Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kr mutu 12 tsamba 118-131
  • Gulu Limene Likutumikira “Mulungu Wamtendere”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gulu Limene Likutumikira “Mulungu Wamtendere”
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Ndidzaika Mtendere Kuti Ukhale Ngati Wokuyang’anira”
  • Zimene Khristu Akuchita Potsogolera Mpingo
  • “Mukhale Zitsanzo Kwa Gulu la Nkhosa”
  • Zimene Akulu Amachita Poweta Nkhosa za Mulungu Masiku Ano
  • Kusintha Kwathandiza Kuti Anthu a Mulungu Akhale Ogwirizana
  • Oyang’anira Amene Amaweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Mverani Atsogoleri
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Abusa, Tsanzirani Abusa Aakulu
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Mpingo wa Chikhristu Umayendetsedwa bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
kr mutu 12 tsamba 118-131

MUTU 12

Gulu Limene Likutumikira “Mulungu Wamtendere”

CHOLINGA CHA MUTUWU

Yehova wakhala akukonza gulu loti lizimutumikira

1, 2. N’chiyani chinasintha pamagazini ya Zion’s Watch Tower ya January 1895, ndipo kodi abale ena ananena chiyani chifukwa cha kusinthaku?

WOPHUNZIRA Baibulo wina wakhama, dzina lake John A. Bohnet, anasangalala kwambiri ndi zimene anaona pamagazini ya Zion’s Watch Tower ya January 1895. Pachikuto cha magaziniyi panali chithunzi cha nsanja yomwe imathandiza anthu oyenda panyanja ndipo m’munsi mwake munali mafunde amphamvu. M’mbali mwa nsanjayo munali mdima ndipo kuwala kochokera pamwamba pa nsanjayo kunkaonekera bwinobwino. Chilengezo chonena za kaonekedwe katsopanoko chimene chinali m’magaziniyi chinali ndi mutu wakuti “Mmene Magazini Yathu Izionekera.”

2 Atasangalala ndi mmene magaziniyi inkaonekera, M’bale Bohnet analembera kalata M’bale Russell. Iye analemba kuti: “Ndasangalala kuona kuti NSANJA imene ili pa magaziniyi ikuoneka bwino kwambiri.” Pofotokoza za mmene chikuto cha magaziniyi chinkaonekera, wophunzira Baibulo wina wokhulupirika dzina lake John H. Brown, analemba kuti: “N’zochititsa chidwi kwambiri kuona kuti mafunde amphamvu akuomba nsanja yomwe ili pamaziko olimba.” Kusintha kumeneku kunali chiyambi chabe chifukwa m’mwezi wa November abale anaonanso kusintha kwina kwakukulu.

3, 4. Kodi Nsanja ya Olonda ya November 15, 1895 inafotokoza vuto liti lomwe linalipo, ndipo magaziniyi inalengeza chiyani komwe kunali kusintha kwakukulu?

3 Nkhani ina imene inatuluka m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya November 15, 1895, inafotokoza za vuto lomwe linali m’gulu la Yehova. Ophunzira Baibulo ankakumana ndi mavuto omwe anali ngati mafunde ndipo ankasokoneza mtendere pakati pawo. Pa nthawiyi abale ankakangana kuti ndi ndani amene ayenera kutsogolera mumpingo. Pofuna kuthandiza abale kudziwa zimene ankayenera kuchita kuti athetse kusagwirizana kumeneku komwe kunkayambitsa mzimu wampikisano, nkhaniyo inayerekeza gulu la Yehova ndi ngalawa. Nkhaniyo inanena mosapita m’mbali kuti abale amene ankatsogolera gulu analephera kukonzekeretsa gululi, lomwe linali ngati ngalawa, kuti lithe kulimbana ndi mavuto omwe anali ngati mafunde. Kodi vuto limeneli likanathetsedwa bwanji?

4 Nkhaniyo inanena kuti woyendetsa ngalawa amaonetsetsa kuti watenga zipangizo zopulumutsira anthu pangozi ndipo anthu ogwira ntchito m’ngalawayo akudziwa zoyenera kuchita ngati mafunde amphamvu atayamba. Mofanana ndi zimenezi, amene ankatsogolera gulu anafunika kuonetsetsa kuti mipingo yonse ndi yokonzeka kulimbana ndi mavuto amene angabwere. Kuti zimenezi zitheke, m’nkhaniyo analengeza za kusintha kwakukulu. Ananena kuti kungoyambira nthawi imeneyo, “mumpingo uliwonse muyenera kusankhidwa akulu” oti “‘akhale oyang’anira’ gulu la nkhosa.”​—Mac. 20:28.

5. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti dongosolo loti mumpingo muzikhala akulu linali la pa nthawi yake? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

5 Kusintha kumeneku kunali kwa pa nthawi yake ndipo inali njira imodzi yothandizira mipingo kuti ikhale yolimba. Kunathandiza abale athu kuti apirire mavuto amene anabwera chifukwa cha nkhondo yoyamba yapadziko lonse. M’zaka zotsatira, zinthu zinanso zinasintha m’gulu ndipo zinathandiza anthu a Mulungu kutumikira Yehova m’njira yoyenera. Kodi ndi ulosi uti wa m’Baibulo womwe unanena za kusintha kumeneku? Kodi inuyo mwaona zinthu ziti zikusintha m’gululi? Nanga kusintha kumeneku kwakuthandizani bwanji?

“Ndidzaika Mtendere Kuti Ukhale Ngati Wokuyang’anira”

6, 7. (a) Fotokozani zimene lemba la Yesaya 60:17 limatanthauza. (b) Kodi mawu akuti “wokuyang’anira” komanso “wokupatsa ntchito” akusonyeza chiyani?

