Tchimo
Tanthauzo: Kwenikweni, kuphonyedwa kwa chizindikiro, mogwirizana ndi kunena kwa malemba apamanja a Baibulo Achihebri ndi Achigiriki. Mulungu mwini amakhazikitsa “chizindikiro” chimene zolengedwa zake zaluntha ziyenera kufikira. Kuphonya chizindikiro chimenecho ndiko tchimo, limenenso liri chisalungamo, kapena kusayeruzika. (Aroma 3:23; 1 Yoh. 5:17; 3:4) Tchimo ndiro kanthu kalikonse kosagwirizana ndi umunthu wa Mulungu, miyezo, njira, ndi chifuniro, zonse zimene ziri zoyera. Lingaphatikizepo khalidwe loipa, kulephera kuchita chimene chiyenera kuchitidwa, kulankhula kosayenera, malingaliro onyasa, kapena zikhumbo kaya zisonkhezero za dyera. Baibulo limasiyanitsa pakati pa tchimo la choloŵa ndi tchimo ladala, pakati pa kuchita tchimo limene munthu amalapa ndi tchimo lochitidwa mwachizoloŵezi.
Kodi zinatheka bwanji kwa Adamu kuchimwa ngati iye anali wangwiro?
Ponena za ungwiro wa Adamu, ŵerengani Genesis 1:27, 31 ndi Deuteronomo 32:4. Pamene Yehova Mulungu analengeza chilengedwe chake cha padziko lapansi, kuphatikizapo mwamuna ndi mkazi, kukhala “zabwino ndithu,” kodi iye anatanthauzanji? Kwa Uyo amene ntchito yake iri yangwiro kukhala atanena kuti zimene adapanga zinali “zabwino ndithu,” ziyenera kukhala zitafikitsa miyezo yake yangwiro.
Kodi ungwiro unafunikiritsa kuti Adamu ndi Hava akhale osakhoza kuchimwa? Wopanga roboti (chinthu chovomera zonse chosazilingalirira chokha) amayiyembekezera kuchita ndendende zimene wailinganizira kuchita. Koma roboti yangwiro sikakhala munthu wangwiro. Mikhalidwe yowoneka kukhala yofunika siiri yofanana. Adamu ndi Hava anali anthu, osati maroboti. Mulungu anapatsa anthu, mphamvu ya kusankha pakati pa chabwino ndi choipa, pakati pa kumvera ndi kusamvera, kupanga zosankha za makhalidwe abwino. Popeza kuti anthu analinganizidwa motere, kusakhoza kupanga zosankha zotere (ndipo osati chosankha chopanda nzeru) ndiko kumene kukanasonyeza kupanda ungwiro.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:19, 20; Yoswa 24:15.
Kuti Adamu ndi Hava ayenerere kukhala atalengedwa ali angwiro, kodi zosankha zawo zonse pambuyo pake zikayenera kukhala zolungama? Kutero kukakhala kofanana ndi kunena kuti analibe ufulu wakudzisankhira. Koma Mulungu sanawapange mwa njira yakuti kumvera kwawo kukangochitika kokha. Mulungu anawapatsa mphamvu ya kusankha, kotero kuti akakhoza kumvera chifukwa chakuti anamkonda. Kapena, ngati analola mitima yawo kukhala yadyera, akakhala osamvera. Kodi ndiziti zimene zimatanthauza zambiri kwa inu—pamene munthu akuchitirani chinthu chifukwa chakuti akukakamizidwa kuchichita kapena chifukwa chakuti akufuna kutero?—Yerekezerani ndi Deuteronomo 11:1; 1 Yohane 5:3.
Kodi ndimotani mmene anthu angwiro otero akanakhalira adyera, kukumatsogolera kumachitachita auchimo? Ngakhale kuli kwakuti analengedwa angwiro, matupi awo sakapitirizabe kugwira ntchito mwanjira yangwiro ngati sanapatsidwe chakudya choyenera. Choteronso, ngati alola maganizo awo kudya malingaliro olakwa, zimenezo zikawaipitsa mwamakhalidwe, kuchimwa. Yakobo 1:14, 15 amalongosola kuti: “Yense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.” Kwa Hava chilakolako cholakwa chinayamba kukula pamene anamvetsera mokondwera kwa Satana, amene anagwiritsira ntchito njoka monga cholankhulira chake. Adamu analabadira chisonkhezero cha mkazi wake cha kugwirizana naye kudya chipatso choletsedwacho. Mmalo mwa kukana malingaliro oipa, onse aŵiri anakulitsa zikhumbo zadyera. Chotulukapo chinali machitidwe a uchimo.—Gen. 3:1-6.
Kodi tchimo la Adamu linali mbali ya “makonzedwe a Mulungu”?
Wonani tsamba 27, pamutu wakuti “Adamu ndi Hava,” ndiponso tsamba 118, pamutu wakuti “Choikidwiratu.”
Kodi palidi chinthu chotchedwa “tchimo” m’masiku ano?
Zitsanzo: Ngati munthu wodwala akanaswa chiwiya chopimira tempichala, kodi kumeneko kukatsimikizira kuti analibe malungo? Ngati mbala inanena kuti sinakhulupirire zimene zalembedwa m’mabukhu amalamulo, kodi zimenezo zikaipangitsa kukhala yopanda liwongo laupanduwo? Mofananamo, chenicheni chakuti anthu ochuluka samakhulupirira kuti nkofunika kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo sichimathetsa tchimo.—Wonani 1 Yoh. 1:8.
Anthu ena angasankhe kuchita zimene Mawu a Mulungu amakaniza. Koma zimenezo sizimatsimikizira Baibulo kukhala lolakwa. Agalatiya 6:7, 8 amachenjeza kuti: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi.” Mliri wa nthenda zopatsirana mwakugonana, mabanja osweka, ndi zina zotero, zikupereka umboni wa kutsimikizirika kwa zimene Baibulo limanena. Mulungu anapanga munthu; Iye amadziŵa zimene zidzatibweretsera chimwemwe cha nthaŵi zonse; Amatiuza m’Baibulo. Kodi sikuli kwanzeru kumvetsera kwa Iye? (Kaamba ka umboni wa kukhalako kwa Mulungu, wonani mutu waukulu wakuti “Mulungu.”)
Kodi mbali yaikulu ya chotchedwa tchimo siiri kokha kuchita zinthu zachibadwa kwa anthu?
Kodi kugonana ndiuchimo? Kodi Adamu ndi Hava anachimwa mwa kugonana? Zimenezo sindizo zimene Baibulo limanena. Genesis 1:28 amanena kuti Mulungu mwiniyo anauza Adamu ndi Hava ‘kubalana ndi kuchuluka ndi kudzaza dziko lapansi.’ Zimenezo zikaloŵetsamo unansi wa kugonana pakati pawo, kodi sichoncho? Ndipo Salmo 127:3 limanena kuti “ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova,” “mphotho.” Kuyenera kudziŵika kuti woyamba kudya chipatso choletsedwacho anali Hava ndipo anatero pamene anali yekha; panali kokha pambuyo pake pamene anapatsa china kwa Adamu. (Gen. 3:6) Mwachiwonekere, mtengo umene unali ndi chipatso choletsedwa unali weniweni. Chimene Baibulo limaletsa sindiwo unansi wakugonana wololedwa ndi lamulo pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, koma machitachita onga dama la chigololo, chigololo, kugonana kwa a ziŵalo zofanana, ndi kugonana ndi zinyama. Zotulukapo za machitachita oipa otero zimasonyeza kuti kuletsako ndiko umboni wa kudera nkhaŵa kwachikondi kwa Uyo amene amadziŵa mmene tinapangidwira.
Gen. 1:27: “Mulungu ndipo adalenga munthu [Adamu] m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye.” (Chifukwa chake, chinthu chachibadwa, chinali chakuti Adamu asonyeze mikhalidwe yoyera ya Mulungu, kulabadira moyamikira chitsogozo cha Mulungu. Kupereŵera pa zimenezi kunali kuphonya chizindikiro, kuchimwa. Wonani Aroma 3:23, ndiponso 1 Petro 1:14-16.)
Aef. 2:1-3: “Ndipo inu [Akristu] amene Mulungu anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu, zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wamzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; amene ife tonsenso tinagonera pakati pawo kale, m’zilakolako zathupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo.” (Monga ana a Adamu wochimwayo, tinabadwira muuchimo. Kuyambira pa kubadwa kumkabe mtsogolo, chikhoterero cha mtima wathu chiri choipa. Ngati sitilamulira zikhoterero zolakwa zimenezo, m’nthaŵi yokwanira tingakhale ozoloŵera njira yotero ya moyo. Kungakhaledi “kozoloŵereka” chifukwa chakuti anthu ena otizinga akuchita zinthu zofananazo. Koma Baibulo limasonyeza cholungama ndi cholakwa m’lingaliro la Mulungu, mogwirizana ndi mmene anapangira munthu ndi chifuno chake kaamba ka anthu. Ngati timvetsera kwa Mlengi wathu ndi kumumvera mwachikondi, moyo udzakhala ndi tanthauzo lolemerera limene sitinali nalo ndi kale lonse, ndipo tidzakhala ndi mtsogolo mwamuyaya. Mlengi wathu akutiitana mwachikondi kulaŵa ndi kuwona mmene iye aliri wabwino.—Sal. 34:8.)
Kodi uchimo umayambukira motani unansi wa munthu ndi Mulungu?
1 Yoh. 3:4, 8: “Yense wakuchita tchimo achitanso kusayeruzika; ndipo tchimo ndiro kusayeruzika. Iye wochita tchimo ali wochokera mwa Mdyerekezi.” (Mawuŵa ngamphamvu chotani nanga! Awo amene mwadala amasankha njira ya uchimo, akumauchita mwachizoloŵezi, amawonedwa ndi Mulungu kukhala apandu. Njira imene iwo asankha ndiyo imene Satana mwiniyo anatenga poyamba.)
Aroma 5:8, 10: “Pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife. . . . pokhala ife adani ake tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake.” (Tawonani kuti ochimwa akutchulidwa kukhala adani a Mulungu. Pamenepo, ndikwanzeru chotani nanga, kuti ife tipindule ndi makonzedwe amene Mulungu wapanga akuyanjanitsidwa naye!)
1 Tim. 1:13: “Anandichitira chifundo [akutero mtumwi Paulo], popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira.” (Koma pamene anasonyezedwa njira yolungama ndi Ambuye, iye sanaleke kuilondola.)
2 Akor. 6:1, 2: “Ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu, (pakuti anena, M’nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza; tawonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, tawonani, tsopano ndiro tsiku la chipulumutso.)” (Tsopano ndiyo nthaŵi pamene mwaŵi wa chipulumutso uli wopezeka. Mulungu sadzapereka kukoma mtima kwachifundo kotero kwa mtundu wa anthu kunthaŵi zonse. Chotero, chisamaliro chifunikira kusonyezedwa kuti tisaphonye chifuno chake.)
Kodi mpumulo kumkhalidwe wathu wauchimo ngwothekera motani?
Wonani mutu waukulu wakuti “Dipo.”