Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya July 2017
JULY 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 15-17
Yehova Anasolola Lupanga Lake
Olamulira a Babulo ndi Igupto anayerekezedwa ndi ziwombankhanga zazikulu. Chiwombankhanga china chinathyola nsonga ya mtengo wa mkungudza mwa kuchotsa Mfumu Yehoyakini pampando n’kuikapo Zedekiya. Ngakhale kuti Zedekiya analonjeza kuti adzakhala wokhulupirika kwa Nebukadinezara, iye anaswa pangano lake pamene anafuna thandizo kwa wolamulira wa Iguputo, yemwe anali chiwombankhanga china chachikulu. Ngati Zedekiya anatchula dzina la Mulungu popanga pangano lake, kuswa panganolo kunanyozetsa dzina la Yehova. Zimenezi zikutithandiza ifenso kuti tiziyesetsa kukwaniritsa zimene talonjeza kuti tisamanyozetse dzina la Yehova. Ndife amwayi chifukwa timadziwika ndi dzina lake monga Mboni za Yehova.—Ezekieli 17:1-21.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Yehova Anasolola Lupanga Lake
Chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu ake, Yuda anayerekezedwa ndi mtengo wa mpesa womwe subereka zipatso ndiponso wongoyenera kukhala nkhuni. (Ezekieli 15:1-8) Anayerekezedwanso ndi khanda lotayidwa lomwe Mulungu analipulumutsa kuchokera ku Iguputo ndipo analilera mpaka kukhala mayi. Kenako Yehova anamutenga kukhala mkazi wake koma iye anayamba kulambira milungu yonyenga, komwe kunali ngati kuchita chigololo, ndipo analangidwa. Komabe, kwa Ayuda okhulupirika, Mulungu ‘anakhazikitsa pangano losatha,’ lomwe ndi pangano latsopano ndi Isiraeli wauzimu.—Ezekieli 16:1-63; Yeremiya 31:31-34; Agalatiya 6:16.
JULY 31-AUGUST 6
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 24-27
si 133 ¶4
Buku la M’Baibulo la Nambala 26—Ezekieli
Umboni wina wosonyeza kuti zimene Ezekieli analemba n’zodalirika umaonekera pa kukwaniritsidwa kwa maulosi ake onena za Turo, Iguputo komanso Edomu. Mwachitsanzo, iye analosera kuti Turo adzawonongedwa ndipo mbali ina ya ulosiwo inakwaniritsidwa pamene Nebukadinezara analanda mzindawo atauzinga kwa zaka 13. (Ezek. 26:2-21) Pa nthawiyi, mzinda wa Turo sunawonongedweretu wonse. Koma Yehova anali atanena kuti mzindawu uyenera kuwonongedwa mpaka kutheratu. Kudzera mwa Ezekieli Yehova ananeneratu kuti: “Ine ndidzapala fumbi lake n’kumusandutsa malo osalala opanda kanthu kalikonse, apathanthwe. . . . Miyala yako, zinthu zako zamatabwa ndi fumbi lako, adzaziponya m’madzi.” (26:4, 12) Ulosi umenewu unakwaniritsidwa patadutsa zaka zoposa 250, pamene Alekizanda Wamkulu anaukira mbali ina ya mzinda wa Turo yomwe inali panyanja. Asilikali a Alekizanda anapala zogumuka zonse za mabwinja a Turo n’kukaziponya m’nyanja kuti apange msewu womwe unali wautali mamita 800 woti adutse pokawononga mzinda wapanyanjawo. Mu 332 B.C.E., iwo anayamba kukwera mpanda wa mzindawo womwe unali wautali mamita 46 kuti aulande. Anthu ambiri a mumzindawo anaphedwa ndipo ena anagulitsidwa kuti akakhale akapolo. Monganso mmene Ezekieli ananenera, Turo anakhala ‘malo osalala apathanthwe lopanda kanthu ndiponso malo oyanikapo makoka.’ (26:14) Komanso Aedomu omwe anachitira Ayuda zinthu mwachinyengo anawonongedwa. Izi zinakwaniritsanso ulosi wa Ezekieli. (25:12, 13; 35:2-9) Maulosi a Ezekieli onena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndiponso kubwezeretsedwa kwa Aisiraeli kuchoka ku ukapolo nawonso anali olondola.—17:12-21; 36:7-14.
ce 216 ¶3
Kodi Baibulo Linauziridwadi ndi Mulungu?
Mzinda wa Turo unali doko lotchuka kwambiri ku Foinike. Anthu a mumzindawu anachitira zoipa Aisiraeli amene ankalambira Yehova omwe anali chakummawa kwa dziko lawo. Kudzera mwa mneneri Ezekieli, Yehova ananeneratu kudakali zaka zoposa 250 kuti mzinda wa Turo udzawonongedwa kotheratu. Yehova ananena kuti: “Ndikutumizira mitundu yambiri ya anthu . . . Mitunduyo idzagwetsa mpanda wa Turo ndi kugumula nsanja zake. Ine ndidzapala fumbi lake n’kumusandutsa malo osalala opanda kanthu kalikonse, apathanthwe. Iye adzakhala malo oyanikapo makoka pakati pa nyanja.” Ezekieli ananeneratunso mtundu umene udzayambirire kuukira Turo komanso mtsogoleri wake. Iye anati: “Ine ndidzatumiza Nebukadirezara mfumu ya Babulo.”—Ezekieli 26:3-5, 7.
it-1 70
Alekizanda
M’malo moti Alekizanda apitirize kuthamangitsa Aperisiya omwe anawagonjetsa pa nkhondo ziwiri za ku Asia Minor (yoyamba ku mtsinje wa Gelenikasi, yachiwiri ku chigwa cha Isase, komwe anagonjetsa asilikali amphamvu a Perisiya pafupifupi 500,000), iye anayamba kulimbana ndi mzinda wa Turo. Zaka zambiri izi zisanachitike, maulosi ananeneratu kuti mipanda, nsanja, nyumba ndiponso fumbi la mzinda wa Turo zidzaponyedwa m’nyanja. (Ezek. 26:4, 12) N’zoonekeratu kuti Alekizanda anatenga zogumuka za mzinda wa Turo umene Nebukadinezara anawononga n’kukamangira msewu wautali mamita 800 kukafika pa mzinda wapanyanja. Mu July 332 B.C.E., iye ndi asilikali ake apanyanja omwe anali ndi zida zamphamvu, anawononga mzindawu omwe unali ngati dona wonyada wapanyanja.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Yehova Anasolola Lupanga Lake
Ezekieli anayenera kuchita chinthu china chachilendo. (Werengani Ezekieli 24:15-18.) Kodi n’chifukwa chiyani mneneriyu sankayenera kusonyeza chisoni pamene mkazi wake anamwalira? Ankafunika kuchita zimenezi posonyeza kuti Ayuda adzasokonezeka chifukwa cha kuwonongedwa kwa Yerusalemu, nzika zake, komanso kachisi. Ezekieli anali atalankhula mokwanira zokhudza nkhaniyi ndipo sankafunikanso kuuza anthu uthenga wina wochokera kwa Mulungu mpaka Yerusalemu atawonongedwa. Mofanana ndi zimenezi, Matchalitchi Achikhristu ndi anthu awo adzasokonezeka pa nthawi imene azidzawonongedwa. Ndipo “chisautso chachikulu” chikamadzayamba, zimene Akhristu odzozedwa omwe ali ngati mlonda akhala akunena zokhudza kuwonongedwa kwa matchalitchiwa zidzakhala zokwanira. (Mateyu 24:21) Pamene “lupanga” la Mulungu lizidzawononga Matchalitchi Achikhristuwa ndi ena, onse ‘adzadziwa kuti iye ndi Yehova.’—Ezekieli 24:19-27.