6 Monga taonera m’Mutu 9, Yehova analosera kudzera mwa Yesaya kuti adzadalitsa anthu ake powonjezera chiwerengero chawo. (Yes. 60:22) Koma Yehova analonjeza kuti adzachitanso zinthu zina zambiri chifukwa ulosiwu umanena kuti: “M’malo mwa mkuwa, ndidzabweretsa golide. M’malo mwa chitsulo, ndidzabweretsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweretsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweretsa chitsulo. Ndidzaika mtendere kuti ukhale ngati wokuyang’anira, ndi chilungamo kuti chikhale ngati wokupatsa ntchito,” (Yes. 60:17) Kodi ulosi umenewu umatanthauza chiyani? Nanga ukukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

Zinthu zimene zikulowa m’malozo ndi zabwino kwambiri kuposa zoyambazo

7 Ulosi wa Yesaya unanena kuti zinthu zina zidzalowedwa m’malo ndi zinthu zina. Onani kuti zinthu zimene zikulowa m’malozo ndi zabwino kwambiri kuposa zoyambazo. Mwachitsanzo, ulosiwu ukunena kuti golide akulowa m’malo mwa mkuwa ndipo kumeneku ndi kusintha kwabwino kwambiri. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ananeneratu kuti gulu la atumiki ake lizidzasintha pang’onopang’ono ndipo kusinthako kudzachititsa kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino kwambiri. Kodi ulosiwu unkanena kuti n’chiyani chidzasinthe? Ponena kuti “wokuyang’anira” komanso “wokupatsa ntchito,” Yehova anasonyeza kuti padzakhala kusintha pa kayendetsedwe ka gulu komanso mmene ankasamalira anthu ake.

8. (a) Kodi ndani amene akuchititsa kuti zinthu zimene zikutchulidwa m’buku la Yesaya zisinthe? (b) Kodi kusintha kumeneku kwatithandiza bwanji? (Onaninso bokosi lakuti, “Anathandizidwa Chifukwa Anali Wodzichepetsa.”)

8 Kodi ndani amene akanachititsa kuti zinthu ziziyenda bwino m’gululi? Yehova ananena kuti: “Ndidzabweretsa golide, . . . ndidzabweretsa siliva” komanso “ndidzaika mtendere.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova, osati munthu wina aliyense, ndi amene wakhala akuchititsa kuti zinthu ziziyenda bwino mumpingo. Ndipo kungoyambira pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu, Yehova wakhala akugwiritsa ntchito Mwana wakeyu kuti asinthe kayendetsedwe ka zinthu mumpingo. Kodi kusintha kumeneku kwatithandiza bwanji? Lemba lija limanenanso kuti kusintha kumeneku kudzabweretsa “mtendere” komanso “chilungamo.” Tikamalola kuti Mulungu azititsogolera n’kumayendera limodzi ndi gulu zinthu zikasintha, timakhala ndi mtendere ndipo kukonda chilungamo kumatichititsa kutumikira Yehova, yemwe mtumwi Paulo anamufotokoza kuti ndi “Mulungu wamtendere.”​—Afil. 4:9.

9. N’chiyani chimathandiza kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo komanso kuti pakhale mgwirizano mumpingo ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Ponena za Yehova, Paulo analembanso kuti: “Mulungu si Mulungu wachisokonezo, koma wamtendere.” (1 Akor. 14:33) Onani kuti Paulo sanasiyanitse chisokonezo ndi kuchita zinthu mwadongosolo, koma anasiyanitsa chisokonezo ndi mtendere. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Taganizirani izi: Kuchita zinthu mwadongosolo pakokha sikubweretsa mtendere. Mwachitsanzo, gulu la asilikali likhoza kupita kunkhondo likuyenda mwadongosolo. Koma cholinga chawo poyenda mwadongosolo ndi kukamenya nkhondo, osati kubweretsa mtendere. Choncho, ifeyo monga Akhristu, tiyenera kukumbukira mfundo yofunika iyi: Ngati gulu la anthu likuchita zinthu mwadongosolo koma cholinga chawo sikubweretsa mtendere, ngakhale patapita nthawi yaitali bwanji lidzalephera. Koma mosiyana ndi zimenezi, mtendere wa Mulungu umachititsa kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo komanso kuti gulu lathu likhalepobe. Ndife osangalala kwambiri kudziwa kuti “Mulungu amene amapatsa mtendere” ndi amene akutsogolera komanso kuyenga gulu lathu. (Aroma 15:33) Mtendere umene Mulungu amapereka umachititsa kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo komanso kuti tizisangalala ndi kuyamikira mgwirizano womwe ulipo m’mipingo yathu padziko lonse.​—Sal. 29:11.

10. (a) M’zaka zoyambirira, kodi ndi zinthu ziti zimene zinasintha m’gulu lathu? (Onani bokosi lakuti, “Mmene Zinthu Zasinthira pa Kayendetsedwe ka Mpingo.”) (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

10 Bokosi lakuti, “Mmene Zinthu Zasinthira pa Kayendetsedwe ka Mpingo,” likufotokoza zinthu zina zimene zinasintha m’gulu lathu m’zaka zoyambirira. Koma kodi Yehova wagwiritsa ntchito Mfumu kusintha zinthu ziti posachedwapa, zomwe tingaziyerekezere kuti ndi mkuwa womwe walowedwa m’malo ndi golide? Kodi kusintha pa nkhani ya kayendetsedwe ka mpingo kwathandiza bwanji kuti mipingo ikhale mwamtendere komanso yogwirizana padziko lonse? Kodi kusintha kumeneku kukukuthandizani bwanji inuyo kutumikira “Mulungu wamtendere”?

Zimene Khristu Akuchita Potsogolera Mpingo

11. (a) Ndi zinthu ziti zimene zinasintha chifukwa chomvetsa bwino nkhani zina za m’Baibulo? (b) Kodi abale a m’bungwe lolamulira anali okonzeka kuchita chiyani?

