Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya June 2017
JUNE 5-11
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 51-52
it-2 360 ¶2-3
Amedi, Mediya
Anaphatikizana ndi Aperisiya pogonjetsa Babulo. M’zaka za m’ma 700 B.C.E., mneneri Yesaya anali ataneneratu kuti Yehova adzachititsa Amedi kuti aukire Babulo. Iye anati: “Iwowa amaona kuti siliva si kanthu, ndipo sasangalala ndi golide. Ndi mauta awo, adzaphwanyaphwanya ngakhale anyamata awo.” (Yes. 13:17-19; 21:2) Palembali, “Amedi” akuphatikizaponso Aperisiya. Tikutero chifukwa chakuti ngakhale olemba mbiri Achigiriki ankakonda kugwiritsa ntchito dzinali pofotokoza za onse, Amedi ndi Aperisiya. Iwo ankaona kuti siliva ndi golide si kanthu chifukwa cholinga chawo chinali kugonjetsa Babulo osati kulanda zinthu zawo. Choncho iwo sakanalandira ziphuphu kapena malipiro aliwonse kuti alephere kukwaniritsa cholinga chawochi. Mofanana ndi Aperisiya, Amedi ankagwiritsa ntchito kwambiri mauta. Iwo ankaponya mivi yambiri ndi mauta awo athabwa omwe nthawi zina ankawakuta ndi mkuwa (yerekezerani ndi Sal. 18:34), ‘pophwanyaphwanya anyamata a ku Babulo,’ kapena kuti powaononga. Amedi ankanola kwambiri mivi yawo n’cholinga choti akabaya izilowa mkati kwambiri.—Yer. 51:11.
Yeremiya (51:11, 28) ananena kuti “mafumu a ku Mediya” adzakhala m’gulu la olimbana ndi Babulo. Potchula kuti mafumu osati mfumu, iye anasonyeza kuti ngakhale pamene Koresi ankalamulira pankakhalanso mfumu kapena mafumu a Amedi amene ankamuthandiza kulamulira. Zimenezi sizinali zachilendo malinga ndi chikhalidwe cha pa nthawiyo. (Yerekezeraninso ndi Yer. 25:25.) N’chifukwa chakenso Ababulo atagonjetsedwa ndi magulu ankhondo ogwirizana a Amedi, Aperisiya, Aelamu ndi mitundu ina yoyandikana nawo, Dariyo Mmedi ndi amene “anaikidwa kukhala mfumu ya ufumu wa Akasidi.” Zimenezi zikusonyeza kuti amene anamupatsa ufumuwo anali Mfumu Koresi ya ku Perisiya.—Dan. 5:31; 9:1.
it-2 459 ¶4
Nabonidus
Pofotokoza zimene zinachitika usiku umene Babulo anawonongedwa, n’zochititsa chidwi kuti Mbiri ya Nabonidus imati: “Magulu a nkhondo a Koresi analowa m’Babulo popanda kumenya nkhondo.” Izi zikutanthauza kuti Koresi analowa mumzinda wa Babulo popanda wolimbana naye ndipo n’zogwirizana ndi zimene ulosi wa Yeremiya unanena kuti ‘Amuna amphamvu a ku Babulo asiya kumenya nkhondo.’—Yer. 51:30.
it-1 237 ¶1
Babulo
M’chaka chosaiwalika cha 539 B.C.E., ulemerero wa Babulo unayamba kuchepa pamene mzindawo unawonongedwa. Ababulo anagalukira Mfumu Dariyo I (Hystaspis) ya ku Perisiya, maulendo awiri ndipo pa nthawi yachiwiriyi, Aperisiya anagonjetsa Babulo. Mfumu Sasta I anadzawononganso mbali ina ya mzindawo itayamba kukonzedwa, chifukwa choti anamupandukira. Alekizanda Wamkulu ankafuna kuti mzinda wa Babulo ukhale likulu la ulamuliro wake, koma pasanapite nthawi anamwalira mu 323 B.C.E. Kenako Niketa anagonjetsa mzindawu m’chaka cha 312 B.C.E. ndipo anatenga zipangizo zosiyanasiyana n’kuwoloka nazo mtsinje wa Tigirisi n’cholinga choti akazigwiritse ntchito pomanga likulu lake latsopano ku Selukeya. Komabe Chikhristu chitangoyamba kumene, mtumwi Petulo ankafika ku Babulo chifukwa kunali Ayuda ena omwe ankakhala kumeneko, monga mmene analembera m’kalata yake. (1 Pet. 5:13) Zolemba zina zakale zomwe zinapezeka, zimasonyeza kuti kachisi wa Ababulo wa Beli anali adakalipo mpaka m’zaka za m’ma 75 C.E. Koma pofika m’zaka za m’ma 300 C.E., mzindawo unali utawonongedwa ndipo sunakhaleponso, unangosanduka “milu yamiyala.”—Yer. 51:37.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 444 ¶9
Phiri
Limaimira maboma. M’Baibulo, nthawi zina mapiri amaimira ufumu kapena maboma. (Dan. 2:35, 44, 45; yerekezerani Yes. 41:15; Chiv. 17:9-11, 18.) Babulo akutchulidwa kuti ndi “phiri lowononga” chifukwa anali ndi asilikali amphamvu ndipo ankagonjetsa mayiko ambiri. (Yer. 51:24, 25) Salimo lina lomwe limayerekezera Yehova akulimbana ndi gulu la ankhondo limati, iye ‘wazunguliridwa ndi kuwala, ndipo ndi wochititsa nthumanzi kuposa mapiri amene muli nyama zodya zinzake.’ (Sal. 76:4) “Mapiri amene muli nyama zodya zinzake” akuimira maufumu ankhanza. (Yerekezerani ndi Nah. 2:11-13) Ponena zimene Yehova anamuchitira, Davide anati: “Munakhazikitsa mwamphamvu phiri langa,” kutanthauza kuti Yehova ndi amene anachititsa kuti ufumu wa Davide ukwezeke komanso kuti ukhazikike. (Sal. 30:7; yerekezerani 2 Sam. 5:12.) Mfundo yoti mapiri amaimira maufumu ingathandize munthu kumvetsa zimene zikufotokozedwa pa Chivumbulutso 8:8, zoti “chinachake chokhala ngati phiri lalikulu chinaponyedwa m’nyanja chikuyaka moto.” Pofotokoza kuti phirili likuyaka, zikusonyeza kuti umenewu ndi ulamuliro wokhala ndi mphamvu zowononga ngati moto.
it-2 882 ¶3
Nyanja
Magulu a asilikali. Yeremiya anafotokoza kuti asilikali amene adzaukire Babulo “phokoso lawo lili ngati phokoso la nyanja yowinduka.” (Yer. 50:42) Choncho pamene ananeneratu kuti “nyanja” idzamiza Babulo, ankatanthauza kuti magulu a asilikali a Amedi ndi Aperisiya adzagonjetsa Babuloyo.—Yer. 51:42; yerekezerani Dan. 9:26.
JUNE 19-25
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 1-5
it-1 1214
Matumbo
Matumbo amagwira ntchito yaikulu kwambiri kuti chakudya chigayidwe. Mfundo imeneyi inafotokozedwa mophiphiritsira pofotokoza zimene zimachitika pogaya chakudya chauzimu. M’masomphenya, Ezekieli anauzidwa kuti adye mpukutu ndipo udzaze m’matumbo (m’chiheberi, me·ʽimʹ) ake. Ezekieli ankafunika kuwerenga komanso kusinkhasinkha mawu a mumpukutu n’kuwasunga mumtima mwake kuti apeze mphamvu. Izi zinamuthandiza kuti akhale wolimba mwauzimu komanso zinamulimbikitsa kuti aziuza ena uthengawo.—Ezek. 3:1-6; yerekezerani ndi Chiv. 10:8-10.