Kumanzere: M’bale akumangidwa chifukwa cholalikira mumzinda wa Eindhoven, ku Netherlands, mu 1945; Kumanja: Kodi kumene mukukhala malamulo amakulolani kulalikira?
GAWO 4
Milandu Imene Ufumu Wawina—Kukhazikitsa Mwalamulo Ntchito ya Uthenga Wabwino
TAYEREKEZERANI kuti pamene mukulalikira khomo ndi khomo mukuona apolisi awiri akukutsatirani. Ndiyeno akukuimitsani ndipo inu ndi mnzanu amene mukuyenda naye mu utumiki mukuima. Apolisiwo akufika pafupi n’kukufunsani kuti: “Kodi ndinu a Mboni za Yehova? Tamva kuti mukusokoneza anthu kwambiri.” Mukuyankha mwaulemu n’kufotokoza kuti mukuuza anthu uthenga wa m’Baibulo. Kodi chichitike n’chiyani?
Zimene zichitike zidalira kwambiri zimene zakhala zikuchitika m’mbuyomu. Kodi boma la dziko lanu limaona bwanji Mboni za Yehova? Kodi m’dziko lanu muli ufulu wachipembedzo? Ngati zili choncho, n’kutheka kuti abale ndi alongo anu auzimu akhala akuyesetsa kwa zaka zambiri “kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.” (Afil. 1:7) Kaya mukukhala kuti, koma kuganizira milandu imene Mboni za Yehova zawina kungalimbitse chikhulupiriro chanu. M’chigawochi tikambirana ina mwa milandu imeneyi. Milandu imene tawina ndi umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni chifukwa sitikanawina milandu yonseyi patokha.