11 Kuyambira m’chaka cha 1964 mpaka mu 1971, Bungwe Lolamulira linatsogolera ntchito yaikulu yofufuza nkhani zina za m’Baibulo imene abale anagwira. Nkhani ina imene anafufuza ndi yokhudza mmene mpingo wachikhristu unkayendetsera zinthu m’nthawi ya atumwi.a Pa kafukufukuyu anapeza kuti, m’nthawi ya atumwi mipingo inkatsogoleredwa ndi bungwe la akulu osati ndi mkulu m’modzi. (Werengani Afilipi 1:1; 1 Timoteyo 4:14.) Atamvetsa mfundo imeneyi, abale a m’bungwe lolamulira anazindikira kuti Yesu, yemwe ndi Mfumu yawo, ankawatsogolera kuti asinthe zinthu pa kayendetsedwe ka zinthu m’gulu la anthu a Mulungu. Abale a m’bungwe lolamulirawa anali okonzeka kutsatira malangizo a Mfumu. Nthawi yomweyo anasintha zinthu kuti atsatire zimene Baibulo limanena posankha akulu mumpingo. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zinasintha chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970?

ANATHANDIZIDWA CHIFUKWA ANALI WODZICHEPETSA

MU Nsanja ya Olonda yachinenero cha Chifinishi ya April 1, 1916, munatuluka kalata imene M’bale Russell analemba. Kalatayi inkapita kwa abale ena a ku Scandinavia, ndipo mmodzi mwa abalewa anali M’bale Kaarlo Harteva. M’bale Russell analemba kuti: “Tikukulimbikitsani nonsenu, abale athu okondedwa m’chikhulupiriro, kuti mubwerere m’choonadi ndiponso kuti mupitirize ntchito imene tiyenera kugwira.” Koma kodi n’chifukwa chiyani M’bale Russell anachita kuwachonderera chonchi abalewa?

Kaarlo Harteva

M’bale Kaarlo Harteva

M’bale Harteva, yemwe anabadwa mu 1882, anali mmodzi mwa anthu oyamba kukhala Ophunzira Baibulo ku Finland. Anabatizidwa mu April 1910 ndipo m’chaka cha 1912, M’bale Russell anavomereza kuti M’bale Harteva azisindikiza Nsanja ya Olonda m’chinenero cha Chifinishi. Zinthu zinkayenda bwino mpaka pa nthawi imene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayamba. Mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1914, M’bale Harteva analemba kuti: “Chifukwa cha mavuto a zachuma, . . . tikukayikira ngati chaka chino Nsanja ya Olonda izikhala ndi masamba onse ndiponso ngati izisindikizidwa monga mwa nthawi zonse.” Komabe, mu 1915, M’bale Harteva ndi abale ena anayambitsa bungwe losindikiza mabuku n’cholinga choti azipeza ndalama. Bungwelo linkadziwika ndi dzina lakuti Ararat ndipo linkasindikiza magazini omwe ankadziwikanso ndi dzina lakuti Ararat.

Chifukwa chakuti M’bale Harteva anayamba kuthera nthawi yambiri akuyang’anira bungweli komanso ntchito yofalitsa magazini ya Ararat, m’bale wina analowa m’malo mwake kuti aziyang’anira ntchito yofalitsa Nsanja ya Olonda m’Chifinishi. M’magazini ya Ararat munkakhala nkhani za m’Baibulo komanso nkhani zina monga za mankhwala achilengedwe ndiponso za chinenero chimene chinali chitangoyamba kumene cha Esperanto. Pasanapite nthawi yaitali, abale anayamba kusokonekera chifukwa cha mmene magazini yatsopanoyi inkafotokozera mfundo za m’Baibulo. Chifukwa chodera nkhawa moyo wawo wauzimu, M’bale Russell anachonderera M’bale Harteva ndi abale ena aja kuti ‘abwerere m’choonadi.’

Kodi M’bale Harteva anatani atalandira kalata ya M’bale Russell? Anasindikiza kalatayi m’magazini ya Ararat pamodzi ndi kalata imene analemba poyankha kalatayo. M’bale Harteva anapepesa chifukwa cha zimene anachitazi ndipo ananena kuti: “Ndiyesetsa kuchita zonse zimene ndingathe kuti ndikonze zimene ndalakwitsa.” Pasanapite nthawi yaitali, M’bale Harteva anapepesanso m’magazini yomaliza ya Ararat chifukwa chosokoneza abale. Iye ananena kuti: “Ndidzayesetsa kukhala wosamala kuti ndizitsatira mfundo iliyonse yokhudza choonadi.” Mosiyana ndi akulu ena omwe anali osadzichepetsa, M’bale Harteva anathandizidwa chifukwa anali wodzichepetsa.

Kenako, M’bale Harteva anayambiranso kuyang’anira ntchito yofalitsa Nsanja ya Olonda m’Chifinishi komanso anayamba kuyang’anira ofesi ya nthambi. Anapitiriza kusamalira maudindo amenewa mpaka mu 1950. Anakhala wokhulupirika kwa Yehova komanso anapitiriza kutsatira choonadi mpaka pamene anamaliza utumiki wake wa padziko lapansi mu 1957. Kunena zoona, anthu amene amadzichepetsa n’kulola kuthandizidwa ndi Yesu, yemwe ndi Mfumu, amayengedwa komanso kudalitsidwa kwambiri ndi Yehova.

12. (a) Kodi n’chiyani chinasintha m’bungwe lolamulira? (b) Fotokozani mmene Bungwe Lolamulira limayendetsera zinthu. (Onani bokosi lakuti, “Mmene Bungwe Lolamulira Limayendetsera Zinthu Zaufumu,” patsamba 130.)

12 Kusintha koyamba kunakhudza bungwe lolamulira lenilenilo. Pa nthawi imeneyo, abale amene anali m’bungwe lolamulira analipo okwana 7 ndipo analinso madailekitala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Koma mu 1971, chiwerengero cha abale a m’bungwe lolamulira chinawonjezeka kuchoka pa 7 kufika 11, ndipo anasiya kudziwika monga madailekitala. Abale a m’bungwe lolamulirawa anayamba kudziona kuti ndi ofanana ndi wina aliyense ndipo chaka chilichonse anayamba kusintha tcheyamani wa bungweli. Ankasinthana udindowu potsatira chilembo choyamba cha dzina la munthu aliyense.

13. (a) Kodi mpingo unkayendetsedwa bwanji kuyambira mu 1932 mpaka mu 1972? (b) Kodi Bungwe Lolamulira linachita chiyani mu 1972?

13 Kusintha kwina kunakhudza mpingo uliwonse. Kuyambira m’chaka cha 1932 mpaka 1972, mpingo uliwonse unali ndi m’bale m’modzi amene ankauyang’anira. M’bale amene ankatsogolera mpingo ankadziwika kuti wotsogolera utumiki ndipo zimenezi zinasintha pofika mu 1936. Dzina la m’baleyu linasintha n’kukhala mtumiki wa gulu, kenako linasintha n’kukhala mtumiki wa mpingo. Patapita nthawi linasinthanso n’kukhala woyang’anira mpingo. Abalewa ankachita khama kwambiri posamalira nkhosa mwauzimu. Nthawi zambiri woyang’anira mpingo ankapanga zosankha zokhudza mpingo wonse popanda kufunsa aliyense. Koma m’chaka cha 1972, Bungwe Lolamulira linasintha zinthu zomwe zinakhudza kwambiri kayendetsedwe ka gulu. Kodi kusintha kumeneku kunali kotani?

14. (a) Kodi ndi kusintha kotani komwe kunayamba kugwira ntchito pa October 1, 1972? (b) Kodi wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu amatsatira bwanji mfundo ya pa Afilipi 2:3?

14 M’malo mokhala ndi m’bale m’modzi monga woyang’anira mpingo, abale ena amene akwaniritsa zimene Malemba amanena anayamba kuikidwa pa udindo monga akulu. Akulu amenewa ankapanga bungwe la akulu loti liziyang’anira mpingo. Kusintha kumeneku kunayamba kugwira ntchito pa October 1, 1972. Masiku ano, wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu sadziona kuti ndi wofunikira kwambiri kuposa akulu onse, koma amadziona kuti ndi “wamng’ono.” (Luka 9:48) Kukhala ndi abale oterewa ndi dalitso lalikulu m’mipingo ya padziko lonse.​—Afil. 2:3.

N’zoonekeratu kuti Mfumu yathu yomwe ndi yanzeru yasankha abusa pa nthawi yake oti aziyang’anira otsatira ake

15. (a) Kodi timapindula bwanji chifukwa chokhala ndi bungwe la akulu m’mipingo? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Mfumu yathu inachita zinthu mwanzeru?

15 Abale amene ali m’bungwe la akulu amagawana zochita pampingo ndipo zimenezi zathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino kwambiri. Taonani mfundo zitatu izi: Choyamba komanso chofunika kwambiri n’chakuti kusintha kumeneku kumachititsa mkulu aliyense, kaya ali ndi udindo waukulu bwanji, kukumbukira kuti Yesu Khristu ndiye Mutu wa mpingo. (Aef. 5:23) Chachiwiri, lemba la Miyambo 11:14 limati: “Pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.” Akulu akamakambirana nkhani zimene zimakhudza moyo wauzimu wa abale mumpingo komanso akamamvetsera pamene m’bale wina akufotokoza maganizo ake, amasankha zinthu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (Miy. 27:17) Yehova amadalitsa zimene abalewa amasankha ndipo zinthu zimayenda bwino. Chachitatu, chifukwa chokhala ndi abale omwe akuyenera kutumikira monga akulu, gulu lakwanitsa kuyang’anira komanso kutsogolera mipingo imene yakhala ikuwonjezeka. (Yes. 60:3-5) Tangoganizani, m’chaka cha 1971, chiwerengero cha mipingo padziko lonse chinali 27,000 koma pofika mu 2013 chinapitirira 113,000. Pamenepa n’zoonekeratu kuti Mfumu yathu yomwe ndi yanzeru yasankha abusa pa nthawi yake oti aziyang’anira otsatira ake.​—Mika 5:5.

MMENE ZINTHU ZASINTHIRA PA KAYENDETSEDWE KA MPINGO

  • 1881​—Pofuna kuthandiza Ophunzira Baibulo amene ankakhala m’dera limodzi kuti azidziwana, M’bale Russell anapempha anthu amene ankasonkhana nthawi zonse kuti adziwitse ofesi ya Watch Tower malo amene amasonkhana.

  • 1895​—Mipingo yonse inalangizidwa kuti isankhe abale amene angatumikire ngati akulu.

  • 1919​—Mpingo uliwonse unayamba kukhala ndi wotsogolera utumiki yemwe ankasankhidwa ndi ofesi ya nthambi ngati wakwaniritsa zimene Malemba amanena. Zina mwa ntchito zimene ankagwira zinali kukonza mmene abale ndi alongo azigwirira ntchito yolalikira komanso kulimbikitsa anthu kuti azigwira nawo ntchitoyi. Akulu ena sanagwirizane ndi mfundo yoti mu mpingo muzikhala woyang’anira utumiki.

  • 1932​—Mpingo unasiya zomasankha akulu chaka chilichonse. M’malo mwake, mpingo unayamba kusankha komiti ya utumiki. M’komitiyi munkakhala abale amene ankagwira ntchito yolalikira mwakhama komanso amene ankachita zinthu zogwirizana ndi dzina latsopano lakuti Mboni za Yehova. Mmodzi mwa abale osankhidwa ndi mpingowo ankaikidwa ndi Sosaite kapena ofesi ya nthambi kuti akhale woyang’anira utumiki.

  • 1937​—Abale amene anali m’gulu la khamu lalikulu anayamba kutumikira m’komiti ya utumiki pamodzi ndi abale odzozedwa.

  • 1938​—Mipingo inayamba kutsatira chigamulo chomwe chinaperekedwa chakuti abale amene akwaniritsa zimene Malemba amanena akhoza kuikidwa kuti azitumikira monga atumiki a mpingo. Zimenezi zinachititsa kuti mipingo isiye kuvota ikamasankha atumiki a mpingo.

Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mmene ankayendetsera mipingo yakale, werengani buku lakuti, Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 204-235.

Abale ndi alongo akusankha akulu mu zaka za m’ma 1920

“Tikafuna kusankha akulu, tinkavota pokweza dzanja lamanja. Kenako m’bale wina ankayenda n’kumawerenga anthu amene avotera m’baleyo.”​—Anatero Mlongo Rose Swingle, wa ku Chicago, Illinois, ku America.

“Mukhale Zitsanzo Kwa Gulu la Nkhosa”

16. (a) Kodi akulu ali ndi udindo wotani? (b) Kodi Ophunzira Baibulo ankaona bwanji langizo la Yesu lakuti: “Weta ana a nkhosa”?

16 Ngakhale m’nthawi ya Ophunzira Baibulo, akulu ankadziwa kuti ali ndi udindo wothandiza okhulupirira anzawo kuti akhale okhulupirika kwa Mulungu. (Werengani Agalatiya 6:10.) Mu 1908, nkhani ina yomwe inatuluka mu Nsanja ya Olonda inafotokoza mawu amene Yesu ananena akuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:15-17) Nkhaniyo inauza akulu kuti: “M’pofunika kuti tizikumbukira mfundo imene Mbuye wathu anatilamula yokhudza nkhosa zake ndipo izikhala pa malo oyamba mumtima mwathu. Zimenezi zingatithandize kuti tiziona kuti tili ndi udindo waukulu wodyetsa komanso kusamalira otsatira a Ambuye.” Mu 1925, nkhani ina imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda inakumbutsa akulu udindo umene ali nawo. Nkhaniyi inati: “Mpingo ndi wa Mulungu, . . .  ndipo adzaimba mlandu aliyense chifukwa cha mmene akuchitira zinthu potumikira abale.”

17. Kodi akulu athandizidwa bwanji kuti ayenerere kukhala abusa?

17 Kodi gulu la Yehova lathandiza bwanji akulu kuti awonjezere luso lawo pa ntchito yoweta, zomwe zili ngati kuchoka pa ‘chitsulo kufika pa siliva’? Gululi lakhala likuphunzitsa akulu. Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yoyamba yomwe inakonzedwa n’cholinga chofuna kuthandiza akulu inachitika mu 1959. Mutu wa nkhani ina imene anaphunzira unali wakuti, “Kuthandiza Munthu Aliyense Payekha.” Abalewa analimbikitsidwa kuti “akonze ndandanda yowathandiza kuti aziyendera ofalitsa kunyumba zawo.” Nkhaniyi inafotokoza njira zosiyanasiyana zimene abusa angatsatire kuti azilimbikitsa abale omwe akuwayenderawo. M’chaka cha 1966, anasinthanso zinthu zina ndi zina mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Mu sukuluyi anakambirana nkhani ya mutu wakuti “Kufunika Kochita Ubusa.” Kodi mfundo yaikulu mu nkhaniyi inali yotani? Inali yakuti amene ali ndi udindo wotsogolera mumpingo “ayenera kuthandizana posamalira nkhosa za Mulungu. Pamene akuchita zimenezi ayenera kusamaliranso mabanja awo komanso kugwira nawo ntchito yolalikira.” Pa zaka zaposachedwapa akulu ambiri alowa mu sukulu imeneyi. Kodi chachitika n’chiyani chifukwa cha maphunziro amene gulu la Yehova lakhala likupereka kwa akulu? Masiku ano, abale ambirimbiri oyenerera akutumikira m’mipingo yachikhristu ngati abusa auzimu.

Abale ali m’kalasi ya Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Philippines, mu 1966

Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yomwe inachitika ku Philippines, m’chaka cha 1966

18. (a) Kodi akulu anapatsidwa udindo waukulu uti? (b) N’chifukwa chiyani Yehova komanso Yesu amakonda kwambiri akulu amene amagwira ntchito mwakhama?

18 Yehova, kudzera mwa Mfumu yathu Yesu, ndi amene anakonza zoti mumpingo muzikhala akulu kuti azigwira ntchito yofunika kwambiri. Ntchito yake ndi yotsogolera nkhosa za Mulungu mu nthawi yovuta komanso yamapeto ino. (Aef. 4:11, 12; 2 Tim. 3:1) Yehova komanso Yesu amakonda kwambiri akulu amene amagwira ntchito mwakhama chifukwa abale amenewa amamvera langizo la m’Malemba lakuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, . . . mofunitsitsa . . . [komanso] ndi mtima wonse . . . . Mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:2, 3) Pali njira zambiri zimene abusa achikhristu amasonyezera kuti ndi zitsanzo zabwino kwa nkhosa, koma m’nkhani ino tikambirana njira ziwiri zokha. Njira zimenezi zimathandiza kuti akulu alimbikitse mtendere komanso kuti abale ndi alongo azikhala osangalala mumpingo.

“TINADABWA KWAMBIRI”

BANJA lina lomwe linkatumikira monga amishonale linatumizidwa kumpingo wina wa ku Asia womwe unakhala zaka zambiri usakukula. Banjali litafika kumpingowo linaona kuti abale ankakondana koma sankatsatira malangizo a kayendetsedwe ka mpingo. Poyamba banjali linayesetsa kugwirizana ndi wofalitsa aliyense wa mumpingomo. Kenako m’baleyo anayamba kuthandiza pang’onopang’ono pa kayendetsedwe ka mpingo kuti kakhale kogwirizana ndi mmene anthu a Yehova amayendetsera mipingo yawo padziko lonse. Kodi zinthu zinayenda bwanji? Patangopita zaka ziwiri, chiwerengero cha anthu osonkhana chinawonjezeka kawiri, anthu atsopano anayamba kugwira nawo ntchito yolalikira ndipo anthu oposa 20 anabatizidwa. Amishonalewa ananena kuti: “Tinadabwa kwambiri. Yehova anatidalitsa kuposa mmene tinkaganizira. Taona kuti kutsatira malangizo amene gulu la Mulungu limapereka kumachititsa kuti abale ndi alongo azikhala osangalala mumpingo.”

Zimene Akulu Amachita Poweta Nkhosa za Mulungu Masiku Ano

19. Fotokozani mmene mumamvera mukalowa muutumiki ndi mkulu.

19 Njira yoyamba ndi yakuti, akulu amagwira ntchito yolalikira ndi ofalitsa mumpingo. Pofotokoza za Yesu, Luka yemwe analemba Uthenga Wabwino wodziwika ndi dzina lake, anati: “Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi.” (Luka 8:1) Potengera chitsanzo cha Yesu yemwe ankalalikira ndi atumwi ake, masiku ano akulu achitsanzo chabwino amagwira ntchito yolalikira pamodzi ndi okhulupirira anzawo. Amadziwa kuti kuchita zimenezi kumathandiza kuti mpingo ukhale wolimba. Kodi abale ndi alongo amawaona bwanji akulu oterewa? Mlongo wina wazaka za m’ma 80, dzina lake Jeannine, anati: “Ndikamalalikira ndi mkulu ndimakhala ndi mwayi wocheza naye komanso womudziwa bwino.” M’bale wina wazaka za m’ma 30, dzina lake Steven, ananena kuti: “Ndikamalalikira khomo ndi khomo ndi mkulu ndimaona kuti akufuna kundithandiza. Kuthandizidwa mwa njira imeneyi kumandichititsa kukhala wosangalala.”

M’busa wapeza nkhosa imene inasochera usiku kukugwa mvula

Akulu amayesetsa kufufuza anthu amene asiya kusonkhana ndi mpingo ngati mmene m’busa amafufuzira nkhosa yotayika

20, 21. Kodi akulu angatsanzire bwanji m’busa wa m’fanizo la Yesu? Perekani chitsanzo. (Onaninso bokosi lakuti, “Kuwayendera Mlungu Uliwonse Kunathandiza Kwambiri.”)

20 Njira yachiwiri ndi yakuti gulu la Yehova lakhala likuphunzitsa akulu kuti azithandiza anthu amene anasiya kusonkhana. (Aheb. 12:12) Koma n’chifukwa chiyani akulu ayenera kuthandiza anthu amene anafooka mwauzimu ndipo ayenera kuchita chiyani pothandiza anthu amenewa? Fanizo limene Yesu anafotokoza lonena za m’busa ndi nkhosa yotayika lingatithandize kuyankha mafunso amenewa. (Werengani Luka 15:4-7.) M’busa wa m’fanizoli ataona kuti nkhosa imodzi yasowa, anayamba kuifufuza ngati kuti anali ndi nkhosa imodzi yokhayo. Kodi masiku ano akulu achikhristu amatsanzira bwanji m’busa ameneyu? M’busa wa m’fanizoli ankaona kuti nkhosa yotayikayo ndi yofunika kwambiri. Mofanana ndi m’busa ameneyu, akulu amaona kuti munthu amene wasiya kusonkhana ndi anthu a Mulungu ndi wofunikabe kwambiri. Akuluwa amaona kuti munthu amene wafooka mwauzimu ali ngati nkhosa yotayika ndipo akamathandiza munthu ameneyu saona ngati akungotaya nthawi. Komanso m’busa uja ndi amene ananyamuka “n’kupita kukafunafuna [nkhosa] imodzi yotayikayo kufikira ataipeza.” Masiku anonso akulu amachita zofanana ndi zimenezi pofufuza ndiponso kuthandiza anthu amene afooka mwauzimu.

21 Kodi m’busa wa m’fanizoli amachita chiyani akapeza nkhosa yotayikayo? “Amainyamula paphewa pake” n’kupita nayo kumene kuli nkhosa zina. Mofanana ndi zimenezi, mawu olimbikitsa amene mkulu amanena amakhala ngati akunyamula komanso kuthandiza munthu amene wafookayo kuti ayambirenso kusonkhana ndi mpingo. Zimenezi n’zimene zinachitikira m’bale wina wa ku Africa, dzina lake Victor, yemwe anasiya kusonkhana ndi mpingo. Iye anati: “Pa zaka 8 zonse zimene sindinkasonkhana, akulu ankayesetsa kundithandiza.” Kodi n’chiyani kwenikweni chimene chinamulimbikitsa? Iye ananena kuti: “Tsiku lina, John, yemwe ndi mkulu amene ndinachita naye Sukulu ya Utumiki Waupainiya, anabwera kudzacheza nane ndipo anandionetsa zithunzi zina zimene anajambula nthawi imene tinkachita sukuluyi. Nditaona zithunzi zimenezi ndinakumbukira zinthu zambiri zosangalatsa moti ndinkafuna kuyambiranso kukhala wosangalala ngati mmene ndinkakhalira pamene ndinkatumikira Yehova.” Patangopita nthawi yochepa Victor anayambiranso kusonkhana. Panopa akutumikiranso ngati mpainiya. Pamenepatu n’zoonekera kuti akulu achikhristu amene amasamalira bwino nkhosa amatithandiza kuti tizikhala osangalala.​—2 Akor. 1:24.b

Abale awiri akukambirana mosangalala ndi m’bale wachikulire yemwe anasiya kusonkhana

KUWAYENDERA MLUNGU ULIWONSE KUNATHANDIZA KWAMBIRI

POFUNA kuthandiza anthu omwe anasiya kusonkhana ndi mpingo amene ali ngati nkhosa zotayika, akulu a mumpingo wina ku America anakonza njira yothandizira anthuwa. Akuluwa anazindikira kuti anthu pafupifupi 30 amene anasiya kutumikira Yehova zaka zambiri zapitazo ankakhalabe m’gawo la mpingo wawo. Ndipo pa nthawiyi ambiri mwa anthu amenewa anali achikulire.

Mmodzi wa akuluwa, dzina lake Alfredo, analemba mayina a anthu amene anasiya kusonkhanawa ndipo anayamba kuwayendera. Iye ananena kuti: “Lachisanu lililonse m’mawa ndinkayendera munthu amene anasiya kusonkhana.” M’bale Alfredo akamacheza ndi munthuyo ankayesetsa kucheza naye momasuka ndipo ankamuuza kuti amamudera nkhawa kuchokera pansi pa mtima. Ankauzanso munthuyo kuti mpingo sunaiwale ntchito zabwino zimene anagwira zokhudza Ufumu wa Yehova. Kenako M’bale Alfredo ananena kuti: “Nditauza m’bale wina wachikulire amene anasiya kusonkhana za maola amene anathera polalikira ndiponso magazini amene anagawira mwezi womaliza umene anapereka lipoti la utumiki mu 1976, misozi inalengeza m’maso mwake.” M’bale Alfredo amawerengeranso anthu amene akuwayendera lemba la Luka 15:4-7, 10 kenako amawafunsa kuti: “Kodi chimachitika n’chiyani nkhosa ikabwerera mumpingo? Kodi sizolimbikitsa kudziwa kuti Yehova, Yesu komanso angelo amasangalala?”

M’bale Alfredo wakhala akuyendera anthu amene anasiya kusonkhanawa kwa zaka ziwiri tsopano. Kodi pali chilichonse chomwe chachitika chifukwa cha khama lakeli? Iye wakwanitsa kuthandiza abale awiri kuti ayambirenso kusonkhana ndi mpingo ndipo amasonkhana Lamlungu lililonse. M’bale Alfredo ananena kuti: “Abalewa atalowa mu Nyumba ya Ufumu ndinagwetsa misozi yachisangalalo. Ngakhale kuti panopa anthuwa anayamba kusonkhana, ndimawayenderabe Lachisanu lililonse chifukwa amandiuza kuti amandiyembekezera. Inenso ndimasangalala kuwayendera mlungu uliwonse.”

Kusintha Kwathandiza Kuti Anthu a Mulungu Akhale Ogwirizana

22. Kodi chilungamo komanso mtendere zimathandiza bwanji kuti anthu akhale ogwirizana mumpingo wachikhristu? (Onaninso bokosi lakuti, “Tinadabwa Kwambiri.”)

22 Monga taonera m’mutu umenewu, Yehova ananeneratu kuti zinthu zizidzasintha pang’onopang’ono pakati pa anthu ake ndipo padzakhala chilungamo komanso anthuwa azidzakhala mwamtendere. (Yes. 60:17) Makhalidwe awiri onsewa amachititsa kuti abale ndi alongo akhale ogwirizana mumpingo. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Pa nkhani ya chilungamo, Malemba amati: “Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.” (Deut. 6:4) Mfundo zimene mipingo yachikhristu imatsatira sizisiyana chifukwa chakuti mipingoyi ili m’mayiko osiyanasiyana. Mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa sizisintha “m’mipingo yonse ya oyerawo.” (1 Akor. 14:33) Choncho, mpingo umayenda bwino ngati ukutsatira mfundo za Mulungu. Pa nkhani ya mtendere, Mfumu yathu imafuna kuti tizikhala mwamtendere komanso kuti tikhale “anthu amene amabweretsa mtendere.” (Mat. 5:9) Ndipotu timayesetsa ‘kutsatira zinthu zobweretsa mtendere.’ Tikasemphana maganizo ndi okhulupirira anzathu timachita zonse zomwe tingathe kuti tithetse kusemphana maganizoko. (Aroma 14:19) Tikamatsatira mfundo imeneyi timalimbikitsa mtendere ndiponso timakhala ogwirizana m’mipingo yathu.​—Yes. 60:18.

23. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova ndi osangalala masiku ano?

23 Mu November 1895, Nsanja ya Olonda itangolengeza kumene kuti mumpingo muzikhala akulu, abale ena amene anali pa udindowu anasonyeza mmene anamvera ndi kusintha kumeneku. Iwo anasonyeza kuti ankafuna komanso ankapemphera kuti kusintha kumeneku kuthandize anthu a Mulungu kuti “ayambe kukhala ogwirizana m’chikhulupiriro.” Tikaona zimene zakhala zikuchitika m’zaka za m’mbuyomu, ndife osangalala chifukwa cha kusintha komwe kwakhala kukuchitika pang’onopang’ono pa nkhani yokhudza oyang’anira mumpingo. Yehova ndi amene wachititsa kusintha kumeneku kudzera mwa Mfumu yathu ndipo zimenezi zatilimbikitsa ndiponso kutithandiza kukhala ogwirizana polambira Mulungu. (Sal. 99:4) Chifukwa cha zimenezi, masiku ano anthu a Yehova padziko lonse lapansi akusangalala pamene akuyenda “mumzimu umodzi,” kutsatira “mapazi amodzimodzi,” ndiponso kutumikira “Mulungu wamtendere” “mogwirizana.”​—2 Akor. 12:18; werengani Zefaniya 3:9.

a Anatulutsa zotsatira za kafukufuku ameneyu m’buku lakuti Aid to Bible Understanding.

b Onani nkhani ya mutu wakuti “Akulu Achikhristu Ndi Antchito Anzathu Otipatsa Chimwemwe,” mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2013 tsamba 27-31.

Kodi Inuyo Mumaona Kuti Ufumu wa Mulungu Ndi Weniweni?

  • Kodi Ufumu wasintha zinthu ziti pa kayendetsedwe ka gulu?

  • Kodi kusintha pa nkhani ya woyang’anira mpingo kwakuthandizani bwanji kutumikira “Mulungu wamtendere”?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene akulu ananena kapena kuchita zimene zinakuchititsani kukhala wosangalala?

  • Kodi inuyo mungachite chiyani pofuna kuthandiza kuti mumpingo mukhale mtendere komanso kuti anthu akhale ogwirizana?

Abale a mu komiti ya Bungwe Lolamulira akukambirana ndi abale owathandiza

MMENE BUNGWE LOLAMULILA LIMAYENDETSERA ZINTHU ZA UFUMU

BUNGWE Lolamulira la Mboni za Yehova limapangidwa ndi abale odzozedwa omwe ndi atumiki a Yehova Mulungu. Monga gulu, abalewa amapanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Abalewa ali ndi udindo wopereka chakudya chauzimu, kupereka malangizo ndiponso kulimbikitsa wofalitsa aliyense padziko lonse kuti azigwira nawo ntchito yolalikira.​—Mat. 24:14, 45-47.

Abale a m’Bungwe Lolamulira amakhala ndi msonkhano wawo mlungu uliwonse ndipo nthawi zambiri msonkhanowu umachitika Lachitatu. Zimenezi zimathandiza abalewa kuti azitumikira mogwirizana. (Sal. 133:1) Abale amene ali m’Bungwe Lolamulirawa amatumikiranso m’makomiti osiyanasiyana. Komiti iliyonse ili ndi ntchito imene imayang’anira pa nkhani zokhudza Ufumu. Tiyeni tikambirane mwachidule ntchito za komiti iliyonse.

  • Abale akukambirana mmene angathandizire anthu amene akumana ndi mavuto enaake

    Komiti ya Ogwirizanitsa

    Abale amene ali m’komiti imeneyi amayang’anira nkhani zamilandu komanso zokhudza kufalitsa nkhani ngati pakufunika kuthandiza anthu kumvetsa molondola zimene timakhulupirira. Amathandizanso pakachitika masoka a chilengedwe, ngati abale athu akuzunzidwa ndiponso pakachitika zinthu zina zadzidzidzi zokhudza abale athu padziko lonse.

  • Anthu a pa Beteli akugwira ntchito zosiyanasiyana

    Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli

    Komitiyi inapatsidwa udindo wothandiza ndiponso kusamalira moyo wauzimu komanso wakuthupi wa abale ndi alongo amene akutumikira m’mabanja a Beteli padziko lonse. Imayang’aniranso ntchito yosankha komanso kuitana abale ndi alongo oti akatumikire ku Beteli. Imayankhanso mafunso alionse okhudza utumiki wa pa Beteli.

  • M’bale akugwira ntchito yosindikiza ndi kutumiza mabuku othandiza pophunzira Baibulo

    Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku

    Komitiyi imayang’anira ntchito yosindikiza komanso kutumiza mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo padziko lonse. Imayang’aniranso nyumba zosindikizira mabuku, zinthu zina zimene zimagwiritsidwa ntchito ndi mabungwe a Mboni za Yehova komanso ntchito ya zomangamanga kuphatikizapo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Amaonetsetsanso kuti ndalama zimene zaperekedwa kuti zithandize pa ntchito ya Ufumu zikugwiritsidwa ntchito moyenera.

  • M’bale akuwerenga ndiponso kufufuza zinthu

    Komiti ya Utumiki

    Abale amene ali m’komiti imeneyi amayang’anira chilichonse chokhudza ntchito yolalikira, nkhani zokhudza mipingo, ofalitsa, apainiya, akulu, oyang’anira oyendayenda ndiponso amishonale. Amayang’aniranso ntchito za Makomiti Olankhulana ndi Achipatala ndiponso zina zambiri.

  • M’bale akukamba nkhani

    Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa

    Komitiyi imapereka malangizo pa misonkhano yadera, yapadera, yachigawo ndiponso yampingo. Imayang’aniranso Sukulu ya Giliyadi, Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, Sukulu ya Utumiki Waupainiya, komanso masukulu ena. Komitiyi imayang’aniranso ntchito yokonza Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, zinthu zomvetsera komanso mavidiyo.

  • Mabuku ndi zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo webusaiti ya jw.org

    Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku

    Abale a m’komitiyi amayang’anira ntchito yokonza chakudya chauzimu chimene chimaperekedwa kwa okhulupirira anzawo komanso anthu omwe si Mboni. Chakudya chauzimu chimenechi chimafalitsidwa kudzera m’mabuku, m’ma CD, ma DVD komanso pa intaneti. Abalewa amayang’aniranso webusaiti ya gulu lathu komanso ntchito yomasulira imene ikuchitika padziko lonse. Amayankhanso mafunso okhudza malemba ena komanso mfundo zina zimene zafotokozedwa m’mabuku athu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena