Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya February 2018
FEBRUARY 5-11
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 12-13
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 12:20
nyale yofuka: Kale, nyale zambiri zomwe ankagwiritsa ntchito zinkakhala zoumba ndipo ankaikamo mafuta a maolivi. Nyalezi zinkakhala ndi kachingwe komwe kankayaka chifukwa cha mafutawo. Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “nyale yofuka,” angatanthauze chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima ndipo lawi lake likuzilala kapena lazima. Ulosi wa pa Yesaya 42:3 unkasonyeza kuti Yesu adzakhala wachifundo ndipo sadzazimitsa chiyembekezo cha anthu odzichepetsa komanso oponderezedwa.
FEBRUARY 12-18
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 14-15
“Yesu Amadyetsa Anthu Ambiri Kudzera Mwa Anthu Ochepa”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 14:21
osawerengera akazi ndi ana aang’ono: Mateyu yekha ndi amene anatchula akazi ndi ana aang’ono pofotokoza za chozizwitsachi. N’kutheka kuti anthu onse omwe anadyetsedwa ndi Yesu panthawiyi anali oposa 15,000.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 15:7
Onyenga: Mawuwa (omwe kenako anayambanso kugwiritsidwa ntchito ndi Aroma) anamasuliridwa kuchokera ku mawu achigiriki akuti hy·po·kri·tesʹ ndipo ankawagwiritsira ntchito potchula anthu ochita zisudzo omwe ankavala zigoba zikuluzikulu kuti akamayankhula mawu awo azimveka amphamvu. N’kupita kwa nthawi mawuwa anayamba kugwiritsidwa ntchito ponena za munthu amene ankabisa zolinga kapena umunthu wake komanso kuchita zinthu zachinyengo pofuna kupusitsa ena. Pavesili Yesu anatchula atsogoleri achipembedzo achiyuda kuti ndi “onyenga.”—Mat. 6:5, 16.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 15:26
ana . . . tiagalu: Popeza Chilamulo cha Mose chinkasonyeza kuti agalu ndi odetsedwa, Malemba ambiri amagwiritsa ntchito mawu oti agalu mopeputsa. (Lev. 11:27; Mat. 7:6; Afil. 3:2; Chiv. 22:15) Komabe, mu Uthenga Wabwino wa Maliko (7:27) komanso wa Mateyu, Yesu anagwiritsa ntchito m’phatikiram’mbuyo wochepetsa ponena kuti “tiagalu” zomwe zinachititsa kuti mawuwo amveke ofewerapo. Zikuoneka kuti Yesu ananena mawuwa posonyeza chikondi chimene anthu amitundu ina ankasonyeza agalu awo oweta, omwe ankatha kuwasunga m’nyumba. Yesu anayerekezera Aisiraeli ndi “ana” komanso anthu amitundu ina ndi “tiagalu.” Apa Yesu ankasonyeza kuti omwe anali ofunika kwambiri anali Aisiraeli. Ngati munthu anali ndi ana komanso agalu m’nyumba mwake ndipo wakonza chakudya, omwe anali ofunika kukhala oyambirira kudyetsedwa anali ana.
FEBRUARY 19-25
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 16-17
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 16:18
Iwe ndiwe Petulo, ndipo pathanthwe ili: Mawu achigiriki akuti peʹtros, amatanthauza “mwala.” Pavesili mawuwa anagwiritsidwa ntchito ngati dzina lamwinimwini (Petulo) lomwe ndi dzina limene Yesu anapatsa Simoni. (Yoh. 1:42) Koma mawu ena achigiriki akuti peʹtra amatanthauza “thanthwe” ndipo nthawi zina angatanthauzenso mwala waukulu kwambiri. Mawu amenewa ndi amene amapezekanso pa Mat. 7:24, 25; 27:60; Luka 6:48; 8:6; Aroma 9:33; 1 Akor. 10:4; 1 Pet. 2:8. Zikuoneka kuti Petulo sankaona kuti iyeyo ndiye thanthwe lomwe Yesu adzamangepo mpingo wake chifukwa iye analemba pa 1 Pet. 2:4-8, ponena za Yesu yemwe anasankhidwa ndi Mulungu, kuti ndi “mwala wapakona” womwe aneneri analosera kalekale. Kuwonjezera pamenepa, mtumwi Paulo anatchula Yesu kuti anali “maziko” komanso “thanthwe lauzimu.” (1 Akor. 3:11; 10:4) Choncho, pavesili Yesu anangogwiritsa ntchito mawu mwaluso. Zinali ngati akunena kuti: ‘Iwe amene ndakutchula kuti Petulo, kapena kuti mwala, wazindikira kuti ndine Khristu, kapena kuti ‘thanthwe ili,’ pomwe padzamangidwe mpingo wachikhristu.’
mpingo: Palembali ndi pamene pamapezeka koyamba mawu Achigiriki akuti ek·kle·siʹa. Mawuwa akuchokera ku mawu awiri a Chigiriki akuti ek ndi akuti ka·leʹo, omwe amatanthauza kuti “kuitana.” Mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za gulu la anthu amene aitanidwa kapena kusonkhanitsidwa pamodzi kuti achite zinazake. Pavesili, Yesu ankalosera zimene zidzachitike mpingo wachikhristu ukamadzakhazikitsidwa. Mpingowu unali woti udzapangidwa ndi Akhristu odzozedwa, omwe ali ngati ‘miyala yamoyo yomwe ikumangidwa n’kukhala nyumba yauzimu.’ (1 Pet. 2:4, 5) Mawu achigiriki amenewa anagwiritsidwa ntchito kwambiri m’Baibulo la Septuagint pomasulira mawu achiheberi otanthauza “mpingo” omwe amaimira gulu lonse la anthu a Mulungu. (Deut. 23:3; 31:30) Pa Mac. 7:38, Aisiraeli omwe anatuluka ku Iguputo ankatchulidwa kuti “mpingo.” Mofanana ndi zimenezi, Akhristu omwe ‘anaitanidwa kuchoka mu mdima’ ‘wa m’dzikoli’ amapanga “mpingo wa Mulungu.”—1 Pet. 2:9; Yoh. 15:19; 1 Akor. 1:2.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 16:19
makiyi a ufumu wakumwamba: M’Baibulo, anthu amene anapatsidwa makiyi enaake, kaya enieni kapena ophiphiritsira, ankakhala kuti apatsidwa udindo waukulu kwambiri. (1 Mbiri 9:26, 27; Yes. 22:20-22) Choncho mawu akuti “kiyi” amaimira mphamvu kapena udindo winawake wapadera. Petulo anagwiritsa ntchito “makiyi” omwe anapatsidwa potsegula mwayi woti Ayuda (Mac. 2:22-41) Asamariya (Mac. 8:14-17) ndiponso anthu a mitundu ina (Mac. 10:34-38) alandire mzimu woyera kuti adzalowe mu Ufumu wakumwamba.
FEBRUARY 26–MARCH 4
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 18-19
“Tizipewa Kuchita Zinthu Zimene Zingakhumudwitse Ena”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 18:6
chimwala cha mphero . . . ngati chimene bulu amayendetsa: Kapena “chimwala chachikulu champhero chokokedwa ndi bulu.” Mwala umenewu unkakhala wozungulira ndipo pakati pake, kuchokera mbali ina kupita mbali ina, unkakhala wautali mamita 1.2 mpaka 1.5. Mwalawu unkakhala wolemera kwambiri moti unkafunika kukokedwa ndi bulu.
nwtsty zithunzi ndi mavidiyo
Mwala wamphero
Miyala yamphero inkagwiritsidwa ntchito popera zinthu komanso popanga mafuta a maolivi. Miyala ina inkakhala yaing’ono moti munthu ankatha kuiyendetsa yekha pomwe ina inkakhala yaikulu kwambiri ndipo inkafunika kuyendetsedwa ndi nyama. N’kutheka kuti mwala wamphero umene Afilisiti anakakamiza Samisoni kuti azikoka unali waukulu ngati umenewu. (Ower. 16:21) Miyala yamphero yoyendetsedwa ndi nyama sinkapezeka ku Isiraeli kokha koma inkapezekanso m’madera ambiri omwe ankalamuliridwa ndi ufumu wa Roma.
Mwala Wamphero Wapamwamba ndi Wapansi
Mwala wamphero waukulu ngati umene wasonyezedwawu unkayendetsedwa ndi nyama monga bulu ndipo unkagwiritsidwa ntchito popera zinthu kapena kuphwanya maolivi. Mwala wamphero wapamwamba unkakhala wautali mamita 1.5 pakati pake kuchokera mbali ina kupita mbali ina, ndipo unkayenda pamwamba pamwala wina waukulu.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 18:7
zopunthwitsa: Ena amanena kuti mawu achigiriki akuti skanʹda·lon, omwe amatanthauza ‘chopunthwitsa’ amanena za msampha. Enanso amati kanali kamtengo ka pamsampha komwe ankaikapo nyambo. Mawuwa anayambanso kutanthauza kanthu kalikonse kamene kangachititse munthu kupunthwa kapena kugwa. Mophiphiritsira mawuwa amatanthauza chinthu chilichonse chimene chingapangitse munthu kuyamba kuchita zoipa kapena kuchita tchimo. Pa Mat. 18:8, 9, pali mawu ofanana ndi amenewa akuti skan·da·liʹzo omwe angatanthauze ‘kupunthwitsa,’ “kukhala msampha kapena kuchititsa kuti wina achimwe.”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 18:9
Gehena: Mawuwa anapangidwa kuchokera ku mawu achiheberi akuti geh hin·nom,ʹ omwe amatanthauza “chigwa cha Hinomu,” chimene chinali kum’mwera chakumadzulo kwa mzinda wa Yerusalemu. (Onani sgd gawo 16A, mapu “Yerusalemu komanso Madera Apafupi.”) M’nthawi ya Yesu chigwachi chinali malo owotcherako zinyalala choncho mawu akuti “Gehena” akuimira chiwonongeko chotheratu.
