Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
JUNE 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AGALATIYA 4-6
“Nkhani ‘Yophiphiritsira’ Yomwe ndi Yofunika Kwambiri kwa Ife”
it-1 1018 ¶2
Hagara
Mogwirizana ndi nkhani yophiphiritsira imene mtumwi Paulo ananena, Hagara akuimira mtundu wa Isiraeli, womwe unkamvera Yehova potsatira pangano la Chilamulo lomwe linakhazikitsidwa paphiri la Sinai. Panganoli ndi limene linachititsa kuti mtunduwu ukhale ngati “akapolo.” Aisiraeli ankalephera kusunga panganoli chifukwa anali anthu ochimwa. Choncho iwo analibe ufulu ndipo anaweruzidwa monga oyenera kufa popeza anali akapolo. (Yoh. 8:34; Aroma 8:1-3) Hagara akuimira Yerusalemu wa m’nthawi ya Paulo. Yerusalemu yemwe anali likulu la Isiraeli, anakhala mu ukapolo limodzi ndi ana ake. Akhristu odzozedwa ndi ana a ‘Yerusalemu wakumwamba’ yemwe ndi mkazi wophiphiritsira wa Mulungu. Mofanana ndi Sara yemwe anali mfulu, Yerusalemu ameneyu sanakhalepo mu ukapolo. Monga mmene zinakhalira kuti Isimaeli ankazunza Isaki, ana a ‘Yerusalemu wakumwamba’ ankazunzidwa ndi ana a Yerusalemu yemwe ali mu ukapolo ndipo anamasulidwa ndi Mwana yemwe ndi Yesu. Koma Hagara ndi mwana wake anathamangitsidwa, zomwe zikuimira zimene Yehova anachita pokana mtundu wa Isiraeli.—Agalatiya 4:21-31; onaninso Yohane 8:31-40.
JUNE 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AEFESO 1-3
“Zimene Ulamuliro wa Yehova Ukuchita”
it-2 837 ¶4
Chinsinsi Chopatulika
Ufumu wa Mesiya. Paulo anafotokoza zambiri zokhudza chinsinsi chopatulika cha Khristu. Palemba la Aefeso 1:9-11, iye ananena zimene Mulungu anachita poulula “chinsinsi chopatulika” cha chifuniro chake. Iye anati: “Chinsinsicho n’chogwirizana ndi zokomera mwiniwakeyo ndiponso zimene anafuna mumtima mwake, kuti akakhazikitse dongosolo lake, ikadzatha nyengo yonse ya nthawi zoikidwiratu. Dongosolo limenelo ndilo kusonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, zinthu zakumwamba ndi zinthu zapadziko lapansi. Inde, kuzisonkhanitsanso mwa iye. Mogwirizana ndi iyeyo tinaikidwa kukhala odzalandira cholowa, pakuti anatisankhiratu mwa kufuna kwake, iye amene amayendetsa zinthu zonse mogwirizana ndi chifuniro chake.” “Chinsinsi Chopatulika” chimenechi ndi chokhudza boma la Mulungu, lomwe ndi Ufumu wa Mesiya. “Zinthu zakumwamba” zimene Paulo anatchula zikuimira Akhristu omwe adzalamulire limodzi ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. “Zinthu zapadziko lapansi” ndi anthu omwe adzakhale nzika za Ufumuwu padzikoli. Yesu anasonyeza kuti chinsinsi chopatulikacho chinali chokhudza Ufumu pamene anauza ophunzira ake kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira chinsinsi chopatulika cha ufumu wa Mulungu.”—Maliko 4:11.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
“Kuti Mudziwe Chikondi cha Khristu”
21 Mawu achigiriki akuti ‘kudziwa’ amatanthauza kuzindikira kapena kumvetsa zinazake chifukwa cha zomwe munthu wakumana nazo. Tikamakonda ena ngati mmene Yesu ankachitira m’pamene tingamvetse mmene ankamvera. Mwachitsanzo, tingadzipereke kuthandiza ena, kuwasonyeza chifundo powapatsa zimene akufunikira komanso kuwakhululukira kuchokera pansi pa mtima. Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti timadziwa “chikondi cha Khristu chimene chimaposa kudziwa zinthu zonse.” Ndipotu tizikumbukira kuti kutsanzira Khristu n’kumene kungatithandize kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova Mulungu wathu wachikondi, amene Yesu ankamutsanzira.
JUNE 17-23
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AEFESO 4-6
“Valani Zida Zonse Zankhondo Zochokera kwa Mulungu”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 1128 ¶3
Kukhala woyera
Mzimu woyera. Mphamvu imene Yehova amagwiritsa ntchito pofuna kukwaniritsa cholinga chake. Popeza kuti mphamvu imeneyi ndi yoyera komanso yopatulika ndipo ndi Mulungu amene amaigwiritsa ntchito, n’chifukwa chake imatchedwa “mzimu woyera.” (Sal. 51:11; Luka 11:13; Aroma 1:4; Aef. 1:13) Mzimu woyera umathandiza munthu kuchita zinthu zoyera kapena kuti zabwino. Koma munthu akamachita zoipa amapangitsa kuti mzimuwo usagwire bwino ntchito mwa iye ndipo ‘amaumvetsa chisoni’. (Aef. 4:30) Ngakhale kuti mzimu woyera si munthu, umafotokozedwa kuti ‘ungamve chisoni’ chifukwa umaimira khalidwe loyera la Mulungu. Makhalidwe oipa ‘amazimitsa moto wa mzimu.’ (1 Ates. 5:19) Ngati munthu akupitiriza kuchita makhalidwe oipa, ‘amakhumudwitsa’ mzimu woyera ndipo zimenezi zingachititse kuti akhale pa udani ndi Mulungu. (Yes. 63:10) Yesu ananena kuti aliyense amene amamvetsa chisoni kapena kulankhula mawu onyoza mzimu woyera, sadzakhululukidwa m’nthawi ino kapena ikubwerayo.—Mateyu 12:31, 32; Maliko 3:28-30.
it-1 1006 ¶2
Umbombo
Umaonekera ndi Zochita. Munthu waumbombo amaonekera ndi zochita zake komanso zimene amalakalaka. Yakobo analemba kuti, chilakolako chikatenga pakati chimabala tchimo. (Yak. 1:14, 15) Choncho n’zosavuta kuzindikira munthu waumbombo pongoona mmene amachitira zinthu. Mtumwi Paulo ananena kuti munthu waumbombo ndi wopembedza mafano. (Aef. 5:5) Munthu waumbombo amaona zinthu zimene akufuna kukhala zofunika kwambiri kuposa kutumikira Mulungu. Choncho zimene amalakalakazo zimakhala ngati mulungu wake.—Aroma 1:24, 25.
JUNE 24-30
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AFILIPI 1-4
“Musamade Nkhawa ndi Kanthu Kalikonse”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 528 ¶5
Nsembe
Nsembe yachakumwa. Aisiraeli atakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa ankapereka nsembe za zakumwa pamodzi ndi nsembe zina zosiyanasiyana. (Num. 15:2, 5, 8-10) Nsembe yachakumwayi inkakhala vinyo (yemwe anali ‘chakumwa choledzeretsa’) ndipo ankathiridwa paguwa la nsembe. (Num. 28:7, 14; yerekezerani ndi Eks. 30:9; Num. 15:10.) Mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Filipi kuti: “Ngakhale kuti ndikudzipereka ngati nsembe yachakumwa imene ikuthiridwa pansembe ndi pa ntchito yotumikira anthu imene chikhulupiriro chakupatsani, ndine wokondwa.” Palembali Paulo anadziyerekezera ndi nsembe yachakumwa pofuna kusonyeza kuti anali wodzipereka kutumikira Akhristu anzake. (Afil. 2:17) Ndipo atatsala pang’ono kufa, analembera Timoteyo kuti: “Pakuti ine ndayamba kale kukhuthulidwa ngati nsembe yachakumwa, ndipo nthawi yakuti ndimasuke yatsala pang’ono kukwana.”—2 Timoteyo 4:6.