Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuphunzitsa Choonadi
    Utumiki Komanso Moyo Wathu—2016 | August
    • MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

      Kuphunzitsa Choonadi

      Kuyambira m’mwezi wa September, Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu izidzakhala ndi chitsanzo cha mmene tingalalikirire cha mutu wakuti, “Kuphunzitsa Choonadi.” Cholinga cha chitsanzochi ndi kutithandiza kuti tizifotokoza mfundo inayake ya m’Baibulo pogwiritsa ntchito funso komanso lemba.

      Tikaona kuti munthu ali ndi chidwi, tikhoza kumupatsa buku kapena kumuonetsa vidiyo ya pa jw.org. Tiyeni tiziyesetsa kubwerera mwachangu kwa anthu onse amene akufuna kudziwa zambiri kuti tikakambirane nawo funso limene tinawasiyira. Chitsanzo chilichonse komanso nkhani za ophunzira zizichokera m’mfundo zachidule za m’buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa. Choncho tikhozanso kuona m’bukuli kuti tidziwe mafunso ena owonjezera komanso Malemba ena oti tidzagwiritse ntchito ulendo wotsatira. M’bukuli tikhozanso kupeza Malemba oti tidzagwiritse ntchito tikamadzaphunzira ndi munthu pogwiritsa ntchito Baibulo lokha.

      Pali njira imodzi yokha yopita ku moyo wosatha. (Mat. 7:13, 14) Choncho tikamalalikira anthu a zipembedzo zosiyanasiyana komanso ochokera kosiyanasiyana, tiyenera kumafotokoza mfundo za m’Baibulo m’njira yoti ziwafike pamtima kuti ayambe kuyenda panjira imeneyi. (1 Tim. 2:4) Tikayesetsa kuzolowera kumalalikira anthu pogwiritsa ntchito chitsanzochi, tidzakhala aluso kwambiri ndipo tidzakhala aphunzitsi ‘ophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.’ Zimenezi zidzachititsa kuti tizisangalala kwambiri ndipo tidzathandiza anthu ochuluka kudziwa mfundo zolondola zomwe zimapezeka m’Baibulo.—2 Tim. 2:15.

  • Tidzagwira Ntchito Yapadera Yogawira Nsanja ya Olonda mu September
    Utumiki Komanso Moyo Wathu—2016 | August
    • MOYO WATHU WACHIKHRISTU

      Tidzagwira Ntchito Yapadera Yogawira Nsanja ya Olonda mu September

      Nsanja ya Olonda Na. 5 2016 | Kodi ndi Ndani Angatithandize Tikakhala Pamavuto?

      Anthu padzikoli akukumana ndi mavuto ambiri ndipo akufunika kuthandizidwa. (Mlal. 4:1) M’mwezi wonse wa September chaka chino, tidzagwira ntchito yapadera yogawira magazini ya Nsanja ya Olonda. Magaziniyi ili ndi nkhani zomwe zingalimbikitse anthu pa mavuto amene akukumana nawo. Tiyeni tidzayesetse kugawira anthu ambiri magazini imeneyi. Popeza tikufuna kudzalankhula ndi anthu pamaso ndi pamaso kuti tiwalimbikitse, tisadzasiye magaziniwa pakhomo lomwe sitinapeze anthu.

      ZIMENE TINGANENE

      Munganene kuti, “Tonse timakumana ndi mavuto ndipo timafunika kulimbikitsidwa. Koma kodi ndi ndani amene angatithandize tikakhala pamavuto? [Werengeni 2 Akorinto 1:3, 4.] Magaziniyi ikufotokoza mmene Mulungu amatithandizira tikamakumana ndi mavuto.”

      Ngati munthuyo akusonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri, m’patseni magaziniyo ndipo kenako, . . .

      MUONETSENI VIDIYO YAKUTI N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPHUNZIRA BAIBULO?

      Kenako m’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo.

      MUFUNSENI FUNSO LIMENE MUDZAKAMBIRANE PA ULENDO WOTSATIRA

      Mwachitsanzo mungamufunse kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena