NYIMBO 137
Akazi Achikhristu Okhulupirika
Losindikizidwa
1. Sara, Esitere, Rute ndi ena,
Iwo anali akazi abwino.
Anali odzipereka kwa M’lungu.
Timawadziwa ndi mayina awo.
Panali ena sanatchulidwe
Nawonso Yehova ankawakondanso.
2. Akaziwatu amatikumbutsa
Makhalidwe omwe tizisonyeza
Monga ubwino ndi kulimba mtima.
Zitsanzo zawo n’zotilimbikitsa.
Alongo a masiku anonso
Khalani zitsanzo kwa ena tonsefe.
3. Amasiye, achemwali, amayi,
Mumachita khama pogwira ntchito.
Mumagonjera, mumadzichepetsa.
Musaope Mulungu ali nanu
Ndipo iye akulimbitseni.
Mukhulupirike, mudzadalitsidwa.
(Onaninso Afil. 4:3; 1 Tim. 2:9, 10; 1 Pet. 3:4, 5.)