Yenderani Limodzi ndi Gareta Lakumwamba la Yehova
‘Ukanene nawo mawu anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva.’—EZEKIELI 2:7.
1, 2. Kodi nchoyendera chachifumu chiti chimene Ezekieli anachiwona, ndipo kodi anauzidwanji?
GARETA lakumwamba la Yehova tsopano likuima pamaso pa atumiki ake. Ndimaso achikhulupiriro, iwo akuwona choyendera chachifumu cha Mfumu Ambuye wawoyo. Nchaulemerero, chowopsa, chachikulu.
2 Choyendera chachifumu chimodzimodzicho chinaima pamaso pa mneneri wa Mulungu Ezekieli m’masomphenya zaka 2,600 zapitazo. Kuchokera pa gareta lokhala ndi mpando wachifumuli—gulu lakumwamba la Mulungu la zolengedwa zauzimu—Yehova anapereka lamulo lamphamvu iri kwa Ezekieli: ‘Anawa, ndiwo achipongwe ndi ouma mtima, ndikutumiza kwa iwo; ndipo ukanene nawo, Atero Yehova Mulungu. Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, pakuti ndiwo nyumba yopanduka, koma adzadziŵa kuti panali mneneri pakati pawo.’—Ezekieli 2:4, 5.
3. Kodi Ezekieli ali ndi mnzake wamakono uti?
3 Ezekieli anagamula kuisamalira ntchitoyo, akumatumikira monga chipangizo chimodzi mdzanja laumulungu. Mofananamo, Mulungu tsopano akulamulira gulu limodzi monga chipangizo chake. Gulu la Ezekieli, otsalira odzozedwa, liri kutsogolo kwantchito ya kupereka umboni womalizira, umene ‘khamu lalikulu’ la “nkhosa zina” nlogwirizana kuuchilikiza. (Chibvumbulutso 7:9, 10; Yohane 10:16) Onse pamodzi akupanga “gulu limodzi,” ndi Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, akumaŵatsogolera pansi pa ufumu wa Wokwera Gareta wamkulu, Yehova Mulungu.
4, 5. Kodi gulu lowoneka ndi maso la Mulungu linakhalako motani, ndipo kodi lakumana ndi chiyani mogwirizana ndi Yesaya 60:22?
4 Pansi pa chitsogozo cha Yehova, gulu lapadziko lonseli lakula kuchokera pachiyambi chaching’ono kukhala chipangizo champhamvu cholengezera lamulo lakuti ‘opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.’ (Chibvumbulutso 14:7) Monga momwe Ezekieli sananyamuke kapena kudziika yekha kukhala mneneri, choteronso gulu lowoneka ndi maso la Mulungu silinadzipange kapena kudziika lokha pathayo lakelo. Silinachokere m’chifuniro kapena kuyesayesa kwa munthu. Wokwera Gareta waumulungu ndiye anachititsa gululi kukhalako. Mwakupatsidwa mphamvu ndi mzimu wa Mulungu ndi kuchilikizidwa ndi angelo oyera, anthu a Yehova akumana ndi kufutukuka kodabwitsa koteroko kwakuti ‘wochepa wasanduka mtundu wamphamvu.’—Yesaya 60:22.
5 Mboni za Yehova zoposa 4,000,000 zikulengeza uthenga Waufumu m’maiko 212. Iwo aikidwa m’magulu a mipingo yoposa 63,000 yolinganizidwa m’madera ndi zigawo. Nyumba zazikulu za maofesi anthambi ndi zosindikizira zikugwira ntchito pansi pa chitsogozo cha Bungwe Lolamulira monga malo apakati a likulu la gululo. Iwo onsewo akuyenda patsogolo, ngati kuti anali munthu mmodzi, akumalalikira mbiri yabwino, naphunzitsa omwe akuvomereza, ndikumanga malo osonkhanira. Inde, gulu lowoneka ndi maso la Yehova likuyendera limodzi ndi gareta lakumwamba ndi Wokwera wake.
6. Kodi chikuphatikizidwa nchiyani ndi kuyendera limodzi ndi gulu lowoneka ndi maso la Yehova?
6 Ngati ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova, kodi mukuyendera limodzi ndi gulu lowoneka ndi maso la Mulungu? Kuchita tero sikupezeka kumisonkhano Yachikristu chabe ndi kuthera nthaŵi muuminisitala. Choyamba, kuyenda kumatanthauza kupita patsogolo ndi kukula kwauzimu. Kumaphatikiza kukhala ndi kapenyedwe kabwino, kuika zinthu zoyenera kuchitidwa choyamba zoyenerera, ndikukhala watsopano nazo. Ngati tikuyendera limodzi ndi gareta lakumwamba la Yehova, miyoyo yathu idzakhala yogwirizana ndi uthenga umene timaulalikira.
7. Kodi nkuwulingaliriranji mkhalidwe wa Ezekieli monga mneneri wa Mulungu?
7 Pankhani yoyendera limodzi, atumiki amakono a Yehova angaphunzire zambiri kuchokera m’chitsanzo cha Ezekieli. Chinkana kuti anaikidwa mwapadera ndi Yehova kukhala mneneri, Ezekieli anali nawobe malingaliro, zodetsa nkhaŵa, ndi zosoŵa. Mwachitsanzo, monga mwamuna wokwatira wachichepere mofanana ndi ena, iye anavutika ndi chisoni cha kuferedwa mkazi wake. Chikhalirechobe, iye sanaiŵale ntchito yake monga mneneri wa Yehova. Mwakulingalira mmene Ezekieli anadzisamalira m’nkhani zinanso, tingadzilimbikitse kuyenderabe limodzi ndi gulu lowoneka ndi maso la Mulungu. Ichi chidzatitheketsa kuyendera limodzi ndi gulu lake losawoneka ndi maso.
Ntchito Inalandiridwa ndi Kukwaniritsidwa
8. Ponena za ntchito yake, kodi nchitsanzo chotani chimene Ezekieli anakhazikitsa?
8 Ezekieli anakhazikitsa chitsanzo chabwino mwa kuvomereza ntchito yake ndi kuikwaniritsa. Komabe, chimvero ndi kulimba mtima zinafunikira poichita, pakuti tikuŵerenga kuti: ‘Wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuwopa mawu awo; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usawopa mawu awo kapena kuwopsedwa ndi nkhope zawo; pakuti ndiwo nyumba yopanduka. Ndipo ukanene nawo mawu anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva; pakuti iwo ndiwo opanduka. Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ichi ndirikunena nawe; usakhale iwe wopanduka, ngati nyumba ija yopanduka.’—Ezekieli 2:6-8.
9. Kodi Ezekieli akakhala wopanda liŵongo lamwazi kokha mwakuchita chiyani?
9 Ezekieli sanafunikire kuchita mphwayi kapena kukhala wamantha, wofunikira kusonkhezeredwa nthaŵi ndi nthaŵi kuti akwaniritse ntchito yake. Iye akakhala wopanda liwongo lamwazi akadakhala wofunitsitsa ndi wolimba mtima kulankhula mawu a Yehova basi. Ezekieli anauzidwa kuti: ‘Koma ukachenjeza woipa, osabwerera iye kuleka choipa chake kapena njira yake yoipa, adzafa mu mphulupulu yake; koma iwe walanditsa moyo wako.’—Ezekieli 3:19.
10. Kodi gulu la Ezekieli latsimikizira motani kukhala lofanana ndi mneneriyo?
10 Mofanana ndi Ezekieli, gulu lodzozedwa la Ezekieli lavomereza ntchito yawo yopatsidwa ndi Mulungu ndipo likuikwaniritsa. Ngati ndife Mboni za Yehova, tiyenera kukumbukira kuti moyo wathu ndi miyoyo ya ena imadalira pa chimvero chathu. (1 Timoteo 4:15, 16) Mboni iriyonse iyenera kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova. Mulungu sadzatimangirira ku gareta lake namatiguza. Kuchita mphwayi ndikukhala ndi mtima wogawanika nkupeputsa Wokwera pa Gareta. Chotero gulu lowoneka ndi maso la Yehova likutilangiza kusungabe zikondwerero zaumulungu kukhala zazikulu m’miyoyo yathu. Kuvomereza kokhazikika malangizowa kumatisungabe ogwirizana ndi gulu la Mulungu ndipo kumakweza uminisitala wathu wopatulika kukhala wapamwamba m’mayendedwe, osati wamba. Ndithudi, anthu a Yehova chapamodzi amasonyeza kudzipereka kodabwitsa. Mbali yathu munthu aliyense payekha njakusungabe mayendedwewo.
Mawu a Mulungu Alandiridwa Mumtima
11. Kodi Ezekieli anakhazikitsa chitsanzo chotani ponena za mawu a Mulungu?
11 Ezekieli anakhazikitsanso chitsanzo chabwino mwakulandira mawu a Mulungu mumtima mwake. Atalamulidwa, iye anadya bukhu lopatsidwa ndi Mulungu, kapena mpukutu. Ezekieli akuti: ‘Mkamwa mwanga munazuna ngati uchi.’ Chinkana kuti mpukutuwo unadzala ndi ‘nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka,’ unali wozuna kwa Ezekieli chifukwa chakuti anayamikira ulemu wa kuimira Yehova. Chinali chokumana nacho chozuna kwa mneneriyo kukwaniritsa ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu. Mulungu anamuuza kuti: ‘Wobadwa ndi munthu iwe, mawu anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m’mtima mwako, utawamva m’makutu mwako.’ (Ezekieli 2:9–3:3, 10) Masomphenyawo anachititsa Ezekieli kukhala wogalamuka kotheratu za chimene Mulungu anamulola kukhalamo ndi phande ndipo analimbitsa unansi wake ndi Yehova.
12. Kodi Ezekieli anachitanji m’zaka zoposa makumi aŵiri zautumiki waulosi?
12 Ezekieli anapatsidwa masomphenya ndi mauthenga a zifuno zosiyanasiyana ndi onka kwa magulu a anthu osiyanasiyana. Anafunikira kumvetsera mosamalitsa kenaka nkulankhula ndi kuchita mogwirizana ndi malangizowo. Mawu ndi njira zatsopano zinavumbulidwa kwa iye nthaŵi ndi nthaŵi mkati mwa zaka 22 zautumiki waulosi. Nthaŵi zina Ezekieli anafotokoza mawu authenga mwapadera. Nthaŵi zinanso, iye anatembenukira ku zifanizo, monga kugona pambali panjerwa yophiphiritsira Yerusalemu. (Ezekieli 4:1-8) Chitsanzo chake m’nkhani zokhudza munthu mwini, monga ngati mmene anayambukiridwira ndi imfa ya mkazi wake, chinaperekanso uthenga. (Ezekieli 24:15-19) Anafunikira kuchita zatsopano, akumapereka uthenga wolondola nthaŵi zonse nachita kachitidwe koyenerana ndi nthaŵi. Ezekieli anaikidwa muunansi wathithithi, wa kugwira ntchito kopitirizabe ndi Yehova.
13. Kodi tingaumange motani unansi wathithithi ndi Yehova?
13 Mofananamo, kuti timange ndikusunga unansi wathithithi ndi Yehova monga antchito anzake, tiyenera kuika Mawu a Mulungu m’mtima mwathu. (1 Akorinto 3:9) Kuyendera limodzi ndi gulu lowoneka ndi maso la Mulungu pankhaniyi kumafunikira kuti tigwirizane ndi kuperekedwa kwa chakudya chauzimu pamene chikugaŵiridwa panthaŵi yake. (Mateyu 24:45-47) “Chinenero choyera” chikukula mokhazikika. (Zefaniya 3:9, NW) Nkokha titakhala oyendera nacho pamodzi mpomwe tidzakhaladi okhoza kuvomereza mwachimvero ku zitsogozo za Wokwera pa Gareta.
14, 15. Kodi ndi dongosolo lotani limene likufunika kuti tisungebe mayendedwe okhazikitsidwa ndi gulu la Mulungu?
14 Kuti tifike apa, timafunikira dongosolo labwino laumwini la pemphero, phunziro laumwini, ndi kukhala ndi phande muuminisitala woyera wa mbiri yabwino. (Aroma 15:16) Kumbukirani chitsanzo cha Ezekieli cha kudya mpukutu wokhala ndi uthenga wa Mulungu. Ezekieli anaudya mpukutu wonsewo, osati wochepa. Iye sanatenge ndikusankha zapamtima pake zomwe zikamsangalatsa kwambiri. Mofananamo, phunziro lathu laumwini la Baibulo ndi mabuku Achikristu liyenera kulinganizidwa kuti tiyendere limodzi ndi zakudya zauzimu zoperekedwa, ndipo tiyenera kudya chakudya chonse choikidwa pagome lauzimu, kuphatikizapo zowonadi zakuya.
15 Kodi timapanga kuyesayesa kwapemphero kuzindikira zakudya zolimba? Kuyendera limodzi kumafunikiritsa kuti chidziŵitso chathu ndi kumvetsetsa kupite patsogolo kuchoka pa zoyambirira, pakuti timaŵerenga kuti: ‘Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mawu a chilungamo; pakuti ali khanda. Koma chakudya chotafuna chiri cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ (Ahebri 5:13, 14) Inde, kupanga kupita patsogolo kwauzimu ndimbali yofunika ya kuyenda paliŵiro limene gulu la Mulungu lakhazikitsa.
Osaletsedwa ndi Mphwayi
16, 17. Kodi Ezekieli anachita motani ndi mphwayi, kusekedwa, ndikusavomereza?
16 Ezekieli anakhazikitsanso chitsanzo chabwino mwa kukhala womvera ndikusadzilola kuletsedwa ndi mphwayi kapena kusekedwa. Mofananamo, mwa kugwirizana ndi kukula kwa chinenero choyera, timazoloŵeretsedwa ndi chitsogozo choperekedwa ndi munthu wachifumu Wokwera pa Gareta. Chotero tiri okonzekeretsedwa kuvomereza malamulo ake, olimbitsidwa kukhala osaletsedwa ndi mphwayi kapena kusekedwa ndi anthu amene timalankhula nawo uthenga wa chiweruzo cha Yehova. Mofanana ndi Ezekieli, Mulungu watichenjezeratu kuti anthu ena adzatsutsa kosalekeza, pokhala ouma mutu ndi ouma mtima. Ena sakamva chifukwa chakuti samafuna kumvetsera kwa Yehova. (Ezekieli 3:7-9) Ena akakhalabe achinyengo, monga mmene Ezekieli 33:31, 32 akunenera kuti: ‘Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mawu ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pawo anena mwachikondi, koma mtima wawo utsata phindu lawo. Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yachikondi ya woimba bwino, woimba limba bwino; pakuti akumva mawu ako, koma osawachita.’
17 Kodi chotulukapo chikakhala chotani? Vesi 33 likuwonjezera kuti: ‘Ndipo pakuchitika ichi, pakuti chifikadi, pamenepo adzadziŵa kuti panali mneneri pakati pawo.’ Mawu amenewo akuvumbula kuti Ezekieli sanaleke chifukwa cha kusavomereza. Mphwayi za ena sizinampange iye kukhala wamphwayi. Kaya anthu anamvetsera kapena ayi, iye anamverabe Mulungu nakwaniritsa ntchito yake.
18. Kodi ndi mafunso otani amene mungadzifunse?
18 Gulu lowoneka ndi maso la Yehova tsopano likukulitsa chilengezo chakuti onse awope Mulungu ndi kumpatsa ulemerero. Kodi mumapirira pamene mwasulizidwa kaamba ka kutenga kaimidwe kolimba ka kupereka umboni wa Ufumu, kaamba ka kukhala wa makhalidwe abwino m’njira yanu ya moyo? Kodi mumaima nji mutakhala chandamali cha kutsendereza chifukwa cha kusavomereza mwazi, kusalambira zizindikiro zautundu, kusakondwerera matchuti akudziko?—Mateyu 5:11, 12; 1 Petro 4:4, 5.
19. Ponena za chitsogozo, kodi tidzachitanji ngati tikuyendera limodzi ndi gareta lakumwamba la Yehova?
19 Njirayi njosapepuka, koma omwe amapirira mpaka mapeto adzapulumutsidwa. (Mateyu 24:13) Ndi thandizo la Yehova, sitidzalola anthu akudziko kutichititsa kufanana nawo ndipo motero kupatuka panjira ya gareta lakumwamba la Yehova. (Ezekieli 2:8; Aroma 12:21) Ngati tiyendera limodzi ndi gulu laungelo longa gareta, tidzagwirizana mwamsanga ndi chitsogozo ndi malangizo olandiridwa kupyolera m’gulu lowoneka ndi maso la Mulungu. Yehova amapereka zimene timazifunikira poyang’anizana ndi kuwukiridwa kwa chikhulupiriro chathu, kusungabe kugwirira kwathu Mawu amoyo, ndi kusunga maso athu olunjikitsidwa pa zenizeni zauzimu zomwe zimalunjikitsidwa pa Wokwera Wachifumu wa gareta lakumwamba.
Osonkhezeredwa Kuyendera Limodzi
20. Kodi ndizinthu zina ziti zolembedwa ndi Ezekieli zimene ziyenera kutisonkhezera kuyendera limodzi?
20 Masomphenya a Ezekieli ayenera kutisonkhezera kuyendera limodzi. Iye sanalengeze kokha ziweruzo za Mulungu pa Israyeli komanso analemba maulosi a kubwezeretsedwa. Ezekieli anasonya kwa Uyo amene akakhala ndi kuyenera kwalamulo kwa kulamulira pampando wachifumu wa Yehova m’nthaŵi yoikika. (Ezekieli 21:27) Mtumiki Wachifumu ameneyo, “Davide,” akasonkhanitsanso anthu a Mulungu ndikuwaŵeta. (Ezekieli 34:23, 24) Ngakhale kuti akawukiridwa ndi Gogi wa Magogi, Mulungu akawapulumutsa, ndipo adani Ake akakakamizidwa ‘kudziŵa Yehova’ kufikira atapita kuchiwonongeko. (Ezekieli 38:8-12; 39:4, 7) Pambuyo pake atumiki a Mulungu akasangalala ndi moyo wosatha m’dongosolo la kulambira kowona kophatikizapo kachisi wauzimu. Madzi amoyo oyenda kuchokera kuchihema akakhala magwero odyetsa ndi kuchiritsa, ndipo dziko lacholowa likaperekedwa monga dalitso lawo.—Ezekieli 40:2; 47:9, 12, 21.
21. Kodi nchifukwa ninji thayo la Mboni za Yehova zamakono nlalikulu kuposa la Ezekieli?
21 Ha, Ezekieli ayenera kukhala anachititsidwa chidwi chotani nanga kulemba maulosiwa! Komabe, thayo la Mboni zamakono za Yehova nlalikulu. Tikukhala ndi moyo mnthaŵi imene ena a maulosiwa akukwaniritsidwa. Kwenikweni, tiri okhalamo ndi phande mokangalika m’kukwaniritsidwa kwinakwake. M’njira imene timakhalira ndi moyo, kodi ife munthu mwini payekha timasonyeza chikhutiro chathu kuti Yesu tsopano akulamulira monga Uyo wokhala ndi kuyenerera kwalamulo? Kodi takhutiritsidwa mwaumwini kuti Yehova posachedwapa adzadziyeretsa mwini ndikupulumutsira m’dziko latsopano anthu amene amayendera limodzi ndi gulu lake? (2 Petro 3:13) Chikhutiro choterocho, chitagwirizana ndi ntchito zachikhulupiriro, chimasonyeza kuti tikuyenderadi limodzi ndi gareta lakumwamba la Yehova.
