Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Muzitsatira Lamulo la Kukoma Mtima Polankhula
    Nsanja ya Olonda—2010 | August 15
    • 18, 19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kutsatira lamulo la kukoma mtima pochita zinthu ndi Akhristu anzathu?

      18 Nthawi zonse tiyenera kusonyeza chikondi kwa atumiki a Yehova anzathu. Sitiyenera kusiya kutsatira lamulo la kukoma mtima ngakhale pamene zinthu zavuta. Yehova sanasangalale pamene kukoma mtima kwa ana a Isiraeli kunakhala “ngati mame akuphwa mamawa.” (Hos. 6:4, 6) Koma Yehova amasangalala ngati anthu akusonyeza kukoma mtima nthawi zonse. Taonani mmene amadalitsira anthu amene amasonyeza kukoma mtima.

  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Nthawi?
    Nsanja ya Olonda—2010 | August 15
    • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Nthawi?

      KUSUNGA nthawi kapena kuchita zinthu pa nthawi yake, n’kovuta. Zinthu zina zimene zimachititsa kuti tisasunge nthawi ndi kuyenda mitunda italiitali, kuchuluka kwa magalimoto pamsewu ndiponso kupanikizika ndi zochita. Komabe, kusunga nthawi n’kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, anthu amaona kuti munthu amene amasunga nthawi kuntchito ndi wodalirika ndiponso wakhama. Koma munthu amene amachedwa kuntchito amasokoneza anzake ndiponso amasokoneza ntchito yonse. Mwana wasukulu akachedwa, saphunzira nawo zinthu zina ndipo izi zingachititse kuti asadzakhoze mayeso. Munthu akapita kuchipatala mochedwa, salandira thandizo loyenerera.

      M’madera ena anthu saona kuti kusunga nthawi n’kofunika. M’madera oterewa, anthu amakhala ndi chizolowezi chochedwa. Ngati kudera lanu kuli chizolowezi chimenechi muyenera kuyesetsa kuti muzichita zinthu pa nthawi yake. Kumvetsa ubwino wosunga nthawi kungatithandize kuti tizichita zinthu pa nthawi yake. Koma n’chifukwa chiyani tiyenera kusunga nthawi? Kodi tingatani kuti tizisunga nthawi? Nanga tingapindule bwanji chifukwa chosunga nthawi?

      Yehova Ndi Mulungu Wosunga Nthawi

      Chifukwa chachikulu chimene tiyenera kusungira nthawi ndi chakuti timafuna kutsanzira Mulungu amene timalambira. (Aef. 5:1) Yehova amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Iye sachedwa. Amachita zinthu ndiponso kukwaniritsa zolinga zake pa nthawi

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena