Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mutu Ndi Ndani?
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
    • m’zilembo zikuluzikulu kuti: “ALEKENI AMUNA AMENEWA CHIFUKWA NGATI NTCHITO IYI IKUCHOKERA KWA MULUNGU, MUKHOZA KUPEZEKA KUTI MUKULIMBANA NDI MULUNGU.” Koma izi sizinaphule kanthu. Pa August 3, 1957, amishonale anatengedwa kupita kubwalo la ndege kuti achoke m’dzikolo.

      ‘Yesu Ndi Mutu’

      Chithunzi patsamba 110

      DM’bale Donald Nowills anayamba kuyang’anira ntchito kunthambi ali ndi zaka 20 zokha

      Kodi zinawathera bwanji abale ndi alongo popeza amishonale onse anathamangitsidwa? Kodi analidi opanda mutu monga mmene mkulu wa apolisi uja ananenera? Ayi, chifukwa Yesu ndi ‘mutu wa thupi, lomwe ndi mpingo.’ (Akol. 1:18) Choncho si zoona kuti anthu a Yehova ku Dominican Republic anali opanda mutu. M’malomwake, Yehova ndi gulu lake anapitiriza kuwasamalira.

      Amishonale atachoka, m’bale wina dzina lake Donald Nowills anapatsidwa udindo woyang’anira ntchito kunthambi. Iye anali ndi zaka 20 zokha ndipo anali atabatizidwa zaka 4 zokha m’mbuyomu. Ngakhale kuti anakhala woyang’anira dera kwa miyezi ingapo, ntchito imene anapatsidwa kunthambi inali yachilendo kwa iye. M’bale Nowills anali ndi ofesi yaing’ono m’nyumba yake. Nyumbayo inali yamatabwa ndi malata ndipo pansi panalibe simenti. Inali kudera loipa lotchedwa Gualey mumzinda umene unali likulu la dzikoli. Iye limodzi ndi M’bale Félix Marte ankapanga fotokope magazini a Nsanja ya Olonda n’kumapereka kwa abale m’dziko lonseli.

      Chithunzi patsamba 111

      Fotokope ya Nsanja ya Olonda ya mu 1958

      Pa nthawiyo, M’bale Enrigue Glass anali kundende ndipo mkazi wake dzina lake Mary ankathandiza M’bale Nowills. Mary anati: “Ndinkaweruka kuntchito 5 koloko madzulo ndipo kenako ndinkapita ku ofesi ya M’bale Nowills kuti ndikatayipe Nsanja ya Olonda. Ndiyeno M’bale Nowills ankapanga fotokope magaziniyi pogwiritsa ntchito makina. Tikamaliza, mlongo wina wochokera ku Santiago ankatenga magaziniwa. Mlongoyu tinkangomutchula kuti ‘mngelo’ n’cholinga choti anthu asadziwe dzina lake lenileni. Iye ankawaika m’chitini cha mafuta chachikulu. Kenako ankawafunditsa nsalu pamwamba pake n’kuikapo chinangwa, mbatata kapena zakudya zina. Ndiyeno pamwamba pake ankayalapo chiguduli. Akatero, ankakwera basi n’kupita kumpoto kwa dzikoli n’kukapereka magazini imodzi pa mpingo uliwonse. Abale ndi alongo ankabwerekana magaziniyi kuti aphunzire monga banja.”

      Mary anati: “Tinkafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri. Apolisi anali paliponse ndipo ankafunitsitsa kudziwa kumene tinkapanga fotokope Nsanja ya Olonda. Koma analephera chifukwa Yehova ankatiteteza.

      Bokosi pamasamba 112, 113
  • Tikanatha Kumangidwa Nthawi Iliyonse
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
    • DOMINICAN REPUBLIC

      Tikanatha Kumangidwa Nthawi Iliyonse

      “Ochenjera Ngati Njoka Koma Oona Mtima Ngati Nkhunda”

      Abale ndi alongo ankafunika kupeza mabuku ndi magazini pa nthawi ya bani koma zinali zovuta kwambiri. Abale ambiri ankagwidwa n’kutsekeredwa m’ndende kawirikawiri.