nwtstg Matanthauzo a Mawu Ena
Gehena
Ndi dzina lachigiriki la chigwa cha Hinomu chomwe chinali kum’mwera chakumadzulo kwa mzinda wakale wa Yerusalemu. (Yer. 7:31) Ulosi wina unanena kuti kumalo amenewa kuzidzapezeka mitembo yokhayokha. (Yer. 7:32; 19:6) Palibe umboni womwe umasonyeza kuti anthu kapena zinyama zinkaponyedwa ku Gehena zili zamoyo kuti zikazunzidwe. Choncho malowa sakuimira kwinakwake kosadziwika bwinobwino komwe munthu amakazunzidwa kwamuyaya m’moto. M’malomwake, Yesu ndi ophunzira ake anagwiritsa ntchito mawuwa pofuna kutanthauza “imfa yachiwiri” yomwe ndi kuwonongedwa kotheratu.—Chiv. 20:14; Mat. 5:22; 10:28.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 18:10
amaona nkhope ya Atate wanga: Kapena “kuona Atate wanga.” Ndi angelo okha omwe amatha kufika pamaso pa Mulungu choncho iwowa ndi amene amaona nkhope yake.—Eks. 33:20.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 18:22
nthawi 77: Mawu ake enieni, “70 kuwirikiza maulendo 7.” Mawu amenewa m’chigiriki angatanthauze “70 kuphatikiza 7” (nthawi 77) kapena “70 kuwirikiza maulendo 7” (nthawi 490). Mawu omwewa ndi amene anagwiritsidwa ntchito m’Baibulo la Septuagint pa Gen. 4:24 pomwe anamasulira mawu achiheberi akuti “nthawi 77.” Zimenezi zikusonyeza kuti mawu achigiriki aja akutanthauza “nthawi 77” osati nthawi 490. Mosasamala kanthu kuti kaya anthu angamve zotani, nambala ya 7 ikabwerezedwa imatanthauza “mopanda malire” kapena “mosalekeza.” Yesu pomuuza Petulo kuti ayenera kukhululuka nthawi 77 osati 7 zokha, ankasonyeza kuti otsatira ake sayenera kuika malire pa nkhani yokhululukira ena. Mosiyana ndi zimenezi, buku lina limanena kuti: “Munthu akamulakwira mnzake koyamba, kachiwiri kapena kachitatu angamukhululukire koma akalakwanso kena kuwonjezera pamenepa sangamukhululukire.”—Babylonian Talmud, Yoma 86b.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 19:7
kalata yothetsa ukwati: Chilamulo chinkapereka mwayi kwa munthu amene akufuna kuthetsa ukwati wake kuti aganizire mofatsa nkhaniyi pomuuza kuti alembe kalata yothetsera ukwati komanso kukumana ndi akulu kuti amuthandize maganizo. Cholinga cha Chilamulo chinali kuchepetsa mchitidwe womangothetsa maukwati mwachisawawa komanso chinkateteza akazi kuti asamaponderezedwe. (Deut. 24:1) Koma m’nthawi ya Yesu, atsogoleri achipembedzo anachititsa kuti kuthetsa ukwati kuzikhala kophweka. Katswiri wina wa mbiri yakale dzina lake Josephus, yemwe anali Mfarisi amene anathetsa banja lake, analemba kuti zinali zotheka “kuthetsa ukwati pa chifukwa chilichonse (ndipo zambiri mwa zifukwa zimene amuna ankathetsera ukwatizi, iwonso ankazichita).”
nwtsty zithunzi ndi mavidiyo
Kalata Yothetsa Ukwati
Kalata yothetsera ukwati imeneyi ndi ya m’ma 71 kapena 72 C.E., ndipo inalembedwa m’Chiaramu. Inapezeka chakumpoto m’mbali mwa mtsinje wotchedwa Wadi Murabbaat womwe uli m’chipululu cha Yudeya. Kalatayi imanena kuti m’chaka cha 6, Ayuda atagalukira ulamuliro wa Roma, Yosefe, mwana wa Naqsan, anathetsa ukwati ndi mkazi wake Miriam, mwana wa Yonatani yemwe ankakhala mumzinda wa Masada.