Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr17 September tsamba 2
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya September 2017

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya September 2017
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2017)
  • Timitu
  • SEPTEMBER 4-10
  • SEPTEMBER 11-17
  • SEPTEMBER 18-24
  • SEPTEMBER 25–OCTOBER 1
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2017)
mwbr17 September tsamba 2

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya September 2017

SEPTEMBER 4-10

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 42–45

it-2 1082 ¶2

Kachisi

Masomphenya a Ezekieli okhudza kachisi. Patadutsa zaka 14 kuchokera pamene Yerusalemu ndi kachisi wa Solomo anawonongedwa mu 593 B.C.E., Ezekieli yemwe anali wansembe komanso mneneri, anaona masomphenya a kachisi wamkulu wa Yehova. (Ezek. 40:1, 2) Ezekieli anauzidwa kuti akafotokozere “nyumba ya Isiraeli” zonse zomwe anaona pofuna kuchititsa manyazi Ayuda omwe anali ku ukapolo, kuwathandiza kuti alape komanso kuti uthengawo ulimbikitse Ayuda okhulupirika ku ukapoloko. (Ezek. 40:4; 43:10, 11) Masomphenyawo anafotokoza za mmene kachisiyo analili kukula kwake. Kachisiyu anamuyeza pogwiritsa ntchito “bango” (lalitali ndi mamita 3.11) komanso “mkono” (wautali ndi masentimita 51.8). (Ezek. 40:5, mawu a m’munsi) Miyezoyi inachititsa anthu ena kukhulupirira kuti kachisi wa m’masomphenya a Ezekieli ndi chitsanzo cha mmene kachisi wa Zerubabele anamangidwira. Komabe palibe umboni weniweni wosonyeza kuti zimenezi anthuwa ananena ndi zoona.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 467 ¶4

Dzina

Aisiraeli analephera kutsatira mfundo zolungama za Mulungu ndipo izi zinachititsa kuti dzina la Mulunguyo lidetsedwe. (Ezek. 43:8; Amosi 2:7) Chifukwa choti iwo anachita zinthu zosakhulupirika, Mulungu anawalanga ndipo anthu amitundu ina anayamba kunyoza dzina la Yehova. (Yerekezerani ndi Sal. 74:10, 18; Yes. 52:5.) Popeza anthuwo sankadziwa kuti Yehova ndi amene akulanga anthu akewo, iwo ankangoona ngati Yehova akulephera kuwateteza. Yehova anabwezeretsa Aisiraeli omwe anali ku ukapolo kudziko lawo n’cholinga choti anthu a mitundu ina asiye kunyoza dzina lake.—Ezek. 36:22-24.

it-2 140

Chilungamo

Yehova amafuna kuti wina aliyense amene akufuna kukhala naye pa ubwenzi azidziwa mfundo zake zolungama ndiponso kumazigwiritsa ntchito. (Yes. 1:17, 18; 10:1, 2; Yer. 7:5-7; 21:12; 22:3, 4; Ezek. 45:9, 10; Amosi 5:15; Mika 3:9-12; 6:8; Zek. 7:9-12)

SEPTEMBER 11-17

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 46-48

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 1001

Mwana wa Munthu

M’malemba Achiheberi, mawuwa amapezeka maulendo ambiri m’buku la Ezekieli. Yehova anatchula mneneriyu kuti “mwana wa munthu” maulendo oposa 90. (Ezek. 2:1, 3, 6, 8) Yehova anagwiritsa ntchito mawu amenewa pofuna kusonyeza kuti mneneri wakeyu anali munthu chabe, ndipo zimenezi zikusonyezanso kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa mneneriyu ndi Mulungu Wam’mwambamwamba amene ankam’patsa uthengawo. Yehova anagwiritsanso ntchito mawu omwewa potchula mneneri Danieli pa Danieli 8:17.

SEPTEMBER 18-24

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DANIELI 1–3

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 382

Mesake

Pali zifukwa zitatu zimene zinawachititsa kuona kuti zakudya zabwino za mfumu zinali zodetsedwa; (1) Ababulo ankadya nyama zomwe Chilamulo cha Mose chinanena kuti ndi zodetsedwa (2) sakanatha kudziwa ngati nyamayo inali yozinga kapena yongopotola; (3) nthawi zambiri mitundu yachikunja inkayamba ndi kupereka nsembe nyama kwa milungu yawo ndipo kudya nyama yoteroyo kunali mbali ya kulambira kwawo.—Dan. 1:8; yerekezerani ndi 1 Akor. 10:18-20, 28.

SEPTEMBER 25–OCTOBER 1

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DANIELI 4-6

Kufufuza Mfundo Zothandiza

w88 10/1 30 ¶3-5

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Munthu wina wachiheberi dzina lake Danieli atakaonekera pamaso pa mfumu, mfumuyo inalonjeza kuti idzamuveka zovala zofiirira ndi mkanda wagolide m’khosi, komanso kumuika kuti akhale wolamulira wachitatu mu ufumu wake. Koma mneneriyo anayankha mwaulemu kuti: “Sungani mphatso zanuzo ndipo mphoto zanuzo mupatse ena. Komabe, ndikuwerengerani zolembedwazi ndipo ndikuuzani kumasulira kwake.”—Danieli 5:17.

Danieli sankafuna kuti alandire chiphuphu kapena malipiro chifukwa cha ntchito imene anagwira yomasulira mawu omwe analembedwa pakhoma. Mfumuyo inkafunika kungosunga mphatsozo kapena kuzipereka kwa munthu wina. Danieli sanamasulire mawuwo pofuna kuti apeze phindu koma chifukwa choti Yehova yemwe ndi Mulungu woona, anali atamuuza kuti achite zimenezo, popeza anali atatsala pang’ono kuwononga Babulo.

Pa Danieli 5:29 pamasonyeza kuti Danieli atawerenga komanso kumasulira mawuwo monga mmene analonjezera, mfumu inanena kuti Danieli apatsidwebe malipirowo. Ndipotu Danieli sanavale yekha zovalazo ndiponso mkanda wagolidewo koma Mfumu Belisazara inachita kulamula kuti amuveke. Choncho zimene zinachitikazi sizikutsutsana ndi zomwe timawerenga pa Danieli 5:17, pomwe mneneriyu ananena kuti salandira chilichonse chifukwa choti wamasulira mawuwo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena