Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 42 tsamba 230-tsamba 233 ndime 5
  • Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvera
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Mfundo Zopatsa Chidziŵitso, Zofotokozedwa Momveka Bwino
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Khutiritsani Omvetsera Anu, Lingalirani Nawo
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Mawu Oyamba Okopa Chidwi
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 42 tsamba 230-tsamba 233 ndime 5

PHUNZIRO 42

Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvera

Kodi muyenera kuchita motani?

Fotokozani mfundo m’njira yothandiza omvera kulingalira ndi kuona kuti akuphunzirapo kanthu kopindulitsa.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Ngati mungouza anthu zinthu zimene akuzidziŵa kale, chidwi chawo sichipita patali.

KUTI nkhani yanu ikhaledi yophunzitsa kanthu omvera, simufunika kungofotokoza nkhani yopindulitsa. Dzifunseni kuti: ‘N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti omvera ameneŵa akaimvetse nkhani imeneyi? Kodi ndikanene chiyani kuti omverawo akaone kuti apinduladi ndi nkhaniyo?’

Ngati ndi m’sukulu, ndipo mwapatsidwa nkhani yosonyeza mmene mungalalikire munthu, mwininyumbayo ndiye amakhala womvera wanu. Koma nthaŵi zina mumalankhula ku mpingo wonse ngati omvera anu.

Zimene Omvera Anu Akudziŵa. Dzifunseni kuti, ‘Kodi omverawo akudziŵa chiyani pa nkhaniyi?’ Mukatero m’pamene mungadziŵe poyambira nkhani yanu. Ngati mukulankhula ku mpingo wokhala ndi Akristu odziŵa zambiri ochuluka, musangobwereza ziphunzitso zoyambirira zimene ambiri akuzidziŵa kale. Zifutukuleni ziphunzitsozo. Koma ngati palinso atsopano ambiri, ganizirani zofunika kwa magulu onse aŵiri.

Sinthani liŵiro la kafotokozedwe kanu malinga ndi zimene omvera anu akuzidziŵa. Ngati mukuphatikizapo mfundo zodziŵika kwa anthu ambiri, zifotokozeni mofulumirirapo. Koma fotokozani mwachifatse mfundo zimene zingakhale zachilendo kwa ochuluka kotero kuti athe kuzimvetsa bwino.

Mfundo Zophunzitsadi Kanthu. Kuti nkhani ikhale yophunzitsadi kanthu sikutanthauza kuti izikhala ndi mfundo yatsopano nthaŵi zonse. Okamba nkhani ena ali ndi luso lofotokoza mfundo za choonadi zozoloŵereka m’njira yomveketsa bwino zinthu moti omvera ambiri kamakhala koyamba kuzimvetsa bwino mfundozo.

Mu utumiki wa kumunda, si kokwanira kungotchula nkhani imene yamveka panyuzi posonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza. Gwiritsani ntchito Baibulo kuti musonyeze tanthauzo la chochitikacho. Zimenezi zidzathandiza mwininyumba kuphunzirapodi kanthu. Mofananamo, potchula za mphamvu ya chilengedwe kapena zomera kapenanso zamoyo zina, cholinga chanu chisakhale kufotokoza mfundo yosangalatsa ya sayansi imene mwininyumbayo sanaimvepo. M’malo mwake, cholinga chanu chizikhala kugwirizanitsa umboni wa chilengedwe ndi mawu a Baibulo posonyeza kuti pali Mlengi amene amatisamala. Zimenezi zidzathandiza mwininyumba kuona nkhaniyo m’njira yatsopano.

Kufotokoza nkhani yoti anthuwo anaimvapo kale nthaŵi zambiri kungakhale kovutirapo. Koma kuti mukhale mphunzitsi wogwira mtima, muyenera kuphunzira mmene mungachitire zimenezo. Kodi mungachite motani?

Kufufuza kumathandiza. M’malo mofotokoza mfundo zimene mwangokumbukira, gwiritsani ntchito zida zofufuzira zimene tafotokoza pamasamba 33 mpaka 38. Kumbukirani maganizo operekedwa pamenepo pa zolinga zimene muyenera kukwaniritsa. Pofufuza, mungapeze kuti chochitika china cha m’mbiri yakale chosadziŵika kwenikweni chikugwirizana ndi nkhani yanu. Kapena mungapeze nkhani yaposachedwa ya panyuzi imene ingathandize kumveketsa mfundo imene mukufuna kukaifotokoza.

Pamene mukupenda mfundozo, khalani mukulingalira mwa kudzifunsa mafunso akuti chiyani? chifukwa chiyani? liti? kuti? ndani ndi motani? Mwachitsanzo: N’zoona motani? Ndingasonyeze motani kuti n’zoonadi? Kodi pali zikhulupiriro zofala zotani zimene zingalepheretse ena kumvetsa mfundo ya m’Baibulo imeneyi? N’chifukwa chiyani ili yofunika? Kodi iyenera kukhudza motani moyo wa munthu? Ndi chitsanzo chotani chimene chingasonyeze phindu logwiritsa ntchito mfundoyo? Kodi mfundo ya m’Baibulo imeneyi imasonyezanji za khalidwe la Yehova? Malinga ndi nkhani imene mukukambirana, mungafunse kuti: Kodi zimenezi zinachitika liti? Kodi mfundo imeneyi ingatithandize motani lerolino? Mungachititse nkhani yanu kukhala yaumoyo mwa kufunsa ndi kuyankha nokha ena mwa mafunso oterowo.

Nkhani yanu ingafune kuti mugwiritse ntchito malemba odziŵika kwa omvera anu. Kodi mungatani kuti poŵerenga malembawo omvera anu aphunzirepodi kanthu? Musangoŵerenga; afotokozeni.

Kufotokoza lemba lodziŵika kungakhale kophunzitsadi ngati mulidula m’magawo, n’kumasonyeza mbali zokhudza mutu wa nkhani yanu, kenako n’kuzifotokoza. Taonani njira zina zimene mungafotokozere lemba ngati Mika 6:8 m’Baibulo la New World Translation. Kodi “chilungamo n’chiyani”? Kodi pamenepa akufotokoza chilungamo cha ndani? Kodi mungafotokoze motani tanthauzo la mawu akuti “kuchita chilungamo”? Kapena “kukonda chifundo”? Kodi kudzichepetsa n’chiyani? Kodi mfundo zimenezo mungazigwiritse ntchito motani pa munthu wachikulire? Mmene mungagwiritsire ntchito mfundozo zimadalira mutu wanu wa nkhani, cholinga chanu, omvera anu, ndi nthaŵi imene muli nayo.

Kutanthauzira mawu m’njira yosavuta kumathandiza nthaŵi zambiri. Kwa anthu ena, chimakhala chinthu chodabwitsa koma chosangalatsa kudziŵa tanthauzo la “ufumu” wotchulidwa pa Mateyu 6:10. Ngakhale kwa Mkristu amene ndi mkhalakale, kukumbutsa tanthauzo la mawu kungam’thandize kuzindikira bwino kwenikweni tanthauzo la lemba. Chitsanzo ndi pamene tiŵerenga 2 Petro 1:5-8 ndi kumasulira mawu osiyanasiyana otchulidwa m’mavesiwo: chikhulupiriro, ukoma, chizindikiritso, chodziletsa, chipiriro, chipembedzo, chikondi cha pa abale, ndi chikondi. Ngati mawu ofananirako apezeka m’lemba limodzi, kuwatanthauzira kungathandize ena kuona kusiyana kwake. Mawu amenewo angakhale ngati nzeru, kudziŵa, kuzindikira, ndi luntha, otchulidwa pa Miyambo 2:1-6.

Komanso, kungakhale kopindulitsa omvera ena mwa kungofotokoza lemba. Anthu ambiri amadabwa pamene azindikira koyamba kuti dziko lapansi limene lidzawonongedwe lotchulidwa pa 1 Yohane 2:17 ndiwo anthu a makhalidwe oipa, chifukwa dziko lapansi lenileni silikhala ndi chilakolako; makamakanso akaŵerenga Salmo 104:5 limene limanenetsa kuti dziko lapansi silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse. Nthaŵi ina, Yesu anadabwitsa Asaduki mwa kuwaŵerengera lemba limene iwonso amati amalikhulupirira la Eksodo 3:6, kenako analifotokoza kuti limatsimikizira za kuuka kwa akufa.—Luka 20:37, 38.

Nthaŵi zina kumathandiza kutchula nkhani yokhudzana ndi lembalo, zochitika pamene lembalo linali kulembedwa, komanso wolankhula kapena womvera mawuwo. Afarisi anali kulidziŵa bwino kwambiri lemba la Salmo 110. Komabe, Yesu anawafotokozera mfundo yofunika kwambiri yopezeka m’vesi yoyamba. Iye anafunsa kuti: “Muganiza bwanji za Kristu? Ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide. Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu am’tchula Iye bwanji Ambuye, nanena, Ambuye anena kwa Ambuye wanga, Ukhale pa dzanja lamanja langa, kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako. Chifukwa chake ngati Davide am’tchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji?” (Mat. 22:41-45) Mukamafotokoza Malemba mmene Yesu anachitira, mudzathandiza anthu kuŵerenga Mawu a Mulungu mosamala kwambiri.

Wokamba nkhani akatchula pamene buku la m’Baibulo linalembedwa kapena pamene chinachake chinachitika, ayeneranso kufotokoza mmene zinthu zinaliri panthaŵiyo. Mwakutero, omvera adzamvetsa kufunika kwa bukulo kapena chochitikacho.

Kuyerekeza zinthu kungathandizenso kuti zimene munena zikhale zowaphunzitsadi kanthu omvera. Mungasonyeze kusiyana pakati pa zimene anthu ambiri amakhulupirira ndi zimene Baibulo limanena pa nkhaniyo. Kapena mungayerekeze nkhani ziŵiri zofanana za m’Baibulo. Kodi zili ndi mbali zina zosiyana? Chifukwa chiyani? Kodi tikuphunzirapo chiyani? Pochita zimenezi mudzathandiza omvera kuona nkhaniyo m’njira yatsopano.

Ngati nkhani yanu ndi yofotokoza mbali ina ya ulaliki wachikristu, kungakhale kopindulitsa ngati muyamba ndi kupereka chithunzi cha zimene mukufuna kunena. Fotokozani zoyenera kuchita, chifukwa chozichitira, ndi mmene zimakhudzira zolinga zathu zazikulu monga Mboni za Yehova. Ndiyeno fotokozani kochitikira ntchitoyo, liti komanso motani.

Bwanji ngati nkhani yanu ikufuna kuti mufotokoze “zakuya za Mulungu”? (1 Akor. 2:10) Ngati muyamba mwa kutchula ndi kufotokoza mbali zina zofunika kwambiri za nkhaniyo, kudzakhala kosavuta kuti amvetse mfundo zinazo. Ndipo ngati potsiriza pake mubwerezanso mfundo zazikulu, omvera anu adzakhala okhutira kuti aphunzirapodi kanthu.

Malangizo pa Moyo Wachikristu. Omvera anu angapindule kwambiri ngati muwathandiza kuona mmene mfundo za nkhani yanu zimakhudzira miyoyo yawo. Pamene mukupenda malemba m’nkhani yoti mukakambe, dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani nkhaniyi inasungidwa m’Malemba mpaka m’nthaŵi yathu ino?’ (Aroma 15:4; 1 Akor. 10:11) Ganizirani mikhalidwe imene omverawo akukumana nayo pa moyo wawo. Perekani malangizo ndi mfundo za makhalidwe abwino za m’Malemba pa mikhalidweyo. M’nkhani yanuyo, sonyezani mmene Malemba angathandizire munthu kutenga njira yanzeru pothana ndi mikhalidweyo. Pewani kunena zinthu mwachisawawa. Fotokozani maganizo ndi machitidwe akutiakuti amene ayenera kuwadziŵa.

Choyamba, gwiritsani ntchito njira imodzi kapena ziŵiri m’nkhani imene mukukonzekera. Pamene mukuyamba kuzoloŵera, onjezerani zina. M’kupita kwa nthaŵi, mudzaona kuti omvera anu azilakalaka kumvera nkhani zanu, pokhala ndi chidaliro kuti adzaphunzirapo kanthu kowapindulitsadi.

MMENE MUNGACHITIRE ZIMENEZO

  • Ganizirani zimene omvera anu akudziŵapo kale pankhaniyo.

  • Sinthasinthani liŵiro la kafotokozedwe kanu—mofulumirirapo pa mfundo zodziŵika bwino, mwachifatse pa mfundo zatsopano.

  • Musangotchula chabe mfundo; fotokozani tanthauzo ndi phindu lake.

  • Limbikitsani maganizo anu kulingalira mwa kudzifunsa kuti: Chiyani? Chifukwa chiyani? Liti? Kuti? Ndani? Motani?

  • Lingalirani Malemba mofatsa; fotokozani mbali zake zofunikira.

  • Yerekezani ndi kusiyanitsa zinthu.

  • Perekani chithunzi choyenera cha nkhani yanu yonse.

  • Sonyezani mmene angagwiritsire ntchito mfundozo kuthetsa mavuto ndi kusankha zochita.

ZOCHITA: (1) Fufuzani kuti mupeze mfundo yophunzitsa kanthu pa lemba lodziŵika, monga Mateyu 24:14 kapena Yohane 17:3. (2) Ŵerengani Miyambo 8:30, 31 ndi Yohane 5:20. Kodi kusinkhasinkha za ubale wa pakati pa Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu, monga afotokozera m’mavesiŵa, kungakuthandizeni motani kuthandiza banja ndi mavesiwo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena