Nyimbo 143
Kuwala M’dziko Lamdima
M’dzikoli mulitu mdima,
Anthu sakumvera.
Koma taona kuwala,
Ngati m’bandakucha.
(KOLASI)
Uthenga wa M’lungu,
Wawala ngati dzuwa
M’dziko lamdimali.
Ukupatsa anthu
Onse chiyembekezo
Mdima watha.
Tidzutse omwe agona,
Poti nthawi yatha.
Ndipo tiwalimbikitse,
Tiwapempherere.
(KOLASI)
Uthenga wa M’lungu,
Wawala ngati dzuwa
M’dziko lamdimali.
Ukupatsa anthu
Onse chiyembekezo
Mdima watha.
(Onaninso Yoh. 3:19; 8:12; Aroma 13:11, 12; 1 Pet. 2:9.)