-
Mmene Yehova Akuyankhira Pemphero Lochokera Pansi PamtimaNsanja ya Olonda—2008 | October 15
-
-
17. Kodi n’chiyani chidzachitike kutsogoloku, ndipo tidzakumbukira chiyani posachedwapa?
17 Tikudziwa kuti nkhondo siinathe. Choncho tipitirizabe kulalikira uthenga wabwino, ngakhale kwa anthu omwe ndi adani athu. (Mat. 24:14, 21) Komabe, mwayi umene adani amenewa ali nawo wakuti alape ndi kupulumutsidwa, utha posachedwapa. Kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kupulumutsidwa kwa anthu. (Werengani Ezekieli 38:23.) Mitundu ya padziko lapansi ikadzagwirizana kuwononga anthu a Mulungu, monga mmene Malemba analoserera, tidzakumbukira pemphero la wamasalmo lakuti: “Achite manyazi, naopsedwe kosatha; ndipo asokonezeke, nawonongeke.”—Sal. 83:17.
18, 19. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikire anthu otsutsa ulamuliro wa Yehova? (b) Kodi nkhani yakuti Yehova posachedwapa atsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira imakukhudzani bwanji?
18 Anthu amene amatsutsa ulamuliro wa Yehova adzawonongedwa mochititsa manyazi. Mawu a Mulungu amanena kuti pa Aramagedo anthu onse “osamvera uthenga wabwino” adzawaweruza kuti alandire “chiwonongeko chamuyaya.” (2 Ates. 1:7-9) Chiwonongeko chimenechi ndiponso kupulumutsidwa kwa anthu amene amalambira Yehova m’choonadi, kudzakhala umboni wotsimikizira kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona. Kupambana kwa Yehova kumeneku sikudzaiwalika m’dziko latsopano. Anthu “olungama ndi osalungama” amene adzaukitsidwe adzaphunzira ntchito zazikulu za Yehova. (Mac. 24:15) M’dziko latsopano limeneli, iwo adzaona umboni wosonyeza kuti ndi nzeru kutsatira ulamuliro wa Yehova. Ndipo anthu ofatsa omwe adzakhalepo sadzavutika kudziwa kuti Yehova ndi Mulungu yekha woona.
-
-
“Ilitu Ndi Dzina Loyera Ndiponso Lalikulu la Mulungu”Nsanja ya Olonda—2008 | October 15
-
-
“Ilitu Ndi Dzina Loyera Ndiponso Lalikulu la Mulungu”
Mawu amenewa ananena ndi Nicholas wa ku Cusa pa ulaliki wake wa m’chaka cha 1430.a Iye anali ndi chidwi m’zinthu zambiri, mwachitsanzo anaphunzira Chigiriki, Chiheberi, zaumulungu, masamu, za kuthambo ndiponso maphunziro a nzeru za anthu. Ali ndi zaka 22, anakhala katswiri wa malamulo a Tchalitchi cha Katolika. Mu 1448, anasankhidwa kukhala kadinala.
Zaka pafupifupi 550 zapitazo, Nicholas wa ku Cusa anakhazikitsa nyumba yosamaliriramo anthu okalamba ku Kues, komwe panopa kumatchedwa kuti Bernkastel-Kues. Tawuni imeneyi ili pamtunda wa makilomita 130 kum’mwera kwa mzinda wa Bonn, ku Germany. Panopa m’nyumba imeneyi mulinso laibulale ya ku Cusa imene ili ndi mipukutu yoposa 310. Umodzi wa mipukutu imeneyi umatchedwa Codex Cusanus 220 mmene mumapezeka ulaliki wa Nicholas wa ku Cusa wa m’chaka cha 1430. Mu ulaliki umenewo, umene mutu wake unali wakuti In principio erat verbum (Pachiyambi Panali Mawu), Nicholas wa ku Cusa anagwiritsa ntchito dzina lakuti Iehoua, lomwe ndi dzina lakuti Yehova mu Chilatini.b Patsamba 56 la mpukutu umenewu, pali mawu onena za dzina la Mulungu. Mawuwa amati: “Ndi dzina limene Mulungu anadzipatsa. Dzina limeneli lili ndi zilembo zinayi. . . . Ilitu ndi dzina loyera ndiponso lalikulu la Mulungu.” Mawu a Nicholas wa ku Cusa amenewa amagwirizana ndi mfundo yakuti dzina la Mulungu limapezeka m’Malemba oyambirira Achiheberi.—Eks. 6:3.
Mpukutu umenewu unalembedwa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1400 ndipo ndi umodzi mwa mipukutu yakale imene ikupezekabe. M’mipukutu imeneyi zilembo zinayi za dzina la Mulungu zimalembedwa kuti “Iehoua.” Zolemba zimenezi ndi umboni winanso wotsimikizira kuti mawu ofanana ndi akuti “Yehova” akhala akugwiritsidwa ntchito kwa zaka zambiri polemba dzina la Mulungu.
-