za kugonana kwa aziŵalo zofanana?
Aroma 1:24-27: “Mulungu anawapereka iwo m’zilakolako za mitima yawo, ku zonyansa, kuchititsana matupi awo wina ndi mnzake zamanyazi . . . Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako zamanyazi: pakuti angakhale akazi awo anasandutsa machitidwe awo achibadidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadidwe cha akazi, natenthetsana ndi chilakolako chawo wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho ya kuyenera kulakwa kwawo.”
1 Tim. 1:9-11: “Lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osayeruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, . . . achigololo, akuchita zoipa ndi amuna . . . ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa; monga mwa uthenga wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka.” (Yerekezerani ndi Levitiko 20:13.)
Yuda 7: “Sodomu ndi Gomora, ndi midzi ya kuizungulira, potsatana nayoyo . . . [iyo] kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.” (Dzina lakuti Sodomu lafikira kukhala magwero a liwu lakuti “usodomu,” limene kaŵirikaŵiri limatanthauza machitachita a kugonana kwa anthu aziŵalo zofanana. Yerekezerani ndi Genesis 19:4, 5, 24, 25.)
Kodi nchiyani chimene chiri mkhalidwe wa Akristu owona kulinga kwa awo amene ali ndi mbiri ya kugonana kwa aziŵalo zofanana?
1 Akor. 6:9-11: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna . . . sadzaloŵa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa mzimu wa Mulungu wathu.” (Mosasamala kanthu ndi chiyambi chotero, ngati anthu tsopano aleka zizoloŵezi zawo zauve zoyambirira, nagwiritsira ntchito miyezo yolungama ya Yehova, nasonyeza chikhulupiriro m’kakonzedwe kake ka kukhululukidwa machimo kupyolera mwa Kristu, angathe kukhala ndi kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu. Pambuyo pa kusintha, iwo angalandiridwe mu mpingo Wachikristu.)
Akristu owona amadziŵa kuti ngakhale zikhumbo zoipa zozika mizu kwambiri, kuphatikizapo zija zimene zingakhale ndi magwero ake m’majini kapena zimene zimachititsidwa ndi mkhalidwe wakuthupi kapena kuchititsidwa ndi malo okhala, siziri zosakhoza kugonjetseka kwa anthu amene amafunadi kukondweretsa Yehova. Mwachibadwa anthu ena ngasontho kwambiri. Mwinamwake kalero anali ofulumira kukwiya kwambiri; koma kudziŵa chifuniro cha Mulungu, chikhumbo cha kumkondweretsa, ndi chithandizo cha mzimu wake zinawakhozetsa kukulitsa kudziletsa. Munthu angakhale chidakwa, koma mwachisonkhezero choyenera, iye angathe kusiya kumwa ndipo motero kupeŵa kukhala chidakwa. Mofananamo, munthuyo angakhale wachimasomaso kwambiri kwa ena aziŵalo zofanana, koma mwa kulabadira uphungu wa Mawu a Mulungu iye angakhoze kukhala woyera ku machitachita a kugonana kwa aziŵalo zofanana. (Wonani Aefeso 4:17-24.) Yehova samatilola kupitirizabe kuganiza kuti khalidwe lolakwa silimapangadi kusiyana; mokoma mtima koma mwamphamvu iye amatichenjeza zotulukapo zake napereka chithandizo chochuluka kwa awo amene afuna ‘kuvula umunthu wakale ndi zizoloŵezi zake, ndi kudziveka [iwo eni] ndi umunthu watsopano.’—Akol. 3:9, 10.
Kodi lingaliro Labaibulo ponena za kugonana liri mwinamwake lachikale ndi loletsa mopambanitsa?
1 Ates. 4:3-8: “Ichi ndichifuniro cha Mulungu . . . kuti mudzipatule kudama . . . iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa mzimu wake woyera kwa inu.” (Lingaliro Labaibulo ponena za kugonana siliri kokha chinthu chimene chinayambidwa ndi anthu amene anakhalako zaka zambiri kalero. Limachokera kwa Mlengi wa anthu; limamveketsa chofunika kuti tikhale ndi chiyanjo chake; limaperekanso malangizo amene amathandiza kukhala ndi mabanja okhazikika ndi abwino, maunansi achimwemwe kunja kwa ukwati. Awo amene amagwiritsira ntchito uphungu uwu amadzitetezera iwo eni ku zipsera zazikulu za maganizo ndi nthenda zonyansa zimene zimayendera limodzi ndi khalidwe lachisembwere. Uphungu Wabaibulo ngwamakono kwambiri m’kukwaniritsa zofunika za awo amene akufuna chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu ndi moyo popanda kugwiritsidwa mwala kosayenera.)
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Kodi nchiyani chimene chiri ganizo lanu kulinga ku kugonana kwa aziŵalo zofanana?’
Mungayankhe kuti: ‘Liri lingaliro losonyezedwa muno m’Baibulo. Ndimakhulupirira kuti zimene limanena nzofunika kwambiri kuposa lingaliro lirilonse la anthu, chifukwa chakuti limeneli limatipatsa malingaliro a Mlengi wa anthu. (1 Akor. 6:9-11) Mudzawona kuti ena a amene anafikira kukhala Akristu poyamba anali ndi chizoloŵezi cha kugonana kwa aziŵalo zofanana. Koma chifukwa cha kukonda kwawo Mulungu, ndi chithandizo cha mzimu wake, anasintha.’
Kapena munganene kuti: ‘M’kuyankha funsolo, ndinganene kuti ndawona kuti ochuluka amene amalingalira kuti palibe chochititsa manyazi chimene chiyenera kugwirizanitsidwa ndi njira ya moyo ya kugonana kwa aziŵalo zofanana samakhulupirira kuti Baibulo ndilo Mawu a Mulungu. Tandilolani ndikufunseni mmene mumawonera Baibulo?’ Ngati munthuyo anena kuti amakhulupirira Baibulo, mwinamwake mungawonjezere kuti: ‘Kugonana kwa aziŵalo zofanana sindiko nkhani yatsopano. Baibulo limasonyeza lingaliro losasintha la Mulungu mwa mawu omvekera bwino kwambiri. (Mwinamwake gwiritsirani ntchito chidziŵitso cha patsamba 180, 181.)’ Ngati munthu asonyeza chikaikiro ponena za kukhalako kwa Mulungu kapena ponena za Baibulo, mungakhoze kuwonjezera kuti: ‘Ngati panalibe Mulungu, ife mwachiwonekere sitikanakhala ndi thayo kwa iye ndipo chotero tikanakhala ndi moyo monga momwe tifunira. Chotero funso lenileni nlakuti, Kodi pali Mulungu ndipo kodi kukhalapo kwanga kukuchokera kwa iye [ndiponso, mwinamwake, Kodi Baibulo nlouziridwa ndi Mulungu]’ (Gwiritsirani ntchito mfundo za patsamba 306-313 kapena 52-62.)’