Nyimbo 12
Mulungu Watilonjeza Moyo Wosatha
Losindikizidwa
1. Mulungu watilonjeza
Moyo womwe sudzatha.
‘Ofatsa ’dzasangalala.’
Zidzachitikadi.
(KOLASI)
Tingakhale nawo
Moyo wosathawo,
Tikamayesetsa,
Tidzaupeza.
2. Paradaiso akubwera,
Anthu adzamasuka.
Padzakhaladi mtendere
Wochoka kwa M’lungu.
(KOLASI)
Tingakhale nawo
Moyo wosathawo,
Tikamayesetsa,
Tidzaupeza.
3. Akufa akadzauka,
Chisoninso chidzatha.
Yehova adzapukuta
Misozi yathu.
(KOLASI)
Tingakhale nawo
Moyo wosathawo,
Tikamayesetsa,
Tidzaupeza.
(Onaninso Yes. 25:8; Luka 23:43; Yoh. 11:25; Chiv. 21:4.)