Pitirizanibe Kuyendera Limodzi
22. Kodi chingachitidwe nchiyani kuti tipeŵe kucheutsidwa kotero kuti tisungebe kapenyedwe kabwino kauzimu?
22 ‘Titagwira khasu,’ sitiyenera kucheuka mokhumbira chirichonse chimene dziko likupereka. (Luka 9:62; 17:32; Tito 2:11-13) Chotero tiyeni tithetse chikhumbo chirichonse cha kusonkhanitsa chuma padziko lapansi, ndipo tiyeni tisunge diso lathu kukhala lakumodzi, lolunjikitsidwa pa Ufumu. (Mateyu 6:19-22, 33) Kupeputsa miyoyo yathu, kuchotsa zolemera zonse zakudziko kutathekera, kudzatithandiza kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova. (Ahebri 12:1-3) Kucheutsidwa kungapuwalitse kuwona kwathu gareta lakumwambalo ndi Wokwera wake. Koma ndithandizo lake, tingasunge kapenyedwe kabwino kauzimu, monga mmene anachitira Ezekieli.
23. Kodi Mboni zokhulupirika zifunikira kuŵachitiranji atsopano?
23 Mbali ya thayo lathu monga Mboni za Yehova limaphatikizapo kuthandiza atsopano ambiri kuyendera limodzi ndi gareta lakumwamba la Mulungu. Mu 1990 pafupifupi 10,000,000 anapezeka ku Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu. Pamene kuli kwakuti anthu ambiri ameneŵa angakhale akupezeka pa misonkhano ingapo Yachikristu, afunikira kuzindikira kufunika kwa kupita patsogolo limodzi ndi gulu lowoneka ndi maso la Yehova. Monga Mboni zokhulupirika, tingawathandize ndi mzimu umene timasonyeza ndi chilimbikitso chimene timapereka.
24. Kodi tiyenera kuchitanji m’nthaŵi zotsirizira zino?
24 Zino ndi nthaŵi zotsirizira. Ndi maso achikhulupiriro, taliwona gareta lakumwamba likuima pamaso pathu. Wokwera Gareta wachifumu wapatsa gulu lake lowoneka ndi maso ntchito ya kulalikira kwa amitundu kotero kuti, pomalizira pake, akadziŵe amene ali Yehova. (Ezekieli 39:7) Ugwiritsireni ntchito kwambiri mwaŵi waukulu koposawu wa kugawana m’kutukula ufumu wa Mulungu ndi kuliyeretsa dzina lake loyera mwa kuyendera limodzi ndi gareta lakumwamba la Yehova.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Ezekieli anakhazikitsa chitsanzo chotani molingana ndi ntchito yake?
◻ Kodi kuyendera limodzi ndi gulu la Mulungu kumatanthauzanji?
◻ Kodi Ezekieli anawalingalira motani mawu a Yehova?
◻ Kodi tingachitsatire motani chitsanzo cha Ezekieli pochita ndi mphwayi?
◻ Kodi nchiyani chimene chiyenera kusonkhezera atumiki a Yehova kuyendera limodzi ndi gareta lake lakumwamba?
[Zithunzi patsamba 15]
Kodi chikufunikira nchiyani kuti tiyendere limodzi ndi gareta lakumwamba la Yehova?
[Chithunzi patsamba 16]
Ezekieli anayamikira mwaŵi wake wopatsidwa ndi Mulungu. Kodi mumatero?