      Mlongo wina dzina lake Juanita Borges anati: “Mu 1953, ndinaphunzira Baibulo ndipo ndinkadziwa kuti nthawi iliyonse ndikhoza kumangidwa chifukwa chokhala wa Mboni za Yehova. Ndiyeno tsiku lina mu November 1958, ndinapita kukaona mlongo wina dzina lake Eneida Suárez. Ndili komweko, apolisi anafika n’kutigwira poganiza kuti tikuchita msonkhano. Tinauzidwa kuti tikhala m’ndende miyezi itatu komanso aliyense alipire chindapusa cha ndalama zokwana mapeso 100 (pa nthawiyo ndalamazo zinali zofanana ndi madola 100 a ku United States).”

      Chithunzi patsamba 115

      Apolisi anali ndi mapepala okhala ndi mayina ndiponso mfundo zina zofunika zokhudza abale ndi alongo athu.

      Boma linachita chilichonse chimene likanatha kuti lilepheretse a Mboni kusonkhana koma sizinatheke. A Mboniwo ankayesetsa kukhala “ochenjera ngati njoka koma oona mtima ngati nkhunda.” (Mat. 10:16) Mlongo wina dzina lake Andrea Almánzar anati: “Tinkafika ku misonkhano pa nthawi zosiyanasiyana. Tikamaliza tinkayenera kuchokanso pa nthawi zosiyana n’cholinga choti anthu asatikayikire. Choncho enafe tinkafika kunyumba usiku.”

      M’bale wina dzina lake Jeremías Glass anabadwa pa nthawi imene bambo ake anali kundende. Iye anakhala wofalitsa ali ndi zaka 7 mu 1957. Abale ndi alongo ankasonkhana m’nyumba yawo ndipo iye akukumbukira zimene ankachita kuti anthu asawadziwe. M’baleyu anafotokoza kuti: “Aliyense amene ankasonkhana ankapatsidwa pepala lokhala ndi nambala imene inkasonyeza nthawi imene ayenera kuchoka pamalopo. Tikamaliza misonkhano, bambo anga ankandiuza kuti ndiime pakhomo kuti ndiziona manambala a anthuwo. Ndinkawauzanso kuti achoke awiriawiri komanso kuti adutse njira zosiyana pochoka.”

      Tinkachitanso misonkhano yathu pa nthawi zimene anthu ambiri sakanadziwa. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Mercedes García anaphunzitsidwa Baibulo ndi amalume ake dzina lawo Pablo González. Amayi a mlongoyu anamwalira iye ali ndi zaka 7 ndipo pa nthawiyo bambo ake anali kundende. Iye anatsala ndi azichimwene ake atatu ndi azichemwali ake 6. Mercedes anabatizidwa ali ndi zaka 9 mu 1959. Pofuna kuti anthu asadziwe, abale anakonza zoti nkhani ya ubatizoyo ikambidwe m’bandakucha. Nkhaniyo inakambidwa kunyumba ya m’bale wina ndipo anthu anabatizidwa mumtsinje wa Ozama umene umadutsa mulikulu la dzikoli. Mercedes anati: “Pa nthawi ya 5:30 m’mawa tinali tikubwerera kunyumba koma anthu ena onse anali atangoyamba kumene kudzuka.”

      Ankawonjezeka Ngakhale Kuti Ankazunzidwa

      Pa nthawi ya bani, chiwerengero cha ofalitsa chinawonjezeka pafupifupi kuwirikiza kawiri ngakhale kuti a Mboniwo ankazunzidwa ndiponso ankanamiziridwa nkhani zosiyanasiyana.

      • 1950 - 292

      • 1960 - 495

  • Sanasiye Kulalikira Ndipo Analandira Ufulu
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
    • DOMINICAN REPUBLIC

      Sanasiye Kulalikira Ndipo Analandira Ufulu

      Ankalalikira Mosamala

      M’bale wina dzina lake Rafael Pared anakhala wofalitsa mu 1957 pamene anali ndi zaka 18. Panopa akutumikira ku Beteli limodzi ndi mkazi wake, Francia. Iye akukumbukira

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena