Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr19 July tsamba 1-4
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
  • Timitu
  • JULY 1-7
  • it-2 169 ¶3-5
  • JULY 8-14
  • JULY 15-21
  • Bodza
  • JULY 22-28
  • JULY 29–​AUGUST 4
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2019)
mwbr19 July tsamba 1-4

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

JULY 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AKOLOSE 1-4

“Vulani Umunthu Wakale N’kuvala Umunthu Watsopano”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 169 ¶3-5

Ufumu wa Mulungu

“Ufumu wa Mwana wake wokondedwa.” Patatha masiku 10 kuchokera pamene Yesu anakwera kumwamba, pa Pentekosite mu 33 C.E., ophunzira ake anaona umboni wosonyeza kuti Yesu anali ‘atakwezedwa kudzanja lamanja la Mulungu.’ Pa nthawiyi ndi pamene Yesu anapereka mzimu woyera kwa ophunzira ake. (Mac. 1:8, 9; 2:1-4, 29-33) Kungochokera patsikuli “pangano latsopano” linayamba kugwira ntchito ndipo ophunzirawo anali ngati maziko a “mtundu woyera” wa Isiraeli wauzimu.​—Aheb. 12:22-24; 1 Pet. 2:9, 10; Agal. 6:16.

Khristu anali atakhala kudzanja lamanja la Atate wake ndiponso anakhala Mutu wa mpingo wachikhristu. (Aef. 5:23; Aheb. 1:3; Afil. 2:9-11) Malemba amasonyeza kuti kungochokera pa Pentekosite mu 33 C.E., Yesu anayamba kulamulira ophunzira ake. Pamene mtumwi Paulo ankalembera Akhristu a mpingo wa ku Kolose, ananena kuti Yesu Khristu anali atayamba kale kulamulira monga mfumu. Iye anati: “[Mulungu] anatilanditsa ku ulamuliro wa mdima, n’kutisamutsira mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa.”​—Akol. 1:13; yerekezerani ndi Mac. 17:6, 7.

Ufumu wa Khristu, womwe unakhazikitsidwa pa Pentekosite mu 33 C.E., unali wauzimu ndipo unkalamulira Isiraeli wauzimu, yemwe akuimira Akhristu omwe anadzozedwa ndi mzimu kuti akhale ana a Mulungu. (Yoh. 3:3, 5, 6) Anthu amenewa akalandira mphoto yawo kumwamba, salamuliridwanso ndi ufumuwu, koma amakhala mafumu n’kumalamulira limodzi ndi Khristu.​—Chiv. 5:9, 10.

JULY 8-14

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 ATESALONIKA 1-5

“Pitirizani Kutonthozana ndi Kulimbikitsana”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 863-864

Dama

Munthu amene wachita dama angachotsedwe mumpingo. (1 Akor. 5:9-13; Aheb. 12:15, 16) Mtumwi Paulo ananena kuti Mkhristu amene wachita dama amachimwira thupi lake chifukwa amakhala akugwiritsira ntchito ziwalo zake m’njira yosayenera. Munthuyo amaononga ubwenzi wake ndi Yehova, amadetsa mpingo wa Mulungu komanso amakhala pangozi yotenga matenda oopsa opatsirana pogonana. (1 Akor. 6:18, 19) Munthu amene wachita dama amaphwanyira ufulu abale ndi alongo ake (1 Ates. 4:3-7) (1) pochita zinthu zodetsa komanso zonyansa kwambiri zomwe zimachititsa manyazi mpingo (Aheb. 12:15, 16), (2) amachititsa munthu amene wachita naye damayo kuti asakhale woyera pamaso pa Mulungu ndipo ngati sanalowe m’banja, zimachititsa kuti asadzalowe m’banja ali woyera, (3) amaipitsa mbiri ya banja lake komanso (4) amakhala atalakwira makolo, mkazi kapena mwamuna wake, kapenanso chibwenzi cha munthu amene wachita naye damayo. Iye samakhala akunyalanyaza munthu koma Mulungu amene amapereka chilango kwa anthu amene amaphwanya malamulo ake.​—1 Ates. 4:8.

JULY 15-21

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 ATESALONIKA 1-3

“Wosamvera Malamulo Adzaonekera”

it-1 972-973

Kudzipereka kwa Mulungu

Pali chinsinsi china chomwe ndi chosiyana kwambiri ndi “chinsinsi chopatulika” cha Yehova. Chimenechi ndi “chinsinsi cha kusamvera malamulo.” Nkhani imeneyi inali chinsinsi kwa Akhristu oona m’nthawi ya Paulo chifukwa “wosamvera malamuloyo” anali asanayambe kuonekera monga gulu. Ngakhale pamene anaonekera, anthu sanamuzindikirebe chifukwa ankachita zoipa mosaonekera komanso ankachita zinthu mwachiphamaso ngati kuti akutumikira Mulungu. Zimene ankachitazi zinkasonyeza kuti anali atayamba mpatuko. Paulo ananena kuti: “Chinsinsi cha kusamvera malamulo” chinali chitayamba kale kugwira ntchito pa nthawiyo chifukwa anthu ena mumpingo wachikhristu anasiya kumvera malamulo ndipo pamapeto pake zinapangitsa kuti pakhale gulu lampatuko. Wosamvera malamuloyu anali woti adzachotsedwa ndi Yesu Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake. Akhristu otsogoleredwa ndi Satanawa, anadzikweza “pamwamba pa aliyense wotchedwa ‘mulungu’ kapena chilichonse chopembedzedwa” (m’Chigiriki, seʹba·sma). Choncho mdani wa Mulungu ameneyu yemwe Satana akumugwiritsira ntchito, anali woti azidzapusitsa anthu komanso kudzaonongetsa anthu ambiri omutsatira. ‘Munthu wosamvera malamuloyu’ ndi woopsa kwambiri chifukwa amachita zinthu zoipa mosaonekera ndipo amaoneka ngati akutumikira Mulungu.​—2 Ates. 2:3-12; yerekezerani ndi Mat. 7:15, 21-23.

it-2 245 ¶7

Bodza

Yehova amalola kuti anthu ena “anyengedwe ndipo azikhulupirira bodza,” m’malo mokhulupirira uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu. (2 Ates. 2:9-12) Mfundo imeneyi imaonekera bwino tikaganizira zomwe zinachitikira Mfumu Ahabu ya ku Isiraeli. Aneneri onyenga anatsimikizira Ahabu kuti akapambana pa nkhondo yolimbana ndi anthu a ku Ramoti-giliyadi. Koma Mikaya, yemwe anali mneneri wa Yehova, anamuuza kuti sizikamuthera bwino. Mikaya anaona masomphenya ndipo m’masomphenyawo, Yehova analola kuti mngelo wina akhale “mzimu wabodza” m’kamwa mwa aneneri a Ahabu. Choncho tingati mngeloyu anagwiritsa ntchito mphamvu zake kuchititsa aneneri a Ahabu kulankhula zinthu zabodza. Aneneriwo analankhula zinthu zomwe zinali m’maganizo mwawo komanso zimene Ahabu ankafuna kumva. Ngakhale anachenjezedwa, Ahabu anasankha kumvera zabodzazo ndipo zimenezi zinapangitsa kuti ataye moyo wake.​—1 Maf. 22:1-38; 2 Mbiri 18.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 834 ¶5

Moto

Petulo analemba kuti “kumwamba kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi, azisungira moto.” Tikaganizira bwino nkhaniyi komanso tikaona mfundo za m’mavesi ena, n’zoonekeratu kuti moto umenewu si weniweni, koma ndi chiwonongeko chotheratu. Mofanana ndi zimene zinachitika pa chigumula cha Nowa, madzi a chigumulacho sanawononge dziko komanso kumwamba kwenikweni. Anangowononga anthu osaopa Mulungu. Ndi mmenenso zidzakhalire Yesu Khristu ndi angelo ake akadzaonekera m’moto walawilawi. Iye adzawononga anthu okhawo omwe ndi oipa komanso dziko la Satanali.​—2 Pet. 3:5-7, 10-13; 2 Ates. 1:6-10; yerekezerani ndi Yes. 66:15, 16, 22, 24.

it-1 1206 ¶4

Kuuziridwa

“Mawu Ouziridwa”​—Oona Komanso Abodza. Mawu achigiriki akuti pneuʹma (mzimu) amagwiritsidwa ntchito mu nkhani zina zomwe atumwi analemba. Mwachitsanzo pa 2 Atesalonika 2:2, Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Tesalonika kuti asamatengeke kapena kugwedezeka maganizo ndi “mawu ouziridwa [mawu ake enieni, “mzimu”] onena kuti tsiku la Yehova lafika . . . ngakhale utakhala uthenga wapakamwa, kapena kalata yooneka ngati yachokera kwa ife.” Apa ndi zodziwikiratu kuti Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti pneuʹma (mzimu) ponena za njira yotumizira uthenga ngati mmene zimakhalira ndi “uthenga wapakamwa” kapena “kalata.” Chifukwa cha mfundoyi, buku lina pothirira ndemanga mawu a palembali linanena kuti, “Ndi mawu amenewa, Paulo anasonyeza kuti pali mawu ouziridwa abodza komanso mawu ouziridwa ochokera kwa Mulungu.” (Lange’s Commentary on the Holy Scriptures, tsamba 126. Lomasuliridwa ndi kukonzedwanso ndi P. Schaff, 1976) Buku linanso linanena kuti mawu akuti “kuuziridwa, angatanthauzenso zimene magulu ena achikhristu amanena n’kumanamizira kuti ndi uthenga wochokera kwa Mulungu.” (Vincent’s Word Studies in the New Testament, 1957, Vol. IV, tsamba 63) Choncho ngakhale kuti m’Mabaibulo ena mawu akuti pneuʹma anawamasulira kuti “mzimu,” M’mabaibulo enanso anawamasulira kuti “uthenga wa mzimu” (AT) “kuneneratu” (JB), “kuuziridwa” (D’Ostervald; Segond [Chifulenchi]), “mawu ouziridwa” (NW).

JULY 22-28

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 TIMOTEYO 1-3

“Yesetsani Kuti Mukhale Oyang’anira”

km 9/78 4 ¶7

Amene ‘Akutumikira Bwino’

7 N’zosavuta kumvetsa zimene Paulo ankatanthauza pamene ankanena za amuna amene ‘akutumikira bwino.’ Anthu ena amaganiza kuti mawuwa amatanthauza kukwezedwa pa maudindo a m’tchalitchi. Mosiyana ndi zimenezi, atumiki othandiza omwe ‘amatumikira bwino’ amadalitsidwa kwambiri ndi Yehova komanso Yesu ndipo abale ndi alongo mumpingo amawalemekeza ndiponso kuwathandiza. N’chifukwa chake Baibulo limati iwo amakhala “ndi ufulu waukulu wa kulankhula za chikhulupiriro, mwa Khristu Yesu.” Abalewa, amayamikiridwa chifukwa cha utumiki umene amachita, amakhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso sachita mantha kuuza ena zimene amakhulupirira.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 914-915

Mibadwo ya Makolo

Kumvetsera kapena kukambirana nkhani zimenezi kunali kopanda phindu. N’chifukwa chake Paulo analangiza Timoteyo kuti asamale ndi nkhani zimenezi. Pa nthawiyo, sizinali zofunikanso kumafufuza zokhudza mzere wa makolo chifukwa Mulungu sankaona kuti pali kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu amitundu ina moti onse anawalola kukhala mumpingo wake. (Agal. 3:28) Komanso zinali zitadziwika kale kuti Khristu anabadwa kudzera m’banja la Davide. Kuwonjezera pamenepa, zikuoneka kuti sipanatenge nthawi yaitali kwambiri kuchokera pamene Paulo ananena zimenezi kudzafika pamene Yerusalemu anawonongedwa limodzi ndi mabuku onse a mibadwo ya makolo. Mulungu sanateteze mabuku amenewa kuti asawonongedwe. Paulo sankafunanso kuti Timoteyo komanso Akhristu ena onse azitaya nthawi yawo pofufuza komanso kutsutsana ndi anthu pa nkhani ya mibadwo ya makolo, zomwe sizikanawathandiza chilichonse pa chikhulupiriro chawo. Zimene zinalembedwa m’Baibulo zokhudza mzere umene Khristu anabadwira, zinali zokwanira kutsimikizira kuti Yesu ndi amene anali Mesiya. Kudziwa zimenezi n’kumene kunali kofunika kwambiri kwa Akhristu. Malemba ena omwe amanena za mibadwo ya makolo amasonyeza kuti Baibulo ndi lolondola pa nkhani yonena za mbiri yakale.

JULY 29–​AUGUST 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 TIMOTEYO 4-6

“Kukhala Wodzipereka kwa Mulungu N’kofunika Kuposa Chuma”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 714 ¶1-2

Kuwerenga Pamaso pa Anthu

Mumpingo Wachikhristu. M’nthawi ya atumwi, kuwerenga pagulu kunali kofunika kwambiri chifukwa ndi anthu ochepa okha amene anali ndi mipukutu ya Baibulo. Mtumwi Paulo analimbikitsa abale kuti aziwerenga mokweza makalata ake akakhala pamisonkhano yampingo. Komanso anawauza kuti azisinthana makalatawo ndi mipingo ina kuti abale a mipingoyo nawonso akawerenge. (Akol. 4:16; 1 Ates. 5:27) N’chifukwa chake analimbikitsa Timoteyo kuti ‘apitirize kukhala wodzipereka powerenga pamaso pa anthu, powadandaulira, ndi powaphunzitsa.”​—1 Tim. 4:13.

Munthu amene akuwerenga pamaso pa anthu ayenera kuchita zimenezi momveka bwino. (Hab. 2:2) Popeza munthu akamawerenga pagulu amafunika kuthandiza anthu kuti amve uthengawo, wowerengayo ayenera kumvetsa zimene akuwerengazo komanso kudziwa cholinga cha wolemba nkhaniyo. Ayenera kusamala kuti asawerenge molakwika n’kusokoneza anthu. Malinga ndi Chivumbulutso 1:3, anthu amene amawerenga mokweza ndiponso amene akumva mawu a ulosi n’kumachita zimene amvazo, amakhala osangalala kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena